Mutu 119
Atengeredwa kwa Anasi, Ndiyeno kwa Kayafa
YESU, womangidwa monga mpandu wodziŵika, akutsogozedwa kwa Anasi, amene kale anali mkulu wa ansembe wotchuka. Anasi anali mkulu wa ansembe pamene Yesu monga mnyamata wazaka 12 zakubadwa anadabwitsa aphunzitsi achirabi pakachisi. Pambuyo pake angapo a ana a Anasi anatumikira monga akulu ansembe, ndipo panthaŵi ino mkamwini wake Kayafa ali ndi malo antchito amenewo.
Mwinamwake Yesu choyamba akupititsidwa kunyumba kwa Anasi chifukwa cha kutchuka kwa nthaŵi yaitali kwa mkulu wa ansembe ameneyu m’moyo wachipembedzo Chachiyuda. Kuima kwakanthaŵi kumeneku kowonana ndi Anasi kukupereka nthaŵi yakuti Mkulu wa Ansembe Kayafa asonkhanitse Sanhedrin, bwalo lamilandu lalikulu Lachiyuda la ziŵalo 71, ndiponso kuti asonkhanitse mboni zonama.
Mkulu Wansembe Anasi tsopano akufunsa Yesu za ophunzira ake ndi za chiphunzitso chake. Komabe, poyankha Yesu akuti: “Ine ndinalankhula zomveka kwa dziko lapansi; ndinaphunzitsa ine nthaŵi zonse m’sunagoge ndi m’kachisi, kumene amasonkhana Ayuda onse; ndipo mobisika sindinalankhule kanthu. Undifunsiranji ine? funsa iwo amene adamva chimene ndinalankhula nawo; tawona, amenewo adziŵa chimene ndinanena ine.”
Atatero, mmodzi wa adindo woimirira pafupi ndi Yesu akumuwomba khofi kumaso, akumati: “Kodi uyankha mkulu wa ansembe chomwecho?”
“Ngati ndalankhula choipa,” Yesu akuyankha motero, “chita umboni wa choipacho, koma ngati bwino, undipandiranji?” Pambuyo pakusinthana mawu kumeneku, Anasi akutumiza Yesu ali chimangidwire kwa Kayafa.
Pakali pano akulu ansembe onse ndi akulu ena ndi alembi, inde, Sanhedrin yonse, ikuyamba kusonkhana. Mwachiwonekere malo awo osonkhanako ndiwo nyumba ya Kayafa. Kuzenga mlandu wotero pausiku wa Paskha nkotsutsanadi ndi lamulo Lachiyuda. Koma zimenezi sizikulepheretsa atsogoleri achipembedzo pachifuno chawo choipa.
Milungu ingapo yapitayo, pamene Yesu anaukitsa Lazaro, ziŵalo za Sanhedrin zinali zitatsimikiza kale pakati pawo kuti iye ayenera kufa. Ndipo masiku aŵiri okha apitawo, pa Lachitatu, atsogoleri achipembedzo anapangana upo wa kugwira Yesu mwamachenjera kuti amuphe. Tangoyerekezerani, iye kwenikwenidi anatsutsidwa asanazengedwe mlandu!
Tsopano zoyesayesa zikuchitidwa kupeza mboni zimene zikapereka umboni wonama kotero kuti pakhale mlandu wotsutsa Yesu. Komabe, mboni sizikupezeka zimene ziri zogwirizana popereka umboni wawo. Potsirizira pake, anthu ena aŵiri akuimirira nati: “Tinamva iye alikunena, kuti, Ine ndidzawononga kachisi uyu womangidwa ndi manja, ndi masiku atatu ndidzamanga wina wosapangidwa ndi manja.”
“Suyankha kanthu kodi?” Akufunsa motero Kayafa. “Nchiyani ichi chimene awa alikuchitira umboni?” Koma Yesu akukhalabe chete. Ngakhale pachinenezo chonama chimenechi, mochititsa manyazi Sanhedrin, mbonizo sizikuchititsa kuti mawu awo agwirizane. Chotero mkulu wa ansembe akuyesa machenjera ena osiyana.
Kayafa amadziŵa mmene Ayuda aliri a mtima wapachala kwa munthu aliyense wodzitcha kukhala Mwana weniweni wa Mulungu. Panthaŵi ziŵiri zapitazo, iwo mofulumira ananeneza Yesu kukhala wochitira mwano woyenerera imfa, panthaŵi ina anayerekezera molakwa kuti anali kudzinenera kukhala wofanana ndi Mulungu. Tsopano Kayafa mochenjera akupempha kuti: “Ndikukulumbiritsa iwe pa Mulungu wamoyo, kuti tiuze ife ngati iwe ndiwe Kristu, Mwana wa Mulungu.”
Mosasamala kanthu za zimene Ayuda akuganiza, Yesu alidi Mwana wa Mulungu. Ndipo kukhala kwake chete kukatanthauziridwa kukhala kulandula kuti iye sali Kristu. Chotero Yesu molimba mtima akuyankha kuti: “Ndine amene; ndipo mudzawona Mwana wa munthu alikukhala kudzanja lamanja lamphamvu, ndi kudza ndi mitambo yakumwamba.”
Pa izi, Kayafa, m’kachitidwe ka mphamvu, akung’amba malaya ake nadzuma kuti: “Achitira Mulungu mwano tifuniranji mboni zina? wonani tsopano mwamva mwanowo; muganiza bwanji?”
“Ali woyenera kumupha,” akudzuma motero a mu Sanhedrin. Pamenepo iwo akuyamba kumseka, ndipo akunena zinthu zambiri zomchitira mwano. Akumuwomba khofi kumaso namlavulira malovu. Ena akuphimba nkhope yake yonse nammenya ndi nkhonya zawo nalankhula molalata kuti: “Utilote ife, Kristu iwe; wakumenya iwe ndani?” Nkhalwe yoipa yosavomerezedwa imeneyi, ikuchitika mkati mwa nthaŵi ya mlandu wozengedwa usikuwo. Mateyu 26:57-68; 26:3, 4; Marko 14:53-65; Luka 22:54, 63-65; Yohane 18:13-24; 11:45-53; 10:31-39; 5:16-18.
▪ Kodi Yesu akutsogozedwa kuti choyamba, ndipo kodi nchiyani chikumchitikira kumeneko?
▪ Kodi kenako Yesu akutengeredwa kuti, ndipo kaamba ka chifuno chotani?
▪ Kodi Kayafa ali wokhoza motani kuchititsa Sanhedrin kulengeza kuti Yesu ngoyenera kufa?
▪ Kodi ndikhalidwe loipa lotani losavomerezedwa, limene likuchitika mkati mwa kuzenga mlanduwo?