Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • dg gawo 8 tsamba 17-19
  • Chifuno cha Mulungu Chiri Pafupi Kukwaniritsidwa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chifuno cha Mulungu Chiri Pafupi Kukwaniritsidwa
  • Kodi Mulungu Amatisamaliradi?
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mfumu Yatsopano ya Dziko Lapansi
  • Olamulira Anzake
  • Kudzilamulira Kudzatha
  • Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?
    Zimene Baibulo Limaphunzitsa
  • Ufumu wa Mulungu—Ulamuliro Watsopano wa Dziko Lapansi
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Ufumu “Woti Sudzawonongeka ku Nthaŵi Zonse”
    Lambirani Mulungu Woona Yekha
Onani Zambiri
Kodi Mulungu Amatisamaliradi?
dg gawo 8 tsamba 17-19

Chigawo 8

Chifuno cha Mulungu Chiri Pafupi Kukwaniritsidwa

1, 2. Kodi Mulungu wakhala akupanga motani makonzedwe akuchotsa kuvutika?

ULAMULIRO wa anthu opanduka ndi ziŵanda wakhala ukududuluza motsendereza banja laumunthu kwa zaka zambiri. Komabe, Mulungu sananyalanyaze mavuto athu. Mmalomwake, mkati mwa zaka mazana ambiri zonsezi, iye wakhala akuchita makonzedwe akumasula anthu munsinga za kuipa ndi kuvutika.

2 Panthaŵi yachipanduko mu Edene, Mulungu anayamba kuvumbula chifuno chake cha kupanga boma limene likapanga dziko lapansi kukhala malo a paradaiso kaamba ka anthu. (Genesis 3:15) Pambuyo pake, monga wolankhulira wamkulu wa Mulungu, Yesu anapanga kudza kwa boma la Mulungu limeneli kukhala mutu wankhani wa kuphunzitsa kwake. Iye ananena kuti likakhala chiyembekezo chokha cha anthu.—Danieli 2:44; Mateyu 6:9, 10; 12:21.

3. Kodi Yesu anatcha boma lilinkudza padziko lapansi kukhala chiyani, ndipo chifukwa ninji?

3 Yesu anatcha boma lilinkudza la Mulungu limenelo “ufumu wakumwamba,” chifukwa chakuti likalamulira kuchokera kumwamba. (Mateyu 4:17) Iye analitchanso “ufumu wa Mulungu,” chifukwa chakuti Mulungu akakhala Magwero ake. (Luka 17:20) Mkati mwa zaka mazana ambiri Mulungu anauza olemba ake kulemba maulosi onena za awo amene akapanga boma limenelo ndi zimene likakwaniritsa.

Mfumu Yatsopano ya Dziko Lapansi

4, 5. Kodi Mulungu anasonyeza motani kuti Yesu anali Mfumu yake yovomerezedwa?

4 Anali Yesu, pafupifupi zaka zikwi ziŵiri zapitazo, amene anakwaniritsa maulosi ambiri onena za uyo amene akakhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. Iye anatsimikizira kukhala wosankhidwa wa Mulungu kukhala Wolamulira wa boma la kumwamba limenelo pamtundu wa anthu. Ndipo pambuyo pa imfa yake, Mulungu anaukitsira Yesu kumoyo wakumwamba monga cholengedwa champhamvu, chauzimu chosakhoza kufa. Panali mboni zochuluka za chiukiliro chake.—Machitidwe 4:10; 9:1-9; Aroma 1:1-4; 1 Akorinto 15:3-8.

5 Pamenepo Yesu “anakhala pa dzanja lamanja la Mulungu.” (Ahebri 10:12) Kumeneku iye anayembekezera nthaŵi pamene Mulungu akampatsa mphamvu ya kuchitapo kanthu monga Mfumu ya Ufumu wakumwamba. Izi zinakwanilitsa ulosi wa Salmo 110:1, kumene Mulungu akumuuza kuti: “Khalani pa dzanja lamanja langa, kufikira nditaika adani anu chopondapo mapazi anu.”

6. Kodi ndi motani mmene Yesu anasonyezera kuti anayeneretsedwa kukhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu?

6 Akali padziko lapansi, Yesu anasonyeza kuti anayeneretsedwa kaamba ka malo a ntchito amenewo. Mosasamala kanthu za chizun’zo, iye anasankha kusunga umphumphu wake kwa Mulungu. Mwakutero, iye anasonyeza kuti Satana ananama pamene adanena kuti palibe munthu akakhala wokhulupirika kwa Mulungu poyesedwa. Yesu, munthu wangwiro, ‘Adamu wachiŵiri,’ anasonyeza kuti Mulungu sanalakwe kupanga anthu angwiro.—1 Akorinto 15:22, 45; Mateyu 4:1-11.

7, 8. Kodi ndi zinthu zabwino ziti zimene Yesu anachita pamene anali padziko lapansi, ndipo kodi iye anasonyezanji?

7 Kodi ndi wolamulira uti anakwaniritsa zabwino zochuluka motero monga momwe anachitira Yesu m’zaka zoŵerengeka za uminisitala wake? Atapatsidwa mphamvu ndi mzimu woyera wa Mulungu, Yesu anachiritsa odwala, opunduka, akhungu, ogontha, osalankhula. Iye anaukitsa ngakhale akufa! Iye anasonyeza pamlingo waung’ono zimene akakhoza kuchitira anthu pamlingo wadziko lonse pamene akadza m’mphamvu ya Ufumu.—Mateyu 15:30, 31; Luka 7:11-16.

