Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • gt mutu 105
  • Kuyamba kwa Tsiku Lofunika Koposa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuyamba kwa Tsiku Lofunika Koposa
  • Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Nkhani Yofanana
  • Kuyambika kwa Tsiku Lowopsya
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Yesu Anagwiritsa Ntchito Mtengo wa Mkuyu Pophunzitsa Anthu za Chikhulupiriro
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Munthu Aliyense Adzakhala Patsinde pa Mkuyu Wake
    Nsanja ya Olonda—2003
  • Kukumbukira Masiku Omaliza a Yesu Padziko
    Nsanja ya Olonda—1998
Onani Zambiri
Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
gt mutu 105

Mutu 105

Kuyamba kwa Tsiku Lofunika Koposa

PAMENE Yesu akuchoka m’Yerusalemu Lolemba madzulo, iye akubwerera ku Betaniya kuchigwa cha kummaŵa kwa Phiri la Azitona. Masiku aŵiri a uminisitala wake womaliza mu Yerusalemu atha. Mosakayikira Yesu kachiŵirinso akuthera usikuwo ndi bwenzi lake Lazaro. Chifikire kuchokera ku Yeriko pa Lachisanu, uno ndiwo usiku wachinayi umene iye wathera mu Betaniya.

Tsopano, mmamaŵa Lachiŵiri, Nisani 11, iye ndi ophunzira ake kachiŵirinso ali paulendo. Limeneli likutsimikizira kukhala tsiku lofunika koposa la uminisitala wa Yesu, lotanganitsidwa koposa. Ndilo tsiku lomaliza limene akuwonekera m’kachisi. Ndipo liri tsiku lomaliza la umininisitala wake wapoyera kuzengedwa mlandu kwake ndi kuphedwa zisanachitike.

Yesu ndi ophunzira ake akudzera njira yofananayo ya ku Phiri la Azitona kumka ku Yerusalemu. Ali m’njira yochokera ku Betaniya, Petro akuzindikira mtengo umene Yesu anatemberera dzulo mmaŵa. “Rabi, wonani!” iye akudzuma motero, “wafota mkuyuwo munautemberera.”

Koma kodi nchifukwa ninji Yesu anafotetsa mtengowo? Iye akusonyeza chifukwa chake pamene akupitiriza kunena kuti: “Indedi ndinena kwa inu, Ngati mukhala nacho chikhulupiliro, osakayikakayika, mudzachita si ichi cha pa mkuyu chokha, koma ngati mudzati ngakhale ku phiri ili, [Phiri la Azitona pa limene aimilirapo] Tanyamulidwa, nuponyedwe m’nyanja, chidzachitidwa. Ndipo zinthu zirizonse mukazifunsa m’kupemphera ndi kukhulupilira, mudzalandira.”

Chotero mwa kuchititsa mtengowo kufota, Yesu akupereka phunzilo la chinthu chowoneka kwa ophunzira ake pakupanda kwawo chikhulupiliro mwa Mulungu. Monga momwe akunenera: “Zinthu zirizonse mukazipempherera ndi kuzipempha, khulupilirani kuti mwazilandira, ndipo mudzakhala nazo.” Ndimfundo yofunika chotani nanga ya kuiphunzira kaamba ka iwo, makamaka polingalira za mayeso aakulu koposa amene ati adze msanga! Komabe, pali kugwirizana kwina pakati pa kufota kwa mtengo wa mkuyu ndi mtundu wopanda chikhulupiliro.

Mtundu wa Israyeli, mofanana ndi mtengo wa mkuyu, uli ndi kawonekedwe konyenga. Ngakhale kuti mtunduwo uli muunansi wa pangano ndi Mulungu ndipo mwachiphamaso ungawonekere kukhala ukusunga malamulo ake, watsimikizira kukhala wopanda chikhulupiliro, wosabala zipatso zabwino. Chifukwa cha kupanda chikhulupiliro, uli kwenikweni m’njira ya kukana Mwana weniweni wa Mulungu! Ndicho chifukwa chake, mwa kuchititsa mtengo wa mkuyu wosabalawo kufota, mophiphiritsira Yesu akusonyeza zimene zidzakhala zotulukapo zake zotsiriza za mtundu wosabala zipatso ndi wopanda chikhulupiliro umenewu.

Posapita nthaŵi, Yesu ndi ophunzira ake akuloŵa mu Yerusalemu, ndipo monga mwa chizoloŵezi chawo, akumka kukachisi, kumene Yesu akuyamba kuphunzitsa. Akulu ansembe ndi akulu ena a mwa anthu, mosakayikira akumakumbukira kachitidwe ka Yesu ka tsiku lapitalo motsutsa osintha ndalama, akuyang’anizana naye nati: “Muchita izi ndi ulamuliro wotani? ndipo ndani anakupatsani ulamuliro wotere?”

Poyankha Yesu akuti: “Nanenso ndikufunsani mawu amodzi, amene ngati mundiuza, inenso ndikuuzani ndiulamuliro wotani ndichita izi. Ubatizo wa Yohane, uchokera kuti? Kumwamba kodi kapena kwa anthu?”

Ansembe ndi akuluwo akuyamba kufunsana pakati pawo za mmene adzayankhira. “Tikati, Kumwamba, iye adzati kwa ife, Munalekeranji kumvera iye? Koma tikati, Kwa anthu, tiwopa khamu la anthu; pakuti onse amuyesa Yohane mneneri.”

Atsogoleriwo sakudziŵa chimene angayakhe. Motero akuyankha Yesu kuti: “Sitidziŵa.”

Yesu, nayenso, akuti: “Inenso sindikuuzani ndiulamuliro wotani ndichita izi.” Mateyu 21:19-27; Marko 11:19-33; Luka 20:1-8.

▪ Kodi Lachiŵiri Nisani 11 liri nzochitika zofunika zotani?

▪ Kodi ndimaphunziro otani amene Yesu akupereka pamene achititsa mtengo wa mkuyu kufota?

▪ Kodi Yesu akuyankha motani awo amene akufunsa kuti amachita zinthu ndi ulamuliro wa yani?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena