Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • sp tsamba 11-12
  • Ziwanda Zimapha

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ziwanda Zimapha
  • Kodi Mizimu ya Akufa Ilipodi?
  • Nkhani Yofanana
  • Yesu Ali ndi Mphamvu Kuposa Ziwanda
    Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso
  • Nthumwi za Zoipa
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Zimene Tiyenera Kudziwa Zokhudza Angelo
    Zimene Baibulo Limaphunzitsa
  • Kodi Ziŵanda Zilipodi?
    Galamukani!—1998
Onani Zambiri
Kodi Mizimu ya Akufa Ilipodi?
sp tsamba 11-12

Ziwanda Zimapha

Satana ndi ziwanda ndi ankhanza ndiponso oopsa. M’mbuyomu, Satana anapha ziweto komanso antchito a Yobu. Kenako anayambitsa “chimphepo” chimene chinagwetsa nyumba n’kupha ana 10 a Yobu. Pomaliza anamudwalitsa “zilonda zopweteka, kuyambira kuphazi mpaka kumutu.”​—Yobu 1:7-19; 2:7.

M’nthawi ya Yesu ziwanda zinkachititsa anthu kuti akhale akhungu komanso osalankhula. (Mateyu 9:32, 33; 12:22) Zinazunzanso munthu wina moti ankadzitematema ndi miyala. (Maliko 5:5) Zinachititsanso mnyamata wina kugwa pansi n’kumachita ngati akuphupha.​—Luka 9:42.

Satana ndi ziwanda zake akuchititsa kuti Yobu adwale zilonda zopweteka komanso kuti munthu wina agwe pansi n’kumachita ngati akuphupha

M’mbuyomu, ziwanda zinkadwalitsa anthu komanso kuwazunza

Masiku anonso Satana ndi ziwanda zake amapha anthu. Kuyambira pamene anagwetsedwa kuchokera kumwamba, akuzunza kwambiri anthu ndipo umboni wake ulipo padziko lonse. Mwachitsanzo, ziwanda zimadwalitsa anthu, kuwalepheretsa kugona chifukwa cha mantha, kuwalotetsa zoopsa ndipo ena zimawagwirira. Anthu ena zimawachititsa misala pomwe ena zimawachititsa kudzipha kapena kupha anthu ena.

Ziwanda zikuchititsa anthu kukhala ankhanza, zikuwalepheretsa kugona komanso zikuwalotetsa zoopsa

Masiku ano ziwanda zimachititsa anthu kukhala ankhanza, zimawalepheretsa kugona ndipo zimawalotetsa zinthu zoopsa

Mayi wina wa ku Suriname dzina lake Lintina, ananena kuti chiwanda chinapha abale ake okwana 16 ndipo chinamuzunza kwa zaka 18. Iye anazindikira kuti ziwanda zimasangalala zikamazunza anthu mpaka kufika powapha.

Koma Yehova ndi wokonzeka kuteteza atumiki ake.​—Miyambo 18:10.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena