Phunziro 1
Mmene Mungadziŵire Zimene Mulungu Amafuna
Kodi ndi chidziŵitso chofunika chotani chimene chimapezeka m’Baibulo? (1)
Kodi mlembi wa Baibulo ndani? (2)
N’chifukwa ninji muyenera kuphunzira Baibulo? (3)
1. Baibulo ndi mphatso yamtengo wapatali yochokera kwa Mulungu. Lili ngati kalata imene atate wachikondi walembera ana ake. Limatiuza choonadi ponena za Mulungu—chimene iye ali ndi zimene amafuna. Limatiuza mochitira ndi mavuto ndi mmene tingapezere chimwemwe choona. Baibulo lokhalo limatiuza zimene tiyenera kuchita kuti tikondweretse Mulungu.—Salmo 1:1-3; Yesaya 48:17, 18.
2. Baibulo linalembedwa ndi amuna osiyanasiyana okwanira ngati 40 panyengo ya zaka 1,600, kuyambira mu 1513 B.C.E. Lapangidwa ndi mabuku aang’ono 66. Olemba Baibulo anauziridwa ndi Mulungu. Analemba malingaliro ake, osati awoawo ayi. Chotero Mulungu wakumwamba ndiye Mlembi Wamkulu wa Baibulo, osati munthu aliyense padziko lapansi.—2 Timoteo 3:16, 17; 2 Petro 1:20, 21.
3. Mulungu anatsimikiza kuti Baibulo linakopedwa molondola ndi kusungidwa. Mabaibulo ambiri asindikizidwa kuposa buku lina lililonse. Si onse amene adzakondwa kukuonani mukuphunzira Baibulo, koma musalole zimenezo kukuletsani. Mtsogolo mwanu mosatha mumadalira pa kudziŵa kwanu Mulungu ndi kuchita chifuniro chake mosasamala kanthu za chitsutso chilichonse.—Mateyu 5:10-12; Yohane 17:3.