Mutu 81
Kuyesayesa Kowonjezereka kwa Kupha Yesu
POPEZA iri nthaŵi yachisanu, Yesu akuyenda mmalo otchingidwa odziŵika monga khumbi la Solomo. Liri m’mphepete mwa kachisi. Munomo Ayuda akumkweteza nayamba kunena kuti: “Kufikira liti musinkhitsasinkhitsa moyo wathu? ngati inu ndinu Kristu, tiuzeni momvekera.”
“Ndakuuzani,” Yesu akuyankha, “ndipo simukhulupirira.” Yesu sanawauze mwachindunji kuti iye anali Kristu, monga momwe anauzira mkazi wa ku Samariya pachitsime. Komabe, iye m’chenicheni, ananena za amene iye ali pamene anawafotokozera kuti anali wochokera kumwamba ndi kuti anakhalapo Abrahamu asanakhale.
Komabe, Yesu, akufuna kuti anthu azidziŵire okha kuti iye ndiye Kristu mwa kuyerekezera ntchito zake ndi zimene Baibulo linaneneratu kuti Kristu akachita. Ndicho chifukwa chake poyambirira analamulira ophunzira ake kusauza aliyense kuti iye anali Kristu. Ndipo ndicho chifukwa chake iye tsopano akupitirizabe kunena kwa Ayuda audani awa kuti: “Ntchitozi ndizichita Ine m’dzina la Atate wanga zimenezi zindichitira umboni. Koma inu simukhulupirira.”
Kodi nchifukwa ninji iwo sakhulupirira? Kodi nchifukwa cha kusoŵa umboni wakuti Yesu ndiye Kristu? Ayi, koma kaamba ka chifukwa chimene Yesu akupereka pamene awauza kuti: “Simuli a mwa nkhosa zanga. Nkhosa zanga zimamva mawu anga, ndipo ine ndizizindikira, ndipo zinditsata ine. Ndipo ine ndizipatsa moyo wosatha; ndipo sizidzawonongeka kunthaŵi yonse, ndipo palibe munthu adzazikwatula m’dzanja langa. Atate wanga, amene anandipatsa izo, ali wamkulu ndi onse, ndipo palibe wina angathe kuzikwatula m’dzanja la Atate.”
Pamenepo Yesu akufotokoza unansi wake wapafupi ndi Atate wake, akumati: “Ine ndi Atate ndife amodzi.” Popeza kuti Yesu ali padziko lapansi ndipo Atate wake ali kumwamba, mwachiwonekere iye sakunena kuti iye ndi Atate wake ali kwenikweni amodzi, kapena thupi limodzi. Mmalomwake, iye akutanthauza kuti iwo ali amodzi m’chifuno, kuti ngogwirizana.
Atakwiya ndi mawu a Yesu, Ayudawo akutola miyala kuti amuphe, monga momwe adachitira poyambirirapo, panthaŵi ya Phwando la Mahema kapena Misasa. Molimba mtima poyang’anizana ndi ofuna kumupha mwambandawo, Yesu akuti: “Ndakuwonetsani inu ntchito zabwino zambiri za kwa Atate; chifukwa cha ntchito iti ya izo mundiponya miyala?”
“Chifukwa cha ntchito yabwino sitikukuponyani miyala,” iwo akutero, “koma chifukwa chamwano; ndi kuti inu, muli munthu, mudziyesera nokha Mulungu.” Popeza kuti Yesu sanadzinenere kukhala mulungu, kodi nchifukwa ninji Ayuda akunena zimenezi?
Mwachiwonekere chiri chifukwa chakuti Yesu akunena kuti ali ndi mphamvu zimene iwo akhulupirira kuti ziri za Mulungu chabe. Mwachitsanzo, iye wangonena kumene za “nkhosa,” kuti “ndizipatsa moyo wosatha,” zimene ziri kanthu kena kamene munthu aliyense sangachite. Komabe, Ayudawo akunyalanyaza chenicheni chakuti Yesu akuvomereza kukhala akulandira ulamulirowo kuchokera kwa Atate wake.
Kuti Yesu akunena kuti ngwamng’ono kuposa Mulungu, iye kenaka akusonyeza mwakufunsa kuti: “Kodi sikulembedwa m’Chilamulo chanu [Salmo 82:6], Ndinati ine, Muli milungu? Ngati anawatcha milungu iwo amene mawu a Mulungu anawadzera, . . . kodi inu munena za iye, amene Atate anampatula namtuma kudziko lapansi, Uchita mwano, chifukwa ndinati, Ndiri Mwana wa Mulungu?”
Popeza kuti Malemba amatcha oweruza aumunthu osalungama kuti “milungu,” kodi nchifukwa chotani chimene Ayuda ameneŵa angapezere Yesu chifukwa cha kunena kuti, “Ndiri Mwana wa Mulungu”? Yesu akuwonjezera kuti: “Ngati sindichita ntchito za Atate wanga musakhulupirira ine. Koma ngati ndichita, mungakhale simukhulupirira ine, khulupirirani ntchitozo; kuti mukadziŵe ndi kuzindikira kuti Atate ali mwa ine ndi ine mwa Atate.”
Pamene Yesu anena izi, Ayuda akuyesa kumgwira. Koma iye akuthaŵa monga momwe anachitira poyambilirapo pa Phwando la Mahema. Iye akuchoka ku Yerusalemu ndi kuwoloka Mtsinje wa Yordano kumene Yohane anayamba kubatiza pafupifupi zaka zinayi zapitazo. Mwachiwonekere malo ameneŵa sali patali ndi gombe lakummwera kwa Nyanja ya Galileya, ulendo wamasiku aŵiri kapena chapompo kuchokera ku Yerusalemu.
Anthu ambiri akufika kwa Yesu pamalo ameneŵa nayamba kunena kuti: “Sanachita chizindikiro Yohane; koma zinthu zirizonse Yohane ananena za iye zinali zowona.” Motero kunoko ambiri akukhulupirira Yesu. Yohane 10:22-42; 4:26; 8:23, 58; Mateyu 16:20.
▪ Kodi Yesu akufuna kuti anthu adziŵe iye monga Kristu mwanjira yotani?
▪ Kodi Yesu ndi Atate wake ali amodzi motani?
▪ Mwachiwonekere, kodi nchifukwa ninji Ayuda, akunena kuti Yesu akudzipanga kukhala Mulungu?
▪ Kodi ndimotani mmene kugwira mawu Masalmo kwa Yesu kumasonyezera kuti iye sakunena kuti ngwolingana ndi Mulungu?