Mutu 95
Maphunziro Onena za Chisudzulo ndi Kukonda Ana
YESU ndi ophunzira ake ali paulendo wawo wa ku Yerusalemu kuti akakhale nawo pa Paskha wa 33 C.E. Iwo akuwoloka Mtsinje wa Yordano ndi kulondola njira yodutsa chigawo cha Pereya. Yesu anali m’Pereya masabata ochepekera apapitawo, koma tsopano iye anaitanidwa ku Yudeya chifukwa chakuti bwenzi lake Lazaro anadwala. Adakali ku Pereyako, Yesu adalankhula kwa Afarisi za chisudzulo, ndipo tsopano akudzutsa nkhaniyo kachiŵirinso.
Pakati pa Afarisi pali anthu a zikhulupiliro zosiyanasiyana zonena za lingaliro la chisudzulo. Mose ananena kuti mkazi akanasudzulidwa chifukwa cha ‘kanthu kosayenera mwa iye.’ Ena amakhulupilira kuti izi zimasonya kokha kuchisembwere. Koma ena amalingalira kuti “kanthu kosayenera” kameneko kamaphatikizapo machimo aang’ono kwambiri. Chotero, kuti ayese Yesu, Afarisiwo akufunsa kuti: “Kodi nkuloledwa kuti munthu achotse mkazi wake pa chifukwa chirichonse?” Iwo ali ndi chidaliro chakuti zirizonse zimene Yesu adzanena zidzamloŵetsa m’vuto kwa Afarisiwo amene ali ndi lingaliro losiyana.
Yesu akuyankha funsolo mwaluso, popanda kufunsira lingaliro laumunthu lirilonse, koma kusonya kumpangidwe woyambilira wa ukwati. “Kodi simunaŵerenga,” iye akufunsa motero, “kuti iye amene adalenga anthu pachiyambi, anawalenga iwo mwamuna ndi mkazi, nati, Chifukwa cha ichi mwamuna adzasiya atate wake ndi amake, nadzaphatikizana ndi mkazi wake, ndipo aŵiriwo adzakhala thupi limodzi? chotero kuti salinso aŵiri koma thupi limodzi. Chifukwa chake ichi chimene Mulungu anachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.”
Chifuno choyambilira cha Mulungu, Yesu akusonyeza motero, ndicho chakuti anthu okwatirana amamatirane pamodzi, kuti asasudzulane. Ngati zimenezi ziri choncho, Afarisiwo akufunsa kuti, “nanga chifukwa ninji Mose analamulira kupatsa kalata wa chilekaniro, ndi kumchotsa?”
“Chifukwa cha kuuma mitima kwanu, Mose anakulolezani kuchotsa akazi anu,” Yesu akuyankha motero, “koma pachiyambi sikunakhala chomwecho.” Inde, pamene Mulungu anakhazikitsa muyezo wowona wa ukwati m’munda wa Edene, iye sanapange makonzedwe a chisudzulo.
Yesu akupitirizabe kuuza Afarisiwo kuti: “Ndinena kwa inu, Amene aliyense akachotsa mkazi wake, kosakhala chifukwa cha chigololo, [kuchokera m’Chigriki, por·neiʹa], nadzakwatira wina, achita chigololo.” Iye mwakutero akusonyeza kuti por·neiʹa, amene ali kugonana koipitsitsa kwa makhalidwe achisembwere, ali kokha maziko ovomerezeka ndi Mulungu a chisudzulo.
Pozindikira kuti ukwati uyenera kukhala mgwirizano wosatha kusiyapo kokha pamaziko a chisudzulo ameneŵa, ophunzirawo akusonkhezereka kunena kuti: “Ngati mlandu wa munthu ndi mkazi wake uli wotere, sikuli kwabwino kukwatira.” Palibe chikayikiro chakuti munthu amene akulingalira za ukwati ayenera kulingalira mwamphamvu zauchikhalire wa chomangira cha ukwati!
Yesu akupitiriza kunena za umbeta. Iye akufotokoza kuti anyamata ena amabadwa ali mfule, kukhala osakhoza kukwatira chifukwa cha kusakhala okhoza kugonana. Ena anawafula anthu, akumakhala opundulidwa mpheto mwankhanza. Pomaliza, ena amatsendereza chikhumbo cha kukwatira ndi cha kusangalala ndi maunansi a kugonana kotero kuti athe kudzipereka mokwanira kuzinthu za Ufumu wakumwamba. “Amene angathe kulandira ichi [umbeta], achilandire,” Yesu akumaliza motero.
Tsopano anthu akuyamba kudzetsa tiana tawo kwa Yesu. Komabe, ophunzira, akudzudzula tianato ndi kuyesa kutichotsa, mosakayikira akufuna kutetezera Yesu kukutsenderezeka kosafunikira. Koma Yesu akuti: “Lolani tiana tidze kwa ine; musatiletse: pakuti Ufumu wa Mulungu uli wa totere. Ndithu ndinena ndi inu, Munthu aliyense wosalandira Ufumu wa Mulungu ngati kamwana, sadzaloŵamo konse.”
Ndiphunziro labwino kwambiri chotani nanga limene Yesu akupereka! Kuti tiloŵe Ufumu wa Mulungu, tiyenera kutsanzira kudzichepetsa ndi kuphunzitsika kwa ana achichepere. Koma chitsanzo cha Yesu chimachitiranso fanizo mmene kuliri kofunika, makamaka kwa makolo, kuthera nthaŵi ndi ana awo. Tsopano Yesu akusonyeza chikondi chake kwa tianato mwa kutiyangata ndi kutidalitsa. Mateyu 19:1-15; Deuteronomo 24:1; Luka 16:18; Marko 10:1-16; Luka 18:15-17.
▪ Kodi ndilingaliro losiyana lotani limene Afarisi ali nalo pa chisudzulo, ndipo motero kodi ndimotani mmene akuyesera Yesu?
▪ Kodi Yesu akuchita motani ndi zoyesayesa za Afarisi za kumyesa, ndipo kodi akusonyezanji monga maziko okha a chisudzulo?
▪ Kodi nchifukwa ninji ophunzira a Yesu akunena kuti sikuli bwino kukwatira, ndipo ndichivomerezo chotani chimene Yesu akupereka?
▪ Kodi Yesu amatiphunzitsanji pakuchita kwake ndi ana aang’ono?