Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • rq phunziro 6 tsamba 12-13
  • Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?
  • Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?
    Zimene Baibulo Limaphunzitsa
  • Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?
    Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu
Onani Zambiri
Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?
rq phunziro 6 tsamba 12-13

Phunziro 6

Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?

Kodi Ufumu wa Mulungu uli kuti? (1) Kodi Mfumu yake ndani? (2)

Kodi pali ena amene amalamulira ndi Mfumuyo? Ngati alipo, ndi angati? (3)

N’chiyani chimasonyeza kuti tili m’masiku otsiriza? (4)

Kodi Ufumu wa Mulungu udzawachitira chiyani anthu mtsogolo? (5-7)

1. Pamene Yesu anali padziko lapansi, anaphunzitsa otsatira ake kupempherera Ufumu wa Mulungu. Ufumu ndiwo boma lolamuliridwa ndi mfumu. Ufumu wa Mulungu uli boma lapadera. Uli kumwamba ndipo udzalamulira dziko lino lapansi. Udzayeretsa dzina la Mulungu. Udzachititsa chifuniro cha Mulungu kuchitika padziko lapansi monga kumwamba.—Mateyu 6:9, 10.

2. Mulungu analonjeza kuti Yesu adzakhala Mfumu ya Ufumu Wake. (Luka 1:30-33) Pamene Yesu anali padziko lapansi, anasonyeza kuti adzakhala Wolamulira wokoma mtima, wolungama, ndi wangwiro. Atabwerera kumwamba, sanakhazikidwe pa mpando wachifumu nthaŵi yomweyo monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. (Ahebri 10:12, 13) Mu 1914, Yehova anapatsa Yesu ulamuliro umene Iye anamlonjeza. Kuyambira pamenepo, Yesu walamulira kumwamba monga Mfumu yoikidwa ya Yehova.—Danieli 7:13, 14.

3. Yehova wasankhanso amuna ndi akazi okhulupirika padziko lapansi kuti apite kumwamba. Iwo pamodzi ndi Yesu adzalamulira pa anthu monga mafumu, oweruza, ndi ansembe. (Luka 22:28-30; Chivumbulutso 5:9, 10) Yesu anatcha olamulira anzake ameneŵa mu Ufumu wake “kagulu ka nkhosa.” Onse pamodzi ali 144,000.—Luka 12:32; Chivumbulutso 14:1-3.

4. Yesu atangokhala Mfumu, anaponyera Satana ndi angelo ake oipa kudziko lapansi kuchokera kumwamba. N’chifukwa chake zinthu padziko lapansi pano zakhala zoipa kwambiri chiyambire 1914. (Chivumbulutso 12:9, 12) Nkhondo, njala, miliri, kuwonjezeka kwa kusayeruzika—zonsezi zili mbali ya “chizindikiro” chosonyeza kuti Yesu akulamulira ndi kuti dongosolo lino lili m’masiku ake otsiriza.—Mateyu 24:3, 7, 8, 12; Luka 21:10, 11; 2 Timoteo 3:1-5.

5. Posachedwa Yesu adzaweruza anthu, kuwalekanitsa monga mbusa alekanitsa nkhosa ndi mbuzi. “Nkhosa” ndizo aja amene adzakhala atasonyeza kuti ali anthu ake okhulupirika. Adzalandira moyo wosatha padziko lapansi. “Mbuzi” ndizo aja amene adzakhala atakana Ufumu wa Mulungu. (Mateyu 25:31-34, 46) Patsogolopa, Yesu adzawononga onse onga mbuzi. (2 Atesalonika 1:6-9) Ngati mukufuna kudzakhala mmodzi wa “nkhosa” za Yesu, muyenera kumvetsera uthenga wa Ufumu ndi kuchita zimene mumaphunzira.—Mateyu 24:14.

6. Tsopano dziko lapansi lagaŵidwa m’maiko ambiri. Lililonse lili ndi boma lakelake. Mitundu imeneyi imamenyana nthaŵi zambiri. Koma Ufumu wa Mulungu udzaloŵa m’malo maboma onse aumunthu. Udzalamulira monga boma lokha padziko lonse lapansi. (Danieli 2:44) Ndiyeno, sikudzakhalanso nkhondo, upandu, ndi chiwawa. Anthu onse adzakhala pamodzi mumtendere ndi umodzi.—Mika 4:3, 4.

7. Mkati mwa Ulamuliro wa Yesu wa Zaka Chikwi, anthu okhulupirika adzakhala angwiro, ndipo dziko lonse lapansi lidzakhala paradaiso. Pofika kumapeto a zaka chikwi, Yesu adzakhala atachita zonse zimene Mulungu anampempha kuchita. Pamenepo adzabwezera Ufumu kwa Atate wake. (1 Akorinto 15:24) Bwanji osauzako mabwenzi anu ndi okondedwa anu zimene Ufumu wa Mulungu udzachita?

[Chithunzi patsamba 13]

Mu ulamuliro wa Yesu, simudzakhalanso udani kapena tsankho

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena