Mutu 20
Chozizwitsa Chachiŵiri Ali m’Kana
PAMENE Yesu akubwerera kugawo lakwawo pambuyo paulaliki wautali m’Yudeya, sinthaŵi yopuma. Mmalomwake, iye akuyamba uminisitala wokulirapo kwambiri mu Galileya, dziko limene anakuliramo. Koma ophunzira ake, mmalo mwa kukhala naye, akubwerera kwawo kumabanja awo ndi kuntchito zawo zakale.
Kodi ndiuthenga wotani umene Yesu wayamba kulalikira? Uwu: “Ufumu wa Mulungu wayandikira; tembenukani mitima, khulupirirani uthenga wabwino.” Ndipo kulabadira kwake? Agalileyawo akulandira Yesu. Iye akuchitiridwa ulemu ndi onse. Komabe, zimenezi siziri makamaka chifukwa cha uthenga wake koma, mmalo mwake, chifukwa chakuti ambiri a iwo analipo ku Paskha ku Yerusalemu miyezi ingapo yapitayo ndipo anawona zozizwitsa zapadera zimene anachita.
Mwachiwonekere Yesu akuyamba uminisitala wake wa ku Galileya m’Kana. Poyambirirapo, mungakumbukire kuti, pobwerera kuchokera ku Yudeya, anasandutsa madzi kukhala vinyo pa phwando laukwati kumeneko. Pachochitika chachiŵiri chino, mwana wa mkulu wina waboma wa Mfumu Herode Antipa akudwala kwambiri. Pakumva kuti Yesu wabwera kuchokera ku Yudeya kuloŵa m’Kana, mkuluyo akuyenda ulendo kuchoka kwawo ku Kapernao kukapeza Yesu. Atagwidwa ndi chisoni, mwamunayo akupempha kuti: ‘Chonde idzani msanga, mwana wanga asanafe.’
Yesu akuyankha kuti: ‘Bwerera kwanu. Mwana wako wachiritsidwa!’ Mdindo wa Herodeyo akukhulupirira nayamba ulendo wake wautali wobwerera kwawo. Panjira akukumana ndi atumiki ake, amene athamanga kudzamuuza kuti zonse ziri bwino—mwana wake wachira! ‘Anayamba kupeza bwino liti?’ iye akufunsa motero.
‘Dzulo pa 1 koloko masana,’ akuyankha motero.
Mkuluyo akuzindikira kuti ndilo ola lenilenilo limene Yesu anati, ‘Mwana wako wachiritsidwa!’ Pambuyo pake, mwamunayo ndi a m’banja lake onse akukhala ophunzira a Kristu.
Motero Kana anafikira kukhala woyanjidwa monga malo amene, podziŵikitsa kubwerera kwake kuchokera ku Yudeya, Yesu anachita zozizwitsa kaŵiri. Zimenezi, ndithudi, siziri zozizwitsa zokha zimene anachita kufikira panthaŵi imeneyi, koma izo ziri zofunika chifukwa zinadziŵikitsa kubwerera kwake kuchokera ku Galileya.
Yesu tsopano akupita kwawo ku Nazarete. Kodi nchiyani chikumdikira kumeneko? Yohane 4:43-54; Marko 1:14, 15; Luka 4:14, 15.
▪ Pamene Yesu abwerera ku Galileya, kodi chikuchitika nchiyani kwa ophunzira ake, ndipo kodi anthu akumulandira motani?
▪ Kodi ndichozizwitsa chotani chimene Yesu akuchita, ndipo chikuyambukira motani awo amene akuphatikizidwa?
▪ Motero Kana akuyanjidwa motani ndi Yesu?