Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • dg gawo 10 tsamba 22-28
  • Dziko Latsopano Lokongola Koposa la Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Dziko Latsopano Lokongola Koposa la Mulungu
  • Kodi Mulungu Amatisamaliradi?
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chilungamo Chiloŵa Mmalo mwa Kuipa
  • Thanzi Langwiro Libwezeretsedwa
  • Akufa Abweranso
  • Dziko Lamtenderedi
  • Dziko Lapansi Lisandulizidwa Kukhala Paradaiso
  • Kukonzetsa Zakale
  • Khalani ndi Moyo Kosatha Padziko Lapansi Laparadaiso
    Kodi Moyo Uli ndi Chifuno?
  • Dziko Latsopano Lopanda Mavuto
    Galamukani!—1990
  • Pambuyo pa Harmagedo, Dziko Lapansi Laparadaiso
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
  • Moyo m’Dziko Latsopano Lamtendere
    Moyo m’Dziko Latsopano Lamtendere
Onani Zambiri
Kodi Mulungu Amatisamaliradi?
dg gawo 10 tsamba 22-28

Chigawo 10

Dziko Latsopano Lokongola Koposa la Mulungu

1, 2. Kodi chidzachitika n’chiyani pambuyo pankhondo yoyeretsa ya Armagedo?

PAMBUYO pa nkhondo ya Mulungu ya Armagedo yoyeretsayo, pamenepo chiyani? Pamenepo, nyengo yatsopano yaulemerero idzayamba. Opulumuka Armagedo, pokhala atatsimikizira kale kukhulupirika kwawo kuulamuliro wa Mulungu, adzaloŵetsedwa m’dziko latsopano. Ndinyengo yochititsa nthumanzi chotani nanga m’mbiri imene idzakhalapo pamene mapindu osangalatsa adzayenda tawatawa kuchokera kwa Mulungu kumka kubanja laumunthu!

2 Motsogozedwa ndi Ufumu wa Mulungu, opulumukawo adzayamba kulima paradaiso. Nyonga zawo zidzagwiritsidwa ntchito kuzochita zopanda dyera zimene zidzapindulitsa amoyo onse panthaŵiyo. Dziko lapansi lidzayamba kusandulizidwa kukhala malo okongola, amtendere, ndi okhutilitsa a mtundu wa anthu.

Chilungamo Chiloŵa Mmalo mwa Kuipa

3. Kodi ndi mpumulo wa panthaŵi yomweyo wotani umene udzamvedwa mwamsanga pambuyo pa Armagedo?

3 Zonsezi zidzatheketsedwa ndi chiwonongeko cha dziko la Satana. Sipadzakhalanso zipembedzo zonyenga zogaŵanitsa, madongosolo a zamakhalidwe a anthu, kapena maboma. Sipadzakhalanso manenanena okopa auchiŵanda onyenga anthu; magulu onse oŵatulutsa adzawonongedwera limodzi ndi dongosolo la Satana. Tangolingalirani: kuchotsedwa kwa mpweya wonse wakupha wa dziko la Satana! Umenewu udzakhala mpumulo wotani nanga!

4. Fotokozani kusintha kwachiphunzitso kumene kudzachitika.

4 Pamenepo malingaliro owononga aulamuliro wa anthu adzaloŵedwa mmalo ndi chiphunzitso cholimbikitsa chimene chidzadza kuchokera kwa Mulungu. “Ana ako onse adzaphunzitsidwa ndi Yehova.” (Yesaya 54:13) Mwamalangizo abwino amenewa ochitidwa chaka ndi chaka, “dziko lapansi lidzadzala ndi odziŵa Yehova monga madzi adzaza nyanja.” (Yesaya 11:9) Anthu sadzaphunziranso zoipa, koma “okhala m’dziko lapansi adzaphunzira chilungamo.” (Yesaya 26:9) Maganizo olimbikitsa ndi ntchito zidzakhala mkhalidwe wa panthaŵiyo.—Machitidwe 17:31; Afilipi 4:8.

5. Kodi chidzachitika n’chiyani kukuipa konse ndi anthu oipa?

5 Chotero, sipadzakhalanso mbanda, chiwawa, kugwirira chigololo, kuba, kapena upandu wina uliwonse. Palibe munthu amene adzavutika chifukwa cha kuchita zoipa kwa ena. Miyambo 10:30 imati: “Wolungama sadzachotsedwa konse; koma oipa sadzakhalabe m’dziko.”

Thanzi Langwiro Libwezeretsedwa

6, 7. (a) Kodi ndi chenicheni chomvetsa chisoni chotani chimene ulamuliro wa Ufumu udzathetsa? (b) Kodi ndi motani mmene Yesu anasonyezera chimenechi pamene anali padziko lapansi?

6 M’dziko latsopano, mudzakhala kuchotsedwa kwa zoipa zonse za chipanduko choyambirira. Mwachitsanzo, ulamuliro wa Ufumu udzachotsa matenda ndi ukalamba. Lerolino, ngakhale ngati muli ndi mlingo wochepekera wathanzi labwino, chowonadi chovutitsa maganizo chili chakuti pamene mukukalamba, maso anu amachita chizimezime, mano anu amawola, makutu anu amagontha, khungu lanu limachita makwinya, ziŵalo zanu zamkati zimanyonyotsoka, kufikira potsirizira pake mufa.

7 Komabe, ziyambukiro zomvetsa chisoni zimenezo zimene tinalandira mwacholoŵa kuchokera kwa makolo athu oyamba zidzatha posachedwapa. Kodi mukukumbukira zimene Yesu anasonyeza ponena za thanzi pamene anali padziko lapansi? Baibulo limati: “Makamu ambiri a anthu anadza kwa iye, ali nawo opunduka miyendo, akhungu, osalankhula, opunduka ziŵalo, ndi ena ambiri, nawakhazika pansi pa mapazi ake: ndipo iye anawachiritsa: kotero kuti khamulo linazizwa, pakupenya wosalankhula nalankhula, opunduka ziŵalo nachira, ndi wopunduka miyendo nayenda, ndi akhungu napenya, ndipo iwo analemekeza Mulungu wa Israyeli.”—Mateyu 15:30, 31.

8, 9. Fotokozani chimwemwe chimene chidzadza m’dziko latsopano pamene thanzi langwiro libwezeretsedwa.

8 N’chimwemwe chachikulu chotani nanga chimene chidzakhalamo m’dziko latsopano pamene nthenda zathu zonse zidzachotsedwa! Kuvutika chifukwa cha thanzi losakhala bwino sikudzativutitsanso. “Wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.” “Pamenepo maso akhungu adzatsegudwa, makutu a ogontha adzatsegulidwa. Pamenepo opunduka adzatumpha ngati nswala ndi lilime la wosalankhula lidzaimba.”—Yesaya 33:24; 35:5, 6.

9 Kodi sikudzakhala kochititsa nthumanzi kudzuka m’mamaŵa uliwonse ndi kuzindikira kuti tsopano mukusangalala ndi thanzi lamphamvu? Kodi sikudzakhala kokondweretsa kwa nkhalamba kudziŵa kuti iwo akubwezeretsedwa kunyonga yotheratu ya unyamata ndipo adzafikira ku ungwiro umene Adamu ndi Hava poyambirira anasangalala nawo? Lonjezo la Baibulo n’lakuti: “Mnofu wake udzakhala see kuposa wa mwana; adzabwerera kumasiku aubwana wake.” (Yobu 33:25) Kudzakhala kokondweretsa chotani nanga kutaya magalasi amenewo, zothandizira kumva, ndodo za opunduka, njinga za opunduka, ndi mankhwala! Zipatala, madokotala, ndi madokotala a mano sadzakhalanso ofunika.

10. Kodi n’chiyani chidzachitika ku imfa?

10 Anthu amene adzasangalala ndi thanzi labwino chotero sadzafuna kufa. Ndipo iwo sadzafunikira kutero chifukwa chakuti anthu sadzakhalanso muukapolo wakupanda ungwiro wa choloŵa ndi imfa. Kristu ‘adzachita ufumu kufikira ataika adani onse pansi pa mapazi ake. Mdani wotsiriza amene adzathedwa ndiye imfa.’ “Mphatso yaulere ya Mulungu ndiyo moyo wosatha.”—1 Akorinto 15:25, 26; Aroma 6:23; wonaninso Yesaya 25:8.

11. Kodi Chivumbulutso chimafotokoza mwachidule motani madalitso a dziko latsopano?

11 Polongosola mwachidule mapindu amene adzatsanuliridwa ndi Mulungu wosamala pabanja laumunthu mu Paradaiso, buku lotsirizira la Baibulo limati: “Ndipo [Mulungu] adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita.”—Chivumbulutso 21:3, 4.

Akufa Abweranso

12. Kodi Yesu anasonyeza motani mphamvu yake yopatsidwa ndi Mulungu ya kuukitsa akufa?

12 Yesu anachita zochuluka koposa kuchiritsa odwala ndi kuchiritsa opunduka. Iye anabwezeretsanso anthu kuchokera kumanda. Chotero iye anasonyeza mphamvu yozizwitsa yachiukiliro imene Mulungu anampatsa. Kodi mukukumbukira chochitika china pamene Yesu analoŵa m’nyumba ya mwamuna wina amene mwana wake wamkazi adafa? Yesu anati kwa msungwana wakufayo: “Buthu, ndinena ndi iwe, uka!” N’chotulukapo chotani? “Ndipo pomwepo buthulo linauka niliyenda.” Atawona zimenezo, anthu kumeneko ‘anadabwa ndi kudabwa kwakukulu.’ Iwo anali ndi chisangalalo chachikulu!—Marko 5:41, 42; wonaninso Luka 7:11-16; Yohane 11:1-45.

13. Kodi ndi anthu amtundu wotani amene adzaukitsidwa?

13 M’dziko latsopano ‘mudzakhala kuuka kwa onse aŵiri olungama ndi osalungama.’ (Machitidwe 24:15) Panthaŵiyo Yesu adzagwiritsira ntchito mphamvu yake yopatsidwa ndi Mulungu kuukitsa akufa chifukwa chakuti, monga momwe ananenera kuti “ine ndine kuuka ndi moyo: wokhulupirira ine, angakhale amwalira, adzakhala ndi moyo.” (Yohane 11:25) Iye anatinso: “Onse amene ali m’manda achikumbukiro [chikumbukiro cha Mulungu] adzamva mawu ake [a Yesu] ndikutulukamo.”—Yohane 5:28, 29, NW.

14. Chifukwa chakuti imfa sidzakhalakonso, kodi n’zinthu ziti zimene zidzachotsedwa?

14 Chisangalalocho chidzakhala chachikulu padziko lonse lapansi pamene kagulu motsatizana ndi kagulu ka anthu akufa kabwezeretsedwa kumoyo kugwirizana ndi okondedwa awo! Sipadzakhalanso zigawo za mauthenga a maliro m’manyuzipepala zodzetsa chisoni kwa opulumuka. Mmalomwake, pangakhaledi zosiyana: zilengezo za awo oukitsidwa chatsopano kudzetsa chisangalalo kwa awo amene anawakonda. Chotero sipadzakhalanso maliro, nyumba za maliro, malo otentherako mitembo, kapena kumanda!

Dziko Lamtenderedi

15. Kodi ulosi wa Mika udzakwaniritsidwa motani m’lingaliro lotheratu?

15 Mtendere weniweni m’mbali zonse za moyo udzakwaniritsidwa. Nkhondo, ochirikiza nkhondo, ndi kupanga zida zankhondo adzatha. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti zikhumbo zogaŵanitsa zautundu, ufuko, ndi mawonekedwe akhungu zidzazimiririka. Pamenepo, m’lingaliro lotheratu, “mtundu wa anthu sudzasamulira mtundu unzake lupanga, kapena kuphunziranso nkhondo.”—Mika 4:3.

16. Kodi Mulungu adzatsimikizira motani kuti nkhondo zikhala zosatheka?

16 Izi zingawonekere kukhala zodabwitsa chifukwa cha mbiri ya anthu ya kukhetsa mwazi m’nkhondo zosalekeza. Komatu zimenezo zachitika chifukwa chakuti anthu akhala akulamulidwa ndi ulamuliro wa anthu ndi wauchiŵanda. M’dziko latsopano, pansi pa ulamuliro wa Ufumu, zidzachitika ndi izi: “Idzani, penyani ntchito za Yehova . . . aletsa nkhondo kumalekezero a dziko lapansi; athyola uta, nadula nthungo; atentha magaleta ndi moto.”—Salmo 46:8, 9.

17, 18. M’dziko latsopano, kodi ndi unansi wotani umene udzakhalapo pakati pa anthu ndi zinyama?

17 Anthu ndi nyama adzakhalanso pamtendere, monga momwe analiri mu Edene. (Genesis 1:28; 2:19) Mulungu amati: “Tsiku lomwelo ndidzawachitira pangano ndi nyama zakuthengo, ndi mbalame zamlengalenga, ndi zokwawa pansi; ndipo . . . ndidzawagonetsa pansi mosatekeseka.”—Hoseya 2:18.

18 Kodi mtendere umenewu udzakhala waukulu chotani? “Mmbulu udzakhala pamodzi ndi mwana wankhosa, ndipo nyalugwe adzagona pansi ndi mwana wa mbuzi; mwana wang’ombe ndi mwana wamkango ndi choweta chonenepa pamodzi; ndipo mwana wamng’ono adzazitsogolera.” Zinyama sizidzakhalanso chiwopsezo kwa anthu kapena pakati pa izo zokha. Ngakhale “mkango udzadya udzu ngati ng’ombe”!—Yesaya 11:6-9; 65:25.

Dziko Lapansi Lisandulizidwa Kukhala Paradaiso

19. Kodi dziko lapansi lidzasandulizidwa kukhala chiyani?

19 Dziko lonse lapansi lidzasandulizidwa kukhala malo a paradaiso a mtundu wonse wa anthu. Ndicho chifukwa chake Yesu anakhoza kulonjeza mwamuna amene anamkhulupilira kuti “udzakhala ndi ine m’paradaiso.” Baibulo limati: “Chipululu ndi malo ouma adzakondwa; ndipo dziko lonse lidzakhala ndi kuphuka ngati duŵa. . . . Pakuti m’chipululu madzi adzatuluka, ndi mitsinje m’dziko loti see.”—Luka 23:43; Yesaya 35:1, 6.

20. Kodi n’chifukwa ninji njala sidzakanthanso mtundu wa anthu?

20 Mu Ufumu wa Mulungu, njala sidzakanthanso mamiliyoni ambiriwo. “M’dzikomo mudzakhala dzinthu dzochuluka pamwamba pamapiri.” “Mitengo yakuthengo idzapereka zobala zawo, ndi nthaka idzapereka zipatso zake, ndipo adzakhazikika m’dziko mwawo.”—Salmo 72:16; Ezekieli 34:27.

21. Kodi chidzachitika n’chiyani kumkhalidwe wakupanda nyumba, nyumba zauve, ndi zitaganya zaupandu?

21 Sikudzakhalanso umphaŵi, anthu opanda malo okhala, nyumba zauve, kapena zitaganya zokanthidwa ndi upandu. “Iwo adzamanga nyumba ndi kukhalamo; ndipo iwo adzawoka minda yampesa, ndi kudya zipatso zake. Iwo sadzamanga ndi wina kukhalamo; sadzawoka ndi wina kudya.” “Adzakhala munthu yense patsinde pa mpesa wake ndi patsinde pamkuyu wake; ndipo sipadzakhala wakuwawopsa.”—Yesaya 65:21, 22; Mika 4:4.

22. Kodi Baibulo limafotokoza motani madalitso aulamuliro wa Mulungu?

22 Anthu adzadalitsidwa ndi zinthu zonse zimenezi, ndi zina zambiri, m’Paradaiso. Salmo 145:16 limati: “[Mulungu] muwoloŵetsa dzanja lanu, nimukwaniritsa zamoyo zonse chikhumbo chawo.” M’posadabwitsa kuti ulosi wa Baibulo umati: “Ofatsa adzalandira dziko lapansi, nadzakondwera nawo mtendere wochuluka . . . Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.”—Salmo 37:11, 29.

Kukonzetsa Zakale

23. Kodi Ufumu wa Mulungu udzakonzetsa motani kuvutika konse kumene takumana nako?

23 Ulamuliro wa Ufumu wa Mulungu udzakonza kuvulazidwa konse kochitidwa pabanja laumunthu, kwazaka zikwi zisanu ndi chimodzi zapitazo. Zisangalalo panthaŵiyo zidzaposa kwambiri mavuto aliwonse amene anthu anakumana nawo. Moyo sudzakhala wododometsedwa ndi zikumbukiro zoipa za kuvutika kwa papitapo. Malingaliro olimbikitsa ndi ntchito zimene zidzakhala zochitika za tsiku ndi tsiku kwa anthu potsirizira pake zidzafafaniza zikumbukiro zachisonizo.

