Mutu 108
Alephera Kukola Yesu
CHIFUKWA chakuti Yesu wakhala akuphunzitsa m’kachisi ndipo wangouza kumene adani ake achipembedzo mafanizo atatu amene amavumbula kuipa kwawo, Afarisi akwiya ndipo akulinganiza kumkola kuti anene kanthu kena kamene kangamchititse kumangidwa. Iwo akulinganiza chiwembu ndi kutumiza ophunzira awo, limodzi ndi otsatira chipani cha Herode, kukayesa kumtchera khwekhwe.
“Mphunzitsi,” anthu ameneŵa akutero, “tidziŵa kuti muli wowona, ndipo muphunzitsa njira ya Mulungu mowona ndithu, ndipo simusamala munthu aliyense; pakuti simuyang’anira pa nkhope ya anthu. Chifukwa chake mutiuze ife, muganiza chiyani? Kuloledwa kodi kupatsa msonkho kwa Kaisara, kapena iyayi?”
Yesu sakupusitsidwa ndi kusyasyalikako. Iye akuzindikira kuti ngati atati, ‘Ayi, nkosaloleka kapena sikuli koyenera kukhoma msonkho,’ adzakhala ndi mlandu wa kupandukira Roma. Komabe, ngati atati, ‘Inde, muyenera kukhoma msonkho,’ Ayudawo, amene amaipidwa ndi kugonjera kwawo Roma, adzamuda. Chotero iye akuyankha kuti: “Mundiyeseranji ine, onyenga inu? Tandiwonetsani ine ndalama yamsonkho.”
Pamene amninkha, iye akufunsa kuti: “Nchayani chithunzithunzi ichi, ndi kulemba kwake?”
“Cha Kaisara,” iwo akuyankha.
“Chifukwa chake, patsani kwa Kaisara zake za Kaisara, ndi kwa Mulungu zake za Mulungu.” Eya, pamene amunaŵa amva yankho la Yesu lalusolo, akuzizwa. Ndipo akuchoka namsiya ali yekha.
Powona kulephera kwa Afarisi kupeza kanthu kotsutsa Yesu, Asaduki, amene amanena kuti kulibe chiukiliro, akumfikira ndi kumfunsa kuti: “Mphunzitsi, Mose anati, Ngati munthu akafa wopanda mwana, mphwake, adzakwatira mkazi wake, nadzamuukitsira mbale wake mbewu. Tsono panali ndi ife abale asanu ndi aŵiri; ndipo wakuyamba anakwatira, namwalira wopanda mbewu, nasiyira mphwake mkazi wake; chimodzimodzi wachiŵiri, ndi wachitatu, kufikira wachisanu ndi chiŵiri. Ndipo pomalizira anamwaliranso mkaziyo. Chifukwa chake m’kuuka kwa akufa, iye adzakhala mkazi wa yani wa asanu ndi aŵiriwo? pakuti onse anakhala naye.”
Poyankha Yesu akuti: “Simusochera nanga mwa ichi, popeza mulibe kudziŵa malembo, kapena mphamvu yake ya Mulungu? Pakuti pamene adzauka kwa akufa, sakwatira, kapena sakwatiwa; koma akhala ngati angelo a kumwamba. Koma za akufa, kuti akaukitsidwa; simunaŵerenga m’kalata wa Mose kodi, za chitsambacho, kuti Mulungu anati kwa iye, nanena, Ine ndine Mulungu wa Abrahamu, ndi Mulungu wa Isake, ndi Mulungu wa Yakobo? Sali Mulungu, wa akufa, koma wa amoyo: musochera inu ndithu.”
Kachiŵirinso makamuwo akuzizwa ndi yankho la Yesu. Ngakhale ena a alembi akuvomereza kuti: “Mphunzitsi, mwanena bwino.”
Pamene Afarisi awona kuti Yesu watontholetsa Asaduki, akudza kwa iye m’kagulu kamodzi. Kuti amuyesebe, mmodzi wa iwo akufunsa kuti: “Mphunzitsi, lamulo lalikulu ndiliti la m’Chilamulo?”
Yesu akuyankha kuti: “Lamtsogolo ndiiri, Mvera, Israyeli; Ambuye Mulungu wathu, Ambuye ndiye mmodzi; ndipo uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse, ndi mphamvu yako yonse. Lachiŵiri ndiiri, Uzikonda mnzako monga udzikonda mwini. Palibe lamulo lina lakuposa awa.” Kwenikweni, Yesu akuwonjezera kuti: “Pamalamulo awa aŵiri mpokoloŵekapo Chilamulo chonse ndi Aneneri.”
“Mphunzitsi, mwanena zowona kuti,” mlembiyo akuvomereza motero. “Ndiye mmodzi; ndipo palibe wina, koma Iye; ndipo: kumkonda iye ndi mtima wonse, ndi nzeru yonse, ndi mphamvu yonse, ndi kukonda mnzake monga adzikonda mwini, ndiko kuposa nsembe zopsereza zamphumphu zonse ndi nsembe zophedwa.”
Pozindikira kuti mlembiyo wayankha mwanzeru, Yesu akumuuza kuti: “Suli kutali ndi Ufumu wa Mulungu.”
Kwa masiku atatu tsopano—Lamulungu, Lolemba, ndi Lachiŵiri—Yesu wakhala akuphunzitsa m’kachisi. Anthu amumvetsera ndi chisangalalo, komabe atsogoleri achipembedzo akufuna kumupha, koma kufikira pano zoyesayesa zawo zalepheretsedwa. Mateyu 22:15-40; Marko 12:13-34; Luka 20:20-40.
▪ Kodi ndichiwembu chotani chimene Afarisi akulinganiza kukola nacho Yesu, ndipo kodi chikachitika nchiyani ngati iye ati apereke yankho lakuti inde kapena ayi?
▪ Kodi Yesu akulepheretsa motani zoyesayesa za Asaduki za kumkola?
▪ Kodi nkuyesayesa kotani kowonjezereka kumene Afarisi akupanga kuyesa Yesu, ndipo chotulukapo chake nchiyani?
▪ Mkati mwa uminisitala wake wotsiriza m’Yerusalemu, kodi Yesu akuphunzitsa kwa masiku angati m’kachisi, ndi chiyambukiro chotani?