Mutu 37
Yesu Achotsa Chisoni cha Mkazi Wamasiye
MWAMSANGA atachiritsa mtumiki wa mkulu wa gulu lankhondo, Yesu akuchoka kumka ku Naini, mzinda wokhala pamtunda wa makilomitala 32 kummwera chakumadzulo kwa Kapernao. Ophunzira ake ndi khamu lalikulu akutsagana naye. Mwinamwake kuli chakumadzulo pamene akuyandikira dera la Naini. Kunoko akukumana ndi kagulu ka olira maliro. Mtembo wa mnyamata wina ukutulutsidwa kunja kwa mzinda kukaikidwa m’manda.
Mkhalidwe wa amake ngwochititsa chisoni kwambiri, popeza kuti iye ngwamasiye ndipo ameneyu ndiye mwana wake yekha. Pamene mwamuna wake anamwalira, iye anatonthozedwa ndi chenicheni chakuti anali ndi mwana wake wamwamuna. Ziyembekezo za mkaziyo, zikhumbo, ndi zolinganiza za mtsogolo zinazikidwa pa tsogolo la mwanayo. Koma tsopano palibe aliyense womtonthoza. Chisoni chakecho nchachikulu pamene anthu a m’tauniyo akutsagana naye kumka kunsitu.
Pamene Yesu awona mkaziyo, mtima wake ukugwidwa ndi chisoni chachikulu. Motero mwachikondi, komabe mwamphamvu imene imapereka chidaliro, iye akuti kwa iye: “Usalire.” Mkhalidwe wake ndi mchitidwe ukuchititsa chidwi khamulo. Chotero pamene akuyandikira ndi kukhudza chithatha chimene mtembowo wanyamulidwirapo, onyamula chithathawo akuima chiliri. Onse ayenera kudabwa ndi chimene ati achite.
Nzowona kuti awo amene ali limodzi ndi Yesu amuwona akuchiritsa mozizwitsa anthu ambiri okhala ndi nthenda. Koma mwachiwonekere iwo sanayambe amuwona akuukitsa aliyense kwa akufa. Kodi iye angachite chinthu chotero? Polankhula ndi mtembowo, Yesu akulamula kuti: “Mnyamata iwe, ndinena ndi iwe, Tauka.” Ndiyeno munthuyo akukhala tsonga! Iye akuyamba kulankhula, ndipo Yesu akumpereka kwa amake.
Pamene anthuwo awona kuti mnyamatayo ngwamoyodi, akuyamba kunena kuti: “Mneneri wamkulu wauka mwa ife.” Ena akuti: ‘Mulungu watembenuzira chisamaliro chake pa anthu ake.’ Mwamsanga mbiri yonena za chochitika chodabwitsachi ikufalikira m’Yudeya yense ndi m’dera lonse lozungulira.
Yohane Mbatizi adakali m’ndendebe, ndipo akufuna kudziŵa zowonjezereka ponena za ntchito zimene Yesu ali wokhoza kuchita. Ophunzira a Yohane akumuuza za zozizwitsa zimenezi. Kodi akulabadira motani? Luka 7:11-18.
▪ Kodi nchiyani chimene chikuchitika pamene Yesu akuyandikira Naini?
▪ Kodi ndimotani mmene Yesu akuyambukiridwira ndi zimene akuwona, ndipo kodi akuchitanji?
▪ Kodi ndimotani mmene anthu akulabadilira kuchozizwitsa cha Yesu?