Mutu 100
Fanizo la Ndalama
MWINAMWAKE Yesu adakali panyumba ya Zakeyu, pamene waima paulendo wake womka ku Yerusalemu. Ophunzira ake akukhulupilira kuti pamene afika ku Yerusalemu, iye adzalengeza kuti ndiye Mesiya ndi kukhazikitsa Ufumu wake. Kuti alungamitse lingaliro limeneli ndi kusonyeza kuti Ufumuwo udakali patalibe, Yesu akupereka fanizo.
“Munthu wa fuko lomveka,” iye akusimba, “ananka kudziko lakutali, kudzilandilira yekha ufumu, ndi kubwerako.” Yesu ndiye “munthu wa fuko lomveka,” ndipo kumwamba ndiko “dziko lakutali.” Pamene Yesu afika kumeneko, Atate wake adzampatsa mphamvu zaufumu.
Komabe, asananyamuke, munthu wa fuko lomvekayo akuitana akapolo khumi ndi kuwapatsa aliyense wa iwo ndalama khumi, akumati: “Chita nazoni malonda kufikira ndibweranso.” Akapolo khumiwo m’kukwaniritsidwa koyamba amaimira ophunzira a Yesu oyambilira. M’kukwaniritsa kokulirapo, amaphiphiritsira awo onse amene ali oloŵa nyumba oyembekezeredwa limodzi naye mu Ufumu wakumwamba.
Ndalama khumi ndizo tizidutswa tamtengo wapatali ta ndalama, kalikonse kali kolingana ndi mtengo wa malipiro apafupifupi miyezi itatu a ogwira ntchito yaulimi. Koma kodi ndalama khumizo zimaimiranji? Ndipo kodi ndimalonda anji amene akapolowo ayenera kuchita nazo?
Ndalama khumi zimaimira chuma chimene ophunzira obadwa ndi mzimu akagwiritsira ntchito potulutsa oloŵa nyumba ena a Ufumu wakumwamba owonjezereka kufikira pamene Yesu akadza monga Mfumu mu Ufumu wolonjezedwa. Pambuyo pa chiukiriro chake ndi kuwonekera kwa ophunzira ake, iye anawapatsa ndalama khumi zophiphiritsira kuti apangire nazo ophunzira owonjezereka ndipo motero kuwonjezera kukagulu ka oloŵa Ufumu wakumwamba.
“Koma,” Yesu akupitiriza, “mfulu za pamudzi pake zinamuda [munthu wa fuko lomvekayo], nizituma akazembe amtsate m’mbuyo ndi kunena, Ife sitifuna munthuyu akhale mfumu yathu.” Mfuluzo ndizo Aisrayeli, kapena Ayuda, kusiyapo ophunzira ake. Yesu atachoka kumka kumwamba, Ayuda ameneŵa mwa kuzunza kwawo ophunzira ake anasonyeza kuti sanamfune iye kukhala mfumu yawo. Mwanjira imeneyi iwo anali kuchita mofanana ndi nzika zimene zinatuma akazembe.
Kodi akapolo khumiwo akugwiritsira ntchito motani ndalama khumi zawozo? Yesu akufotokoza kuti: “Ndipo kunali pakubwera iye, atalandira ufumuwo, anati aitanidwe kwa iye akapolo aja, amene adawapatsa ndalamazo, kuti adziŵe umo anapindulira pochita malonda. Ndipo anafika woyamba, nanena, Mbuye ndalama yanu inachita niwonjeza ndalama khumi. Ndipo anati kwa iye, Chabwino, kapolo wabwino iwe; popeza unakhala wokhulupirika m’chaching’onong’ono, khala nawo ulamuliro pamidzi khumi. Ndipo anadza wachiŵiri, nanena, Ambuye, ndalama yanu yapindula ndalama zisanu. Ndipo anati kwa iyenso, Khala iwenso woweruza midzi isanu.”
Kapolo wokhala ndi ndalama khumiyo amaphiphiritsira kagulu, kapena gulu, la ophunzira kuyambira pa Pentekoste wa 33 C.E. kufikira tsopano limene limaphatikizapo atumwi. Kapolo amene anapindula ndalama zisanu nayenso amaimira kagulu kokhala mkati mwanyengo yofananayo kamene, malinga ndi mwaŵi wawo ndi maluso, amawonjezera chuma cha mfumu yawo padziko lapansi. Timagulu tiŵiri tonseto timalalikira mbiri yabwino mwachangu, ndipo monga chotulukapo, amitima yowongoka ambiri amakhala Akristu. Asanu ndi anayi a akapolowo anachita malondawo mwachipambano ndi kuwonjezera chuma chawo.
“Ndipo,” Yesu akupitirizabe kuti, “wina anadza, nanena, Mbuye, tawonani, siyi ndalama yanu, ndaisunga m’kansalu; pakuti ndikuwopani, popeza inu ndinu munthu wouma mtima: munyamula chimene simunachiika pansi, mututa chimene simunachifesa. Ananena kwa iye, Pakamwa pako ndikuweruza, kapolo woipa iwe. Unadziŵa kuti ine ndine munthu wouma mtima, wonyamula chimene sindinachiika, ndi wotuta chimene sindinachifesa; ndipo sunapereka bwanji ndalama yanga pokongoletsa ndipo ine pakudza ndikadaitenga ndi phindu lake? Ndipo anati kwa iwo akuimirirapo, Mchotsereni ndalamayo, nimuipatse kwa iye wakukhala nazo ndalama khumi.”
Kwa kapolo woipayo, kutayikiridwa ndi ndalama yophiphiritsirayo kumatanthauza kutayikiridwa ndi malo mu Ufumu wakumwamba. Inde, iye amatayikiridwa ndi mwaŵi wa kulamulira, pamizinda khumi kapena mizinda isanu, kunena kwake titero. Wonaninso, kuti kapoloyo sakulengezedwa kukhala woipa chifukwa cha kuipa kulikonse kumene amachita koma, mmalo mwake, chifukwa cha kulephera kugwira ntchito ya kuwonjezeredwa kwa chuma cha ufumu wa mbuye wake.
Pamene ndalama ya kapolo woipayo iperekedwa kwa kapolo woyamba, chitsutso chikupangidwa chakuti: “Mbuye, ali nazo ndalama khumi.” Komabe, Yesu akuyankha kuti: “Kwa yense wakukhala nacho kudzapatsidwa; koma kwa iye amene alibe kanthu, chingakhale chimene ali nacho chidzachotsedwa. Koma adani anga aja osafuna kuti ndidzakhala mfumu yawo, bwerani nawo kuno, nimuwaphe pamaso panga.” Luka 19:11-27; Mateyu 28:19, 20.
▪ Kodi nchiyani chimene chikusonkhezera fanizo la Yesu la ndalama khumi?
▪ Kodi ndani amene ali munthu wa fuko lomveka, ndipo kodi nchiyani chimene chiri dziko limene akupita?
▪ Kodi ndani amene ali akapolo, ndipo kodi nchiyani chimene chikuimiriridwa ndi ndalama khumi?
▪ Kodi nzika ndiwo ayani, ndipo amasonyeza motani udani wawo?
▪ Kodi nchifukwa ninji kapolo mmodzi akutchedwa kuti woipa, ndipo kodi kutayikiridwa ndi ndalama yakeko kumatanthauzanji?