Mutu 18
Yehova Alonjeza Danieli Mphotho Yodabwitsa
1, 2. (a) Kodi wothamanga pampikisano amafunikira mkhalidwe wotani kuti apambane? (b) Kodi mtumwi Paulo anayerekeza motani moyo wokhulupirika potumikira Yehova ndi makani akuthamanga?
WOTHAMANGA pampikisano tsopano akuwongola kulinga ku mzera womalizira. Iye watopa kwambiri, koma poona mzera womalizirawo patsogolo pake, akulimbikira ndi nyonga yonse yotsala mwa iye kuti amalize mtunda wotsalawo! Kenako, atakunga nyama zonse za m’thupi mwake, akudutsa mzerawo! Ndiyeno nkhope yake ikuŵala ndi chimwemwe cha kupambana. Inde, kupirira mpaka pomalizira kwam’pindula.
2 Kumapeto kwa Danieli chaputala 12, tikumuona mneneri wokondedwayo akuyandikira mzera womalizira wa “makani” ake—moyo wake wotumikira Yehova. Atapereka zitsanzo zosiyanasiyana za chikhulupiriro pakati pa atumiki a Yehova okhalako chisanayambe Chikristu, mtumwi Paulo analemba kuti: “Chifukwa chake ifenso, popeza tizingidwa nawo mtambo waukulu wotere wa mboni, titaye cholemetsa chilichonse, ndi tchimoli limangotizinga, ndipo tithamange mwachipiriro makaniwo adatiikira, ndi kupenyerera woyambira ndi womaliza wa chikhulupiriro chathu, Yesu, ameneyo, chifukwa cha chimwemwe choikidwacho pamaso pake, anapirira mtanda, nanyoza manyazi, nakhala pa dzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.”—Ahebri 12:1, 2.
3. (a) N’chiyani chinasonkhezera Danieli ‘kuthamanga mwachipiriro’? (b) Ndi zinthu zitatu zotani zimene mngelo wa Yehova anauza Danieli?
3 Pakati pa ‘mtambo waukulu wa mboni’ umenewo, panalinso Danieli. Iye anali mmodzi amene ‘anathamanga mwachipiriro,’ ndipo chikondi chozama cha pa Mulungu ndicho chinam’limbikitsa kutero. Yehova anali atavumbulira Danieli zambiri ponena za tsogolo la maboma a dziko, koma tsopano anam’tumizira chilimbikitso chachindunji ichi: “Koma iwe, muka mpaka chimaliziro; pakuti udzapumula, nudzaima m’gawo lako masiku otsiriza.” (Danieli 12:13) Mngelo wa Yehova anali kuuza Danieli zinthu zitatu: (1) kuti Danieli amuke “mpaka chimaliziro,” (2) kuti ‘adzapumula,’ ndipo (3) kuti ‘adzaimanso’ m’tsogolo. Kodi mawu ameneŵa angalimbikitsenso motani Akristu lerolino kuti apirire mpaka akafike pamzera womalizira pa mpikisano wa moyo?
“MUKA MPAKA CHIMALIZIRO”
4. Kodi mngelo wa Yehova anatanthauzanji ponena kuti “muka mpaka chimaliziro,” ndipo n’chifukwa chiyani zimenezo zinali zovuta kwa Danieli?
4 Kodi mngeloyo anatanthauzanji pouza Danieli kuti: “Koma iwe, muka mpaka chimaliziro”? Chimaliziro cha chiyani? Chabwino. Popeza Danieli anali ndi zaka pafupifupi 100, mwachionekere mngeloyo anali kunena za chimaliziro cha moyo wake, chimene chinalidi pafupi.a Mngeloyo amalimbikitsa Danieli kuti apirire mokhulupirika mpaka imfa. Koma kuchita zimenezo sikunali kwapafupi. Danieli anakhalapobe ndi moyo mpaka anaona ndi maso ake Babulo pogwetsedwa komanso Ayuda andende otsalira pobwerera ku Yuda ndi Yerusalemu. Zimenezo ziyenera kuti zinam’patsa chisangalalo chachikulu mneneri wokalambayo. Koma sitinaŵerengepo pena paliponse kuti iye anapita nawo paulendowo. Panthaŵiyo ayenera kuti anali wokalamba kwambiri ndi wofooka. Mwinanso chinali chifuniro cha Yehova kuti iye akhalebe m’Babulo. Mulimonsemo, mwachibadwa tingaganizebe kuti Danieli anasirira pamene anthu akwawo anali kubwerera ku Yuda.
5. Kodi pali umboni wotani wosonyeza kuti Danieli anapirira mpaka chimaliziro?
5 Mwachidziŵikire, Danieli analimbikitsidwa kwambiri ndi mawu okoma a mngelo akuti: “Muka mpaka chimaliziro.” Tingakumbukire mawu amene Yesu Kristu ananena pafupifupi zaka mazana asanu ndi limodzi pambuyo pake kuti: “Iye wakulimbika chilimbikire kufikira kuchimaliziro, yemweyo adzapulumuka.” (Mateyu 24:13) N’zimene Danieli anachitadi zimenezo. Analimbikira kufikira mapeto, akumathamanga makani a moyo mpaka pomalizira penipenipo. Chimenecho chingakhale chifukwa chimodzi chimene anathokozedwa nacho m’Mawu a Mulungu pambuyo pake. (Ahebri 11:32, 33) Nanga n’chiyani chinatheketsa Danieli kupirira? Mbiri ya moyo wake imatithandiza kupeza yankho.
KUPIRIRA MONGA WOPHUNZIRA MAWU A MULUNGU
6. Timadziŵa bwanji kuti Danieli anali wophunzira Mawu a Mulungu wakhama?
6 Kwa Danieli, kupirira mpaka chimaliziro kunaphatikizapo kuphunzira ndi kusinkhasinkha mozama malonjezo osangalatsa a Mulungu. Timadziŵa kuti Danieli anali wophunzira Mawu a Mulungu wakhama. Kupanda kutero, akanatha bwanji kudziŵa lonjezo la Yehova kwa Yeremiya lakuti kundendeko akakhala zaka 70? Danieli mwiniyo analemba kuti: “Ine . . . ndinazindikira mwa mabuku . . . chiŵerengo chake cha zaka.” (Danieli 9:2; Yeremiya 25:11, 12) Mosakayika, Danieli ankaŵerenga mabuku a m’masiku amenewo a Mawu a Mulungu. Zolemba za Mose, Davide, Solomo, Yesaya, Yeremiya, Ezekieli—zilizonse zomwe zinalipo—zinam’sangalatsa Danieli poziŵerenga ndi kusinkhasinkhamo.
7. Tikayerekeza nthaŵi zathu ndi nthaŵi za Danieli, ndi mwayi wotani umene ifeyo tili nawo pophunzira Mawu a Mulungu?
7 Kuphunzira Mawu a Mulungu, kuzama mmenemo, n’kofunika kuti tikulitse chipiriro lerolino. (Aroma 15:4-6; 1 Timoteo 4:15) Ndipo tili ndi Baibulo lathunthu, mmene mulinso nkhani zolembedwa zosonyeza mmene maulosi ena a Danieli anakwaniritsidwira patapita zaka mazana ambiri. Komanso, tili odalitsika pokhala mu “nthaŵi ya chimaliziro,” yonenedwa pa Danieli 12:4. M’masiku athu ano, odzozedwa adalitsika ndi chidziŵitso chauzimu, ndipo akumaŵala ngati mauniko a choonadi m’dziko lamdimali. Pachifukwa chimenecho, maulosi ambiri ozama a m’buku la Danieli, ena amene Danieli sanawamvetse, ali ndi tanthauzo kwambiri kwa ife. Choncho, tiyeni tipitirize kuphunzira Mawu a Mulungu masiku onse, ndi kusatenga zinthu zimenezi mopepuka. Kuteroko kudzatithandiza kupirira.
DANIELI ANALIMBIKIRA KUPEMPHERA
8. Kodi Danieli anapereka chitsanzo chotani pankhani ya pemphero?
8 Pemphero linathandizanso Danieli kupirira mpaka chimaliziro. Tsiku ndi tsiku anatembenukira kwa Yehova Mulungu nalankhula naye momasuka ndi mtima wodzala chikhulupiriro ndi chidaliro. Iye anadziŵa kuti Yehova anali “Wakumva pemphero.” (Salmo 65:2; yerekezani ndi Ahebri 11:6.) Mtima wa Danieli utapsinjika ndi chisoni poona khalidwe lopanduka la Israyeli, anam’dandaulira Yehova. (Danieli 9:4-19) Ngakhale pamene Dariyo analamula kuti anthu onse apemphe kwa iye yekha kwa masiku 30, Danieli sanalole zimenezo kum’lepheretsa kupemphera kwa Yehova Mulungu. (Danieli 6:10) Kodi sizikutikhudza poona mmene nkhalamba yokhulupirikayo inalolera kuponyedwa m’dzenje la mikango kusiyana n’kuti itaye mwayi wamtengo wapatali wa pemphero? N’zosakayikitsa kuti Danieli anamka ku chimaliziro chake ali wokhulupirika, akumapemphera ndi mtima wonse kwa Yehova tsiku ndi tsiku.
