Mutu 29
Kuchita Ntchito Zabwino pa Sabata
NDI ngululu ya 31 C.E. Miyezi yoŵerengeka yapita chiyambire pamene Yesu analankhula kwa mkazi pachitsime cha ku Samariya pamene anali paulendo wochokera ku Yudeya kumka ku Galileya.
Tsopano, pambuyo pa kuphunzitsa kwakukulu mu Galileya yense, Yesu kachiŵirinso akupita ku Yudeya, kumene akulalikira m’masunagoge. Poyerekezera ndi chisamaliro chimene Baibulo limapereka kuuminisitala wake mu Galileya, limanena zochepekera za ntchito ya Yesu mu Yudeya mkati mwa ulendo umenewu ndi mkati mwa miyezi imene anathera ali kuno pambuyo pa Paskha wapapitapo. Mwachiwonekere utumiki wake sunalandire chilabadiro chachiyanjo mu Yudeya monga unachitira mu Galileya.
Mwamsanga Yesu ali paulendo wake kumka kumzinda waukulu wa Yudeya, Yerusalemu, kaamba ka Paskha wa 31 C.E. Kunoko, pafupi ndi Chipata cha Nkhosa cha mzindawu, pali thamanda lotchedwa Betesda, kumene odwala ambiri, akhungu, ndi opuwala amadza. Iwo amakhulupirira kuti anthu angachiritsidwe mwa kuloŵa m’madzi a pathamandali pamene madzi ameneŵa avundulidwa.
Nditsiku la Sabata, ndipo Yesu akuwona munthu pathamandapo amene wakhala akudwala kwazaka 38. Pozindikira nyengo yaitali ya nthenda ya munthuyo, Yesu akumfunsa kuti: “Ufuna kuchiritsidwa kodi?”
Iye akuyankha Yesu kuti: “Ambuye, ndilibe wondiviika ine m’thamanda paliponse madzi avundulidwa; koma mmene ndirinkudza ine, wina atsika ndisanatsike ine.”
Yesu akumuuza kuti: “Tauka, yalula mphasa yako, nuyende.” Pomwepo munthuyo mwamsanga achira, nayalula mphasa yake, nayamba kuyenda!
Koma pamene Ayuda awona munthuyo, iwo akuti: “Ndi Sabata, ndipo sikuloledwa kwa iwe kuyalula mphasa yako.”
Munthuyo akuwayankha kuti: “Iye amene anandichiritsa, yemweyu anati kwa ine, Yalula mphasa yako, nuyende.”
“Munthuyo ndani wonena ndi iwe, Yalula mphasa yako, nuyende?” iwo akufunsa motero. Yesu anali atapatukira kwina chifukwa cha khamulo, ndipo wochiritsidwayo sanadziŵe dzina la Yesu. Komabe, pambuyo pake, Yesu ndi munthuyo akukumana m’kachisi, ndipo munthuyo akuzindikira amene anamchiritsa.
Chotero munthu wochiritsidwayo akufunafuna Ayudawo kuti awauze kuti ndiye Yesu amene anamchiritsa. Podziŵa zimenezi, Ayuda akupita kwa Yesu. Kaamba ka chifukwa chotani? Kuti akadziŵe kodi kuti ndimwanjira yanji imene iye ali wokhoza kuchita nayo zinthu zodabwitsa zimenezi? Ayi. Koma kukampezera chifukwa chakuti akuchita zinthu zabwino zimenezi pa la Sabata. Ndipo akuyambadi kumvuta! Luka 4:44; Yohane 5:1-16.
▪ Kodi ndipafupifupi kwanthaŵi yaitali yotani chiyambire nthaŵi yotsiriza pamene Yesu anacheza ku Yudeya?
▪ Kodi nchifukwa ninji thamanda lotchedwa Betesda liri lotchuka motero?
▪ Kodi Yesu akuchita chozizwitsa chotani pathamandapo, ndipo kodi nchiyani chimene chiri kulabadira kwa Ayudawo?