Mutu 32
Kodi Chololeka Nchiyani pa Sabata?
LIRI tsiku lina la Sabata limene Yesu akupita kusunagoge wapafupi ndi Nyanja ya Galileya. Pamenepo pali munthu amene ali ndi dzanja lopuŵala. Alembi ndi Afarisi akuyang’anitsitsa kuwona kaya ngati Yesu adzamchiritsa. Potsiriza iwo akufunsa kuti: “Nkololeka kodi kuchiritsa tsiku la Sabata?”
Atsogoleri achipembedzo Chachiyuda amakhulupirira kuti kuchiritsa tsiku la Sabata kuli kololeka kokha ngati moyo uli pangozi. Mwachitsanzo, iwo amaphunzitsa, kuti tsiku la Sabata nkosaloleka kuwongola kapena kumanga fupa loguluka. Chotero alembi ndi Afarisi akufunsa Yesu poyesayesa kumpezera mlandu.
Komabe, Yesu, akudziŵa zolingalira zawo. Panthaŵi imodzimodziyo, iye akuzindikira kuti ali ndi lingaliro lomkitsa, losagwirizana ndi malemba lonena za chimene chimapanga kuswedwa kwa lamulo loletsa kugwira ntchito tsiku la Sabata. Chotero Yesu akuyala maziko a mkangano wochititsa chidwi mwa kuuza munthu wa dzanja lopuŵalayo kuti: “Taimirira pakati.”
Tsopano, potembenukira kwa alembi ndi Afarisi, Yesu akuti: “Munthu ndani wa inu, amene ali nayo nkhosa imodzi, ndipo ngati idzagwa m’dzenje tsiku la Sabata, kodi sadzaigwira, ndi kuitulutsa?” Popeza nkhosa imaimira chuma chosungidwa, sakanaisiya m’dzenje mpaka tsiku lotsatira, mwina mwake ikadwala ndi kuwatayitsa phindu. Ndiponso, Malemba amati: “Wolungama asamalira moyo wa choŵeta chake.”
Akumasonyeza kufananako, Yesu akupitiriza kuti: “Nanga kuposa kwake kwa munthu ndi nkhosa nkotani! Chifukwa cha ichi nkololeka kuchita zabwino tsiku la sabata.” Atsogoleri achipembedzo saali okhoza kukana lingaliro lotsimikizirika, la chifundo lotero, ndipo akhala chete.
Moipidwa, ndiponso kumva chisoni chifukwa cha liuma lawo lautsiru, Yesu akuunguzaunguza. Pamenepo akuuza mwamunayo kuti: “Tansa dzanja lako.” Ndipo iye akulitansa ndipo dzanjalo likuchiritsidwa.
Mmalo mwa kukondwa kuti dzanja la munthuyo labwerezetsedwa, Afarisiwo akutuluka ndipo mwamsanga akuchita chiwembu ndi otsatira chipani cha Herode kupha Yesu. Mwachiwonekere chipani chandale chimenechi chimaphatikizapo ziŵalo za Asaduki a chipembedzo. Mwachibadwa chipani chandale zadziko chimenechi ndi Afarisi amatsutsana poyera, koma iwo ngogwirizana mwamphamvu m’kutsutsana kwawo ndi Yesu. Mateyu 12:9-14; Marko 3:1-6; Luka 6:6-11; Miyambo 12:10; Eksodo 20:8-10.
▪ Kodi nchiyani chimene chinali mkhalidwe wa chochititsa mkangano pakati pa Yesu ndi atsogoleri achipembedzo Achiyuda?
▪ Kodi nchiyani chimene atsogoleri achipembedzo Achiyuda ameneŵa amakhulupirira ponena za kuchiritsa patsiku la Sabata?
▪ Kodi ndifanizo lotani limene Yesu akugwiritsira ntchito kutsutsa malingaliro awo olakwa?