9. N’chifukwa chiyani sitiyenera konse kutenga mopepuka mwayi wa pemphero?
9 Pemphero ndi chinthu chosavuta. Titha kupemphera nthaŵi ina iliyonse, kwina kulikonse, mokweza mawu kapena mumtima. Komabe, sitiyenera konse kupeputsa mwayi wamtengo wapatali umenewu. Baibulo limagwirizanitsa pemphero ndi kupirira, kulimbikira, kukhala maso mwauzimu. (Luka 18:1; Aroma 12:12; Aefeso 6:18; Akolose 4:2) Kodi sizonyaditsa kuti tili ndi lamya, titero kunena kwake, yosalipira komanso yosakana kugwira, yolankhulana ndi wamkulukulu woposa wina aliyense m’chilengedwe chonse? Ndipo iye amamvetseradi! Kumbukirani chochitika chija pamene Danieli anapemphera, ndipo Yehova poyankha anam’tumizira mngelo. Mngeloyo anafika Danieli akali m’kati mwa pemphero! (Danieli 9:20, 21) Zoona, ife sitikukhala m’nthaŵi yofikiridwa ndi angelo. Koma Yehova sanasinthe. (Malaki 3:6) Monga mmene anamvera pemphero la Danieli, adzamvetseranso mapemphero athu. Ndipo tikamapemphera, tidzayandikana ndi Yehova, tikumaumba unansi umene udzatithandiza kupirira mpaka chimaliziro, muja anachitira Danieli.
KUPIRIRA MONGA MPHUNZITSI WA MAWU A MULUNGU
10. N’chifukwa chiyani kuphunzitsa choonadi cha Mawu a Mulungu kunali kofunika kwambiri kwa Danieli?
10 Danieli anayenera ‘kumuka mpaka chimaliziro,’ m’ganizo linalakenso. Anayenera kupirira monga mphunzitsi wa choonadi. Sanaiŵale konse kuti anali mmodzi wa anthu osankhika amene Malemba amanena kuti: “Inu ndinu mboni zanga, ati Yehova, ndi mtumiki wanga, amene ndakusankha.” (Yesaya 43:10) Danieli anachita chilichonse chotheka kuti akwaniritse ntchitoyo. Mwachionekere, ntchito yake inaphatikizapo kuphunzitsa anthu ake omwe anali m’Babulomo monga andende. Timadziŵa zochepa kwambiri pa zochita zake ndi Ayuda anzake, kupatulapo atatu otchedwa “anzake”—Hananiya, Misaeli, ndi Azariya. (Danieli 1:7; 2:13, 17, 18) Ubwenzi wawo wokondana unathandiza kwambiri aliyense wa iwo kupirira. (Miyambo 17:17) Danieli, atadalitsidwa ndi Yehova pom’patsa chidziŵitso chapadera, anali n’zambiri zophunzitsa anzakewo. (Danieli 1:17) Koma anafunikira kuphunzitsa anthu enanso.
11. (a) Kodi chachilendo chinali chiyani pa ntchito ya Danieli? (b) Kodi Danieli anali wogwira mtima motani pochita ntchito yake yachilendoyo?
11 Mosiyana ndi mneneri wina aliyense, Danieli anali ndi ntchito yolalikira kwa anthu olemekezeka Akunja. Ngakhale kuti nthaŵi zambiri anafunikira kulengeza mauthenga osawasangalatsa, iye sananyoze olamulirawo kapena kuwaona ngati otsika kwa iye. Analankhula kwa iwo mwaulemu ndi mwaluso. Analipo ena monga akalonga ansanje ndi achiwembu aja amene anafuna kuwononga Danieli. Komabe, olemekezeka ena amam’lemekeza iyenso. Chifukwa Yehova anakhozetsa Danieli kumasulira zinsinsi zimene zinakanika mafumu ndi amuna anzeru, mneneriyo anakwezeka kwambiri. (Danieli 2:47, 48; 5:29) Zoona, mmene amakalamba, sanalinso wachangu muja analili paunyamata wake. Koma anamukadi ku chimaliziro chake adakali ndi mtima wofuna njira iliyonse yotumikira monga mboni ya Mulungu wake wokondeka.
12. (a) Kodi ifeyo monga Akristu, timachita ntchito yotani yophunzitsa lerolino? (b) Kodi tingatsatire motani uphungu wa Paulo wa ‘kuyenda munzeru kulinga kwa akunja’?
12 Mumpingo wachikristu lero, tingapeze anzathu okhulupirika amene tingathandizane nawo kupirira, muja anathandizirana Danieli ndi anzake atatuwo. Komanso timaphunzitsana ndi “kulimbikitsana.” (Aroma 1:11, 12, NW) Monga Danieli, tapatsidwa ntchito yochitira umboni kwa anthu osakhulupirira. (Mateyu 24:14; 28:19, 20) Choncho, tiyenera kunola maluso athu kuti ‘tilunjike nawo bwino mawu a choonadi’ polankhula kwa anthu za Yehova. (2 Timoteo 2:15) Ndipo tidzathandizika kwambiri ngati timvera uphungu wa mtumwi Paulo wakuti: ‘Muyende munzeru ndi iwo akunja.’ (Akolose 4:5) Nzeru yoteroyo imaphatikizapo kukhala ndi maganizo abwino kulinga kwa aja osakhala nafe m’chikhulupiriro. Sitinyoza anthu oterowo, kuona ngati tili pamwamba pawo ayi. (1 Petro 3:15) M’malo mwake, tiyenera kuwakopera ku choonadi, tikumagwiritsa ntchito Mawu a Mulungu mwanzeru ndi mwaluso kuti tifikire mitima yawo. Pamene tikwanitsa kum’fika wina pamtima, chimwemwe chathu chimakhala chodzaza tsaya! Chimwemwe choterocho chimatithandiza kupirira mpaka chimaliziro, monga anachitira Danieli.
“UDZAPUMULA”
13, 14. N’chifukwa chiyani chiyembekezo cha imfa chinali choopsa kwambiri kwa Ababulo ambiri, koma kaonedwe ka Danieli kanali kosiyana motani?
13 Kenako mngeloyo anatsimikizira Danieli kuti: “Udzapumula.” (Danieli 12:13) Kodi mawuwo anatanthauza chiyani? Eya, Danieli anadziŵa kuti imfa yake inali pafupi. Kwa anthu onse, imfa yakhala mapeto osapeŵeka kuchokera m’tsiku la Adamu mpaka lero. N’chifukwa chake Baibulo limatcha imfa kuti “mdani.” (1 Akorinto 15:26) Koma kwa Danieli, chiyembekezo cha imfa yake chinali chosiyana ndi cha Ababulo om’zungulira. Kwa iwo, pokhala ozama m’kulambira kocholoŵana kwa milungu yonama yokwana ngati 4,000, imfa inali chiyembekezo chochititsa mantha a mtundu uliwonse. Iwo ankakhulupirira kuti anthu amene anakhala ndi moyo wovutika kapena amene anafa imfa yachiwawa, pambuyo pa imfa amasanduka mizimu yolipsira imene inkavutitsa amoyo. Ababulo ankakhulupiriranso kuti panali dziko la akufa, lokhalamo zilombo zoopsa, zina monga zianthu, zina monga zinyama.
14 Koma kwa Danieli, chiyembekezo cha imfa chinalibe chilichonse cha zinthuzo. Zaka mazana ambiri Danieli asanakhalepo, Mfumu Solomo anauziridwa ndi Mulungu kunena kuti: “Akufa sadziŵa kanthu bi.” (Mlaliki 9:5) Ndipo kunena za munthu amene wafa, wamasalmo anaimba kuti: “Mpweya [“mzimu,” NW] wake uchoka, abwerera kumka ku nthaka yake; tsiku lomwelo zotsimikiza mtima zake zitayika.” (Salmo 146:4) Choncho Danieli anadziŵa kuti zimene mngelo anamuuza zikachitikadi. Imfa inatanthauza kupumula. Osaganiza chilichonse, osamva chisoni chilichonse, osazunzika ndi chilichonse komanso popanda zilombo zoopsa zilizonse. Yesu Kristu ananenanso chimodzimodzi pamene Lazaro anamwalira. Iye anati: “Lazaro bwenzi lathu ali m’tulo.”—Yohane 11:11.
15. Kodi tsiku lakumwalira lingapose bwanji tsiku lakubadwa?
15 Taonani chifukwa china chimene Danieli sanaopere imfa. Mawu a Mulungu amati: “Mbiri yabwino iposa zonunkhira zabwino; ndi tsiku lakumwalira liposa tsiku lakubadwa.” (Mlaliki 7:1) Ndi motani mmene tsiku la imfa, limene limakhala lachisoni, lingaposere tsiku lobadwa, limene limadzetsa chisangalalo? Yankho lake lili m’mawuwo akuti “mbiri.” “Zonunkhira zabwino” zingakhale zamtengo wokwera kwambiri. Tsiku lina Mariya mlongo wa Lazaro, anadzoza mapazi a Yesu mafuta onunkhira ogula ndalama za malipiro pafupifupi a chaka chonse! (Yohane 12:1-7) Kodi ndi motani mmene mbiri yokha ingakhalire yamtengo wapatali kuposa pamenepo? Pa Mlaliki 7:1, Baibulo lachigiriki lotchedwa Septuagint, m’malo mwa mawu akuti “mbiri yabwino” limati, “dzina labwino.” Mtengo wake suli m’dzina lokhalo ayi, koma zimene limaimira. Pobadwa, mwinidzina sakhala ndi mbiri iliyonse, sakhala ndi mbiri ya ntchito zabwino, sakhala ndi moyo wabwino kapena mikhalidwe yabwino imene angaikumbukire. Koma munthuyo akamwalira, dzina lake limaimira zonsezo. Ndipo ngati lili dzina labwino m’maso mwa Mulungu, limakhala lamtengo woposa chuma chakuthupi chilichonse chimene munthu angakhale nacho.
16. (a) Kodi Danieli anayesetsa motani kukhala ndi dzina labwino kwa Mulungu? (b) N’chifukwa chiyani Danieli akanatha kukapuma ndi chidaliro chakuti anapambana pokhala ndi dzina labwino kwa Yehova?
16 M’moyo wake wonse, Danieli anachita chilichonse chotheka kuti akhale ndi dzina labwino kwa Mulungu, ndipo Yehova sananyalanyaze chilichonse cha zoyesayesa zimenezi. Iye anayang’anira Danieli ndi kusanthula mtima wake. Mulungu anachitanso chimodzimodzi kwa Mfumu Davide, amene anaimba kuti: “Munandisanthula, Yehova, nimundidziŵa. Inu mudziŵa kukhala kwanga ndi kuuka kwanga, muzindikira lingaliro langa muli kutali.” (Salmo 139:1, 2) Zoona, Danieli sanali wangwiro. Anali mbadwa ya Adamu komanso wochokera ku mtundu wochimwa. (Aroma 3:23) Koma Danieli analapa kuchimwa kwake nayesetsa kuyenda ndi Mulungu wake m’njira yolungama. N’chifukwa chake mneneri wokhulupirikayo anali ndi chidaliro chakuti Yehova akakhululuka machimo ake ndi kusawakumbukiranso. (Salmo 103:10-14; Yesaya 1:18) Yehova amasankha kukumbukira ntchito zabwino za atumiki ake okhulupirika. (Ahebri 6:10) Choncho kaŵiri konse, mngelo wa Yehova anatcha Danieli kuti “munthu wokondedwatu iwe.” (Danieli 10:11, 19) Zimenezi zinatanthauza kuti Danieli anali wokondeka wa Mulungu. Danieli anatha kumka kokapuma ali wokhutira, podziŵa kuti anali atakhala ndi dzina labwino kwa Yehova.
17. N’chifukwa chiyani sitiyenera kuchedwa kukhala ndi dzina labwino kwa Yehova lerolino?
17 Aliyense wa ife ayenera kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndili ndi dzina labwino kwa Yehova?’ Tikukhala m’nthaŵi zovuta. Kuganiza kuti tsiku lililonse imfa ingatenge aliyense wa ife si mantha ayi, koma kuona zinthu monga mmene zilili. (Mlaliki 9:11) N’kofunika motani nanga, kuti aliyense wa ife atsimikize mtima kukhala ndi dzina labwino kwa Mulungu tsopano lino, nthaŵi isanathe. Tikatero, sitidzaopa imfa. Imakhala kupumula basi—ngati tulo. Ndipo monga tulo, tidzauka!
“UDZAIMA”
18, 19. (a) Kodi mngeloyo anatanthauzanji pamene ananeneratu kuti Danieli ‘akaima’ m’tsogolo? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti Danieli anali kudziŵa za chiyembekezo cha kuuka kwa akufa?
18 Buku la Danieli limafika kumapeto kwake ndi limodzi la malonjezo abwino koposa amene Mulungu wapereka kwa munthu. Mngelo wa Yehova anauza Danieli kuti: “Udzaima m’gawo lako masiku otsiriza.” Kodi anatanthauzanji mngeloyo? Eya, popeza kuti ‘kupumula’ kumene anali atanenako kumatanthauza imfa, lonjezo lakuti Danieli ‘adzaima’ panthaŵi ina m’tsogolo linangotanthauza chinthu chimodzi—kuuka kwa akufa!b Ndi iko komwe, akatswiri a Baibulo ena anena kuti pa Danieli chaputala 12 ndi pamene timapeza mawu oyamba onena mwachindunji za chiukiriro chopezeka m’Malemba Achihebri. (Danieli 12:2) Komabe pamfundoyi, iwo n’ngolakwa. Danieli ankadziŵa bwino kwambiri za chiyembekezo cha kuuka.
19 Mwachitsanzo, Danieli anadziŵa ndithu mawu aŵa amene Yesaya analemba zaka mazana aŵiri m’mbuyomo: “Akufa anu adzakhala ndi moyo; mitembo yawo idzauka. Ukani muimbe, inu amene mukhala m’fumbi; chifukwa . . . dziko lapansi lidzatulutsa mizimu [“anthu opanda mphamvuwo ali mu imfa,” NW].” (Yesaya 26:19) Zaka zambiri izi zisanachitike, Eliya ndi Elisa anapatsidwa mphamvu ndi Yehova yakuti aukitse akufa. (1 Mafumu 17:17-24; 2 Mafumu 4:32-37) Ngakhale m’mbuyo kwambiri, Hana, mayi wa mneneri Samueli, anavomereza kuti Yehova akhoza kuutsa anthu kumanda. (1 Samueli 2:6) M’mbuyonso kwambiri, Yobu wokhulupirikayo anatchula za chiyembekezo chake ndi mawu aŵa: ‘Atafa munthu, adzakhalanso ndi moyo kodi? Ndidzayembekeza masiku onse a nkhondo yanga, mpaka kutafika kusandulika kwanga. Mudzaitana, ndipo ndidzakuyankhani; mudzakhumba ntchito ya manja anu.”—Yobu 14:14, 15.
20, 21. (a) Kodi Danieli ali wotsimikizika kudzakhala nawo pa kuuka kuti? (b) Kodi zikuoneka kuti kuuka m’Paradaiso kukachitika m’njira yotani?
20 Mofanana ndi Yobu, Danieli anali ndi chifukwa chokhalira ndi chidaliro chakuti Yehova akakhumba kumuukitsa tsiku lina m’tsogolo. Komanso, kuyenera kuti kunali kotonthoza kwambiri kumva munthu wamphamvu wauzimu akutsimikizira za chiyembekezo chimenecho. Inde, Danieli adzaima pa “kuuka kwa olungama,” kumene kudzachitika mu Ulamuliro wa Kristu wa Zaka Chikwi. (Luka 14:14) Kodi zimenezo zidzakhala motani kwa Danieli? Mawu a Mulungu amatiuza zambiri pankhaniyi.
21 Yehova si “Mulungu wa chisokonezo koma wa mtendere.” (1 Akorinto 14:33) Pamenepo, n’zoonekeratu kuti kuukako m’Paradaiso kudzachitika mwadongosolo lake. Mwina padzapita nthaŵi kaye itadutsa Armagedo. (Chivumbulutso 16:14, 16) Zotsalira zonse za dongosolo lakale la zinthu zidzakhala zitachotsedwa, ndipo mosakayika, makonzedwe adzakhazikitsidwa olandirira akufa. Ponena za mmene akufawo ati adzaukire, Baibulo limati: “Yense m’dongosolo lake la iye yekha.” (1 Akorinto 15:23) Zikuoneka kuti ponena za “kuuka kwa olungama ndi osalungama,” olungama ndiwo ati adzayambe kuukitsidwa. (Machitidwe 24:15) Mwa njira imeneyo, amuna okhulupirika akale onga Danieli, adzakhoza kudzathandiza kuyendetsa zinthu padziko lapansi, komanso kudzaphunzitsa mabiliyoni a “osalungama” amene adzaukitsidwanso.—Salmo 45:16.
22. Kodi ndi mafunso ena ati amene mwachionekere Danieli adzafuna kuti adzayankhidwe?
22 Koma Danieli asanayambe ntchito imeneyo, ndithudi adzakhala ndi mafunso amene adzafuna kudzafunsa. Ndi iko komwe, ponena za maulosi ozama omwe anapatsidwa, iye anati: “Ndinachimva ichi, koma osachizindikira.” (Danieli 12:8) Ha, mmene adzasangalalira pomvetsa zinsinsi zaumulungu zimenezi! Ndithudi, adzafuna kudziŵa zonse zokhudza Mesiya. Danieli adzachitanso chidwi kumva za mndandanda wa maulamuliro amphamvu padziko lonse kuyambira m’tsiku lake mpaka m’tsiku lathu, ponena za “opatulika a Wam’mwambamwamba” omwe anapirira mazunzo m’kati mwa “nthaŵi ya chimaliziro,” komanso za mmene Ufumu Waumesiya wa Mulungu unawonongera maufumu onse a anthu.—Danieli 2:44; 7:22; 12:4.
GAWO LA DANIELI M’PARADAISO—KOMANSO LA INU!
23, 24. (a) Kodi dziko limene Danieli adzaukitsidwamo lidzasiyana motani ndi limene ankalidziŵa? (b) Kodi Danieli adzakhala ndi malo m’Paradaiso, ndipo tikudziŵa bwanji zimenezo?
23 Danieli adzafuna kudziŵa za dziko limene adzakhalamo panthaŵiyo—dziko losiyana kwambiri ndi la m’tsiku lake. Padzakhala palibiretu chizindikiro chilichonse cha nkhondo ndi zitsenderezo zimene zinaipitsa dziko limene ankalidziŵa. Padzakhala palibe chisoni, matenda, kapena imfa. (Yesaya 25:8; 33:24) M’malo mwake, padzakala chakudya cha mwana alirenji, nyumba zokwanira aliyense, ndi ntchito yosangalatsa onse. (Salmo 72:16; Yesaya 65:21, 22) Anthu onse adzakhala banja limodzi lachimwemwe ndi logwirizana.
24 Ndithudi, Danieli adzakhala ndi malo m’dziko limenelo. Mngelo uja anamuuza kuti: ‘Udzaima m’gawo lako.’ Liwu lachihebri lotembenuzidwa kuti “gawo” pano, n’lofanana ndi limene limatanthauza malo enieni a dziko.c Danieli ayenera kuti anali kudziŵa za ulosi wa Ezekieli wonena za kugaŵa dziko lobwezeretsedwa la Israyeli. (Ezekieli 47:13–48:35) Pakukwaniritsidwa kwake kwa m’Paradaiso, kodi ulosi wa Ezekieli umasonyeza chiyani? Umasonyeza kuti anthu onse a Mulungu adzakhala ndi malo m’Paradaiso, ndipo dziko lidzagaŵidwa mwadongosolo komanso mwachilungamo. Koma gawo la Danieli m’Paradaiso lidzaphatikizapo mbali zina osati malo okha. Lidzaphatikizapo udindo wake pa cholinga cha Mulungu mmenemo. Mphotho imene Danieli analonjezedwa n’njotsimikizirika.
25. (a) Kodi ndi zinthu zotani za m’Paradaiso zimene zimakukopani mtima inuyo? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti Paradaiso ndiye kwawo kwa anthu?
25 Bwanji nanga za gawo lanu? Malonjezowo angakhalenso chimodzimodzi kwa inu. Yehova amafuna kuti anthu omvera ‘akaime’ m’gawo lawo, kuti akakhale ndi malo m’Paradaiso. Tangoganizani! Kudzakhaladi kosangalatsa kumuona Danieli pamaso m’pamaso, limodzinso ndi amuna ndi akazi ena okhulupirika a m’nthaŵi za m’Baibulo. Kenako, padzakhalanso ena ambiri oukitsidwa kwa akufa, ofunikira kuphunzitsidwa kudziŵa Yehova Mulungu ndi kum’konda. Tadziyerekezani nokha kuti mukusamalira mudzi wathuwu dziko lapansi ndipo mukuthandiza pousandutsa kukhala paradaiso wa zinthu zosiyanasiyana ndi kukongola kosafwifwa. Taganizani za kuphunzitsidwa ndi Yehova, kuphunzira mmene tingakhalire ndi moyo umene pachiyambi anaukonzera anthu. (Yesaya 11:9; Yohane 6:45) Inde, malo muli nawo m’Paradaiso. Ngakhale kuti Paradaiso angamveke ngati chinthu chosatheka kwa anthu ena lerolino, kumbukirani kuti poyamba Yehova analenga anthu kuti akhale m’malo oterowo. (Genesis 2:7-9) M’ganizo limenelo, Paradaiso ndiwo mudzi wawo weniweni wa mabiliyoni a anthu okhala padziko lapansi. Ndiko kwawo kwa anthu. Kufika mmenemo kudzakhala ngati kubwerera kumudzi.
26. Kodi Yehova akusonyeza motani kuti amamvetsa kuti kudikira mapeto a dongosolo la zinthu lilipoli n’kovuta kwa ife?
26 Mitima yathu ikusefukira ndi chiyamikiro pamene tiganizira zonsezi, si choncho nanga? Kodi inuyo simukhumba kukhala mmenemo? Ndiye chifukwa chake sitiyenera kudabwa poona Mboni za Yehova zikumakhala zofunitsitsa kudziŵa pamene mapeto a dongosolo la zinthu lilipoli adzafika! Kudikira si kwapafupi. Yehova amadziŵanso zimenezo, pakuti amatilimbikitsa ‘kulindirira’ mapetowo ngakhale ‘atachedwa.’ Akutanthauza kuti angaoneke kukhala atachedwa malinga ndi kuona kwathu, pakuti m’lemba limodzimodzilo, timatsimikiziridwa kuti: ‘Sadzazengereza.’ (Habakuku 2:3; yerekezani ndi Miyambo 13:12.) Inde, chimaliziro chidzafika ndendende panthaŵi yake.
27. Kodi muyenera kuchitanji kuti mukaime pamaso pa Mulungu ku umuyaya wonse?
27 Kodi muyenera kuchitanji pamene mapeto akuyandikira? Monga anachitira mneneri wa Yehova wokondeka Danieli, pirirani mokhulupirika. Phunzirani Mawu a Mulungu mwakhama. Pempherani mochokera pansi pa mtima. Yanjanani mwachikondi ndi okhulupirira anzanu. Kangalikani pakuphunzitsa ena choonadi. Poona dongosolo loipali likuyandikira mapeto ake tsiku ndi tsiku, tsimikizani mtima kukhalabe mtumiki wokhulupirika wa Wam’mwambamwamba komanso wochirikiza Mawu ake molimba. Mwa kuchita chilichonse chotheka, samalani ulosi wa Danieli! Ndipo Ambuye Mfumu Yehova akupatsenitu mwayi wakuima pamaso pake mosangalala ku umuyaya wonse!
[Mawu a M’munsi]
a Danieli anatengeredwa ukapolo ku Babulo mu 617 B.C.E., mwachionekere ali wachinyamata. Analandira masomphenya ake m’chaka chachitatu cha Koresi, kapena mu 536 B.C.E.—Danieli 10:1.
b Malinga ndi buku lotchedwa The Brown-Driver-Briggs Hebrew and English Lexicon, liwu lachihebri lotembenuzidwa kuti “kuima” pano, limatanthauza “kuuka pambuyo pa imfa.”
c Liwu lachihebrilo limafanana ndi liwu lotanthauza “nkhulungo,” chifukwa miyala ing’onoing’ono inkagwiritsidwa ntchito pochita maere. Nthaŵi zina malo ankagaŵidwa mwa njira imeneyi. (Numeri 26:55, 56) Buku lotchedwa A Handbook on the Book of Daniel limati, pano liwuli limatanthauza “chimene (Mulungu) wapatulira munthu.”
KODI MWAZINDIKIRA CHIYANI?
• Kodi chinathandiza Danieli kupirira mpaka chimaliziro n’chiyani?
• N’chifukwa chiyani chiyembekezo cha kufa sichinam’patse mantha Danieli?
• Kodi lonjezo la mngelo lakuti Danieli ‘adzaima m’gawo lake’ lidzakwaniritsidwa motani?
• Kodi inuyo panokha mwapindula motani mwa kupenda ulosi wa Danieli?
[Chithunzi chachikulu patsamba 307]
[Chithunzi patsamba 318]
Mofanana ndi Danieli, kodi mumasamalira mawu aulosi a Mulungu?