Phunziro 2
Kodi Mulungu Ndani?
Kodi Mulungu woona ndani, ndipo dzina lake ndani? (1, 2)
Kodi ali ndi thupi lotani? (3)
Kodi mikhalidwe yake yapadera n’jotani? (4)
Kodi tiyenera kugwiritsira ntchito mafano ndi zizindikiro pomlambira? (5)
Kodi ndi njira ziŵiri ziti zimene tingaphunzirire za Mulungu? (6)
1. Anthu amalambira zinthu zambiri. Koma Baibulo limatiuza kuti pali Mulungu WOONA mmodzi yekha. Analenga zonse zakumwamba ndi zapadziko lapansi. Chifukwa anatipatsa moyo, ndi Iye yekha amene tiyenera kulambira.—1 Akorinto 8:5, 6; Chivumbulutso 4:11.
2. Mulungu ali ndi maina aulemu ambiri koma ali ndi dzina limodzi lokha. Dzinalo ndi YEHOVA. M’Mabaibulo ochuluka, dzina la Mulungu lachotsedwamo ndipo m’malo mwake aikamo AMBUYE kapena MULUNGU. Koma pamene Baibulo linalembedwa, dzinalo Yehova linalimo nthaŵi ngati 7,000!—Eksodo 3:15; Salmo 83:18.
3. Yehova ali ndi thupi, koma n’losiyana ndi lathu. “Mulungu ndiye mzimu,” limatero Baibulo. (Yohane 4:24) Mzimu ndiwo chamoyo chamtundu wapamwamba kutiposa. Kulibe munthu anaonapo Mulungu. Yehova amakhala kumwamba, koma atha kuona zonse. (Salmo 11:4, 5; Yohane 1:18) Nanga kodi mzimu woyera n’chiyani? Suli munthu monga Mulungu. M’malo mwake, ndiyo mphamvu ya Mulungu yogwira ntchito.—Salmo 104:30.
4. Baibulo limatiuza za umunthu wa Yehova. Limasonyeza kuti mikhalidwe yake yapadera ndiyo chikondi, chilungamo, nzeru, ndi mphamvu. (Deuteronomo 32:4; Yobu 12:13; Yesaya 40:26; 1 Yohane 4:8) Baibulo limatiuza kuti alinso wachifundo, wokoma mtima, wokhululuka, wopatsa, ndi woleza mtima. Ife, monga ana omvera, tiyenera kuyesayesa kumtsanzira iye.—Aefeso 5:1, 2.
5. Kodi tiyenera kugwadira kapena kupempherera mafano, zithunzithunzi, kapena zizindikiro polambira? Iyayi! (Eksodo 20:4, 5) Yehova amati tiyenera kumlambira iye yekha. Sagaŵana ulemerero wake ndi wina aliyense kapena chinthu china chilichonse. Mafano alibe mphamvu yakuti angatithandize nayo.—Salmo 115:4-8; Yesaya 42:8.
6. Kodi ndi motani mmene tingam’dziŵire bwino Mulungu? Njira imodzi ndiyo mwa kuona zinthu zimene analenga ndi kulingalira mwakuya zimene zinthuzo zimatiuza. Zolenga za Mulungu zimatisonyeza kuti iye ali ndi mphamvu yaikulu ndi nzeru. Timaona chikondi chake m’zinthu zonse zimene anapanga. (Salmo 19:1-6; Aroma 1:20) Njira ina imene tingaphunzirire za Mulungu ndiyo mwa kuphunzira Baibulo. Mmenemo amatiuza zambiri ponena za mtundu wa Mulungu amene iye ali. Amatiuzanso za chifuno chake ndi zimene afuna kuti ife tichite.—Amosi 3:7; 2 Timoteo 3:16, 17.
[Zithunzi patsamba 5]
Timaphunzira za Mulungu kuchokera ku chilengedwe ndi m’Baibulo