Mutu 89
Ulendo Wokasonyeza Chifundo m’Yudeya
MILUNGU ingapo yapitayo, panthaŵi ya Phwando la Kukonzanso mu Yerusalemu, Ayuda anayesa kupha Yesu. Chotero iye anamka kumpoto, mwachiwonekere kuchigawo chimene sichinali kutali ndi Nyanja ya Galileya.
Posachedwapa, wakhala akumkanso kummwera molunjika Yerusalemu, akumalalikira m’njiramo m’midzi ya Pereya, chigawo cha kummaŵa kwa Mtsinje wa Yordano. Atatha kusimba fanizo la munthu wachuma ndi Lazaro, iye akupitirizabe kuphunzitsa ophunzira ake zinthu zimene anawaphunzitsa pachiyambiyambipo pamene anali mu Galileya.
Mwachitsanzo, kuti, kukakhala bwino kwambiri kwa munthu ‘ngati mphero inakoloŵekedwa m’khosi mwake naponyedwa m’nyanja’ koposa kuti iye achititse mmodzi wa ‘aang’ono’ a Mulungu kukhumudwa. Iye akugogomezeranso kufunika kwa kukhululukira, akumafotokoza kuti: “Ndipo akakuchimwira [mbale] kasanu ndi kaŵiri pa tsiku lake, nakakutembenukira kasanu ndi kaŵiri ndi kunena, Ndalapa ine; uzimkhululukira.”
Pamene ophunzirawo apempha kuti, “Mutiwonjezere chikhulupiriro,” Yesu akuyankha kuti: “Mukakhala nacho chikhulupiriro ngati kambewu kampiru, mukanena kwa mtengo uwu wamkuyu, Uzulidwe, nuwokedwe m’nyanja; ndipo ukadamvera inu.” Chotero ngakhale chikhulupiriro chochepa chingachite zinthu zazikulu.
Kenako, Yesu akusimba mkhalidwe weniweni wamoyo umene umafotokoza mwafanizo kaimidwe kamaganizo koyenerera ka mtumiki wa Mulungu wamphamvuyonse. “Koma ndani mwa inu ali naye kapolo wolima, kapena woŵeta nkhosa,” Yesu akutero, “amene pobwera iye kuchokera kumunda adzanena kwa iye, Loŵa tsopano, khala pansi kudya; wosanena naye makamaka, Undikonzere chakudya ine, nudzimangire, nunditumikire kufikira ndadya ndi kumwa; ndipo nditatha ine udzadya nudzamwa iwe? Kodi ayamika kapoloyo chifukwa anachita zolamulidwa? Chotero inunso mmene mutachita zonse anakulamulirani, nenani, ife ndife akapolo opanda pake, tangochita zimene tiyenera kuzichita.” Motero, atumiki a Mulungu sayenera kulingalira kuti akuchitira ubwino Mulungu mwa kumtumikira. Mmalomwake, iwo ayenera kukumbukira nthaŵi zonse mwaŵi umene ali nawo wa kumlambira monga ziŵalo zokhulupirika za banja lake.
Mwachiwonekere kuli mwamsanga Yesu atasimba fanizo limeneli kuti mthenga wina akufika. Iye anatumidwa ndi Mariya ndi Marita, alongo ake a Lazaro, amene amakhala ku Betaniya wa Yudeya. “Ambuye, wonani, amene mumkonda adwala,” akutero wamthengayo.
Yesu akuyankha kuti: “Kudwala kumene sikuli kwa imfa, koma chifukwa cha ulemerero wa Mulungu, kuti Mwana wa Mulungu alemekezedwe nako.” Atakhala masiku aŵiri kumene iye ali, Yesu akuti kwa ophunzira ake: “Tiyeni tipitenso ku Yudeya.” Komabe, iwo akumkumbutsa kuti: “Ambuye, Ayuda analikufuna kukuponyani miyala tsopano apa; ndipo mumukanso komweko kodi?”
“Kodi sikuli maora khumi ndi aŵiri usana?” Yesu akufunsa powayankha. “Ngati munthu ayenda usana sakhumudwa, chifukwa apenya kuunika kwa dziko lino lapansi. Koma ngati munthu ayenda usiku, akhumudwa, chifukwa mulibe kuunika mwa iye.”
Mwachiwonekere zimene Yesu akutanthauza nzakuti ‘maora amasana,’ kapena nthaŵi imene Mulungu wagaŵira kaamba ka uminisitala wa padziko lapansi wa Yesu, sinathe ndipo kufikira iyo itatero palibe munthu amene angamuvulaze. Iye afunikira kugwiritsira ntchito mokwanira nthaŵi yomtsalira ya “usana,” pakuti pambuyo pake “usiku” uzadza pamene adani adzakhala atamupha.
Yesu akuwonjezera kuti: “Lazaro bwenzi lathu ali m’tulo; koma ndimuka kukamuukitsa iye tulo take.”
Mwachiwonekere polingalira kuti Lazaro wagona tulo ndi kuti ichi chiri chizindikiro chotsimikizirika chakuti adzachira, ophunzirawo akuyankha kuti: “Ambuye, ngati ali m’tulo adzachira.”
Pamenepo Yesu akuwauza momvekera bwino kuti: “Lazaro wamwalira. Ndipo ndikondwera chifukwa cha inu kuti kunalibe ine komweko, chakuti mukakhulupirire; koma tiyeni, tipite kwa iye.”
Pozindikira kuti Yesu angaphedwe m’Yudeya, komabe pokhumba kumchirikiza, Tomasi akulimbikitsa anzake kuti: “Tipite ifenso kuti tikafere naye pamodzi.” Chotero moika paupandu miyoyo yawo, ophunzirawo akutsagana ndi Yesu paulendo wake wokasonyeza chifundo umenewu wa ku Yudeya. Luka 13:22; 17:1-10; Yohane 10:22, 31, 40-42; 11:1-16.
▪ Kodi Yesu wakhala akulalikira kuti posachedwapa?
▪ Kodi ndiziphunzitso zotani zimene Yesu akubwereza, ndipo ndi mkhalidwe wowona wa moyo wotani umene iye akufotokoza kuchitira fanizo mfundo iti?
▪ Kodi ndimbiri yotani imene Yesu akulandira, ndipo kodi iye akutanthauzanji mwakunena kuti “usana” ndipo “usiku”?
▪ Kodi Tomasi akutanthauzanji pamene anena kuti, “Tipite ifenso kuti tikafere naye pamodzi”?