Mutu 42
Yesu Adzudzula Afarisi
NGATI kuli mwamphamvu ya Satana imene iye amachotsera nayo ziŵanda, Yesu akutsutsa motero, pamenepo Satana ngwogaŵanika. “Ukakoma mtengo chipatso chake chomwe chikoma,” iye akupitiriza motero, “Ukaipa mtengo, chipatso chake chomwe chiipa pakuti ndi chipatso mtengo udziŵika.”
Ndiwo utsiru kunena kuti chipatso chabwimo cha kutulutsa ziŵanda chiri chotulukapo cha kuti Yesu akutumikira Satana. Ngati chipatsocho chiri chabwino, mtengo wake sungakhale woipa. Kumbali ina, chipatso choipa cha Afarisi cha zinenezo zosayenera ndi chitsutso chopanda maziko zochitidwa pa Yesu ndicho umboni wakuti iwo eni ali oipa. “Akubadwa inu a njoka,” Yesu akulengeza motero, “mungathe bwanji kulankhula zabwino, inu akukhala oipa? pakuti mkamwa mungolankhula mwa kusefuka kwake kwa mtima.”
Popeza kuti mawu athu amasonyeza mkhalidwe wa mitima yathu, zimene timanena zimapereka maziko a chiweruzo. “Ndinena kwa inu,” Yesu akutero, “kuti mawu onse opanda phindu amene anthu adzalankhula, adzaŵawerengera mlandu wake Tsiku Lakuweruza. Pakuti udzayesedwa wolungama ndi mawu ako, ndipo mawu ako omwe udzatsutsidwa.”
Mosasamala kanthu za ntchito zamphamvu za Yesu, alembi ndi Afarisiwo akupempha kuti: “Mphunzitsi, tifuna kuwona chizindikiro cha inu.” Ngakhale kuti anthu enieni ameneŵa ochokera ku Yerusalemu angakhale asanadziwonere zozizwitsa zake, umboni wowona ndi maso wozitsimikizira ulipo. Chotero Yesu akuuza atsogoleri Achiyuda kuti: “Akubadwa oipa achigololo afunafuna chizindikiro; ndipo sichidzapatsidwa kwa iwo chizindikiro, komatu chizindikiro cha Yona mneneri.”
Pofotokoza zimene akutanthauza, Yesu akupitiriza kuti: “Monga Yona anali m’mimba mwa chinsomba masiku atatu ndi usiku wake, chomwechonso Mwana wa munthu adzakhala mumtima mwa dziko lapansi masiku atatu ndi usiku wake.” Atamezedwa ndi chinsomba, Yona anatulukamo monga ngati kuti waukitsidwa kwa akufa, chotero Yesu akuneneratu kuti iye adzafa ndipo patsiku lachitatu adzaukitsidwa. Komabe, atsogoleri Achiyuda, ngakhale pambuyo poti Yesu waukitsidwa, akukana “chizindikiro cha Yona.”
Motero Yesu akunena kuti anthu a ku Nineve amene analapa pakulalikira kwa Yona adzauka panthaŵi ya chiweruzo kudzatsutsa Ayuda amene akukana Yesu. Mofananamo, iye akugwirizanitsanso ndi mfumukazi ya ku Seba, imene inadza kuchokera kudziko lakutali kudzamva nzeru ya Solomo ndi kuzizwa ndi zimene anawona ndi kumva. “Ndipo, wonani!” Yesu akusonyeza kuti, “wakuposa Solomo ali pano.”
Pamenepo Yesu akupereka fanizo la munthu amene mzimu wonyansa utuluka mwa iye. Komabe, munthuyo, sakudzadza malo opanda kanthuwo ndi zinthu zabwino, chotero iye akugwidwanso ndi mizimu ina yoipa isanu ndi iŵiri. “Kotero kudzakhalanso kwa oipa amakono,” Yesu akutero. Mtundu wa Israyeli unali utayeretsedwa ndipo unalandira kukonzedwanso—monga ngati kuchotsedwa kwakanthaŵi chabe kwa mzimu woipa. Koma kukana kwa mtunduwo aneneri a Mulungu, kukumakula m’kutsutsa kwake Kristu weniweniyo, kumavumbula mkhalidwe wawo woipawo kukhala woipitsitsa koposa chiyambi chake.
Pamene Yesu ali chilankhulire, amake ndi abale ake akufika nakhala kumapeto kwa khamulo. Chotero munthu wina akunena kuti: “Wonani, amayi wanu ndi abale anu aima pabwalo, akufunafuna kulankhula nanu.”
“Amayi wanga ndani? ndi abale anga ndi ayani?” Yesu akufunsa motero. Potansira dzanja lake kwa ophunzira ake, iye akuti: “Penyani amayi wanga ndi abale anga! Pakuti aliyense adzachita chifuniro cha Atate wanga wakumwamba, yemweyo ndiye mbale wanga, ndi mlongo wanga, ndi amayi wanga.” Mwanjira imeneyi Yesu akusonyeza kuti mosasamala kanthu za mmene mgwirizanowo uliri wamtengo wapatali umene umagwira ntchito kwa abale ake, wofunikadi kwambiri ndiwo unansi wake ndi ophunzira ake. Mateyu 12:33-50; Marko 3:31-35; Luka 8:19-21.
▪ Kodi Afarisi akulephera motani kupangitsa zonse ziŵiri “mtengo” ndi “chipatso” kukhala zabwino?
▪ Kodi nchiyani chimene chiri “chizindikiro cha Yona,” ndipo kodi ndimotani mmene chikukanidwira pambuyo pake?
▪ Kodi mtundu wa Israyeli wa m’zaka za zana loyamba ngwofanana motani ndi munthu amene mzimu woipa unatuluka mwa iye?
▪ Kodi ndimotani mmene Yesu akugogomezera unansi wake ndi ophunzira ake?