8 Yesu anachita zabwino zochuluka akali padziko lapansi kotero kuti wophunzira wake Yohane anati: “Koma palinso zina zambiri zimene Yesu anazichita, zoti zikadalembedwa zonse phe, ndilingalira kuti dziko lapansi silikadakhala nawo malo a mabuku amene akadalembedwa.”—Yohane 21:25.a

9. Kodi n’chifukwa ninji anthu owona mtima anadza muunyinji wawo kwa Yesu?

9 Yesu anali wokoma mtima ndi wachifundo, wokhala ndi chikondi chachikulu pa anthu. Iye anathandiza aumphaŵi ndi otsenderezedwa, koma iye sanachite mosankha kwa achuma kapena aukumu. Anthu owona mtima analabadira kuchiitano chachikondi cha Yesu pamene iye anati: “Idzani kuno kwa ine nonsenu akulema ndi akuthodwa, ndipo ine ndidzakupumulitsani inu. Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa ine; chifukwa ine ndili wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu. Pakuti goli langa lili lofewa ndi katundu wanga ali wopepuka.” (Mateyu 11:28-30) Anthu owopa Mulungu anadza muunyinji wawo kwa iye nayembekezera ulamuliro wake.—Yohane 12:19.

Olamulira Anzake

10, 11. Kodi ndani amene adzagaŵana ndi Yesu m’kulamulira dziko lapansi?

10 Monga momwe maboma aumunthu alili ndi olamulira anzawo, choteronso Ufumu wakumwamba wa Mulungu. Ena kuwonjezera pa Yesu adzakhala ndi phande m’kulamulira dziko lapansi, pakuti Yesu analonjeza atsamwali ake apafupi kuti akalamulira limodzi naye monga mafumu pa anthu.—Yohane 14:2, 3; Chivumbulutso 5:10; 20:6.

11 Chifukwa chake, limodzi ndi Yesu, chiŵerengero chochepa cha anthu chikuukitsidwira kumoyo wakumwamba. Iwo amapanga Ufumu wa Mulungu umene udzabweretsa madalitso osatha kwa mtundu wa anthu. (2 Akorinto 4:14; Chivumbulutso 14:1-3) Chotero mkati mwa zaka mazana ambiriwo, Yehova wayala maziko aulamuliro umene udzabweretsa madalitso osatha kubanja laumunthu.

Kudzilamulira Kudzatha

12, 13. Kodi Ufumu wa Mulungu wakonzekera kuchita chiyani tsopano?

12 M’zaka za zana lino Mulungu waphatikizidwa mwachindunji m’zochitika za dziko lapansi. Monga momwe Chigawo 9 cha brosha lino chidzalongosolera mwatsatanetsatane, ulosi wa Baibulo umasonyeza kuti Ufumu wa Mulungu mwa Kristu unakhazikitsidwa mu 1914 ndi kuti tsopano uli wokonzekera kuwononga dongosolo lonse la Satana. Ufumu umenewu uli wokonzekera ‘kuchita ufumu pakati pa adani [a Kristu].’—Salmo 110:2.

13 Ponena za zimenezi ulosi wa Danieli 2:44 umati: “Ndipo m’masiku a mafumu aja [amene alipo tsopano] Mulungu wakumwamba adzaika ufumu [kumwamba] woti sudzawonongeka kunthaŵi zonse, ndipo ulamuliro wake sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu [ulamuliro wa anthu sudzaloledwanso], koma [Ufumu wa Mulungu] udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse nudzakhala chikhalire.”

14. Kodi ndi mapindu ena ati amene adzakhalapo pakutha kwa ulamuliro wa anthu?

14 Pamene ulamuliro wonse wosadalira pa Mulungu uchotsedwa, ulamuliro wa Ufumu wa Mulungu padziko lapansi udzakhala wachikwanekwane. Ndipo chifukwa chakuti Ufumuwo ukulamulira uli kumwamba, uwo sungaipitsidwe konse ndi anthu. Mphamvu zolamulira zidzakhala kumene zinali poyambirira, ndiko kuti kumwamba, ndi Mulungu. Ndipo popeza kuti ulamuliro wa Mulungu udzalamulira dziko lonse lapansi, sipadzakhalanso munthu wina aliyense wosochezedwa ndi chipembedzo chonyenga kapena ziphunzitso za anthu zopanda ungwirozo ndi nthanthi za ndale zadziko. Palibe chilichonse cha zinthu zimenezi chimene chidzaloledwa kukhalako.—Mateyu 7:15-23; Chivumbulutso, chaputala 17 mpaka 19.

[Mawu a M’munsi]

a Kuti mumve zonse za moyo wa Yesu, wonani buku la Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako, lofalitsidwa mu 1992 ndi Watchtower Society.

[Chithunzi patsamba 18]

Pamene anali padziko lapansi Yesu anachiritsa odwala naukitsa akufa kusonyeza zimene iye akachita m’dziko latsopano

[Chithunzi patsamba 19]

Ufumu wakumwamba wa Mulungu udzatsogolera magulu a angelo kuwononga psiti mipangidwe yonse ya ulamuliro wa anthu wosadalira pa iye

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena