Mutu 124
Aperekedwa Natengedwa
PAMENE Pilato, mosonkhezeredwa ndi mkhalidwe wa kulama maganizo wa Yesu wozunzidwayo, kachiŵirinso ayesa kummasula, akulu ansembe akukwiya moposerapo. Iwo ali otsimikiza kusalola kalikonse kudodometsa chifuno chawo choipa. Chotero akuyambanso kufuula kuti: “Mpachikeni, mpachikeni.”
“Mtengeni iye inu nimumpachike,” Pilato akuyankha motero. (Mosiyana ndi zonena zawo zoyamba, Ayuda angakhale anali ndi ukumu wa kupha apandu kaamba ka zolakwa zachipembedzo zimene ziri zoopsa kwambiri.) Pamenepo, kwapafupifupi nthaŵi yachisanu, Pilato akulengeza Yesu kukhala wopanda liwongo, akumati: “Sindipeza chifukwa mwa iye.”
Ayudawo, atawona kuti zinenezo zawo zandale zadziko zalephera kuchitika, akutembenukiranso kuzinenezo zachipembedzo za kuchitira mwano Mulungu kwa Yesu zogwiritsidwa ntchito maola angapo apitawo pamaso pa Sanhedrin. “Tiri nacho chilamulo ife,” iwo akutero, “ndipo monga mwa chilamulocho ayenera kufa, chifukwa anadziyesera Mwana wa Mulungu.”
Chinenezo chimenechi nchatsopano kwa Pilato, ndipo chikumchititsa kukhala ndi mantha mowonjezereka. Pofika tsopano wazindikira kuti Yesu sali munthu wamba, monga momwedi maloto a mkazi wake ndi nyonga yapadera yaumunthu wa Yesu zikusonyezera. Koma kodi ali “Mwana wa Mulungu”? Pilato akudziŵa kuti Yesu ngwochokera ku Galileya. Komabe, kodi iye mwinamwake angakhale atakhalapo ndi moyo kalelo? Pomtengeranso m’pretorio, Pilato akufunsa kuti: “Muchoka kuti?”
Yesu akukhala chete. Poyambirirapo anali atauza Pilato kuti iye ndiye mfumu koma kuti Ufumu wake suli mbali ya dzikoli. Tsopano palibe mafotokozedwe ena amene akatumikira chifuno chopindulitsa. Komabe, kunyada kwa Pilato kwavulazidwa chifukwa cha kukana kuyankhako, ndipo akukalipira Yesu ndi mawu akuti: “Simukulankhula ndi ine kodi? simudziŵa kodi kuti ulamuliro ndiri nawo wakukumasulani, ndipo ndiri nawo ulamuliro wakukupachikani?”
“Simukadakhala nawo ulamuliro uliwonse pa ine, ngati sukadapatsidwa kwa inu kuchokera kumwamba,” Yesu akuyankha mwaulemu. Iye akunena za kupereka ukumu kwa Mulungu kwa olamulira adziko wa kuyendetsa zochitika za padziko lapansi. Yesu akuwonjezera kuti: “Chifukwa cha ichi iye wondipereka ine kwa inu ali nalo tchimo loposa.” Ndithudi, mkulu wa ansembe Kayafa ndi mabwenzi ake ndi Yudase Isikariote onsewo ali ndi thayo lalikulu koposa la Pilato kaamba ka kuchitira Yesu chisalungamo.
Pochititsidwa chidwi mowonjezereka ndi Yesu ndi kuwopa kuti Yesu angakhale ndi chiyambi chaumulungu, Pilato akuyambanso zoyesayesa zake za kummasula. Komabe, Ayudawo akukanira Pilato kwa mtuwagalu. Iwo akubwerezanso chinenezo chawo chandale zadziko, mwamachenjera akumawopseza kuti: “Ngati mumasula ameneyo, simuli bwenzi la Kaisara; yense wodziyesera yekha mfumu atsutsana naye Kaisara.”
Mosasamala kanthu za malingaliro oipawo, Pilato akutulutsira Yesu kunja kachiŵirinso. “Tawonani, Mfumu yanu!” akuchondereranso kachiŵiri.
“Chotsani, chotsani, mpachikeni iye!”
“Ndipachike Mfumu yanu kodi?” Pilato akufunsa mothedwa nzeru.
Ayuda avutika ndi ulamuliro wa Aroma. Ndithudi, iwo amanyoza ulamuliro wa Roma! Komabe, mwachinyengo, akulu ansembe akuti: “Tiribe Mfumu koma Kaisara.”
Powopera malo ake andale zadziko ndi mbiri yake, Pilato pomalizira pake akugonjera kupempho lakhama la Ayuda. Iye akupereka Yesu. Asilikali akuvula Yesu chibakuwacho namveka chovala chake chakunja. Pamene Yesu akutengeredwa kukapachikidwa, akumnyamulitsa mtengo wake wozunzirapo.
Pakali pano ndi Lachisanu pakatikati pa mmaŵa, Nisani 14; mwinamwake dzuŵa liri pafupi kufika pamutu. Yesu sanagone chiyambire Lachinayi mmaŵamaŵa, ndipo wakumana ndi zochitika zoŵawa motsatizanatsatizana. Momvekera bwino, nyonga yake ikutha mwamsanga atalemedwa ndi mtengowo. Chotero munthu wina woyenda m’njira, Simoni wa ku Kurene mu Afrika, akuumirizidwa kuchita utumiki wa kumnyamulira mtengowo. Pamene akupita, anthu ambiri, kuphatikizapo akazi, akutsatira, akumadziguguda pachifuwa ndi kulirira Yesu.
Potembenukira kwa akaziwo, Yesu akuti: “Ana aakazi inu a Yerusalemu, musandilirire ine, koma mudzilirire nokha ndi ana anu. Chifukwa tawonani masiku alinkudza, pamene adzati, Odala ali ouma ndi mimba yosabala, ndi maŵere osayamwitsa. . . . Pakuti ngati azichitira izi mtengo wauŵisi, nanga kudzatani ndi wouma?”
Yesu akunena mtengo wa mtundu wa Ayuda, umene udakali ndi uŵisi wa moyo chifukwa cha kukhalapo kwa Yesu ndi kukhalapo kwa otsalira amene amamkhulupirira. Koma pamene ameneŵa achotsedwa mumtunduwo, padzatsala kokha mtengo wakufa mwauzimu, inde, gulu lamtundu louma. Kalanga ine, mmene padzakhalira cholilitsa nanga pamene magulu ankhondo Aroma, otumikira monga magulu akupha a Mulungu, apululutsa mtundu Wachiyudawo! Yohane 19:6-17; 18:31; Luka 23:24-31; Mateyu 27:31, 32; Marko 15:20, 21.
▪ Kodi ndichinenezo chotsutsa Yesu chotani chimene atsogoleri achipembedzo akupanga pamene zinenezo zawo zandale zadziko zikulephera?
▪ Kodi nchifukwa ninji Pilato akufikira kukhala wamantha mowonjezereka?
▪ Kodi ndani amene ali ndi tchimo lalikulu kaamba ka zimene zikuchitikira Yesu?
▪ Pomalizira pake, kodi ansembe akuchititsa motani Pilato kupereka Yesu kukaphedwa?
▪ Kodi nchiyani chimene Yesu akuuza akazi amene akumlirira, ndipo kodi akutanthauzanji mwa kutchula mtengo kukhala “wauŵisi” ndiyeno “wouma”?