Mbali 7
Chifuno cha Mulungu Chidzakwaniritsidwa Posachedwapa
1 Ngakhale kuti Mulungu walola kupanda ungwiro ndi kuvutika kwa nthaŵi yaitali malinga ndi kulingalira kwa anthu, iye sadzalola mikhalidwe yoipa kupitiriza kunthaŵi yosadziŵika. Baibulo limatiuza kuti Mulungu ali ndi nyengo yanthaŵi yakutiyakuti yakulola zinthu zimenezi kuchitika.
2 “Kanthu kalikonse kali ndi nthaŵi yake.” (Mlaliki 3:1) Pamene nthaŵi yoikika ya Mulungu yakulola kuipa ndi kuvutika ifika kumapeto, pamenepo iye adzaloŵerera m’zochita za anthu. Iye adzathetsa kuipa ndi kuvutika ndipo adzakwaniritsa chifuno chake choyambirira chakukhala ndi dziko lapansi lodzazidwa ndi banja la anthu angwiro, achimwemwe akumasangalala ndi mtendere wokwanira ndi chisungiko chachuma m’mikhalidwe ya Paradaiso.
Ziweruzo za Mulungu
3 Tawonani oŵerengeka a maulosi ambiri a m’Baibulo amene amanena zimene kuloŵererapo kwa Mulungu, ndiko kuti, zotulukapo za ziweruzo zake, zidzatanthauza posachedwapa ku banja la anthu:
4 “Pakuti oongoka mtima adzakhala m’dziko, angwiro nadzatsalamo. Koma oipa adzalikhidwa m’dziko, achiwembu adzazulidwamo.”—Miyambo 2:21, 22.
5 “Pakuti ochita zoipa adzadulidwa: koma iwo akuyembekeza Yehova, iwowa adzalandira dziko lapansi. Katsala kanthaŵi ndipo woipa adzatha psiti . . . Koma ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.”—Salmo 37:9-11.
6 “Yembekeza Yehova, nusunge njira yake, ndipo iye adzakukweza kuti ulandire dziko: pakudulidwa oipa udzapenya. Tapenya wangwiro, ndipo tawona woongoka mtima! Pakuti ku matsiriziro ake a munthuyo kuli mtendere. Koma olakwa adzawonongeka pamodzi: matsiriziro a oipa adzadulidwa.”—Salmo 37:34, 37, 38.
7 Chotero, polingalira za mtsogolo mwabwino koposa mwa awo amene amazindikira kuyenera kwa Mlengi wamphamvuyonse kutilamulira, tikusonkhezeredwa kuti: “Mtima wako usunge malangizo anga; pakuti adzakuwonjezera masiku ambiri, ndi zaka za moyo ndi mtendere.” Kwenikwenidi, moyo wamuyaya udzapatsidwa kwa awo amene amasankha kuchita chifuniro cha Mulungu! Chotero, Mawu a Mulungu akutilangiza kuti: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachilikizika pa luntha lako; umlemekeze m’njira zako zonse, ndipo iye adzawongola mayendedwe ako.”—Miyambo 3:1, 2, 5, 6.
Ulamuliro Wakumwamba wa Mulungu
8 Mulungu adzakwaniritsa kuyeretsa dziko lapansi mwa boma labwino koposa limene anthu sanakhalepo nalo. Ndiboma limene limasonyeza nzeru yakumwamba chifukwa limalamulira lili kumwamba pansi pa chitsogozo cha Mulungu. Ndipo Ufumu wakumwamba umenewo udzachotsa mitundu yonse ya ulamuliro wa anthu padziko lapansi. Anthu sadzakhalanso ndi chosankha chakuyesa kulamulira mosadalira pa Mulungu.
9 Pankhani imeneyi, ulosi wa pa Danieli 2:44 umati: “Ndipo masiku a mafumu aja [maboma alipowa] Mulungu wa kumwamba adzaika ufumu [kumwamba] woti sudzawonongeka ku nthaŵi zonse, ndi ulamuliro wake sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu [anthu sadzaloledwanso kulamulira mosadalira pa Mulungu], koma udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse [amene alipo tsopano], nudzakhala chikhalire.”—Onaninso Chivumbulutso 19:11-21; 20:4-6.
