Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • rq phunziro 11 tsamba 22-23
  • Zikhulupiriro ndi Miyambo Yosakondweretsa Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zikhulupiriro ndi Miyambo Yosakondweretsa Mulungu
  • Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?
  • Nkhani Yofanana
  • Miyambo Yofala Yosamkondweretsa Mulungu
    Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya
  • Isitala kapena Chikumbutso Kodi Muyenera Kusunga Chiti?
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Khalani ndi Cholinga Choti Muzilambira Mulungu
    Zimene Baibulo Limaphunzitsa
  • N’chifukwa Chiyani a Mboni za Yehova Sakondwerera Isitala?
    Mafunso Ofunsidwa Kawirikawiri
Onani Zambiri
Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?
rq phunziro 11 tsamba 22-23

Phunziro 11

Zikhulupiriro ndi Miyambo Yosakondweretsa Mulungu

Kodi ndi zikhulupiriro ndi miyambo iti imene ili yolakwa? (1)

Kodi Akristu ayenera kukhulupirira kuti Mulungu ali Utatu? (2)

Kodi n’chifukwa ninji Akristu oona samakondwerera Krisimasi, Isitala, kapena masiku akubadwa? (3, 4)

Kodi akufa angavulaze amoyo? (5) Kodi Yesu anafera pamtanda? (6) Kodi kukondweretsa Mulungu n’kofunika motani? (7)

1. Sikuti zikhulupiriro zonse ndi miyambo yonse njoipa. Koma Mulungu samazivomereza ngati zichokera ku chipembedzo chonyenga kapena ngati zimasemphana ndi ziphunzitso za Baibulo.—Mateyu 15:6.

2. Utatu: Kodi Yehova ndi Utatu—anthu atatu mwa Mulungu mmodzi? Iyayi! Yehova, Atate, ndiye “Mulungu woona yekha.” (Yohane 17:3; Marko 12:29) Yesu ndiye Mwana Wake woyamba kubadwa, ndipo amagonjera Mulungu. (1 Akorinto 11:3) Atate ngwamkulu kwa Mwanayo. (Yohane 14:28) Mzimu woyera si munthu; ndiwo mphamvu ya Mulungu yogwira ntchito.—Genesis 1:2; Machitidwe 2:18.

3. Krisimasi ndi Isitala: Yesu sanabadwe pa December 25. Anabadwa cha ku ma October 1, nthaŵi ya chaka pamene abusa ankasunga zifuyo zawo kunja usiku. (Luka 2:8-12) Yesu sanalamule Akristu kukondwerera kubadwa kwake. M’malo mwake, anauza ophunzira ake kusunga, kapena kukumbukira, imfa yake. (Luka 22:19, 20) Krisimasi ndi miyambo yake zinachokera ku zipembedzo zakale zonyenga. Chimodzimodzinso ndi miyambo ya Isitala, monga kugwiritsira ntchito mazira ndi akalulu. Akristu oyambirira sanakondwerere Krisimasi kapena Isitala, ngakhalenso Akristu oona lerolino samatero.

4. Masiku Akubadwa: Mapwando aŵiri okha a masiku akubadwa otchulidwa m’Baibulo anachitidwa ndi anthu amene sanali kulambira Yehova. (Genesis 40:20-22; Marko 6:21, 22, 24-27) Akristu oyambirira sanakondwerere masiku akubadwa. Mwambo wa kukondwerera masiku akubadwa unachokera ku zipembedzo zakale zonyenga. Akristu oona amapatsana mphatso ndipo amachezera pamodzi panthaŵi zina mkati mwa chaka.

5. Kuwopa Akufa: Akufa satha kuchita kanthu kapena kumva kanthu. Sitingawathandize, ndipo iwo sangativulaze. (Salmo 146:4; Mlaliki 9:5, 10) Sou imafa; simakhala ndi moyo pambuyo pa imfa. (Ezekieli 18:4, NW) Koma nthaŵi zina angelo oipa, otchedwa ziŵanda, amayerekeza kukhala mizimu ya akufa. Mwambo uliwonse wokhudza kuwopa akufa kapena kuwalambira ngwolakwa.—Yesaya 8:19.

6. Mtanda: Yesu sanafere pamtanda. Anafera pamlongoti, kapena mtengo. Liwu lachigiriki lotembenuzidwa “mtanda” m’Mabaibulo ambiri linatanthauza mtengo umodzi chabe. Chizindikiro cha mtanda chinachokera ku zipembedzo zakale zonyenga. Akristu oyambirira sanagwiritsire ntchito mtanda kapena kuulambira. Chotero, kodi muganiza kuti kuli bwino kugwiritsira ntchito mtanda polambira?—Deuteronomo 7:26; 1 Akorinto 10:14.

7. Kungakhale kovuta kusiya zina za zikhulupiriro ndi miyambo imeneyi. Achibale anu ndi mabwenzi angayese kukulimbikitsani kusasiya zikhulupiriro zanu. Koma kukondweretsa Mulungu ndiko kofunika kwambiri kuposa kukondweretsa anthu.—Miyambo 29:25; Mateyu 10:36, 37.

[Chithunzi patsamba 22]

Mulungu sali Utatu

[Chithunzi patsamba 23]

Krisimasi ndi Isitala zinachokera ku zipembedzo zakale zonyenga

[Chithunzi patsamba 23]

Palibe chifukwa cholambirira akufa kapena kuwawopa

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena