Mutu 106
Avumbulidwa ndi Mafanizo a Munda Wampesa
YESU ali pakachisi. Iye wangogonjetsa kumene atsogoleri achipembedzo amene anafuna kudziŵa kuti anali kuchita zinthu ndi ulamuliro wa yani. Asanatsitsimuke kukusokonekera kwawo maganizo, Yesu akuwafunsa kuti: “Nanga mutani?” Ndiyeno mwanjira ya fanizo, akuwasonyeza mtundu wa anthu amene iwo alidi.
“Munthu anali nawo ana aŵiri,” Yesu akusimba motero. “Nadza iye kwa woyamba nati, Mwanawe, kagwire lero ntchito kumunda wampesa. Koma iye anakana, nati, Sindifuna ine; koma pambuyo pake analapa mtima napita. Ndipo anadza kwa winayo, natero momwemo. Ndipo iye anavomera, nati, Ndipita mbuye; koma sanapite. Ndani wa aŵiriŵo anachita chifuniro cha atate wake?” Yesu akufunsa.
“Woyambayo,” adani ake akuyankha motero.
Chotero Yesu akufotokoza kuti: “Indetu ndinena kwa inu, kuti amisonkho ndi akazi achiwerewere amatsogolera inu, kuloŵa mu ufumu wa Kumwamba.” M’chenicheni, amisonkho ndi ndi achiwerewere, poyamba anakana kutumikira Mulungu. Koma tsopano, mofanana ndi mwana wachiŵiri uja, analapa namtumikira. Kumbali ina, atsogoleri achipembedzo, mofanana ndi mwana woyamba uja, anadzinenera kukhala akutumikira Mulungu, komabe, monga momwe Yesu akunenera: “Popeza Yohane [Mbatizi] anadza kwa inu m’njira ya chilungamo, ndipo simunamvera iye; koma, amisonkho ndi akazi achiwerewere anamvera iye; ndipo inu, mmene munachiwona, simunalapa pambuyo pake, kuti mumvere iye.”
Kenako Yesu akusonyeza kuti kulephera kwa atsogoleri achipembedzo ameneŵa sikukusonyezedwa kokha m’kunyalanyaza kutumikira Mulungu. Ayi, koma iwo kwenikweni ali anthu amphulupulu ndi oipa. “Panali munthu, mwini banja,” Yesu akusimba motero, “amene analima munda wamphesa, nauzunguniza linga, nakumba umo moponderamo mphesa, namanga nsanja, naukongoletsa kwa olima munda, namuka kwina. Pamene nyengo ya zipatso inayandikira, anatumiza akapolo ake kwa olima mundawo kukalandira zipatso zake. Ndipo olimawo anatenga akapolo ake, nampanda mmodzi, wina namupha, wina namponya miyala. Anatumizanso akapolo ena, akuchuluka oposa akuyambawa; ndipo anawachira iwo momwemo.”
“Akapolo” ndiwo aneneri amene “mwini banja,” Yehova Mulungu, anawatumiza kwa “olima” a ‘munda wake wampesa.’ Olima munda ameneŵa ndiwo oimira otsogolera a mtundu wa Israyeli, mtundu umene Baibulo limaudziŵikitsa kukhala “munda wampesa” wa Mulungu.
Popeza kuti “olima” akuchitira moipa ndi kupha “akapolo,” Yesu akufotokoza kuti: “Koma pambuyo pake [mwini munda wampesa] anatumiza kwa iwo mwana wake, nati, Adzachitira mwana wanga ulemu. Koma olimawo mmene anawona mwanayo, ananena wina ndi mnzake, Uyu ndiye woloŵa nyumba; tiyeni timuphe, ndipo ife tidzatenga choloŵa chake. Ndipo anamtenga iye, namponya kunja kwa munda, namupha.”
Tsopano, polankhula ndi atsogoleri achipembedzo, Yesu akufunsa kuti: “Tsono atabwera mwini munda, adzachitira olimawo chiyani?”
“Adzawononga koipa oipawo,” atsogoleri achipembedzowo akuyankha motero, “nadzapereka mundawo kwa olima ena, amene adzambwezera iye zipatso panyengo zake.”
Motero iwo mosadziŵa akudziperekera chiweruzo chawo, popeza kuti akuphatikizidwa pakati pa ‘alimi’ Achisrayeli a “munda wampesa” wa Yehova wa mtundu wa Israyeli. Chipatso chimene Yehova akuyembekezera kwa olima oterowo ndicho chikhulupiliro mwa Mwana wake, Mesiya wowona. Chifukwa cha kulephera kugaŵira kwawo chipatso choterocho, Yesu akuchenjeza kuti: “Kodi simunaŵerenga konse m’Malembo [pa Salmo 118:22, 23], Mwala umene anaukana omanga nyumba womwewu unakhala mutu wapangodya: Ichi chinachokera kwa Ambuye, ndipo chiri chozizwitsa m’maso mwathu? Chifukwa chake ndinena kwa inu, Ufumu wa Mulungu udzachotsedwa kwa inu, nudzapatsidwa kwa anthu akupatsa zipatso zake. Ndipo iye wakugwa pa mwala uwu adzaphwanyika; koma pa iye amene udzamgwera, udzampera iye.”
Alembi ndi akulu ansembe tsopano akudziŵa kuti Yesu akunena za iwo, ndipo afuna kumupha, “woloŵa malo” woyenerayo. Chotero mwaŵi wa kukhala olamulira mu Ufumu wa Mulungu udzachotsedwa kwa iwo monga mtundu, ndipo mtundu watsopano wa ‘olima munda wampesa’ udzalengedwa, umene udzabala zipatso zabwino.
Chifukwa chakuti atsogoleri achipembedzo akuwopa makamuwo, amene akulingalira Yesu kukhala mneneri, iwo sakuyesa kupha Yesu panthaŵi imeneyi. Mateyu 21:28-46; Marko 12:1-12; Luka 20:9-19; Yesaya 5:1-7.
▪ Kodi ana aŵiri a m’fanizo la Yesu loyamba amaimira ayani?
▪ M’fanizo lake lachiŵiri, kodi ndani amene akuimiriridwa ndi “mwini banja,” “munda wampesa,” “olima,” “akapolo,” ndi ‘woloŵa nyumba’?
▪ Kodi nchiyani chimene chidzachitika kwa ‘olima munda wampesa,’ ndipo ndani amene adzawaloŵa m’malo?