Mutu 35
Ulaliki Wotchuka Woposa Wonse Umene Unaperekedwa
CHOCHITIKACHO ndicho chimodzi chokumbukirika koposa m’mbiri ya Baibulo: Yesu wakhala mphepete mwa phiri, akumapereka Ulaliki wake wotchuka wa pa Phiri. Malowo ndiwo pafupi ndi Nyanja ya Galileya, mwinamwake pafupi ndi Kapernao. Pambuyo pakutha usiku wonse akupemphera, Yesu wangosankha kumene 12 a ophunzira ake kukhala atumwi. Pamenepo, pamodzi ndi onsewo, akutsikira kumalo athyathyathya paphiripo.
Pakali pano, mukaganiza kuti, Yesu akakhala wotopa kwambiri ndipo akafunikira kugona. Koma makamu aakulu adza, ena kuchokera ku Yudeya ndi Yerusalemu, mtunda wa makilomitala 96 kufikira ku 112. Ena achokera kumalo akugombe la nyanja ya Turo ndi Sidoni cha kumpoto. Iwo afika kudzamva Yesu ndi kudzachiritsidwa matenda awo. Palidi anthu amene ali ovutitsidwa ndi ziŵanda, angelo oipa a Satana.
Pamene Yesu akutsika, anthu odwala akuyandikira pafupi naye kudzamkhudza, ndipo akuchiritsa onsewo. Pambuyo pake, Yesu mwachiwonekere akukwera pamalo okwera kwambiri pa phiripo. Pamenepo akukhala pansi nayamba kuphunzitsa makamu aakulu amene anakhala pamalo athyathyathya ponsepo pamaso pake. Ndipo tangoganizani za zimenezo! Tsopano palibe ngakhale munthu mmodzi mwa omvetsera onsewo amene akuvutika ndi matenda aakulu!
Anthu ali ofunitsitsa kumva mphunzitsi amene ali wokhoza kuchita zozizwitsa zodabwitsa zimenezi. Komabe, Yesu, akupereka ulaliki wake makamaka kaamba kaphindu la ophunzira ake, amene mwinamwake asonkhana chapafupinaye momzungulira. Koma kuti nafenso tipindule, onse aŵiriwo Mateyu ndi Luka aulemba.
Cholembedwa cha Mateyu cha ulaliki chiri pafupifupi choŵirikiza kanayi kutalika kuposa cholembedwa cha Luka. Ndiponso, zigawo zimene Mateyu akulemba, Luka akuzipereka kukhala zonenedwa ndi Yesu panthaŵi ina mkati mwa ulaliki wake, monga momwe kungawonedwere mwa kuyerekezera Mateyu 6:9-13 ndi Luka 11:1-4, ndi Mateyu 6:25-34 ndi Luka 12:22-31. Komabe zimenezi siziyenera kukhala zodabwitsa. Yesu mwachiwonekere anaphunzitsa zinthu zimodzimodzizo koposa kamodzi, ndipo Luka anasankha kulemba zina za ziphunzitso zimenezi m’njira yosiyana.
Chimene chikupangitsa ulaliki wa Yesu kukhala wamtengo wapatali sindiko kuya kokha kwa zolembedwamo zake komanso njira mu imene akufeŵetsera ndi kumveketsera chowonadi chimenechi. Iye akutchula zochitika zozoloŵereka ndipo akugwiritsira ntchito zinthu zimene ziri zozoloŵereka kwa anthu, motero kupangitsa malingaliro ake kukhala omvedwa mosavuta ndi onse amene akufunafuna moyo wabwino kwambiri m’njira ya Mulungu.
Kodi Ndani Amene Alidi Odala?
Aliyense amafuna kukhala wodala. Pozindikira zimenezi, Yesu akuyamba Ulaliki wake wa pa Phiri mwa kufotokoza awo amene alidi odala. Monga mmene tingayerekezerere, mwamsanga zimenezi zikugwira chisamaliro cha nakatindi wa omvetsera ake. Ndipo komabe kwa ambiri mawu ake oyamba ayenera kuwonekera kukhala odzitsutsa.
Polankhula mawu ake kwa ophunzira ake, Yesu akuyamba ndi kuti: “Odala osauka inu; chifukwa uli wanu ufumu wa Mulungu. Odala inu akumva njala tsopano; chifukwa mudzakhuta. Odala inu akulira tsopano; chifukwa mudzaseka. Odala inu pamene anthu adzada inu, . . . Kondwerani tsiku lomweli, tumphani ndi chimwemwe; pakuti wonani, mphoto zanu nzazikulu kumwamba.”
Ichi ndi cholembedwa cha Luka cha mawu oyamba aulaliki wa Yesu. Koma malinga ndi cholembedwa cha Mateyu, Yesu akunenanso kuti ofatsa, achifundo, oyera mtima, ndi amtendere ali odala. Ameneŵa ngodala, Yesu akutero, chifukwa chakuti adzalandira dziko lapansi, adzasonyezedwa chifundo, adzawona Mulungu, ndipo adzatchedwa ana a Mulungu.
Komabe, zimene Yesu akutanthauza mwa kukhala odala, siziri kokha kukhala wosangalala kapena wokondwa, monga pamene munthu asangalala ndi kanthu kena. Chimwemwe chowona nchakuya, chokhala ndi lingaliro la chikhutiro, lingaliro la kukhutiritsidwa ndi kukwaniritsidwa m’moyo.
Chotero awo amene alidi odala, Yesu akusonyeza kuti, ali anthu amene amazindikira chosoŵa chawo chauzimu, amamva chisoni ndi mkhalidwe wawo wauchimo, nafikira pakudziŵa ndi kutumikira Mulungu. Pamenepo, ngakhale ngati adedwa, kapena kuzunzidwa chifukwa cha kuchita chifuniro cha Mulungu, ngodala chifukwa amadziŵa kuti akukondweretsa Mulungu ndipo adzalandira mphotho yake ya moyo wosatha.
Komabe, ambiri a omvetsera a Yesu, monga momwe aliri anthu ena lerolino, akukhulupirira kuti kukhala wokhuphuka ndi kukondwera ndi zosangalatsa ndizo zimene zimapangitsa munthu kukhala wachimwemwe. Yesu amadziŵa zimenezi mosiyana. Akumapanga kusiyana kumene kuyenera kudabwitsa ambiri a omvetsera ake, iye akuti:
“Tsoka inu eni chuma! chifukwa mwalandira chisangalatso chanu. Tsoka inu okhuta tsopano! chifukwa mudzamva njala. Tsoka inu, akuseka tsopano! chifukwa mudzachita maliro ndi kulira misozi. Tsoka inu, pamene anthu onse adzanenera inu zabwino, pakuti makolo awo anawatero momwemo aneneri onama.”
Kodi Yesu akutanthauzanji? Kodi nchifukwa ninji kukhala ndi chuma, kulondola mosekera zinthu zokondweretsa, ndi kusangalala ndi thamo la anthu kumadzetsa tsoka? Chiri chifukwa chakuti pamene munthu ali ndipo akonda zinthu zimenezi, pamenepo utumiki kwa Mulungu, umene uli wokhawo wodzetsa chimwemwe chowona, sumaphatikizidwa m’moyo wake. Panthaŵi imodzimodziyo, Yesu sakutanthauza kuti kukhala chabe waumphaŵi, wanjala, ndi wolira kumapangitsa munthu kukhala wachimwemwe. Komabe, kaŵirikaŵiri, anthu ovutika oterowo angalabadire kuziphunzitso za Yesu, ndipo motero ali odalitsidwa ndi chimwemwe chowona.
Kenako, polankhula ndi ophunzira ake, Yesu akuti: “Inu ndinu mchere wadziko lapansi.” Ndithudi iye sakutanthauza kuti, iwo alidi mchere weniweni. Mmalomwake, mchere umatetezera zinthu. Mulu waukulu wa mchere uli pafupi ndi guwa la nsembe la Yehova pakachisi, ndipo ansembe ogwira ntchito kumeneko anaugwiritsira ntchito kukoleretsera nsembe.
Ophunzira a Yesu ali “mchere wadziko lapansi” m’chakuti iwo ali ndi chiyambukiro chotetezera pa anthu. Ndithudi, uthenga umene ali nawo udzasunga miyoyo ya onse amene akuulabadira! Udzadzetsa kumiyoyo ya anthu oterowo mikhalidwe ya kukhalitsa, kukhulupirika, ndi chikhulupiriro, zikumapeŵetsa kuvunda kwauzimu kulikonse ndi kwa makhalidwe mwa iwo.
“Inu ndinu kuunika kwa dziko lapansi,” Yesu akuuza ophunzira ake motero. Nyali siikidwa pansi pa mtanga koma pamwamba pachoikapo, chotero Yesu akuti: “Chomwecho muwalitse inu kuunika kwanu pamaso pa anthu.” Ophunzira a Yesu amachita zimenezo mwa kuchitira umboni kwawo poyera, ndiponso mwa kutumikira monga zitsanzo zounikira zamakhalidwe amene amagwirizana ndi malamulo a makhalidwe abwino a Baibulo.
Muyezo Wapamwamba wa Otsatira Ake
Atsogoleri achipembedzo akulingalira Yesu kukhala wochimwira Lamulo la Mulungu ndipo posachedwapa achita ngakhale upo kuti amuphe. Chotero pamene Yesu akupitiriza Ulaliki wake wa pa Phiri, iye akufotokoza kuti: “Musaganize kuti ndinadza ine kudzapasula Chilamulo kapena Aneneri sindinadza kupasula, koma kukwaniritsa.”
Yesu amachitira ulemu waukulu kaamba ka Chilamulo cha Mulungu ndipo amalimbikitsa ena kukhalanso otero. Kwenikweni, iye akuti: “Chifukwa chake yense wakumasula limodzi la malangizo ameneŵa aang’onong’ono, nadzaphunzitsa anthu chomwecho, adzatchulidwa wamng’onong’ono mu ufumu wa kumwamba,” kutanthauza kuti munthu wotero sadzaloŵa konse mu Ufumuwo.
Mosiyana kwambiri ndi kunyalanyaza Chilamulo cha Mulungu, Yesu akutsutsa ngakhale mkhalidwe wamaganizo umene umachirikiza munthu kukuchiswa. Atasonyeza kuti Chilamulocho chimati, “Usaphe,” Yesu akuwonjezera kuti: “Koma ine ndinena kwa inu, kuti yense wokwiyira mbale wake wopanda chifukwa adzakhala wopalamula mlandu.”
Popeza kuti kupitirizabe kukwiyira bwenzi lanu ndiko chinthu chowopsa kwambiri, mwinamwake ngakhale kutsogolera kukupha, Yesu akunena mwafanizo mlingo umene munthu angafikire kuti apeze mtendere. Iye akulangiza kuti: “Chifukwa chake ngati ulikupereka mtulo wako paguwa la nsembe, ndipo pomwepo ukakumbukira kuti mbale wako ali ndi kanthu pa iwe, usiye pomwepo mtulo wako kuguwako, nuchoke, nuyambe kuyanjana ndi mbale wako, ndipo pamenepo idza nupereke mtulo wako.”
Potembenukira ku lachisanu ndi chiŵiri la Malamulo Khumi, Yesu akupitiriza kuti: “Munamva kuti kunanenedwa Usachite chigololo.” Komabe, Yesu akutsutsa ngakhale khalidwe lokhotelera ku chigololo. “Ine ndinena kwa inu, kuti yense wakuyang’ana mkazi kumkhumba, pamenepo watha kuchita naye chigololo mumtima mwake.”
Yesu panopa sakungonena za lingaliro la kusadzisungira kwa kugonana lopita ndi maganizo koma ponena za ‘kupitirizabe kuyang’ana.’ Kuyang’ana kopitirizabe kotero kumadzutsa nyere, imene, ngati mwaŵi uloleza, ingatsogolere kuchigololo. Kodi munthu angapeŵe motani zimenezi kuti zisachitike? Yesu akuchitira fanizo mmene masitepe aakulu angafunikirire akumati: “Koma ngati diso lako lamanja likulakwitsa iwe, ulikolowole, nulitaye; . . . Ndipo ngati dzanja lako lamanja likulakwitsa iwe, ulidule, nulitaye.”
Kaŵirikaŵiri anthu amafunitsitsa kutayikiridwa ndi chiŵalo chenicheni chimene chiri ndi matenda kuti apulumutse miyoyo yawo. Koma malinga ndi kunena kwa Yesu, kulidi kofunika mowonjezereka ‘kutaya’ chirichonse, ngakhale chimene chiri cha mtengo wapatali monga diso kapena dzanja, kupeŵa maganizo ndi machitidwe a chisembwere cha kugonana. Apo phuluzi, Yesu akufotokoza kuti, anthu otero adzaponyedwa m’Gehena (dzala ladzinyalala loyaka moto pafupi ndi Yerusalemu), limene limaphiphiritsira chiwonongeko chosatha.
Yesu akukambanso za mmene angachitire ndi anthu amene amapangitsa chivulazo ndi kukhumudwitsa. “Musakanize munthu woipa,” ndiwo uphungu wake. “Koma amene adzakupanda iwe patsaya lako lamanja, umtembenuzire linanso.” Yesu sakutanthauza kuti munthu sayenera kudzitchinjiriza kapena banja lake ngati liukiridwa. Khofu silimamenyedwa kuti livulaze munthu mwakuthupi koma, mmalomwake, kumnyazitsa. Chotero, zimene Yesu akunena nzakuti ngati aliyense ayesa kuputa ndewu kapena mkangano, kaya mwa kumenyadi khofu kapena mwa mawu opweteka, kubwezera kukakhala koipa.
Atachititsa chisamaliro kusumikidwa palamulo la Mulungu la kukonda mnansi, Yesu akuti: “Koma ine, ndinena kwa inu, Kondanani nawo adani anu, ndi kupempherera iwo akuzunzani inu.” Popereka chifukwa champhamvu cha kuchitira zimenezo, iye akuwonjeza kuti: “Kotero kuti mukakhale ana a Atate wanu wa kumwamba; chifukwa iye amakwezera dzuŵa lake pa oipa ndi pa abwino.”
Yesu akumaliza mbali imeneyi ya ulaliki wake mwakulangiza kuti: “Chifukwa chake inu mukhale angwiro, monga Atate wanu wa kumwamba ali wangwiro.” Yesu sakunena kuti anthu angakhale angwiro munjira yotheratu. Mmalomwake, iwo angathe mwa kutsanzira Mulungu, kukulitsa chikondi chawo kuti chiphatikizepo ngakhale adani awo. Cholembedwa cha Luka chofanana nacho chimati ponena za mawu a Yesu: “Khalani inu achifundo monga Atate wanu ali wachifundo.”
Pemphero, ndi Chidaliro mwa Mulungu
Pamene Yesu akupitiriza ndi ulaliki wake, akutsutsa chinyengo cha anthu amene amadziwonetsera kukhala kwawo opembedza. “Pamene paliponse upatsa mphatso zachifundo,” iye akutero, “usamawomba lipenga patsogolo pako, monga amachita onyenga.”
“Ndipo,” Yesu akupitiriza, “pamene mupemphera, musakhale monga onyengawo; chifukwa iwo akonda kuimirira ndi kupemphera m’masunagoge, ndi pamphambano za makwalala kuti awonekere kwa anthu.” Mmalomwake, iye akulangiza kuti: “Popemphera, loŵa m’chipinda chako, nutseke chitseko chako, nupemphere Atate wako ali m’tseri.” Yesu mwiniyo ananena mapemphero apoyera, chotero iye sakutsutsa ameneŵa. Chimene akutsutsa ndiwo mapemphero amene amanenedwa kuti achititse chidwi omvetsera ndi kuwachititsa kunena mawu oyamikira.
Yesu akupitirizabe kupereka uphungu kuti: “Popemphera musabwerezebwereze chabe iyayi, monga amachita anthu akunja.” Yesu sakutanthauza kuti kubwerezedwa kwa mawu mwa iko kokha nkolakwa. Panthaŵi ina, iye mwini anagwiritsira ntchito kubwereza ‘liwu limodzimodzilo’ popemphera. Koma chimene iye sakuvomereza ndicho kunenedwa kwa mawu oloŵezedwa mumtima ‘mobwerezabwereza,’ m’njira imene oŵerenga mikanda amachitira pamene abwereza mapemphero awo moloŵeza pamtima.
Kuthandiza omvetsera ake kupemphera, Yesu akupereka pemphero lachitsanzo limene limaphatikizapo mapempho asanu ndi aŵiri. Atatu oyambawo moyenerera amasonyeza kuzindikiridwa kwa ulamuliro wa Mulungu ndi zifuno zake. Iwo ndiwo mapempho a kuyeretsedwa kwa dzina la Mulungu, Ufumu wake kudza, ndi chifuno chake kuchitidwa. Anayi otsalawo ndiwo mapempho aumwini, ndiko kuti, kaamba ka chakudya cha tsiku ndi tsiku, kaamba ka kukhululukidwa machimo, kusayesedwa kupyola chipiriro cha munthu, ndi kupulumutsidwa kwa woipayo.
Popitiriza, Yesu akutchula msampha wakuika chigogomezero chosayenera pazinthu zakuthupi. Iye akufulumiza kuti: “Musadzikundikire nokha chuma padziko lapansi, pamene njenjete ndi dzimbiri ziwononga ndi pamene mbala ziboola ndi kuba.” Si kokha kuti chuma choterocho chimawonongeka komanso sichimapanga unansi wabwino ndi Mulungu.
Ndicho chifukwa chake, Yesu akuti: “Koma mudzikundikire nokha chuma m’mwamba.” Zimenezi zimachitidwa mwa kuika utumiki wa Mulungu poyamba m’moyo wanu. Palibe amene angalande unansi wopezedwa ndi Mulungu kapena mphotho yake yaikuluyo. Pamenepo Yesu akuwonjezera kuti: “Kumene kuli chuma chako, komwe kudzakhala mtima wakonso.”
Popitirizabe kunena za msampha wokondetsa zinthu zakuthupi, Yesu akupereka fanizo lakuti: “Diso ndilo nyali ya thupi; chifukwa chake ngati diso lako liri la kumodzi, thupi lako lonse lidzakhala lowalitsidwa. Koma ngati diso lako liri loipa, thupi lako lonse lidzakhala lodetsedwa.” Diso limene limagwira ntchito moyenera liri monga nyali kuthupi yoyatsidwa m’malo amdima. Koma kuti liwone bwino, diso liyenera kukhala lakumodzi, ndiko kuti, liyenera kuyang’ana pachinthu chimodzi. Diso losawona bwino limatsogolera kukuyerekezera zinthu molakwa, mwa kuika kulondoledwa kwa zinthu zakuthupi patsogolo pautumiki wa Mulungu, ndi chotulukapo chakuti “thupi lako lonse” limakhala lamdima.
Yesu akumaliza nkhaniyi ndi fanizo lamphamvu lakuti: “Palibe munthu angathe kukhala kapolo wa ambuye aŵiri pakuti pena adzamuda mmodziyo, ndi kukonda winayo; pena adzakangamira kwa mmodzi nadzanyoza wina. Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa Chuma.”
Atapereka uphungu umenewu, Yesu akutsimikiziritsa omvetsera ake kuti safunikira kukhala odera nkhaŵa ndi zosoŵa zawo zakuthupi ngati aika utumiki wa Mulungu poyamba. “Yang’anirani mbalame zakumwamba,” iye akutero, “kuti sizimafesa mbewu ayi, kapena sizimatema ayi, kapena sizimatutira m’nkhokwe; ndipo Atate wanu wakumwamba azidyetsa.” Ndiyeno akufunsa kuti: “Nanga inu mulibe kusiyana nazo kuziposa kodi?”
Kenako, Yesu akusonyeza akakombo a kuthengo ndipo akunena kuti “ngakhale Solomo muulemerero wake wonse sanavala monga limodzi la amenewa. Koma ngati,” akupitiriza motero, “Mulungu aveka chotero maudzu a kuthengo, . . . nanga siinu kopambana ndithu, inu akukhulupirira pang’ono?” Chifukwa cha chimenecho Yesu akumaliza kuti: “Musadere nkhaŵa, ndi kuti, Tidzadya chiyani? kapena Tidzamwa chiyani? kapena Tidzavala chiyani? . . . pakuti Atate wanu wakumwamba adziŵa kuti musoŵa zonse zimenezo. Koma muthange mwafuna ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzawonjezedwa kwa inu.”
Njira ya Kumoyo
Njira ya kumoyo ndiyo ya kumamatira kuziphunzitso za Yesu. Koma zimenezi sizosavuta kuchita. Mwachitsanzo, Afarisi, amayedzamira pakuweruza ena mwankhanza, ndipo mwachiwonekere ambiri amawatsanzira. Chotero pamene Yesu apitirizabe Ulaliki wake wa pa Phiri, akupereka chilangizo ichi: “Musaweruze, kuti mungaweruzidwe. Pakuti ndi kuweruza kumene muweruza nako, inunso mudzaweruzidwa.”
Kutsatira njira yosuliza monkitsa ya Afarisi nkwaupandu. Malinga ndi cholembedwa cha Luka, Yesu akupereka fanizo laupandu umenewu mwakuti: “Kodi munthu wakhungu angathe kutsogolera mnzake wakhungu? kodi sadzagwa onse aŵiri m’mbuna?”
Kukhala wosuliza ena kwambiri, kukulitsa zolakwa zawo ndi kuwasinjirira, ndiko kupalamula mlandu kwakukulu. Chotero Yesu akufunsa kuti: “Udzati bwanji kwa kwa mbale wako, Tandilola ndichotse kachitsotso m’diso lako; ndipo wona, mtandawo ulimo m’diso lakoli. Wonyenga iwe! tayamba kuchotsa m’diso lako mtandawo ndipo pomwepo udzapenyetsa kuchotsa kachitsotso m’diso la mbale wako.”
Zimenezi sizikutanthuza kuti ophunzira a Yesu sayenera kugwiritsira ntchito luntha mogwirizana ndi anthu ena, pakuti iye akuti: “Musamapatsa chopatulikacho kwa agalu, musamaponya ngale zanu patsogolo pa nkhumba.” Chowonadi chochokera m’Mawu a Mulungu nchoyera. Chiri ngati ngale zophiphiritsira. Koma ngati ena, amene ali ngati agalu kapena nkhumba, asonyeza kusayamikira kaamba ka chowonadi cha mtengo wapatali chimenechi, ophunzira a Yesu ayenera kusiya anthu otero ndi kufunafuna awo amene ali olabadira.
Ngakhale kuti Yesu wakamba za pemphero poyambirirapo mu Ulaliki wake wa pa Phiri, iye tsopano akugogomezera kufunika kwa kuchita khama. “Pemphani,” iye akufulumiza motero, “ndipo chidzapatsidwa kwa inu.” Kuchitira fanizo la kukhala wokonzekera kwa Mulungu m’kuyankha mapemphero, Yesu akufunsa kuti: “Munthu ndani wa inu, amene pompempha mwana wake mkate—adzampatsa iye mwala? . . . Chomwecho, ngati inu, muli oipa, mudziŵa kupatsa ana anu mphatso zabwino, kopambana kotani nanga Atate wanu wakumwamba adzapatsa zinthu zabwino kwa iwo akumpempha iye?”
Kenako Yesu akupereka chimene chafikira kukhala lamulo lotchuka la makhalidwe, mofala lotchedwa kuti Lamulo Lamakhalidwe Abwino. Iye akuti: “Chifukwa chake zinthu zonse mukafuna kuti anthu achitire inu, inunso muwachitire iwo zotero.” Kukhala ndi moyo mogwirizana ndi lamulo limeneli kumaphatikizapo mchitidwe wotsimikizirika m’kuchita zabwino kwa ena, kuchita monga momwe mufuna kuti akuchitireni.
Kuti njira yomka kumoyo siri yosavuta kukuvumbulidwa ndi chilangizo cha Yesu: “Loŵani pachipata chopapatiza; chifukwa chipata chiri chachikulu, ndi njira yakumuka nayo kukuwonongeka iri yotakata; ndipo ali ambiri amene aloŵa pa icho. Pakuti chipata chiri chopapatiza, ndi ichepetsa njirayo yakumuka nayo kumoyo, ndimo akuchipeza chimenecho ali oŵerengeka.”
Upandu wa kunyengedwa ngwaukulu koposa, chotero Yesu akuchenjeza kuti: “Yang’anirani mupeŵe aneneri onyenga, amene adza kwa inu ndi zovala zankhosa, koma mkati mwawo ali afisi olusa.” Monga momwedi mitengo yabwino ndi mitengo yoipa ingazindikiridwe ndi zipatso zake, Yesu akusonyeza kuti, aneneri onyenga angazindikiridwe ndi khalidwe lawo ndi ziphunzitso.
Popitiriza, Yesu akufotokoza kuti sikuli kokha zimene munthu amanena zimene zimampangitsa kukhala wophunzira Wake koma zimene amachita. Anthu ena amadzinenera kuti Yesu ndiye Mbuye wawo, koma ngati sachita chifuniro cha Atate wake, iye akuti: “Ndidzafukulira iwo Sindinakudziŵani inu nthaŵi zonse; chokani kwa ine, inu akuchita kusayeruzika.”
Potsirizira pake, Yesu akupereka mapeto osaiŵalika a ulaliki wake. Iye akuti: “Yense amene akamva mawu anga ameneŵa, ndi kuwachita, ndidzamfanizira iye ndi munthu wochenjera, amene anamanga nyumba yake pathanthwe; ndipo inagwa mvula, nidzala mitsinje, ndipo zinaomba mphepo, zinagunda panyumbayo; koma siinagwa; chifukwa inakhazikika pathanthwepo.”
Kumbali ina, Yesu akulengeza kuti: “Yense amene akamva mawu anga ameneŵa, ndi kusawachita adzafanizidwa ndi munthu wopusa, yemwe anamanga nyumba yake pamchenga; ndipo inagwa mvula, nidzala mitsinje, ndipo zinaomba mphepo, zinagunda panyumbayo; ndipo inagwa; ndipo kugwa kwake kunali kwakukulu.’
Pamene Yesu amaliza ulaliki wake, makamuwo akuzizwa ndi njira yake yophunzitsa, pakuti akuwaphunzitsa monga munthu wokhala ndi ulamuliro ndipo osati monga atsogoleri awo achipembedzo. Luka 6:12-23; Mateyu 5:1-12; Luka 6:24-26; Mateyu 5:13-48; 6:1-34; 26:36-45; 7:1-29; Luka 6:27-49.
▪ Kodi Yesu ali kuti pamene akupereka ulaliki wake wosaiŵalika koposa, ndipo ndani amene alipo, ndipo chachitika nchiyani asanaupereke?
▪ Kodi nchifukwa ninji kuli kosadabwitsa kuti Luka akulemba ziphunzitso zina za ulalikiwo munjira ina?
▪ Kodi nchiyani chikupangitsa ulaliki wa Yesu kukhala wamtengo wapatali?
▪ Kodi ndani amene alidi odala, ndipo chifukwa ninji?
▪ Kodi ndani akulandira tsoka, ndipo chifukwa ninji?
▪ Kodi ophunzira a Yesu ali “mchere wadziko lapansi” ndi “kuunika kwa dziko lapansi” motani?
▪ Kodi ndimotani mmene Yesu akusonyezera kuchitira ulemu kwakukulu kaamba ka Chilamulo cha Mulungu?
▪ Kodi Yesu akupereka chilangizo chotani kuchotsa nakatande wakuchita mbanda ndi chigololo?
▪ Kodi Yesu akutanthauzanji pamene akunena za kutembenuzira tsaya lina?
▪ Kodi tingakhale motani angwiro monga Mulungu aliri wangwiro?
▪ Kodi ndimalangizo otani a pemphero amene Yesu akupereka?
▪ Kodi nchifukwa ninji chuma chakumwamba chiri choposa, ndipo chimapezedwa motani?
▪ Kodi ndimafanizo otani amene akuperekedwa kuthandiza munthu kupeŵa kukondetsa zinthu zakuthupi?
▪ Kodi nchifukwa ninji Yesu akunena kuti palibe chifukwa cha kudera nkhaŵa?
▪ Kodi Yesu akunenanji za kuŵeruza ena; komabe akusonyeza kuti ndimotani mmene ophunzira ake afunikira kugwiritsira ntchito luntha ponena za anthu?
▪ Kodi Yesu akupitiriza kunenanji ponena za pemphero, ndipo ndilamulo lanji la makhalidwe limene akupereka?
▪ Kodi ndimotani mmene Yesu akusonyezera kuti njira ya kumoyo sikakhala yosavuta ndi kuti pali upandu wa kunyengedwa?
▪ Kodi Yesu akumaliza motani ulaliki wake, ndipo ndichiyambukiro chotani chimene ukukhala nawo?