24, 25. (a) Kodi n’chiyani chimene Yesaya adaneneratu kuti chikachitika? (b) Kodi n’chifukwa ninji tingatsimikizire kuti zikumbukiro zapapitapo zakuvutika zidzazimiririka?

24 Mulungu wosamalayo amati: “Ndilenga kumwamba kwatsopano [boma latsopano lakumwamba lolamulira pamtundu wa anthu] ndi dziko lapansi latsopano [gulu la anthu olungama]; ndipo zinthu zakale sizidzakumbukika, kapena kulowa mumtima. Koma khalani inu okondwa ndi kusangalala kunthaŵi zonse ndi ichi ndichilenga.” “Dziko lonse lapuma, lili duu; iwo ayamba kuyimba nyimbo.”—Yesaya 14:7; 65:17, 18.

25 Chotero mwa Ufumu wake, Mulungu adzasanduliza mkhalidwe woipa umene wakhalako kwanthaŵi yaitaliwo. Kuumuyaya wonse iye adzasonyeza chisamaliro chake chachikulu pa ife mwakutsanulira madalitso amene adzakhala ochulukitsitsa powayerekezera ndi chivulazo chilichonse chimene tinalandira m’moyo wathu wapapitapo. Pamenepo mavuto apitawo amene tinali nawo adzazimiririka m’chikumbukiro; ngati ndi iko komwe tingadzafune kuwakumbukira.

26. Kodi n’chifukwa ninji Mulungu adzatilipira kaamba ka kuvutika kwathu konse kwapita?

26 Umu ndimo mmene Mulungu adzatilipirira kaamba kakuvutika kumene tingakhale titapilira nako m’dziko lino. Iye amadziŵa kuti sichinali chifukwa chathu kuti tinabadwa tili opanda ungwiro, pakuti tinalandira kupanda ungwiro mwa choloŵa kuchokera kwa makolo athu oyamba. Sichinali chifukwa chathu kuti tinabadwira m’dziko la Satana, pakuti mmalomwake ngati Adamu ndi Hava akanakhulupirika tikanabadwira m’paradaiso. Chotero mwakukoma mtima kwakukulu Mulungu adzachita zambiri koposa kutibwezera molingana ndi zoipa zimene tinakanthidwa nazo kale.

27. Kodi ndi maulosi otani amene adzakwaniritsidwa modabwitsa m’dziko latsopano?

27 M’dziko latsopano, mtundu wa anthu udzasangalala ndi ufulu wonenedweratu pa Aroma 8:21, 22: “Kuti cholengedwa chomwe chidzamasulidwa kuukapolo wachivundi ndi kuloŵa kuufulu waulemerero wa ana a Mulungu. Pakuti tidziŵa kuti cholengedwa chonse chibuula, ndi kugwidwa m’zowawa pamodzi kufikira tsopano.” Pamenepo anthu adzawona kukwaniritsidwa kotheratu kwa pempherolo: “Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga kumwamba, chomwecho pansi pano.” (Mateyu 6:10) Mikhalidwe yabwino kwambiriyo pa Paradaiso wapadziko lapansi idzasonyeza mikhalidwe yakumwamba.

[Zithunzi patsamba 23]

M’dziko latsopano, okalamba adzabwerera kuthanzi launyamata

[Chithunzi patsamba 24]

M’dziko latsopano nthenda zonse ndi kupunduka zidzachotsedwa

[Chithunzi patsamba 25]

M’dziko latsopano, akufa adzaukitsidwiranso kumoyo

[Chithunzi patsamba 26]

‘Sadzaphunziranso nkhondo’

[Zithunzi patsamba 27]

Anthu ndi zinyama adzakhala mumtendere wotheratu m’Paradaiso

[Chithunzi patsamba 27]

‘Mulungu adzatambasula dzanja lake ndi kukhutitsa chikhumbo cha chamoyo chilichonse’

[Chithunzi patsamba 28]

Ufumu wa Mulungu udzachita zoposa chabe kutilipira kaamba ka kuvutika konse kumene takumana nako

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena