Mutu 26
Abwerera Kwawo ku Kapernao
POFIKA tsopano mbiri ya Yesu yamveka konsekonse, ndipo anthu ambiri akuyenda ulendo kumka kumalo akutaliwo kumene akukhala. Komabe, pambuyo pa masiku angapo, akubwerera ku Kapernao kudzera ku Nyanja ya Galileya. Mwamsanga mbiri ikufalikira mumzinda wonse kuti wabwera, ndipo ambiri akufika kunyumba kumene iye ali. Afarisi ndi aphunzitsi Achilamulo akudzanso kuchokera kutali monga ku Yerusalemu.
Khamulo liri lalikulu kotero kuti likupanikizana pakhomo, ndipo mulibe malo akuti munthu aloŵe mkati. Chochitikacho chikukonzekeretsa chochitika chapadera. Chimene chikuchitika panthaŵi imeneyi nchofunika kwambiri, pakuti chimatithandiza kuzindikira kuti Yesu ali ndi mphamvu ya kuchotsa nakatande wa kuvutika kwa anthu ndi kubwezeretsa umoyo wabwino kwa onse amene asankha.
Pamene Yesu ali chiphunzitsire khamulo, amuna ena anayi akubweretsa kunyumbayo munthu wopuŵala pakama. Iwo akufuna kuti Yesu achiritse bwenzi lawo, koma chifukwa cha khamulo, sangathe kuloŵa mkati. Nkogwiritsa mwala chotani nanga! Komabe iwo sakuleka. Iwo akukwera padenga lathyathyathyalo, naboola chiboo, natsitsira kama wokhala ndi munthu wopuŵalayo pansi pafupi ndi Yesu.
Kodi Yesu akukwiya chifukwa cha chidodometsocho? Kutalitali! Mmalomwake, iye akuchititsidwa chidwi ndi chikhulupiriro chawo. Iye akunena kwa wopuŵalayo kuti: “Machimo ako akhululukidwa.” Koma kodi Yesu angakhululukiredi machimo? Alembi ndi Afarisi sakuganiza choncho. Iwo akulingalira m’mitima mwawo kuti: “Munthu amene atero bwanji? achita mwano; akhoza ndani kukhululukira machimo, koma mmodzi, ndiye Mulungu?”
Podziŵa malingaliro awo, Yesu akuti kwa iwo: “Muganiza bwanji zinthu izi m’mitima yanu? Chapafupi nchiti, kapena kuuza wodwala manjenje kuti, Machimo ako akhululukidwa, kapena kuti, Nyamuka, senza mphasa yako, nuyende?”
Pamenepo Yesu akulola khamulo, kuphatikizapo omtsutsa, kuwona chisonyezero chapadera chimene chidzavumbula kuti ali ndi ulamuliro wa kukhululukira machimo padziko lapansi ndi kuti iye alidi munthu wamkulu woposa onse amene anakhalako. Akutembenukira kwa wopuŵalayo ndi kunena: “Nyamuka, senza mphasa yako, numuke kwanu.” Ndipo nthaŵi yomweyo iye akutero, akumatuluka ndi kama wake pamaso pa onse! Modabwitsidwa anthuwo akulemekeza Mulungu ndi kufuula kuti: “Zotere sitinaziwona ndi kale lonse!”
Kodi mwawona kuti Yesu akugwirizanitsa machimo ndi nthenda ndi kuti chikhululukiro cha machimo nchogwirizana ndi kupeza moyo wabwino wakuthupi? Baibulo limafotokoza kuti kholo lathu loyamba, Adamu, anachimwa ndi kuti tonsefe tiri ndi choloŵa cha zotulukapo za uchimo umenewo, ndiko kuti, matenda ndi imfa. Koma pansi pa ulamuliro wa Ufumu wa Mulungu, Yesu adzakhululukira machimo a anthu onse amene amakonda Mulungu ndi Kumtumikira, ndipo pamenepo matenda onse adzachotsedwa. Zimenezo zidzakhala zosangalatsa chotani nanga! Marko 2:1-12; Luka 5:17-26; Mateyu 9:1-8; Aroma 5:12, 17-19.
▪ Kodi nchiyani chinali mkhalidwe wa chochitika chenicheni chapadera?
▪ Kodi ndimotani mmene wopuŵala anafikira kwa Yesu?
▪ Kodi nchifukwa ninji tonsefe tiri ochimwa, koma kodi ndimotani mmene Yesu anaperekera chiyembekezo chakuti chikhululukiro cha machimo athu ndi moyo wangwiro nzothekera?