Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • pr gawo 4 tsamba 16-19
  • Dziko Lachikristu Lanyengeza Mulungu ndi Baibulo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Dziko Lachikristu Lanyengeza Mulungu ndi Baibulo
  • Kodi Moyo Uli ndi Chifuno?
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Ziphunzitso Zosakhala za m’Baibulo
  • Zochita Zopanda Umulungu
  • Sali Achikristu
  • Chiweruzo cha Mulungu Motsutsana ndi “Munthu Wosayeruzika”
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Chikristu cha Dziko Chavumbulidwa Monga Chopititsa Patsogolo Kulambira Konyenga
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Bwenzi Lonyenga la Baibulo
    Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu?
  • Chiweruzo cha Yehova pa Aphunzitsi Onama
    Nsanja ya Olonda—1994
Onani Zambiri
Kodi Moyo Uli ndi Chifuno?
pr gawo 4 tsamba 16-19

Mbali 4

Dziko Lachikristu Lanyengeza Mulungu ndi Baibulo

1 Anthu a m’maiko ambiri apeŵa Baibulo ndipo sanalilemekeze chifukwa cha khalidwe loipa la awo amene amadzinenera kuti amalitsatira. M’maiko ena kwanenedwa kuti Baibulo ndibuku loyambitsa nkhondo, kuti ndibuku la azungu, ndi kuti ndibuku limene limachilikiza utsamunda. Komatu amenewo ndimalingaliro olakwika.

2 Baibulo, limene linalembedwera ku Middle East, silimachilikiza nkhondo zautsamunda ndi kudyerana masuku pamutu kwaumbombo kumene kwachitidwa m’dzina Lachikristu kwa nthaŵi yaitali motero. Mosemphana, mwakuŵerenga Baibulo ndi kuphunzira ziphunzitso za Chikristu chowona chophunzitsidwa ndi Yesu, mudzawona kuti Baibulo limatsutsa mwamphamvu nkhondo, makhalidwe oipa, ndi kudyera ena masuku pamutu. Vuto lili ndi anthu aumbombo, osati Baibulo. (1 Akorinto 13:​1-6; Yakobo 4:​1-3; 5:​1-6; 1 Yohane 4:​7, 8) Chotero musalole kuti khalidwe loipa la anthu adyera amene amakhala mosemphana ndi uphungu wabwino wa Baibulo likulepheretseni kupeza mapindu ake.

3 Anthu ndi maiko a Dziko Lachikristu aphatikizidwa pakati pa anthu amene samalabadira uphungu wa Baibulo. “Dziko Lachikristu” lamasuliridwa kukhala mbali ya dziko kumene Chikristu chili chofala. Makamaka lili dziko la Kumadzulo ndi matchalitchi ake, limene linakhala lotchuka pafupifupi m’zaka za zana lachinayi C.E. Dziko Lachikristu lakhala ndi Baibulo kwa zaka mazana ambiri, ndipo atsogoleri ake achipembedzo amadzinenera kuti amaliphunzitsa ndi kuti ndiwo oimira a Mulungu. Koma kodi atsogoleri achipembedzo ndi amishonale a Dziko Lachikristu amaphunzitsa chowonadi? Kodi zochita zawo zimaimiradi Mulungu ndi Baibulo? Kodi Chikristu nchofala m’Dziko Lachikristu? Ayi. Kuyambira pamene chipembedzo chake chinatchuka m’zaka za zana lachinayi, Dziko Lachikristu ladzisonyeza kukhala mdani wa Mulungu ndi Baibulo. Inde, zochitika za m’mbiri zimasonyeza kuti Dziko Lachikristu lanyengeza Mulungu ndi Baibulo.

Ziphunzitso Zosakhala za m’Baibulo

4 Ziphunzitso zazikulu za Dziko Lachikristu sizinazikidwe pa Baibulo koma pa nthano zamakedzana​—⁠zija za ku Girisi, Igupto, Babulo, ndi zina. Ziphunzitso zonga ngati kusafa kwa moyo wa munthu, chizunzo chosatha m’moto wahelo, purigatoriyo, ndi Utatu (anthu atatu mwa Mulungu mmodzi) sizimapezeka m’Baibulo.

5 Mwachitsanzo, talingalirani za chiphunzitso chakuti anthu oipa adzazunzidwa kosatha m’helo wamoto. Kodi mumamva motani ndi lingaliro limeneli? Ambiri amanyansidwa nalo. Iwo amakuwona kukhala kopanda nzeru kuti Mulungu akhoza kuzunza anthu kosatha, akumawamvetsa ululu wopweteka. Lingaliro lauchiŵanda limenelo nlosemphana ndi Mulungu wa Baibulo, popeza kuti “Mulungu ndiye chikondi.” (1 Yohane 4:⁠8) Baibulo limanena momvekera bwino kuti chiphunzitso chimenecho ‘sichinaloŵa m’mtima’ mwa Mulungu Wamphamvuyonse.​—⁠Yeremiya 7:31; 19:5; 32:⁠35.

6 Zipembedzo zambiri lerolino, kuphatikizapo matchalitchi a Dziko Lachikristu, zimaphunzitsa kuti anthu ali ndi moyo wosafa, umene umapita kumwamba kapena ku helo pamene munthu afa. Chimenechi sichiphunzitso cha m’Baibulo. M’malomwake, Baibulo limanena momvekera bwino kuti: “Amoyo adziŵa kuti tidzafa; koma akufa sadziŵa kanthu bi, . . . pakuti mulibe ntchito ngakhale kulingirira ngakhale kudziŵa, ngakhale nzeru, kumanda ulikupitako.” (Mlaliki 9:​5, 10) Ndipo wamasalmo amanena kuti pa imfa munthu “abwerera kumka ku nthaka yake; tsiku lomwelo zotsimikiza mtima zake zitayika.”​—⁠Salmo 146:⁠4.

7 Kumbukiraninso kuti pamene Adamu ndi Hava anaswa lamulo la Mulungu, chilango sichinali kusafa. Imeneyo ikanakhala mfupo, osati chilango! M’malomwake, iwo anauzidwa kuti “[aka]bwerera kunthaka: chifukwa kuti m’menemo [ana]tengedwa.” Mulungu anagogomezera kwa Adamu kuti: “Chifukwa kuti ndiwe fumbi, ndi kufumbiko udzabwerera.” (Genesis 3:19) Motero, chiphunzitso cha kusafa kwa moyo sichili m’Baibulo koma Dziko Lachikristu linachitenga kwa anthu osakhala Akristu amene anakhalako icho chisanakhaleko.

8 Ndiponso, chiphunzitso cha Utatu cha Dziko Lachikristu chimachititsa Mulungu kuwoneka ngati Mulungu wachinsinsi wokhala atatu mwa mmodzi. Koma chiphunzitso chimenecho sichipezekanso m’Baibulo. Mwachitsanzo, pa Yesaya 40:​25, Mulungu amanena momvekera bwino kuti: “Mudzandifanizira Ine ndi yani tsono, kuti ndilingane naye.” Yankho nlodziŵikiratu: Palibe amene angalingane naye. Ndiponso, lemba la Salmo 83:18 limanena mosavuta kuti: “Inu nokha, dzina lanu ndinu Yehova, ndinu Wam’mwambamwamba pa dziko lonse lapansi.”​—⁠Onaninso Yesaya 45:5; 46:9; Yohane 5:19; 6:38; 7:⁠16.

9 Ziphunzitso za Baibulo zonena za Mulungu ndi zifuno zake nzomvekera bwino, zosavuta kumva, ndi zanzeru. Koma ziphunzitso za matchalitchi a Dziko Lachikristu sizili choncho. Choipa koposa nchakuti zimatsutsana ndi Baibulo.

Zochita Zopanda Umulungu

10 Kuwonjezera pa ziphunzitso zonyenga, Dziko Lachikristu lanyengeza Mulungu ndi Baibulo mwa zochita zake. Zimene atsogoleri achipembedzo ndi matchalitchi achita zaka mazana apitawo, ndi zimene akupitiriza kuchita m’nthaŵi yathu, nzotsutsananso ndi zimene Mulungu wa Baibulo amafuna ndipo nzotsutsana ndi zimene Woyambitsa Chikristu, Yesu Kristu, anaphunzitsa ndi kuchita.

