Mutu 99
Yesu Aphunzitsa ku Yeriko
MWAMSANGA Yesu ndi makamu oyenda naye limodzi akufika ku Yeriko, umene uli mzinda wokhala pamtunda wa ulendo wa tsiku limodzi kuchokera ku Yerusalemu. Mwachiwonekere Yeriko uli mzinda wa mbali ziŵiri, mzinda wakale Wachiyuda wokhala pafupifupi mtunda kilomitala imodzi ndi theka kuchokera m’mzinda watsopano wa Aroma. Pamene makamuwo atuluka mumzinda wakalewo ndi kuyandikira watsopano, akhungu aŵiri opemphapempha akumva phokoso. Mmodzi wa iwo dzina lake ndilo Bartimeyu.
Pakumva kuti Yesu ndiye amene akudutsa, Bartimeyu ndi mnzake winayo akuyamba kufuula kuti: “Mutichitire ife chifundo, inu Mwana wa Davide!” Pamene khamulo liwauza mwamphamvu kutonthola, iwo akufuula ngakhale mowonjezereka ndi mawu aakulu kuti: “Ambuye, mutichitire chifundo, inu Mwana wa Davide!”
Pomva phokosolo, Yesu akuima. Iye akupempha awo amene akuyenda naye kuti aitane anthu amene akufuulawo. Ameneŵa akupita kwa opemphapempha akhunguwo nati kwa mmodzi wa iwo: “Limba mtima nyamuka, akuitana.” Limodzi ndi chikondwerero chachikulu, munthu wakhunguyo akutaya chovala chake chakunja, nanyamuka, ndi kumka kwa Yesu.
“Mufuna kuti ndikuchitireni chiyani?” Yesu akufunsa.
“Ambuye, kuti maso athu apenye,” amuna aŵiri akhunguwo akuchondelera.
Pomva chisoni, Yesu akukhudza maso awo. Malinga nkunena kwa cholembedwa cha Marko, Yesu akuti kwa mmodzi wa iwo: “Muka; chikhulupiriro chako chakupulumutsa iwe.” Nthaŵi yomweyo akhungu opemphapemphawo akupenya, ndipo mosakayikira aŵiriwo akuyamba kulemekeza Mulungu. Pamene anthu onse awona zimene zachitika, nawonso akutamanda Mulungu. Popanda kuchedwa, Bartimeyu ndi mnzakeyo akuyamba kutsata Yesu.
Pamene Yesu akudutsa m’Yeriko, makamuwo ngaakulu kwambiri. Aliyense akufuna kuwona munthu amene wachiritsa amuna akhungu aja. Anthu akudza kwa Yesu kuchokera kumbali zonse, ndipo monga chotulukapo, ena sangathe ngakhale kumsuzumira. Pakati pa ameneŵa pali Zakeyu, mkulu wa amisonkho mkati ndi kunja kwa Yeriko. Iye ngwamfupi kwambiri koti sangawone zimene zikuchitika.
Chotero Zakeyu akuthamangira kutsogolo kuti akakwere mumtengo wamkuyu umene uli m’njira imene Yesu akudzera. Kuchokera pamwamba pamenepo, iye angathe kuwona zonse. Pamene makamuwo ayandikira, Yesu akumuitana kuchoka mumtengowo nati: “Zakeyu, fulumira, nutsike; pakuti lero ndiyenera kukhala m’nyumba mwako.” Zakeyu akutsika ndi chikondwerero ndipo akufulumira kumka kunyumba kukakonzekerera mlendo wake wolemekezeka.
Komabe, pamene anthu akuwona zimene zikuchitika, iwo onse akuyamba kudandaula. Iwo kulingalira zimenezi kukhala zosayenera kuti Yesu akhale mlendo wa munthu woteroyo. Mwawona nanga, Zakeyu anafikira kukhala wolemera mwakulanda ndalama kosawona mtimako m’ntchito yake yokhometsa msonkho.
Anthu ambiri akutsatira, ndipo pamene Yesu aloŵa m’nyumba ya Zakeyu, iwo akudandaula kuti: “Analoŵa amchereze munthu ali wochimwa.” Komabe Yesu akuwona mwa Zakeyu kuthekera kwa kulapa. Ndipo Yesu ali wosagwiritsidwa mwala, popeza kuti Zakeyu akuimilira ndi kulengeza kuti: “Tawonani Ambuye, gawo limodzi la zanga zonse zogaŵika pakati ndipatsa osauka; ndipo ngati ndalanda kanthu kwa munthu monyenga, ndimbwezera kanayi.”
Zakeyu akupereka umboni wakuti kulapa kwake nkowona mtima mwa kupatsa theka la zinthu zake kwa osauka ndi mwa kugwiritsira ntchito theka lina kubwezera awo amene iye anawabera. Mwachiwonekere iye angaŵerengere mtengowo kuchokera m’zolembapo zake za msonkho kuti ndindalama zingati zimene ali nazo mangaŵa ndi anthu ameneŵa. Chotero iye akulumbira kubwezera kuŵirikiza kanayi, mogwirizana ndi lamulo la Mulungu limene limati: ‘Ngati munthu ataba nkhosa, iye ayenera kubwezera ndi nkhosa zinayi kaamba ka nkhosa imodzi.’
Yesu akukondwera ndi njira imene Zakeyu akulonjeza ya kugaŵira zinthu zake, pakuti Iye akuti: “Lero chipulumutso chagwera nyumba iyi, popeza iyenso ndiye mwana wa Abrahamu. Pakuti Mwana wa munthu anadza kufunafuna ndi kupulumutsa chotayikacho.”
Osati kale kwambiri, Yesu anafotokoza mwa fanizo mkhalidwe wa ‘otayika’ m’fanizo lake lonena za mwana woloŵelera. Tsopano tiri ndi chitsanzo chenicheni chamoyo wa munthu wotayika amene wapezedwanso. Ngakhale kuti atsogoleri achipembedzo ndi awo amene amawatsatira akung’ung’udza ndi kudandaula ponena za chisamaliro cha Yesu pa anthu onga Zakeyu, Yesu akupitirizabe kufunafuna ndi kubwezeretsa ana otayika ameneŵa a Abrahamu. Mateyu 20:29-34; Marko 10:46-52; Luka 18:35–19:10; Eksodo 22:1.
▪ Mwachiwonekere, kodi nkuti, kumene Yesu akukumana ndi akhungu opemphapempha, ndipo akuwachitiranji?
▪ Kodi Zakeyu ndani, ndipo kodi nchifukwa ninji akukwera mumtengo?
▪ Kodi Zakeyu akupereka umboni wa kulapa kwake motani?
▪ Kodi ndiphunziro lanji limene tingaphunzire m’kuchita kwa Yesu ndi Zakeyu?