10 Motero, mtundu wa anthu sudzakhalanso ndi mitundu yoipa ya ulamuliro, popeza Mulungu atathetsa dongosolo ili lazinthu, ulamuliro wa anthu osadalira pa iye sudzakhalakonso. Ndipo Ufumu wolamulira kumwambawo sudzaipitsidwa, popeza kuti Mulungu ndiye Wouyambitsa ndi Mtetezi wake. M’malomwake, udzagwira ntchito m’njira yokondweretsa nzika zake zaumunthu. Pamenepo chifuniro cha Mulungu chidzachitidwa padziko lonse lapansi monga kumwamba. Nchifukwa chake Yesu anaphunzitsa ophunzira ake kupemphera kwa Mulungu kuti: “Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga kumwamba chomwecho pansi pano.”—Mateyu 6:10.
Kodi Tili Pafupi Motani?
11 Kodi tili pafupi motani ndi mapeto a dongosolo la zinthu losakhutiritsa limeneli ndi kuyambika kwa dziko latsopano la Mulungu? Ulosi wa m’Baibulo umatipatsa yankho lomvekera bwino. Mwachitsanzo, Yesu mwiniyo ananeneratu za zinthu zimene tingafune kuti tidziŵe kotero kuti titsimikizire kaimidwe kathu mogwirizana ndi, monga momwe Baibulo limanenera, “chimaliziro cha dongosolo la zinthu.” (NW) Zimenezi zalembedwa m’Mateyu chaputala 24 ndi 25, Marko 13, ndi Luka 21. Ndiponso, monga momwe zalembedwera pa 2 Timoteo chaputala 3, mtumwi Paulo ananeneratu kuti kudzakhala nyengo ya nthaŵi yotchedwa “masiku otsiriza” pamene zochitika zosiyanasiyana zikatsimikizira nthaŵi imene tilimo.
12 Yesu ananena kuti nyengo ya nthaŵi imeneyi ikayamba ndi zochitika izi: “Pakuti mtundu umodzi wa anthu udzaukirana ndi mtundu wina, ndi ufumu ndi ufumu wina; ndipo kudzakhala njala ndi zivomezi m’malo akutiakuti.” (Mateyu 24:7) Lemba la Luka 21:11 limasonyeza kuti iye anatchulanso kuti “miliri m’malo akutiakuti.” Ndipo anachenjezanso za “kuchuluka kwa kusayeruzika.”—Mateyu 24:12.
13 Mtumwi Paulo ananeneratu kuti: “Koma zindikira ichi, kuti masiku otsiriza zidzafika nthaŵi zoŵaŵitsa. Pakuti anthu adzakhala odzikonda okha, okonda ndalama, odzitamandira, odzikuza, amwano, osamvera akuwabala, osayamika, osayera mtima, opanda chikondi chachibadwidwe, osayanjanitsika, akudyerekeza, osakhoza kudziletsa, aukali, osakonda abwino, achiwembu, aliuma olimbirira, otukumuka mtima, okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu; akukhala nawo mawonekedwe a chipembedzo, koma mphamvu yake adaikana . . . Koma anthu oipa ndi onyenga, adzaipa chiipire, kusokeretsa ndi kusokeretsedwa.”—2 Timoteo 3:1-5, 13.
14 Kodi zinthu zimene Yesu ndi Paulo ananeneratu zachitika m’nthaŵi yathu? Inde, izo zachitikadi. Nkhondo Yadziko I inali nkhondo yoipitsitsa panthaŵiyo. Inali nkhondo yoyamba yadziko ndipo inali posinthira m’mbiri yamakono. Nkhondo imeneyo inatsagana ndi njala, miliri ya matenda, ndi masoka ena. Zochitika zimenezo zoyambira mu 1914 kumka mtsogolo, zinali, monga momwe Yesu ananenera, “zoŵaŵa zoyamba.” (Mateyu 24:8) Zinayambitsa nyengo ya nthaŵi yonenedweratu yotchedwa “masiku otsiriza,” kuyamba kwa mbadwo womalizira pamene Mulungu akalola kuipa ndi kuvutika.
15 Mosakayikira mumadziŵa zochitika za m’zaka za zana la 20 lino. Mumadziŵa za chipolowe chimene chabuka. Pafupifupi anthu 100 miliyoni aphedwa m’nkhondo. Mamiliyoni mazana ena afa ndi njala ndi matenda. Zivomezi zapha anthu osaŵerengeka. Kusasamala moyo ndi chuma kukuwonjezeka. Kuwona upandu kwakhala mbali ya moyo watsiku ndi tsiku. Miyezo ya makhalidwe abwino yanyalanyazidwa. Kuchuluka kwa chiŵerengero cha anthu kukuchititsa mavuto omwe sakuthetsedwa. Kuipitsa kukuwononga mtundu wa moyo ndipo ngakhale kuuika paupandu. Ndithudi, takhala m’masiku otsiriza kuyambira 1914 ndipo tikuyandikira kaindeinde wa maulosi a Baibulo a nthaŵi yathu.
16 Kodi masiku otsiriza ameneŵa adzakhalapobe kwa utali wotani? Yesu ananena motere za nyengo imene ikawona “zoŵaŵa zoyamba” kuchokera 1914 kumka mtsogolo: “Mbadwo uwu sudzatha kuchoka, kufikira zinthu zonsezi zidzachitidwa.” (Mateyu 24:8, 34-36) Chotero, mbali zonse za masiku otsiriza ziyenera kuchitika m’nthaŵi ya mbadwo umodzi, mbadwo wa 1914. Chotero anthu ena amene anali ndi moyo mu 1914 adzakhala akali ndi moyo pamene dongosolo lino lifika kumapeto ake. Anthu a mbadwo umenewo akalamba tsopano, kusonyeza kuti sikunatsale nthaŵi yaitali kuti Mulungu athetse dongosolo la zinthu lilipoli.
17 Ulosi wina wosonyeza kuti mapeto a dongosolo ili ali pafupi kwambiri unaperekedwa ndi mtumwi Paulo, amene ananeneratu kuti: “Tsiku la [Yehova, NW] lidzadza monga mbala usiku. Pamene angonena, Mtendere ndi [chisungiko!, NW], pamenepo chiwonongeko chobukapo chidzawagwera, . . . ndipo sadzapulumuka konse.”—1 Atesalonika 5:2, 3; onaninso Luka 21:34, 35.
18 Lerolino Nkhondo Yoputana ndi Mawu yatha, ndipo nkhondo yapadziko lonse siilinso chiwopsezo chachikulu. Chotero mitundu ingalingalire kuti ili pafupi kwambiri ndi dongosolo la dziko latsopano. Koma pamene alingalira kuti zoyesayesa zawo zikupambana, zidzatanthauza zotsutsana ndi zimene adzalingalira, popeza kuti chimenecho chidzakhala chizindikiro chomalizira chakuti kuwonongedwa kwa dongosololi kochitidwa ndi Mulungu kwayandikira. Kumbukirani kuti, kukambitsirana kwa zandale ndi mapangano sizikuchititsa kusintha kwenikweni mwa anthu. Sizikuchititsa anthu kukondana wina ndi mnzake. Ndipo atsogoleri adziko sakuletsa upandu, ndiponso sakuthetsa matenda ndi imfa. Chotero musakhulupirire zochita za anthu zilizonse za mtendere ndi chisungiko ndi kuganiza kuti dzikoli latsala pang’ono kuthetsa mavuto ake. (Salmo 146:3) Zimene mfuu imeneyo idzatanthauza kwenikweni nzakuti dzikoli lili pafupi kwenikweni ndi mapeto ake.
