Mutu 27
Kuitanidwa kwa Mateyu
MWAMSANGA pambuyo pakuchiritsa wopuŵala, Yesu akuchoka m’Kapernao kumka ku Nyanja ya Galileya. Kachiŵirinso makamu a anthu akudza kwa iye, ndipo akuyamba kuwaphunzitsa. Pamene akuyenda, akuwona Mateyu amene amatchedwanso Levi, atakhala m’nyumba yamsonkho. “Nditsate ine,” ndicho chiitano cha Yesu.
Mwachiwonekere, Mateyu ali wozoloŵerana kale ndi ziphunzitso za Yesu, monga momwedi analiri Petro, Andreya, Yakobo, ndi Yohane pamene anaitanidwa. Ndipo mofanana nawo, nthaŵi yomweyo Mateyu akulabadira chiitanocho. Akunyamuka, nasiya ntchito yake monga wokhometsa msonkho, natsatira Yesu.
Pambuyo pake, mwinamwake kusangalalira kulandira chiitano chake, Mateyu akupanga phwando lalikulu kunyumba kwake. Kuwonjezera pa Yesu ndi ophunzira Ake, mabwenzi a Mateyu apapitapo aliponso. Kaŵirikaŵiri amuna ameneŵa amanyozedwa ndi Ayuda anzawo chifukwa chakuti amakhometsa ndalama zamsonkho wa ulamuliro wodedwa wa Roma. Ndiponso, iwo kaŵirikaŵiri mosawona mtima amalipiritsa anthu ndalama zambiri koposa chiŵerengelo chozoloŵereka cha msonkho.
Powona Yesu paphwandolo ndi anthu otero, Afarisi akufunsa ophunzira ake kuti: “Nchifukwa ninji mphunzitsi wanu alinkudya pamodzi ndi amisonkho ndi ochimwa?” Pakumva funsolo, Yesu akuyankha Afarisi kuti: “Olimba safuna sing’anga ayi, koma odwala. Koma mukani, muphunzire nchiyani ichi, Ndifuna chifundo, sinsembe ayi; pakuti sindinadza kudzaitana olungama, koma ochimwa.”
Mwachiwonekere, Mateyu waitana amisonkho ameneŵa kunyumba kwake kotero kuti adzamvetsere kwa Yesu kuti achiritsidwe mwauzimu. Chotero Yesu akuyanjana nawo ndi kuwathandiza kupeza unansi wabwino ndi Mulungu. Yesu sanyoza anthu otero, monga momwe amachitira Afarisi odzikonda. Mmalomwake, posonkhezeredwa ndi chifundo iye m’chenicheni, amatumikira monga sing’anga wauzimu kwa iwo.
Motero kusonyeza chifundo kwa Yesu kulinga kwa ochimwa sindiko kulekerera machimo awo koma ndiko chisonyezero cha malingaliro achikondi amodzimodziwo amene anawasonyeza kwa odwala mwakuthupi. Mwachitsanzo, kumbukirani, pamene mwachifundo anatansira dzanja ndi kukhudza wakhate, akumanena kuti: “Ndifuna, takonzeka.” Mofananamo tisonyezetu chifundo mwakuthandiza anthu osoŵa, makamaka kuwathandiza m’njira yauzimu. Mateyu 8:3; 9:9-13; Marko 2:13-17; Luka 5:27-32.
▪ Kodi Mateyu ali kuti pamene Yesu akumuwona?
▪ Kodi ntchito ya Mateyu njotani, ndipo kodi nchifukwa ninji anthu otero amanyozedwa ndi Ayuda ena?
▪ Kodi ndikudandaula kotani kumene kukupangidwa motsutsana ndi Yesu, ndipo kodi iye akuyankha motani?
▪ Kodi nchifukwa ninji Yesu amayanjana ndi ochimwa?