11 Mwachitsanzo, Yesu anaphunzitsa otsatira ake kusaloŵerera m’nkhani zandale zadziko kapena kuloŵa m’nkhondo zake. Iye anawaphunzitsanso kukhala okonda mtendere, osunga lamulo, ndi kukonda anthu anzawo mopanda tsankho, ngakhale kukhala ofunitsitsa kupereka miyoyo yawo m’malo mwa kupha ena.​—⁠Yohane 15:13; Machitidwe 10:​34, 35; 1 Yohane 4:​20, 21.

12 Ndithudi, Yesu anaphunzitsa kuti kukonda anthu ena kukakhala chizindikiro chodziŵikitsa Akristu owona mwa Akristu onama, onyengezera. Iye anauza amene akamtsatira kuti: “Ndikupatsani inu lamulo latsopano, kuti mukondane wina ndi mnzake; monga ndakonda inu, kuti inunso mukondane wina ndi mnzake. Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.”​—⁠Yohane 13:​34, 35; 15:⁠12.

13 Komabe, kwa zaka mazana ambiri, atsogoleri achipembedzo a Dziko Lachikristu aloŵerera m’ndale zadziko ndipo achilikiza nkhondo za maiko awo. Iwo achilikizanso ngakhale magulu otsutsana nawo m’nkhondo za m’Dziko Lachikristu, monga ngati nkhondo ziŵiri zadziko za m’zana lino. M’nkhondo zimenezo atsogoleri achipembedzo a mbali iliyonse anapempherera chilaliko, ndipo ziŵalo za chipembedzo china za dziko limodzi zinali kupha ziŵalo za chipembedzo chimodzimodzicho za m’dziko lina. Koma mmenemo ndi mmene Baibulo limanenera kuti ana a Satana amachitira, osati a Mulungu. (1 Yohane 3:​10-12, 15) Motero, pamene kuli kwakuti atsogoleri achipembedzo ndi otsatira awo adzinenera kukhala Akristu, iwo atsutsana ndi ziphunzitso za Yesu Kristu, amene anauza otsatira ake ‘kubweza lupanga.’​—⁠Mateyu 26:​51, 52.

14 Kwa zaka mazana ambiri matchalitchi agwirizana ndi maulamuliro andale zadziko a Dziko Lachikristu pamene maiko amenewo anagonjetsa, kumanga ukapolo, ndi kunyazitsa anthu ena m’nyengo yautsamunda. Ndimo mmene zinaliri mu Afirika kwa zaka mazana ambiri. Ku China nakonso kunali zimenezi, pamene maiko a Kumadzulo anapeza malo olamulira mwankhondo, monga m’nthaŵi ya nkhondo zolimbirana lamulo lakugulitsa chamba zotchedwa Nkhondo za Opium ndi chipanduko chotchedwa Boxer Rebellion.

15 Zipembedzo za Dziko Lachikristu zakhalanso patsogolo m’kuzunza, kusautsa, ndipo ngakhale kupha amene sanagwirizane nazo mkati mwa zaka mazana a mbiri yotchedwa Nyengo Zamdima. M’nthaŵi ya Nkhondo za Mtanda, zimene zinamenyedwa kwa zaka mazana angapo, machitachita auchiŵanda, monga ngati kuzunza ndi kupha mwambanda, anavomerezedwa ndi kuchitidwa kwa anthu ofatsa, opanda liŵongo. Ochilikiza ake anali atsogoleri achipembedzo ndi otsatira awo, onse odzinenera kukhala Akristu. Iwo anafikira pakuyesayesa kuchotseratu Baibulo kotero kuti anthu wamba asaliŵerenge.

Sali Achikristu

16 Ayi, maiko ndi matchalitchi a Dziko Lachikristu sanali, ndipo sali Achikristu. Iwo sali atumiki a Mulungu. Mawu ake ouziridwa amati ponena za iwo: “Avomereza kuti adziŵa Mulungu, koma ndi ntchito zawo amkana iye, popeza ali onyansitsa, ndi osamvera, ndi pa ntchito zonse zabwino osatsimikizidwa.”​—⁠Tito 1:⁠16.

17 Yesu ananena kuti chipembedzo chonyenga chikakhoza kudziŵika ndi zimene chinatulutsa, zipatso zake. Iye anati: “Yang’anirani mupewe aneneri onyenga, amene adza kwa inu ndi zovala zankhosa, koma mkati mwawo ali afisi olusa. Mudzawazindikira ndi zipatso zawo. . . . Chomwecho mtengo wabwino uliwonse upatsa zipatso zokoma; koma mtengo wamphuchi upatsa zipatso zoipa. Sungathe mtengo wabwino kupatsa zipatso zoipa, kapena mtengo wamphuchi kupatsa zipatso zokoma. Mtengo uliwonse wosapatsa chipatso chokoma, audula, nautaya kumoto. Inde chomwecho pa zipatso zawo mudzawazindikira [aneneri onyengawo].”​—⁠Mateyu 7:​15⁠-20.

18 Motero, mwa zimene zaphunzitsa ndi kuchita, zipembedzo za Dziko Lachikristu zasonyeza kuti kudzinenera kwawo kwakuti zimakhulupirira Baibulo ndi kuwopa Mulungu ndi kuti Nzachikristu kuli kwabodza. Izo zanyengeza Mulungu ndi Baibulo. Mwakuchita zimenezo, izo zanyansa anthu mamiliyoni ambiri ndi kuwachititsa kusakhulupirira Wokhalako Wamkulu.

19 Komabe, kulephera kwa atsogoleri achipembedzo ndi matchalitchi a Dziko Lachikristu, limodzinso ndi kulephera kwa zipembedzo zina zakunja kwa Dziko Lachikristu, sikumatanthauza kuti Baibulo lalephera. Ndiponso sikumatanthauza kuti Mulungu walephera. M’malomwake, Baibulo limatiuza za Wokhalako Wamkulu amene alipo ndipo amatisamalira ife ndi mtsogolo mwathu. Limasonyeza mmene adzafupira anthu owona mtima amene amafuna kuchita zolungama, amene amafuna kuwona chilungamo ndi mtendere zikufalikira padziko lonse lapansi. Limasonyezanso chifukwa chake Mulungu walola kuipa ndi kuvutika kukhalapo ndi mmene adzachotsera padziko lapansi awo amene amavulaza anthu anzawo, limodzinso ndi awo amene amadzinenera kuti akumtumikira koma sakutero.

[Study Questions]

1, 2. Kodi nchifukwa ninji anthu ena samalemekeza Baibulo, koma kodi Baibulo limanenanji?

3. Kodi zochitika za m’mbiri zimasonyezanji ponena za Dziko Lachikristu?

4, 5. Kodi nziphunzitso zosakhala za m’Baibulo zotani zimene matchalitchi amaphunzitsa?

6. Kodi Baibulo limatsutsa motani chiphunzitso cha kusafa kwa moyo?

7. Kodi nchiyani chimene chinali chilango cha Adamu ndi Hava chifukwa cha kuswa lamulo la Mulungu?

8. Kodi Baibulo limatsutsa motani chiphunzitso cha Utatu cha Dziko Lachikristu?

9. Kodi tinganene chiyani za ziphunzitso za Baibulo ndi ziphunzitso za matchalitchi a Dziko Lachikristu?

10, 11. Kodi ndimwanjira zotani mmene ziphunzitso za Baibulo zimafunira zosiyana ndi zimene matchalitchi a Dziko Lachikristu akhala akuchita?

12. Kodi Yesu anati nchiyani chimene chidzazindikiritsa Akristu owona?

13, 14. Kodi nchiyani chimene chimasonyeza kuti matchalitchi a Dziko Lachikristu samaimira Mulungu?

15. Kodi nzoipa zotani zimene zachilikizidwa ndi Dziko Lachikristu?

16, 17. Kodi nchifukwa ninji tinganene kuti matchalitchi sali Achikristu?

18. Kodi nchiyani chachitika chifukwa cha ziphunzitso ndi zochita za Dziko Lachikristu?

19. Kodi kulephera kwa Dziko Lachikristu kumatanthauzanso kulephera kwa Mulungu ndi Baibulo?

[Pictures on page 17]

“Helo” wa Dante

Utatu wa Dziko Lachikristu

[Credit Line]

Chithunzithunzi cha Doré cha Barrators​—⁠Giampolo cha mu Divine Comedy ya Dante

Utatu wa Chihindu

[Credit Line]

Mwachilolezo cha The British Museum

Utatu wa Chiigupto

[Credit Line]

Museo Egizio, Turin

[Pictures on page 18]

Mosemphana ndi ziphunzitso za Yesu, atsogoleri achipembedzo a mbali zonse ziŵiri anachilikiza nkhondo

[Credit Line]

Chithunzithunzi cha U.S. Army

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena