Phunziro 16
Chosankha Chanu cha Kutumikira Mulungu
Kodi muyenera kuchitanji kuti mukhale bwenzi la Mulungu? (1, 2)
Kodi mungadzipatulire motani kwa Mulungu? (1)
Kodi ndi liti pamene muyenera kubatizidwa? (2)
Kodi mungapeze motani nyonga kuti mukhalebe wokhulupirika kwa Mulungu? (3)
1. Kuti mukhale bwenzi la Mulungu, muyenera kupeza chidziŵitso chabwino cha choonadi cha Baibulo (1 Timoteo 2:3, 4), kukhulupirira zinthu zimene mwaphunzira (Ahebri 11:6), kulapa machimo anu (Machitidwe 17:30, 31), ndi kutembenuka pa moyo wanu. (Machitidwe 3:19) Ndiyeno chikondi chanu pa Mulungu chiyenera kukusonkhezerani kudzipatulira kwa iye. Zimenezi zikutanthauza kuti muyenera kumuuza m’pemphero lapanokha, lamseri kuti mukudzipereka kwa iye kuchita chifuniro chake.—Mateyu 16:24; 22:37.
2. Mutadzipatulira kwa Mulungu, muyenera kubatizidwa. (Mateyu 28:19, 20) Ubatizo umadziŵitsa aliyense kuti munadzipatulira kwa Yehova. Chotero ubatizo uli wa aja okha amene ali achikulire okhoza kupanga chosankha cha kutumikira Mulungu. Pamene munthu akubatizidwa, thupi lake lonse liyenera kumizidwa m’madzi kwakanthaŵi.a—Marko 1:9, 10; Machitidwe 8:36.
3. Mutadzipatulira, Yehova adzafuna kuti mukwaniritse lonjezo lanu. (Salmo 50:14; Mlaliki 5:4, 5) Mdyerekezi adzayesa kukuletsani kutumikira Yehova. (1 Petro 5:8) Koma yandikirani kwa Mulungu m’pemphero. (Afilipi 4:6, 7) Phunzirani Mawu ake tsiku ndi tsiku. (Salmo 1:1-3) Mamatirani ku mpingo. (Ahebri 13:17) Mwa kuchita zonsezi, mudzapeza nyonga kuti mukhalebe wokhulupirika kwa Mulungu. Ku umuyaya wonse mungakhoze kuchita zimene Mulungu afuna kwa inu!
[Mawu a M’munsi]
a Pamafunikira kuphunzira buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?, kapena lina lofanana nalo lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova pokonzekera ubatizo.