Mutu 103
Kufika Pakachisi Kachiŵirinso
YESU ndi ophunzira ake angothera kumene usiku wawo wachitatu mu Betaniya chifikire kuchokera ku Yeriko. Tsopano mmamaŵa pa Lolemba, Nisani 10, ukuwapeza ali kale paulendo wawo wa ku Yerusalemu. Yesu ali ndi njala. Chotero pamene awona mtengo wa mkuyu wokhala ndi masamba, iye akupita pomwepo kuti akawone kaya ngati uli ndi nkhuyu.
Masamba a mtengowo afulumira kuphuka nthaŵi isanakwanire, popeza kuti nthaŵi ya nkhuyuzo sinakhale kufikira June, ndipo kuli kokha kumapeto kwa March. Komabe, mwachiwonekere Yesu akulingalira kuti popeza kuti masambawo afulumira kuphuka, nkhuyuzo zingakhalenso zitafulumira. Koma iye akugwiritsidwa mwala, masambawo apereka kawonekedwe konyenga ka mtengowo. Pamenepo Yesu akutembelera mtengowo, akumati: “Munthu sadzadyanso zipatso zako nthaŵi zonse.” Zotulukapo za kachitidwe ka Yesu ndi tanthauzo lake zikudziŵidwa mmaŵa bwake.
Popitilira, mwamsanga Yesu ndi ophunzira ake akufika ku Yerusalemu. Iye akupita kukachisi, amene anamzonda masana apitawo. Komabe, lero, akuchita kanthu kena, monga mmene anachitira zaka zitatu zapitazo pamene anadza ku Paskha mu 30 C.E. Yesu akuthamangitsa awo amene akugulitsa ndi kugula m’kachisi ndi kugubuduza magome a osintha ndalama ndi mipando ya ogulitsa nkhunda. Iye sakulola ngakhale aliyense kutenga chotengera kuloŵa nacho m’kachisi.
Podzudzula osintha ndalamawo ndi ogulitsa nyama m’kachisi, iye akuti: “Sichinalembedwa kodi, Nyumba yanga idzatchedwa nyumba ya kupemphereramo anthu amitundu yonse? koma inu mwaiyesa phanga la achifwamba.” Iwo ndiwo mbala chifukwa chakuti amafuna ndalama zokwera mtengo kwa osauka kuti agule nyama zofunika kaamba ka nsembe. Chotero Yesu akulingalira kuchitidwa kwa malonda kumeneku monga mpangidwe wa kulanda kapena umbala.
Pamene akulu ansembe, alembi, ndi anthu ena odziŵika amva zimene Yesu wachita, kachiŵirinso akufunafuna njira yoti aphedwe nayo. Motero iwowo akutsimikizira kuti sakhoza kukonzeka. Komabe, iwo sakudziŵa mmene angaphere Yesu, popeza kuti anthu onse akupitirizabe kumka kwa iye kukamumvetsera.
Kuphatikiza Ayuda akuthupi, nawonso Akunja adza ku Paskha. Ameneŵa ndiwo otembenuka, kutanthauza kuti atembenukira kuchipembedzo cha Ayuda. Mwachiwonekere, Agiriki ena, otembenuzidwa, tsopano akufika kwa Filipo ndi kupempha kuwona Yesu. Filipo akumka kwa Andireya, mwinamwake kukamfunsa kaya ngati kuwonana naye kotero kukakhala koyenerera. Mwachiwonekere Yesu pakali pano adakali kukachisi, kumene Agirikiwo angakhoze kumuwonera.
Yesu akudziŵa kuti ali ndi masiku ochepa otsala a moyo wake, chotero iye akuchitira fanizo mkhalidwe wakewo bwino lomwe kuti: “Yafika nthaŵi, kuti Mwana wa munthu alemekezedwe. Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Ngati mbewu ya tirigu siigwa m’nthaka, nifa, ikhala pa yokha iyo; koma ngati yafa, ibala chipatso chambiri.”
Mbewu imodzi yatirigu siri yopindulitsa. Komabe, bwanji ngati ibzalidwa m’nthaka ndi ‘kufa,’ ikumathetsa moyo wake monga mbewu? Pamenepo imamera ndipo m’nthaŵi yokwanira imakula kukhala kamtengo kamene kamabala mbewu zambirimbiri za tirigu. Mofananamo, Yesu ali kokha munthu mmodzi wangwiro. Koma pamene afa ali wokhulupirika kwa Mulungu, iye afikira kukhala njira yoperekera moyo wosatha kwa anthu okhulupirika amene ali ndi mzimu wofananawo wa kudzimana umene iye ali nawo. Motero, Yesu akuti: “Iye wokonda moyo wake adzautaya; ndipo wodana ndi moyo wake m’dziko lino lapansi adzausungira kumoyo wosatha.”
Mwachiwonekere Yesu sakuganiza kokha za iye mwini, pakuti kenako akufotokoza kuti: “Ngati wina anditumikira ine, anditsate; ndipo kumene kuli ine, komwekonso kudzakhala mtumiki wanga. Ngati wina anditumikira ine, Atate adzamchitira ulemu iyeyu.” Ndimphotho yodabwitsani chotani nanga kaamba ka kutsatira Yesu ndi kumtumikira! Ndiyo mphotho ya kulemekezedwa ndi Atate kuyanjana ndi Kristu mu Ufumuwo.
Poganizira za kuvutika kwakukulu ndi imfa yomvetsa ululu zimene zikumuyembekezera, Yesu akupitiriza kuti: “Moyo wanga wavutika tsopano; ndipo ndidzanena chiyani? Atate, ndipulumutseni ine kunthaŵi iyi.” Kokha ngati zimene zikumuyembekezera zikanapeŵedwa nanga! Koma, ayi, monga momwe iye akunenera kuti: “Chifukwa cha ichi ndinadzera nthaŵi iyi.” Yesu ali wogwirizana ndi makonzedwe athunthu a Mulungu, kuphatikizapo imfa ya nsembe ya iye mwini. Mateyu 21:12, 13, 18, 19; Marko 11:12-18; Luka 19:45-48; Yohane 12:20-27.
▪ Kodi nchifukwa ninji Yesu akuyembekeza kupeza nkhuyu ngakhale kuti siri nthaŵi yake?
▪ Kodi nchifukwa ninji Yesu akutcha awo amene akugulitsa m’kachisi kuti “achifwamba”?
▪ Kodi ndim’njira yotani imene Yesu ali wofanana ndi mbewu ya tirigu imene imafa?
▪ Kodi ndimotani mmene Yesu akulingalirira za kuvutika ndi imfa imene ikumuyembekezera?