Kulalikira Mbiri Yabwino
19 Ulosi wina umene umasonyeza kuti takhala m’masiku otsiriza kuyambira 1914 ndiumene Yesu anapereka wakuti: “Ndipo uthenga wabwino uyenera uyambe kulalikidwa kwa anthu a mitundu yonse.” (Marko 13:10) Kapena monga momwe lemba la Mateyu 24:14 limanenera kuti: “Uthenga uwu wabwino wa ufumu udzalalikidwa pa dziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.”
20 Lerolino kuposa ndi kale lonse m’mbiri, mbiri yabwino ya mapeto a dzikoli ndi dziko latsopano Laparadaiso likudzalo mu ulamuliro wa Ufumu wa Mulungu ikulalikidwa padziko lonse lapansi. Ndi yani? Ndi mamiliyoni a Mboni za Yehova. Izo zikulalikira m’dziko lililonse padziko lapansi.
21 Kuwonjezera pa kulalikira kwawo za Ufumu wa Mulungu, Mboni za Yehova zimayenda m’kayendedwe kamene kamazizindikiritsa monga otsatira owona a Kristu, popeza iye analengeza kuti: “Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.” Chotero, Mboni za Yehova nzogwirizana mu ubale wapadziko lonse ndi chomangira chosasweka cha chikondi.—Yohane 13:35; onaninso Yesaya 2:2-4; Akolose 3:14; Yohane 15:12-14; 1 Yohane 3:10-12; 4:20, 21; Chivumbulutso 7:9, 10.
22 Mboni za Yehova zimakhulupirira zimene Baibulo limanena kuti: “Mulungu alibe tsankhu; koma m’mitundu yonse, wakumuwopa iye ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye.” (Machitidwe 10:34, 35) Zimawona Mboni zinzawo za m’maiko onse monga abale ndi alongo auzimu, mosasamala kanthu za fuko kapena khungu. (Mateyu 23:8) Ndipo chenicheni chakuti ubale wapadziko lonse umenewo ulipo m’dziko lerolino chimawonjezera umboni wakuti chifuno cha Mulungu chidzakwaniritsidwa posachedwapa.
[Study Questions]
1, 2. Kodi nchifukwa ninji tingakhale otsimikizira kuti Mulungu adzachitapo kanthu kuthetsa kuipa ndi kuvutika?
3, 4. Kodi buku la Miyambo limafotokoza motani zotulukapo za kuloŵererapo kwa Mulungu?
5, 6. Kodi lemba la Salmo 37 limasonyeza motani zimene zidzachitika pamene Mulungu aloŵererapo?
7. Kodi ndiuphungu wanzeru wotani umene Mawu a Mulungu amatipatsa?
8, 9. Kodi Mulungu adzayeretsa dziko lapansi ndi chiyani?
10. Kodi nchifukwa ninji tingakhale otsimikizira kuti pansi pa Ufumu wakumwamba wa Mulungu, sipadzakhalanso kupotoza ulamuliro?
11. Kodi nkuti m’Baibulo kumene timapeza maulosi amene adzatithandiza kudziŵa kuti tili pafupi motani ndi mapeto a dongosolo ili?
12, 13. Kodi Yesu ndi Paulo ananenanji ponena za nthaŵi yamapeto?
14, 15. Kodi zochitika za m’zaka za zana lino la 20 zimatsimikizira motani kuti tikukhaladi m’masiku otsiriza?
16. Kodi masiku otsiriza amatenga nyengo ya nthaŵi yaitali motani?
17, 18. Kodi ndiulosi wotani umene umasonyeza kuti tili pafupi kwambiri ndi mapeto a dzikoli?
19, 20. Kodi ndiulosi uti wonena za kulalikira m’masiku otsiriza umene tikuwona ukukwaniritsidwa?
21, 22. Kodi nchiyani makamaka, chimene chimazindikiritsa Mboni za Yehova kukhala Akristu owona?
[Picture on page 26]
Ufumu wolungama wakumwamba wa Mulungu udzakhala ulamuliro wokhawo wa anthu m’dziko latsopano