Phunziro 15
Kuthandiza Ena Kuchita Chifuniro cha Mulungu
Kodi n’chifukwa ninji muyenera kuuza ena zimene mukuphunzira? (1)
Kodi ndani amene mungauzeko uthenga wabwino? (2)
Kodi khalidwe lanu lingawakhudze motani ena? (2)
Kodi ndi liti pamene mungalalikire limodzi ndi mpingo? (3)
1. Pofika pano, mwaphunzira zinthu zambiri zabwino m’Baibulo. Chidziŵitso chimenechi chiyenera kukusonkhezerani kukulitsa umunthu wachikristu. (Aefeso 4:22-24) Chidziŵitso chimenecho n’chofunika kwambiri kuti mukapeze moyo wosatha. (Yohane 17:3) Komabe, ena afunikanso kumva uthenga wabwino kuti nawonso akapulumuke. Akristu oona onse ayenera kuchitira umboni kwa ena. Ndi lamulo la Mulungu.—Aroma 10:10; 1 Akorinto 9:16; 1 Timoteo 4:16.
2. Mungayambe mwa kuuza aja okhala pafupi nanu zinthu zabwino zimene mukuphunzira. Zisimbeni ku banja lanu, mabwenzi, anzanu akusukulu, ndi akuntchito. Mukhale wokoma mtima ndi woleza mtima pochita zimenezo. (2 Timoteo 2:24, 25) Kumbukirani kuti anthu nthaŵi zambiri amayang’anira kwambiri khalidwe la wina kuposa zonena zake. Chotero khalidwe lanu labwino lingakope ena kuti amvetsere uthenga umene muwauza.—Mateyu 5:16; 1 Petro 3:1, 2, 16.
3. M’kupita kwa nthaŵi, mungayambe kupita kukalalikira limodzi ndi mpingo wakwanuko wa Mboni za Yehova. Njira imeneyi njofunika kwambiri pa kupita kwanu patsogolo. (Mateyu 24:14) Mudzasangalala kwambiri ngati mudzatha kuthandiza wina kukhala mtumiki wa Yehova ndi kupeza moyo wamuyaya!—1 Atesalonika 2:19, 20.