Phunziro 4
Kodi Mdyerekezi Ndani?
Satana Mdyerekezi—kodi anachokera kuti? (1, 2)
Kodi Satana amawasokeretsa motani anthu? (3-7)
Kodi n’chifukwa ninji muyenera kumkaniza Mdyerekezi? (7)
1. Liwulo “mdyerekezi” limatanthauza munthu amene amanena mabodza anjiru ponena za munthu wina. “Satana” limatanthauza mdani kapena wotsutsa. Awa ndiwo maina opatsidwa kwa mdani wamkulu wa Mulungu. Poyamba, iye anali kumwamba ndi Mulungu monga mngelo wangwiro. Komabe, pambuyo pake anaganiza modzitukumula nafuna kulambira kumene Mulungu ndiye mwini wake.—Mateyu 4:8-10.
2. Mngelo ameneyu, Satana, analankhula kwa Hava kupyolera mwa njoka. Mwa kumuuza mabodza, anamchititsa kusamvera Mulungu. Motero Satana anaukira chimene chimatchedwa “uchifumu” wa Mulungu, kapena malo ake monga Wammwambamwamba. Satana anachititsa chikayikiro chakuti kaya Mulungu amalamulira mwanjira yoyenera ndi yabwino kwa anthu Ake. Satana anabutsanso chikayikiro chakuti kaya ngati munthu aliyense angakhale wokhulupirika kwa Mulungu. Mwa kuchita zimenezi, Satana anadzipanga yekha mdani wa Mulungu. N’chifukwa chake anayamba kutchedwa Satana Mdyerekezi.—Genesis 3:1-5; Yobu 1:8-11; Chivumbulutso 12:9.
3. Satana amayesa kunyenga anthu kuti amlambire. (2 Akorinto 11:3, 14) Njira imodzi imene amasokeretsa nayo anthu ndiyo chipembedzo chonyenga. Ngati chipembedzo chimaphunzitsa mabodza ponena za Mulungu, chimatumikiradi chifuno cha Satana. (Yohane 8:44) Anthu azipembedzo zonyenga angakhulupirire ndi mtima wonse kuti akulambira Mulungu woona. Koma kwenikweni amatumikira Satana. Ndiye ‘mulungu wa dziko lino.’—2 Akorinto 4:4.
4. Kukhulupirira mizimu ndiko njira ina imene Satana amachititsa nayo anthu kukhala pansi pa ulamuliro wake. Iwo angaitanire mizimu kuti iwatetezere, kuvulaza ena, kulosera zamtsogolo, kapena kuchita zozizwitsa. Satana ndiye mphamvu yoipa yochirikiza machitachita ameneŵa. Kuti tikondweretse Mulungu, tiyenera kupeŵeratu kukhulupirira mizimu.—Deuteronomo 18:10-12; Machitidwe 19:18, 19.
5. Satana amasokeretsanso anthu mwa kunyada kwa fuko kopambanitsa ndi kulambira mabungwe andale. Ena amaganiza kuti mtundu wawo kapena fuko lawo n’labwino kuposa la ena. Koma zimenezi si zoona. (Machitidwe 10:34, 35) Anthu ena amayembekezera mabungwe andale kuthetsa mavuto a munthu. Mwa kuchita zimenezo, amakana Ufumu wa Mulungu. Uwo ndiwo mankhwala okha pa mavuto athu.—Danieli 2:44.
6. Njira ina imene Satana amasokeretsa nayo anthu ndiyo kuwayesa ndi zikhumbo zauchimo. Yehova amatiuza kupeŵa machitachita auchimo chifukwa adziŵa kuti angativulaze. (Agalatiya 6:7, 8) Anthu ena angafune kuti mugwirizane nawo pa machitachita amenewo. Koma, kumbukirani kuti kwenikweni ali Satana amene akufuna kuti muchite zimenezo.—1 Akorinto 6:9, 10; 15:33.
7. Satana angagwiritsirenso ntchito chizunzo kapena chitsutso kuti inu musiye Yehova. Ena mwa okondedwa anu angakwiye kwambiri chifukwa mukuphunzira Baibulo. Ena angakusekeni. Koma kodi ndani anakupatsani moyo? Satana amafuna kukuwopsani kuti muleke kuphunzira za Yehova. Musalole Satana kupambana! (Mateyu 10:34-39; 1 Petro 5:8, 9) Mwa kumkaniza Mdyerekezi, mukhoza kukondweretsa Yehova ndi kusonyeza kuti mukuchirikiza ulamuliro Wake.—Miyambo 27:11.
[Zithunzi patsamba 9]
Chipembedzo chonyenga, kukhulupirira mizimu, ndi utundu zimasokeretsa anthu
[Chithunzi patsamba 9]
Kanizani Satana mwa kupitiriza kuphunzira za Yehova