Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • gt mutu 69
  • Nkhani ya Utate

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Nkhani ya Utate
  • Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Nkhani Yofanana
  • Funso la Utate
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Kodi Atate Wawo Anali Abulahamu Kapena Mdyerekezi?
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Abulahamu Anali “Bwenzi” la Yehova
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
  • Kodi Abulahamu Anali Ndani?
    Nsanja ya Olonda—2012
Onani Zambiri
Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
gt mutu 69

Mutu 69

Nkhani ya Utate

MKATI mwa phwandolo, kukambitsirana kwa Yesu ndi atsogoleri Achiyudawo kukukula. “Ndidziŵa kuti muli mbewu ya Abrahamu,” Yesu akuvomereza, “koma mufuna kundipha ine, chifukwa mawu anga alibe malo mwa inu. Zimene ndinawona ine kwa Atate, ndilankhula; ndipo inunso muchita chimene mudamva kwa atate wanu.”

Ngakhale kuti sakudziŵikitsa atate wawo, Yesu akumveketsa bwino kuti atate wawo ali wosiyana ndi wake. Posadziŵa amene Yesu akumlingalira, atsogoleri Achiyudawo akuyankha kuti: “Atate wathu ndiye Abrahamu.” Iwo akulingalira kuti iwo ali ndi chikhulupiliro chofanana ndi cha Abrahamu, amene anali bwenzi la Mulungu.

Komabe, Yesu akuwadabwitsa ndi yankho lakuti: “Ngati muli ana a Abrahamu, mukadachita ntchito za Abrahamu.” Ndithudi, mwana weniweni amatsanzira atate wake. “Koma tsopano mufuna kundipha ine,” Yesu akutero, “ndine munthu amene ndinalankhula ndi inu chowonadi, chimene ndinamva kwa Mulungu; ichi Abrahamu sanachita.” Chotero Yesu akutinso: “Inu muchita ntchito za atate wanu.”

Iwo sakuzindikirabe za amene Yesu akunena. Iwo akudzinenerabe kuti ali ana a palamulo a Abrahamu, akumati: “Sitinabadwa ife m’chigololo.” Chifukwa cha chimenecho, podzinenera kukhala olambira owona mofanana ndi Abrahamu, akulengeza kuti: “Tiri naye Atate mmodzi ndiye Mulungu.”

Koma kodi Mulungu alidi Atate wawo? “Mulungu akadakhala Atate wanu,” Yesu akuyankha motero, “mukadakonda ine; pakuti ine ndinatuluka, ndi kuchokera kwa Mulungu; pakuti sindinadza kwa ine ndekha, koma iyeyu anandituma ine. Simuzindikira malankhulidwe anga chifukwa ninji?”

Yesu wayesa kusonyeza atsogoleri achipembedzo ameneŵa zotulukapo za kumkana kwawo. Koma tsopano iye akunena mosapita m’mbali kuti: “Inu muli ochokera mwa atate wanu Mdyerekezi, ndipo zolakalaka zake za atate wanu mufuna kuchita.” Kodi Mdyerekezi ali atate wamtundu wanji? Yesu akumdziŵikitsa iye kukhala wambanda ndiponso: “Ali wabodza, ndi atate wake wabodza.” Chotero Yesu akumaliza kuti: “Iye wochokera kwa Mulungu amva zonena za Mulungu; inu simumva chifukwa chakuti simuli a kwa Mulungu.”

Pokwiyitsidwa ndi chitsutso cha Yesu, Ayudawo akuyankha kuti: “Kodi sitinenetsa kuti inu ndinu Msamariya, ndipo muli ndi chiŵanda?” Liwu lakuti “Msamariya” limagwiritsiridwa ntchito monga liwu la chipongwe ndi kutonza, popeza Asamariya ndiwo anthu odedwa ndi Ayuda.

Ponyalanyaza chipongwe chawo chakuti iye ali Msamariya, Yesu akuyankha kuti: “Ndiribe chiŵanda ine; koma ndilemekeza Atate wanga, ndipo inu mundipeputsa.” Popitirizabe, Yesu akupereka lonjezo lowadabwitsa kuti: “Munthu akasunga mawu anga, sadzawona imfa nthaŵi yonse.” Zowona, Yesu sakutanthauza kuti omtsatira onsewo sadzawona imfa mwalingaliro lenileni. Mmalomwake, iye akutanthauza kuti sadzawona konse chiwonongeko chamuyaya, kapena “imfa yachiŵiri,” imene iribe chiukiliro.

Komabe, Ayudawo akutenga mawu a Yesu mosaphiphiritsa. Chifukwa cha chimenecho, iwo akuti: “Tsopano tazindikira kuti muli ndi chiŵanda. Abrahamu anamwalira, ndi aneneri; ndipo inu munena, Munthu akasunga mawu anga, sadzalaŵa imfa kunthaŵi yonse. Kodi inu ndinu wamkulu ndi atate wathu Abrahamu, amene anamwalira? ndipo aneneri anamwalira: mudziyesera nokha muli yani?”

M’kukambitsirana konseku, kuli kwachiwonekere kuti Yesu akusonyeza anthu ameneŵa chenicheni chakuti iye ali Mesiya wolonjezedwayo. Koma mmalo mwa kuyankha funso lawo mwachindunji ponena za amene iye ali, Yesu akuti: “Ngati ine ndidzilemekeza ndekha, ulemelero wanga uli chabe; Atate wanga ndiye wondilemekeza ine; amene munena za iye, kuti ndiye Mulungu wanu; ndipo inu simunamdziŵa iye; koma ine ndimdziŵa iye; ndipo ngati ndinena kuti sindimdziŵa iye, ndidzakhala wonama chimodzimodzi ndi inu.”

Popitirizabe, Yesu akusonyanso kwa Abrahamu wokhulupirikayo kuti: “Atate wanu Abrahamu anakondwera kuwona tsiku langa; ndipo anawona, nasangalala.” Inde ndi maso achikhulupiliro, Abrahamu anayang’ana kutsogolo kukufika kwa Mesiya wolonjezedwayo. Mosakhulupilira, Ayudawo akuyankha kuti: “Simunafikire zaka makumi asanu, ndipo munawona Abrahamu kodi?”

“Indetu, indetu, ndinena kwa inu,” Yesu akuyankha motero, “asanayambe kukhala Abrahamu ndipo ine ndiripo.” Ndithudi, Yesu akusonyeza kukukhalapo kwake asanakhale munthu monga munthu wauzimu wamphamvu kumwamba.

Atakwiyitsidwa ndi kudzinenera kwa Yesu kukhala atakhalako Abrahamu asanakhale, Ayudawo akutola miyala kuti amponye nayo. Koma iye akubisala natuluka m’kachisimo wosavulazidwa. Yohane 8:37-59; Chivumbulutso 3:14; 21:8.

▪ Kodi Yesu akusonyeza motani kuti iye ndi adani ake ali ndi atate osiyana?

▪ Kodi nchiyani chimene chiri tanthauzo la kutchula kwa Ayuda Yesu kuti Msamariya?

▪ Kodi ndim’lingaliro lotani limene Yesu akutanthauza pamene akunena kuti otsatira ake sadzawona imfa konse?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena