Uthenga wa Ufumu Na. 34
Nchifukwa Ninji Moyo Uli Ndi Mavuto Ochuluka Motere?
Kodi paradaiso wopanda mavuto ali wotheka?
MAVUTO AAKULU AKUIPIRAIPIRA—CHIFUKWA NINJI?
Anthu akhala ndi mavuto nthaŵi zonse. Ngakhale kuti ambiri anaganiza kuti sayansi yopanga zinthu yamakono ikawathetsa, mavuto aakulu akuipiraipira.
Upandu: Pali anthu oŵerengeka chabe amene amamva kukhala osungika poyenda m’makwalala kapena ngakhale pokhala m’nyumba zawo. M’dziko lina la ku Ulaya, pafupifupi munthu 1 pa 3 anakumana ndi upandu m’chaka china posachedwapa.
Malo Okhala: Kuipitsa mpweya, nthaka, ndi madzi kukufalikira mowonjezerekawonjezereka. M’maiko osatukuka, gawo limodzi mwa anayi la anthu alibe madzi oyera.
Umphaŵi: Pali anthu osauka ndi anjala ochuluka kwambiri kuposa ndi kalelonse. Oposa pa 90 peresenti ya anthu m’maiko ena akukhala mu umphaŵi; 30 peresenti ya antchito padziko lonse, pafupifupi 800 miliyoni, ali malova kapena akugwira ntchito yosakwanira—ndipo ziŵerengerozo zikukula.
Njala: Ngakhale ngati inuyo muli nacho chakudya chokwanira, mamiliyoni omawonjezereka alibe. M’maiko osatukuka, chaka chilichonse anthu pafupifupi 13 miliyoni, makamaka ana, amafa chifukwa cha njala.
Nkhondo: Zikwi mazana ambiri aphedwa m’ziwawa za mafuko zaposachedwapa. Ndipo m’zaka za zana la 20, nkhondo zapha anthu oposa pa mamiliyoni zana limodzi.
Mavuto Ena: Kuwonjezera pa zotchulidwazo, palinso kusamvana m’banja komakulakula, anakubala osakwatiwa omachuluka, kusoŵa nyumba komawonjezereka, kugwiritsira ntchito molakwa anamgoneka kofalikira, uchiwerewere wochuluka. Yemwe kale anali mmodzi wa aphungu a pulezidenti wa United States ananena bwino lomwe kuti: “Pali zizindikiro zochuluka kwambiri za . . . kuvunda kwa kutsungula.” M’nyengo yaposachedwapa ya zaka 30, chiŵerengero cha anthu mu United States chinawonjezereka ndi 41 peresenti, koma chiwawa chinakwera kufika pa 560 peresenti, kubadwa kwa ana apathengo 400 peresenti, zisudzulo 300 peresenti, achinyamata odzipha okha oposa 200 peresenti. Mkhalidwewo ngwofanana ndi m’maiko ena.
Kodi Nchifukwa Ninji Mavuto Afika Poipa?
Mlengi wathu amapereka yankho. Mawu ake amatcha nthaŵi zodzala ndi mavuto zino kukhala “masiku otsiriza,” nyengo pamene “nthaŵi zoŵaŵitsa” zikakhalapo. (2 Timoteo 3:1) Masiku otsiriza a chiyani? Eya, Baibulo limanena za “mapeto a dziko.”—Mateyu 24:3, King James Version.
Mavuto omakulakula a lerolino ali umboni woonekeratu wakuti mapeto a dongosolo lino la zinthu ali pafupi, kuphatikizapo mapeto a zoipa ndi amene amazichita. (Mateyu 24:3-14; 2 Timoteo 3:1-5; Chivumbulutso 12:7-12) Posachedwapa Mulungu adzaloŵererapo ndi kuthetseratu mavuto onse a lerolino.—Yeremiya 25:31-33; Chivumbulutso 19:11-21.
ZIPEMBEDZO ZA DZIKOLI ZALEPHERA
M’malo mothandiza kuthetsa mavuto a lerolino, zipembedzo za dzikoli zikuwonjezerapo ena. M’nthaŵi za nkhondo, Akatolika amapha Akatolika, Aprotesitanti amapha Aprotesintanti—amaphana mamiliyoni. Posachedwapa m’Rwanda, kumene ambiri ndi Akatolika, anthu anaphana zikwi mazana ambiri! (Onani chithunzicho kumanzere.)
Kodi Yesu akanapita kunkhondo ndi mfuti kapena lupanga ndi kupha ophunzira ake chifukwa chakuti mtundu wawo unali wosiyana ndi wake? Ndithudi sakanatero! Baibulo limati: “Amene akonda Mulungu akondenso mbale wake.” (1 Yohane 4:20, 21) Zipembedzo za dzikoli zalephera kuchita chimenecho. “Avomereza kuti adziŵa Mulungu, koma ndi ntchito zawo amkana iye.”—Tito 1:16.
Ndiponso, mwa kusachirikiza miyezo ya Baibulo ya chikhalidwe, zipembedzo za dziko zimawonjezera kuwonongeka kwa makhalidwe kochititsa kakasi padziko lonse lapansi.
Yesu anati mungasiyanitse chipembedzo chonyenga ndi chipembedzo choona ‘ndi zipatso zake’—mwa machitidwe a ziŵalo zake. Iye anatinso: “Mtengo uliwonse wosapatsa chipatso chokoma, audula, nautaya kumoto.” (Mateyu 7:15-20) Mawu a Mulungu amatisonkhezera kutuluka m’chipembedzo chobala zipatso zoipa chimene chikuyang’anizana ndi chiwonongeko.—Chivumbulutso 18:4.
Chipembedzo Choona Sichinalephere
Chipembedzo choona ‘chipatsa zipatso zokoma,’ makamaka chikondi. (Mateyu 7:17; Yohane 13:34, 35) Kodi ndi gulu liti la Akristu a ubale wogwirizana wa mitundu yonse limene limasonyeza chikondi chotero? Ndani kodi amene amakana kupha a chipembedzo chawo kapena wina aliyense?—1 Yohane 3:10-12.
Mboni za Yehova zili ndi mbiri ya kubala ‘chipatso chokoma’ chimenecho. Kuzungulira dziko lonse, m’maiko oposa 230, ‘zasula malupanga awo kukhala zolimira.’ (Yesaya 2:4) Chikondi chawo kwa anthu chikusonyezedwanso mwa kulabadira kwawo lamulo la Kristu la kulalikira ‘uthenga wabwino’ wa Ufumu wa Mulungu padziko lonse. (Mateyu 24:14) Zimasunga ndi kuchirikizanso makhalidwe abwino koposa ophunzitsidwa m’Baibulo.—1 Akorinto 6:9-11.
Chipembedzo choona sichinalephere ayi. Chimatsogoza anthu kwa Uyo yekha amene akhoza kuthetsa mavuto a mtundu wa anthu. Posachedwapa Iyeyo adzabweretsa dziko latsopano kwenikweni. Kodi Iyeyo ndani? (Chonde onani patsamba la kumbuyo.)
DZIKO LOPANDA MAVUTO NLOTSIMIKIZIRIKA
Mukanakhala wokhoza, kodi simukanathetsa mavuto onse amene ali kusautsa mtundu wa anthu? Ndithudi mukanatero! Kodi tiyenera kulingalira kuti Mlengi wathu wachikondi, yekhayo wokhala ndi mphamvu ndi nzeru yothetsera mavuto a mtundu wa anthu, adzachita zocheperapo?
Baibulo limasonyeza kuti Mulungu adzaloŵerera m’nkhani za anthu mwa kugwiritsira ntchito boma lake lakumwamba lokhala m’manja mwa Yesu Kristu. Ilo ‘lidzaphwanya’ maboma onse achinyengo pa dziko lapansi. (Danieli 2:44; Mateyu 6:9, 10) Chifukwa ninji? Polankhula kwa Mulungu, wamasalmo akuyankha kuti: “Kuti adziŵe kuti inu nokha, dzina lanu ndinu Yehova, ndinu Wam’mwambamwamba pa dziko lonse lapansi.”—Salmo 83:18.
Pamene dzikoli litha, kodi padzakhala opulumuka? Baibulo limati: “Dziko lapansi lipita, . . . koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthaŵi yonse.” (1 Yohane 2:17) Kodi opulumuka amenewo adzakhala ku nthaŵi yonse kuti? Baibulo limayankha kuti: “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.”—Salmo 37:9-11, 29; Miyambo 2:21, 22.
M’dziko latsopano la Mulungu, “sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa.” (Chivumbulutso 21:4) Sipadzakhalanso upandu, umphaŵi, njala, matenda, chisoni, kapena imfa! Inde, ngakhale akufa adzakhalanso ndi moyo! “Kudzakhala kuuka.” (Machitidwe 24:15) Ndipo dziko lapansi lidzasandutsidwa paradaiso weniweni.—Yesaya 35:1, 2; Luka 23:43.
Kodi tiyenera kuchitanji kuti tikasangalale ndi moyo m’dziko latsopano la Mulungu? Yesu anati: “Moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziŵe inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munamtuma.” (Yohane 17:3) Mamiliyoni a anthu oona mtima kuzungulira dziko lonse akupeza chidziŵitso chimenechi. Icho chimawakhozetsa kupirira mavuto ambiri amene amakumana nawo tsopano, koma chofunika koposa nchakuti, icho chimawapatsa chidaliro chokwana chakuti mavuto amene sakhoza kuwathetsa mwa mphamvu yawo adzathetsedweratu m’dziko latsopano la Mulungu.
[Mawu a Chithunzi patsamba 2]
Chithunzi cha WHO chojambulidwa ndi P. Almasy
[Mawu a Chithunzi patsamba 3]
Jerden Bouman/Sipa Press