Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • jt tsamba 19-21
  • Njira Zimene Amagwiritsa Ntchito Pokuuzani Uthengawo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Njira Zimene Amagwiritsa Ntchito Pokuuzani Uthengawo
  • Mboni za Yehova—Kodi Iwo Ndani? Kodi Amakhulupirira Chiyani?
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • KULALIKIRA MWA KUPEREKA CHITSANZO
  • Kodi Ndani Akulalikira Uthenga Wabwino?
    Nsanja ya Olonda—2011
  • “Mbiri Yabwino Iyenera Kulalikidwa Choyamba”
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Phindu la Uthenga Wabwino
    Nsanja ya Olonda—2002
  • Kufalitsa “Uthenga Wabwino wa Zinthu Zabwino”
    Nsanja ya Olonda—2005
Onani Zambiri
Mboni za Yehova—Kodi Iwo Ndani? Kodi Amakhulupirira Chiyani?
jt tsamba 19-21

Njira Zimene Amagwiritsa Ntchito Pokuuzani Uthengawo

AKRISTU analamulidwa kuti ‘aphunzitse anthu a mitundu yonse,’ koma zimenezi sizitanthauza kuti iwo ayenera kuumiriza anthu kapena kuwatembenuza mwa kugwiritsa ntchito mphamvu ayi. Ntchito ya Yesu inali ‘kulalikira mawu abwino kwa ofatsa,’ ‘kumangirira osweka mtima,’ ndi ‘kutonthoza akulira maliro.’ (Mateyu 28:19; Yesaya 61:1, 2; Luka 4:18, 19) Mboni za Yehova zimayesetsa kuchita zimenezi mwa kulengeza uthenga wabwino wochokera m’Baibulo. Mofanana ndi mneneri Ezekieli wakaleyo, Mboni za Yehova lerolino zimayesetsa kupeza ‘anthu akuusa moyo ndi kulira chifukwa cha zonyansa zonse zikuchitidwa.’—Ezekieli 9:4.

Njira yabwino koposa yodziŵika yopezera anthu amene akuvutika maganizo chifukwa cha mikhalidwe ilipoyi ndiyo mwa kupita ku nyumba ndi nyumba. Mwakutero, a Mboniwo amayesetsa kuwafikira anthu, monga momwe Yesu anachitira pamene “anayendayenda kumizinda ndi kumidzi, kulalikira ndi kuwauza Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu.” Ophunzira ake oyambirira anachitanso zimenezo. (Luka 8:1; 9:1-6; 10:1-9) Lerolinonso, ngati kuli kotheka, a Mboni za Yehova amayesetsa kufikira nyumba iliyonse nthaŵi zambiri pachaka, pofuna kuti alankhule ndi eninyumbawo kwa mphindi zochepa pankhani za kumaloko kapena za padziko lonse lapansi zimene zimawasangalatsa kapena zimene zimawakhudza. Amapempha kuti akambirane lemba limodzi kapena aŵiri, ndipo ngati mwininyumbayo wasonyeza chidwi, Mboniyo imalonjeza kudzabweranso panthaŵi yoyenera kuti adzapitirize kukambirana. Amasonyeza mabaibulo ndi mabuku ofotokoza za m’Baibulo, ndipo ngati mwininyumbayo akufuna, amayamba kuphunzira naye Baibulo kwaulere panyumba pake. Mamiliyoni a maphunziro a Baibulo othandiza ameneŵa akuchititsidwa nthaŵi zonse kwa anthu ndi mabanja kuzungulira dziko lonse lapansi.

Njira ina imene amalengezera “uthenga wabwino wa ufumu” kwa ena ndiyo mwa misonkhano imene imachitikira pa Nyumba za Ufumu za kumadera akwawo. A Mboniwo amachita misonkhano imeneyo mlungu uliwonse. Umodzi wa misonkhanoyo umakhala nkhani yapoyera yokhudza mikhalidwe yapanthaŵiyo. Kenako pamatsatira kuphunzira nkhani ya m’Baibulo kapena ulosi, mwa kugwiritsa ntchito magazini ya Nsanja ya Olonda. Msonkhano wina ndi sukulu yophunzitsa Mboni kukhala alengezi aluso a uthenga wabwino, kenakonso pamadzabwera gawo lokambirana ntchito yochitira umboni m’dera lakwawo. Ndiponso, kamodzi pamlungu, a Mboni amasonkhana m’nyumba za abale anzawo, m’magulu ang’onoang’ono, kumene amaphunziranso Baibulo.

Pa misonkhano yonseyi, munthu aliyense amaloledwa kufikapo. Sipakhala kusonkhetsa ndalama ayi. Ndipo misonkhano imeneyi imakhala yopindulitsa onse. Baibulo limati: “Tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino, osaleka kusonkhana kwathu pamodzi, monga amachita ena, komatu tidandaulirane, ndiko koposa monga momwe muona tsiku lilikuyandika.” Inde, kuphunzira ndi kufufuza m’mabuku kwa munthu payekha n’kofunika, komanso kusonkhana pamodzi ndi ena kumakhala kolimbikitsa: “Chitsulo chinola chitsulo; chomwecho munthu anola nkhope ya mnzake.”—Ahebri 10:24, 25; Miyambo 27:17.

A Mboni amagwiritsanso ntchito mipata yokambirana za uthenga wabwino pamene alankhulana ndi anthu m’moyo wawo wa tsiku ndi tsiku. Mwina kungakhale kucheza pang’ono ndi mnansi wawo kapena wapaulendo mnzawo m’basi kapena m’ndege. Mwinanso kungakhale kukambirana kotalikirapo ndithu ndi bwenzi lawo kapena wachibale, kapenanso pocheza ndi mnzawo wa kuntchito popuma masana. Umboni wochuluka umene Yesu anachita pamene anali padziko lapansi unali wa mtundu umenewu—poyenda m’mphepete mwa nyanja, pokhala pansi m’mbali mwa phiri, pachakudya kunyumba ya winawake, kuphwando la ukwati, kapena paulendo wa m’ngalawa ya asodzi pa Nyanja ya Galileya. Iye anaphunzitsa m’masunagoge ndi pakachisi ku Yerusalemu. Kulikonse kumene anali, anapeza mipata yolankhula za Ufumu wa Mulungu. Mboni za Yehova zimayesetsa kutsatira mapazi ake pankhani imeneyinso.—1 Petro 2:21.

KULALIKIRA MWA KUPEREKA CHITSANZO

Palibe iliyonse ya njira zokuuzirani uthenga wabwino zimenezi imene ingakhale yatanthauzo kwa inu ngati wokuuzaniyo sagwiritsa ntchito zimene amaphunzitsa. Kunena zinthu zosemphana ndi zimene umachita ndiko chinyengo, ndipo chinyengo chachipembedzo chapangitsa mamiliyoni a anthu kukana Baibulo. Koma si koyenera kupatsa mlandu Baibulo. Alembi ndi Afarisi anali ndi Malemba Achihebri, koma Yesu anawatsutsa ndi kuwatcha onyenga. Iye analankhula za kuŵerenga kwawo Chilamulo cha Mose, ndiyeno anati kwa ophunzira ake: “Zinthu zilizonse zimene iwo akauza inu, chitani nimusunge; koma musatsanza ntchito zawo; pakuti iwo amalankhula, koma samachita.” (Mateyu 23:3) Chitsanzo chabwino cha Mkristu cha khalidwe labwino chimakhudza ena kwambiri kuposa ulaliki wapakamwa. Zimenezi zinatchulidwa kwa akazi okhala ndi amuna osakhulupirira: “Akakodwe opanda mawu mwa mayendedwe a akazi; pakuona mayendedwe anu oyera.”—1 Petro 3:1, 2.

Chotero, a Mboni za Yehova amayesa kulengeza uthenga wabwino kwa ena mwa njira imeneyinso: mwa kukhala chitsanzo chabwino m’khalidwe lawo lachikristu limene amalalikira kwa ena. Amayesa ‘kuchitira ena zimene akafuna kuti anthu awachitire iwo.’ (Mateyu 7:12) Amayesa kukhala mwa njira imeneyi kwa anthu onse, osati chabe kwa Mboni zinzawo, mabwenzi awo, anansi awo, kapena achibale awo okha ayi. Pokhala anthu opanda ungwiro, si kuti nthaŵi zonse amachita bwino ayi. Koma ndi cholinga chawo cha mtima wonse kuti achitire anthu onse zabwino, osati chabe powauza za uthenga wabwino wa Ufumu komanso powathandiza m’mbali iliyonse imene angathe.—Yakobo 2:14-17.

[Chithunzi patsamba 19]

Hawaii

[Chithunzi patsamba 19]

Venezuela

[Chithunzi patsamba 19]

Yugoslavia

[Zithunzi patsamba 20]

Nyumba za Ufumu, zomangidwa bwino, zili malo ophunzirirako Baibulo

[Zithunzi patsamba 21]

M’moyo wawo wa banja, limodzinso ndi pochita zinthu ndi anthu ena, a Mboni amayesetsa kuchita moona mtima zinthu zimene amalalikira kwa ena

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena