Mutu 102
Kuloŵa m’Yerusalemu Kwachipambano kwa Kristu
MMAŴA mwake, Lamulungu, Nisani 9, Yesu akuchoka m’Betaniya ndi ophunzira ake kumka kutsidya ku Phiri la Azitona cha ku Yerusalemu. M’nthaŵi yochepa, iwo akuyandikira Betefage, wokhala pa Phiri la Azitona. Yesu akuuza aŵiri a ophunzira ake kuti:
“Mukani kumudzi wopenyana ndi inu, ndipo pomwepo mudzapeza bulu womangidwa, ndi mwana wake pamodzi naye, masulani iwo, mudze nawo kwa ine. Ndipo munthu akanena kanthu ndi inu, mudzati Ambuye asoŵa iwo, ndipo pomwepo adzawatumiza.”
Ngakhale kuti poyambapo ophunzirawo sakuzindikira kuti malangizo ameneŵa akuphatikizapo kanthu kena koloŵetsamo kukwaniritsidwa kwa ulosi wa Baibulo, iwo akuzindikira zimenezi pambuyo pake. Mneneri Zekariya ananeneratu kuti Mfumu yolonjezedwa ndi Mulungu ikakwera pabulu kuloŵa m’Yerusalemu, inde “wokwera pa bulu, ndi mwana wamphongo wa bulu.” Mfumu Solomo anakwera mwana wa bulu mofananamo pakudzozedwa kwake.
Pamene ophunzirawo aloŵa mu Betefage ndi kutenga mwana wa bulu ndi amake, ena a amene ali chiriri pafupi nawo akuti: “Muchita chiyani?” Koma pamene auzidwa kuti nyamazo zikufunidwa ndi Ambuye, anthuwo akuleka ophunzirawo kumka nazo kwa Yesu. Ophunzira akuyala malaya awo akunja pamsana wa mayi wabuluyo ndi mwana wake, koma Yesu akukwera mwana wa buluyo.
Pamene Yesu akuloŵa m’Yerusalemu atakwera pabulu, khamu likuwonjezereka. Anthu ochuluka akuyala malaya awo akunja m’njira, pamene ena akudula nthambi za m’mitengo ndi kuziyala. “Wodala ndiye Wakudza m’dzina la Yehova!” iwo akufuula motero. “Mtendere kumwamba, ndipo ulemelero m’mwambamwamba!”—NW.
Afarisi ena m’khamulo akukwiya ndi zilengezo zimenezi ndipo akudandaulira Yesu kuti: “Mphunzitsi, dzudzulani ophunzira anu.” Koma Yesu akuyankha kuti: “Ndinena ndi inu, ngati awa akhala chete miyala idzafuula.”
Pamene Yesu akuyandikira ku Yerusalemu, iye awona mzindawo nayamba kuulirira, akumati: “Ukadazindikira tsiku iri, inde iwetu zinthu za mtendere! koma tsopano zibisika pamaso pako.” Chifukwa cha kusamvera kwake kodzifunira, Yerusalemu ayenera kulipira mtengo wake, monga momwe Yesu akuneneratu kuti:
“Adani ako [Aroma motsogozedwa ndi Kazembe Tito] adzakuzingira linga, nadzakuzungulira iwe kwete, nadzakutsekereza ponsepo; ndipo adzakupasula iwe, ndi ana ako mwa iwe; ndipo sadzasiya mwa iwe mwala wina pa mwala unzake.” Chiwonongeko cha Yerusalemu chimenechi chonenedweratu ndi Yesu kwenikweni chikuchitika zaka 37 pambuyo pake, m’chaka cha 70 C.E.
Milungu yoŵerengeka chabe poyambilira, ambiri a m’khamulo anali atawona Yesu akuukitsa Lazaro. Tsopano ameneŵa akuuzabe ena za chozizwitsa chimenecho. Chotero pamene Yesu akuloŵa m’Yerusalemu, mzinda wonse ukupokosera. “Ndani uyu?” anthuwo afuna kudziŵa. Ndipo makamuwo akulengezabe kuti: “Uyu ndimneneri Yesu wa ku Nazarete wa ku Galileya!” Powona zimene zikuchitika, Afarisi akudandaula kuti sakuwonedwa monga kanthu kotheratu, popeza kuti, monga mmene akunenera: “Dziko litsata pambuyo pake pa iye.”
Monga mwachizoloŵezi chake pocheza ku Yerusalemu, Yesu akumka kukachisi kukaphunzitsa. Kumeneko akhungu ndi opunduka akudza kwa iye, ndipo akuwachiritsa! Pamene akulu ansembe ndi alembi awona zinthu zodabwitsa zimene Yesu akuzichita ndi pamene amva anyamata achichepere m’kachisi akumafuula kuti, “Hosana kwa Mwana wa Davide!” akupsa mtima. “Muli nkumva kodi chimene alikunena awa?” iwo akutsutsa motero.
“Inde,” Yesu akuyankha. “Simunaŵerenga kodi, M’kamwa mwa makanda ndi oyamwa munafotokozera zolemekeza?”
Yesu akupitirizabe kuphunzitsa, ndipo akuyang’ana mozungulira zinthu za m’kachisiyo. Mwamsanga kwada. Chotero iye akuchoka, limodzi ndi ophunzira ake 12, ndi kuyenda ulendo wa makilomitala 3 kapena cha pompo kumka ku Betaniya. Kumene akukhalako usiku wa Lamulungu, mwinamwake panyumba ya bwenzi lake Lazaro. Mateyu 21:1-11, 14-17; Marko 11:1-11; Luka 19:29-44; Yohane 12:12-19; Zekariya 9:9.
▪ Kodi ndiliti ndipo ndim’njira yotani imene Yesu akuloŵa nayo m’Yerusalemu monga Mfumu?
▪ Kodi nkofunika motani kuti makamu atamande Yesu?
▪ Kodi Yesu akulingalira motani pamene akuwona Yerusalemu, ndipo ndiulosi wotani umene akunena?
▪ Kodi nchiyani chimene chikuchitika pamene Yesu akumka kukachisi?