Mutu 92
Akhate Khumi Achiritsidwa Mkati mwa Ulendo Wotsirizira wa Yesu Womka ku Yerusalemu
YESU akulepheretsa zoyesayesa za Sanhedrin za kumupha mwa kuchoka mu Yerusalemu kumka kumzinda wa Efraimu, mwinamwake makilomitala 24 okha kapena chapompo chakumpoto kummaŵa kwa Yerusalemu. Kumeneko akukhalako iye ndi ophunzira ake, kutali ndi adani ake.
Komabe, nthaŵi ya Paskha wa 33 C.E. ikuyandikira, ndipo mwamsanga Yesu ali paulendonso. Iye akudzera mu Samariya ndi kukwera kuloŵa mu Galileya. Uwu ndiwo ulendo wake womalizira kuchigawo chimenechi imfa yake isanachitike. Akali m’Galileya, mwachiwonekere iye ndi ophunzira ake akugwirizana ndi ena amene akupita ku Yerusalemu kuphwando la Paskha. Iwo akutenga njira yodzera m’chigawo cha Pereya, kummaŵa kwa Mtsinje wa Yordano.
Kuchiyambiyambi kwa ulendowo, pamene Yesu akuloŵa m’mudzi kaya wa Samariya kapena wa Galileya, iye akukumana ndi amuna khumi amene ali ndi khate. Nthenda yowopsa imeneyi imadya ziŵalo zamunthu pang’onopang’ono—zala zake zakumanja, zala zake zakumiyendo, makutu ake, mphuno yake, ndi milomo yake. Kutetezera ena kuti asayambukiridwe, Chilamulo cha Mulungu chimati ponena za wakhate: “Namphimbe iye mlomo wake wa m’mwamba, nafuule, Wodetsedwa, wodetsedwa! Masiku onse nthenda ikali pa iye azikhala wodetsedwa. . . . agone payekha.”
Akhate khumiwo amalabadira ziletso za Chilamulo kwa akhate ndipo akuimilira patali ndi Yesu. Koma, iwo akufuula ndi mawu aakulu kuti: “Mbuye, mutichitire chifundo.”
Powawonera patali, Yesu akuwalamula kuti: “Pitani, kadziwonetseni nokha kwa ansembe.” Yesu akunena izi chifukwa chakuti Chilamulo cha Mulungu chimaloleza ansembe kulengeza akhate amene achiritsidwa kukhala atachira panthenda yawoyo. Mwanjira iyi anthu otere amaloledwa kukakhalanso ndi anthu athanzi labwino.
Akhate khumiwo ali ndi chidaliro mumphamvu zozizwitsa za Yesu. Chotero iwo akumka mofulumira kwa ansembe, ngakhale kuti iwo sanachiritsidwebe. Ali panjira, chikhulupiriro chawo mwa Yesu chikufupidwa. Iwo akuyamba kuwona ndi kumva thanzi lawo lobwezeretsedwa!
Asanu ndi anayi mwa akhate ochiritsidwawo akupitirizabe ulendo wawo, koma wakhate mmodzi, m’Samariya, akubwerera kukafunafuna Yesu. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti iye akuyamikira kwambiri ponena za zimene zamchitikira. Iye akutamanda Mulungu ndi mawu ofuula, ndipo pamene apeza Yesu, akugwera pamapazi ake, akumamthokoza.
Poyankha Yesu akuti: “Kodi sanakonzedwa khumi? koma, ali kuti asanu ndi anayi aja? Akubwera kulemekeza Mulungu sanapezeka mmodzi kodi, koma mlendo uyu?”
Pamenepo iye akuuza mwamuna wa ku Samariya ameneyo kuti: “Nyamuka; nupite, chikhulupiriro chako chakupulumutsa iwe.”
Pamene tiŵerenga za kuchiritsa akhate khumiwo kochitidwa ndi Yesu tiyenera kulabadira phunziro lopereka tanthauzo ndi funso lake lakuti: “Koma ali kuti asanu ndi anayi aja?” Kusayamikira kumene kunasonyezedwa ndi asanu ndi anayiko ndiko cholakwa chachikulu. Kodi ife, mofanana ndi m’Samariyayo tidzasonyeza kukhala oyamikira kaamba ka zinthu zimene timalandira kuchokera kwa Mulungu, kuphatikizapo lonjezo la moyo wosatha m’dziko latsopano lolungama la Mulungu? Yohane 11:54, 55; Luka 17:11-19; Levitiko 13:16, 17, 45, 46; Chivumbulutso 21:3, 4.
▪ Kodi Yesu akulepheretsa motani zoyesayesa za kumupha?
▪ Kodi kenako Yesu akumka kuti, ndipo kodi ulendo wakewo ngwakuti?
▪ Kodi nchifukwa ninji akhate akuima patali, ndipo kodi nchifukwa ninji Yesu akuwauza kupita kwa ansembe?
▪ Kodi ndi phunziro lotani limene tiyenera kuphunzira kuchokera m’chochitika chimenechi?