Mutu 22
Ophunzira Anayi Aitanidwa
PAMBUYO pakuyesayesa kufuna kupha mwambanda moyo wa Yesu m’tauni yakwawo ku Nazarete, iye akusamukira kumzinda wa Kapernao pafupi ndi Nyanja ya Galileya. Zimenezi zikukwaniritsa ulosi wina wa Yesaya. Ndiwo umene unaneneratu kuti anthu a ku Galileya okhala pafupi ndi nyanja adzawona kuunika kwakukulu.
Pamene Yesu akupitiriza ntchito yake yonyamula kuunika ya kulalikira Ufumu kunoko, iye akupeza anayi a ophunzira ake. Ameneŵa anayendapo naye poyambirirapo koma anamka kubizinesi lawo la usodzi pamene anabwerera ndi Yesu kuchokera ku Yudeya. Mwachiwonekere, Yesu akuwafunafuna, popeza kuti ndiyo nthaŵi yabwino ya kukhala ndi othandiza a nthaŵi zonse amene angawaphunzitse kupitiriza uminisitala iye atapita.
Chotero pamene Yesu akuyenda m’mphepete mwa nyanja nawona Simoni Petro ndi atsamwali ake akutsuka makoka awo, akupita kwa iwo. Akukwera bwato la Petro ndi kumuuza kuti akankhe pang’ono bwatolo. Pamene apalasa pang’ono, Yesu akukhala pansi m’bwato ndi kuyamba kuphunzitsa makamu amene ali m’mphepete mwanyanja.
Pambuyo pake, Yesu akunena kwa Petro kuti: “Kankhira kwakuya, nimuponye makoka anu kukasodza.”
“Ambuye,” Petro akuyankha motero, “tinagwiritsa ntchito usiku wonse osakola kanthu, koma pamawu anu ndidzaponya makoka.”
Pamene makoka aponyedwa, nsomba zambiri zedi zikugwidwa kwakuti makoka akuyamba kung’ambika. Mofulumira, amunawo akukodola anzawo a m’bwato lapafupipo kuti abwere kudzawathandiza. Mwamsanga mabwato onse aŵiri adzaza ndi nsomba zambiri kwakuti akuyamba kumira. Powona zimenezi, Petro akugwada pamaso pa Yesu nanena kuti: “Muchoke kwa ine Ambuye, chifukwa ndine munthu wochimwa.”
“Usawope,” Yesu akuyankha motero. “Kuyambira tsopano udzakhala msodzi wa anthu.”
Yesu akuitananso mbale wa Petro Andreya. “Tiyeni pambuyo panga,” akuwafulumiza motero, “Ndidzakusandutsani asodzi a anthu.” Mabwenzi awo osodza nawo Yakobo ndi Yohane, ana a Zebedayo, akupatsidwa chiitano chimodzimodzicho, ndipo nawonso akulabadira mosazengeleza. Chotero anayi ameneŵa akusiya bizinesi lawo losodza nakhala otsatira oyamba anayi okhazikika, a Yesu. Luka 5:1-11; Mateyu 4:13-22; Marko 1:16-20; Yesaya 9:1, 2.
▪ Kodi nchifukwa ninji Yesu akuitana ophunzira ake kumtsatira, ndipo ameneŵa ndani?
▪ Kodi ndichozizwitsa chotani chimene chikuchititsa mantha Petro?
▪ Kodi ndikusodza kotani kumene Yesu akuitanira ophunzira ake kuchita?