Mutu 101
Ku Betaniya, m’Nyumba ya Simoni
PAMENE Yesu akuchoka ku Yeriko, akumka ku Betaniya. Ulendowo umatenga mbali yaikulu yatsiku lonse, popeza uli ulendo wokwera chigwa chovuta cha mtunda wa makilomitala 19. Yeriko ali pamalo apafupifupi mamitala 250 kuchokera pamlingo wanyanja, ndipo Betaniya ali pafupifupi mamitala 760 kuchokera pamlingo wanyanja. Inu mungakumbukire kuti, Betaniya, ndiko kwawo kwa Lazaro ndi alongo ake. Mudzi waung’onowu uli pafupifupi mtunda wa makilomitala 3 kuchokera ku Yerusalemu, wokhala pachigwa cha kummaŵa kwa Phiri la Azitona.
Ambiri afika kale m’Yerusalemu kaamba ka Paskha. Iwo afika mwamsanga kuzadziyeretsa mwamwambo. Mwinamwake iwo anakhudza mtembo kapena kuchita kanthu kena kamene kamawapanga kukhala odetsedwa. Chotero amachita mwambo wa kudziyeretsa kotero kuti asunge Paskha ali ovomerezeka. Pamene ofika mwamsanga ameneŵa asonkhana pakachisi, ambiri akukayikira ponena za kuti kaya Yesu azadza ku Paskhayo kapena ayi.
Yerusalemu ndiye chimake cha mkangano wonena za Yesu. Liri lingaliro lodziŵika kuti atsogoleri achipembedzo akufuna kumgwira ndi kumupha. Kwenikweni, iwo apereka malamulo akuti ngati aliyense adziŵa kumene Yesu ali, ayenera kuwauza. Katatu m’miyezi yaposachedwapa—pa Phwando la Misasa, pa Phwando la Kukonzanso, ndiponso ataukitsa Lazaro—atsogoleri ameneŵa ayesa kumupha. Chotero, anthuwo akudabwa kuti, kodi Yesu adzawonekeranso poyera nthaŵi ina? “Muyesa bwanji inu, sadzadza kuphwando kodi?” iwo akufunsana.
Pakali pano, Yesu akufika m’Betaniya masiku asanu ndi limodzi Paskha asanachitidwe, amene amachitika pa Nisani 14 malinga ndi kalendala Yachiyuda. Yesu akufika m’Betaniya panthaŵi ina Lachisanu madzulo, kumene kuli kuchiyambiyambi kwa Nisani 8. Iye sakanatha kupanga ulendo wa ku Betaniya pa Loŵeruka chifukwa kuyenda ulendo pa Sabata—kuyambira kuloŵa kwa dzuŵa Lachisanu kufikira kuloŵa kwadzuŵa Loŵeruka—nkoletsedwa ndi lamulo Lachiyuda. Mwinamwake Yesu akumka kunyumba ya Lazaro, monga mmene wachitira poyamba, nakhala usiku wa Lachisanu kumeneko.
Komabe, munthu wina wokhala m’Betaniya akuitana Yesu ndi mabwenzi ake kuchakudya cha madzulo pa Loŵeruka. Munthuyo ndiye Simoni, amene poyamba anali wakhate, amene mwinamwake poyambilirapo anali atachiritsidwa ndi Yesu. Monga mwachizolowezi chake cha kuchita changu, Marita akutumikira alendowo. Koma, monga momwe kunayembekezeredwa, Mariya akumvetsera Yesu, panthaŵi ino m’njira imene ikuyambitsa mkangano.
Mariya akutsegula chotengera cha mafuta, kapena nsupa, imene imaloleza mafuta onunkhira okwanira 0.5 kilogalamu, ‘a nardo weniweni.’ Ameneŵa ngamtengo wapatali kwambiri. Ndithudi, mtengo wake ngwofanana ndi malipiro apafupifupi chaka chimodzi! Pamene Mariya akutsanulira mafutawo pamutu wa Yesu ndi pamiyendo yake ndi kupukuta miyendo yake ndi tsitsi lake, kununkhira kosangalatsako kukudzaza nyumba yonseyo.
Ophunzira akukwiya ndipo akufunsa kuti: “Chifukwa ninji kuwononga kumeneku?” Ndiyeno Yudase Iskariote akuti: “Nanga mafuta onunkhira awa sanagulitsidwa chifukwa ninji ndi malupiya atheka mazana atatu ndi kupatsidwa kwa osauka.” Koma Yudase kwenikweni sakudera nkhaŵa ndi osauka, pakuti wakhala akumaba m’bokosi la ndalama losungidwa ndi ophunzirawo.
Yesu akutchinjiriza Mariya. “Mlekeni,” iye akulamula motero. “Mumvutiranji? wandichitira ine ntchito yabwino. Pakuti muli nawo aumphaŵi pamodzi ndi inu masiku onse, ndipo paliponse pamene mukafuna mukhoza kuwachitira zabwino; koma ine simuli nane masiku onse. Iye wachita chimene wakhoza; anandidzozeratu thupi langa kukuikidwa m’manda. Ndipo ndithu ndinena ndi inu, pamene padzalalikidwa uthenga wabwino kudziko lonse lapansi, ichinso chimene anachita mkazi uyu chidzanenedwa, chikhale chomkumbukira nacho.”
Yesu wakhala ali ku Betaniya tsopano koposa maola 24, ndipo mbiri ya kudza kwake yafala. Chifukwa cha chimenecho, ambiri akudza kunyumba ya Simoni kudzawona Yesu, komanso akudzawona Lazaro, amenenso ali konko. Chotero akulu ansembe akupangana kupha osati Yesu yekha komanso ngakhale Lazaro. Zimenezi ziri chifukwa chakuti anthu ambiri akukhulupilira Yesu chifukwa cha kuwona munthu amene anamuukitsa kwa akufa ali wamoyo! Ndithudi, atsogoleri achipembedzo ameneŵa ngoipa chotani nanga! Yohane 11:55–12:11; Mateyu 26:6-13; Marko 14:3-9; Machitidwe 1:12.
▪ Kodi ndimakambitsirano otani amene akuchitika pakachisi m’Yerusalemu, ndipo chifukwa ninji?
▪ Kodi nchifukwa ninji Yesu ayenera kukhala atafika mu Betaniya pa Lachisanu mmalo mwa pa Loŵeruka?
▪ Pamene Yesu akufika mu Betaniya, kodi iye mwachiwonekere akuthera kuti Sabata?
▪ Kodi ndikachitidwe kotani ka Mariya kamene kakuyambitsa mkangano, ndipo kodi Yesu akumtchinjiriza motani?
▪ Kodi nchiyani chimene chimafotokoza mwa fanizo kuipa kwakukulu kwa akulu ansembe?