Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • gt mutu 79
  • Mtundu Wotayika, Koma Osati Wonse

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mtundu Wotayika, Koma Osati Wonse
  • Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Nkhani Yofanana
  • Mtundu Wotaika, Koma Osati Wonse
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Ayuda Ankayembekezera Kuwonongedwa
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Munthu Aliyense Adzakhala Patsinde pa Mkuyu Wake
    Nsanja ya Olonda—2003
  • Yesu Anagwiritsa Ntchito Mtengo wa Mkuyu Pophunzitsa Anthu za Chikhulupiriro
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
Onani Zambiri
Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
gt mutu 79

Mutu 79

Mtundu Wotayika, Koma Osati Wonse

MWAMSANGA pambuyo pa kukambitsirana kwa Yesu ndi amene anali atasonkhana kunja kwa nyumba ya Mfarisi, ena akumuuza “za Agalileya, amene [kazembe Wachiroma Pontiyo] Pilato anasanganiza mwazi wawo ndi nsembe zawo.” Agalileya ameneŵa mwinamwake ndiwo awo amene anaphedwa pamene Ayuda zikwi zambiri anatsutsa kugwiritsira ntchito kwa Pilato ndalama za m’nyumba yosungiramo m’kachisi kuti amangire ngalande yobweretsa madzi m’Yerusalemu. Awo amene akusimba nkhaniyi kwa Yesu angakhale akupereka lingaliro lakuti Agalileyawo anakanthidwa ndi tsokalo chifukwa cha ntchito za iwo eni zoipa.

Komabe, Yesu, akuwalungamitsa, nawafunsa kuti: “Kodi muyesa kuti Agalileya aja anali anthu akuchimwa koposa Agalileya onse, chifukwa anamva zowawa izi? Ndinena kwa inu, Iyayitu,” Yesu akuyankha motero. Ndiyeno iye akugwiritsira ntchito chochitikacho kuchenjezera Ayudawo kuti: “Koma ngati inu simutembenuka mtima, mudzawonongeka nonse momwemo.”

Popitiriza, Yesu akukumbutsa za tsoka lina lamomwemo, mwinamwake nlogwirizanitsidwanso ndi kumangidwa kwa ngalandeyo. Iye akufunsa kuti: “Kapena iwo aja khumi ndi asanu ndi atatu, amene nsanja yaitali ya m’Siloamu inawagwera, ndi kuwapha; kodi muyesa kuti iwo anali olakwa koposa anthu onse akukhala m’Yerusalemu?” Ayi, sichinali chifukwa cha kuipa kwa anthu ameneŵa kuti anafa, Yesu akutero. Mmalomwake, ‘nthaŵi ndi zochitika zosawonedweratu’ kaŵirikawiri ndizo ziri ndi thayo la matsoka oterowo. Komabe, Yesu, kachiŵirinso akugwiritsira ntchito chochitikacho kuchenjeza kuti: “Koma ngati simutembenuka mtima, mudzawonongeka nonse chimodzimodzi.”

Pamenepo Yesu akupitiriza kupereka fanizo loyenerera, akumafotokoza kuti: “Munthu wina anali ndi mkuyu wooka m’munda wake wamphesa. Ndipo anadza nafuna chipatso pa uwu, koma anapeza palibe. Ndipo anati kwa wosungira munda wamphesa, Tawona, zaka zapita zitatu ndimadza ine kudzafuna chipatso pamkuyu uwu, ndipo ndimapeza palibe: taulikha; uyeseranjinso nthaka yopanda pake? Ndipo iye anayankha nanena naye, Mbuye, baulekani ngakhale chaka chino chomwe, kufikira ndidzaukumbira kwete, ndithirepo ndowe; ndipo ngati udzabala chipatso kuyambira pamenepo, chabwino; koma ngati iyayi, mudzaulikhatu.”

Yesu wayesa kwa zaka zoposa zitatu kukulitsa chikhulupiliro pakati pa mtundu Wachiyuda. Koma ophunzira mazana oŵerengeka chabe angaŵerengeredwe monga chipatso cha ntchito zake. Tsopano, mkati mwa chaka chachinayi cha utumiki wake chimenechi, iye akukulitsa zoyesayesa zake, mwakukumba mophiphiritsira ndi kuthira ndowe mokweteza mtengo wamkuyu wa Ayudawo mwa kulalikira kwachangu ndi kuphunzitsa m’Yudeya ndi Pereya. Komabe mosaphula kanthu! Mtunduwo ukukana kulapa ndipo motero iwo uli panjira yomka kuchiwonongeko. Otsalira okha a mtunduwo akulabadira.

Mwamsanga pambuyo pake Yesu akuphunzitsa m’sunagoge pa Sabata. Mmenemo iye akuwona mkazi amene, chifukwa cha chiŵanda chosautsa, wakhala wothifuka kwa zaka 18. Mwachifundo, Yesu akunena naye kuti: “Mkaziwe, wamasulidwa kudwala kwako.” Polankhula zimenezo akuika dzanja lake pa iye, ndipo nthaŵi yomweyo iye akuwongoka ndi kuyamba kulemekeza Mulungu.

Komabe, mkulu wa sunagoge, wakwiya. “Alipo masiku asanu ndi limodzi, mmenemo anthu ayenera kugwira ntchito,” iye akutsutsa motero. “Chifukwa chake idzani kudzachiritsidwa momwemo, koma tsiku la Sabata ayi.” Motero mkuluyo akuvomereza mphamvu ya Yesu ya kuchiritsa koma akudzudzula anthuwo kaamba ka kudzachiritsidwa pa tsiku la Sabata!

“Onyenga inu,” Yesu akuyankha motero, “kodi munthu aliyense wa inu samaimasula ng’ombe yake, kapena bulu wake kuchodyeramo, tsiku la Sabata, kupita nayo kukaimwetsa madzi? Ndipo mkazi uyu, ndiye mwana wa Abrahamu, amene Satana anammanga, wonani, zaka khumi ndi zisanu ndi zitatu, nanga sikuyenera kodi, kuti amasulidwe nsinga yake imeneyi tsiku la Sabata?”

Eya, pakumva izi, otsutsa Yesuwo akuyamba kuchita manyazi. Komabe, khamulo, likusangalala ndi zinthu zonse za ulemelero zimene akuwona Yesu akuchita. Poyankha Yesu akubwereza mafanizo aŵiri aulosi onena za Ufumu wa Mulungu, amene iye ananena m’ngalaŵa pa Nyanja ya Galileya pafupifupi chaka chimodzi chapitacho. Luka 13:1-21; Mlaliki 9:11; Mateyu 13:31-33.

▪ Kodi ndimasoka otani amene panopa akutchulidwa, ndipo kodi ndiphunziro lotani limene Yesu akusonyeza?

▪ Kodi ndikugwiritsiridwa ntchito kotani kumene kungapangidwe ponena za mtengo wa mkuyu wosabala zipatso, ndiponso ponena za zoyesayesa za kuupangitsa kukhala wobala?

▪ Kodi ndimotani mmene mkulu wa sunagoge akuvomerezera luso la Yesu la kuchiritsa, komabe kodi ndimotani mmene Yesu akuvumbulira chiyengo cha munthuyo?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena