Mukhoza Kunola Luso Lanu Lokumbukira Zinthu
YEHOVA MULUNGU polenga ubongo wa munthu anaikamo luso lodabwitsa lokumbukira zinthu. Anaukonza ngati nkhokwe yoti n’kutapamo koma zinthu zamtengo wapatali zoikidwa mmenemo osathamo ayi. Ubongo unapangidwa mogwirizana ndi cholinga cha Mulungu chakuti anthu akhale ndi moyo kosatha.—Sal. 139:14; Yoh. 17:3.
Koma mwina inu mumaona kuti zambiri zimene mumaika mu ubongo wanu zimatayika. Mukazifuna zimaiŵalika. Kodi mungatani kuti munole luso lanu lokumbukira zinthu?
Khalani ndi Chidwi
Chidwi ndi chinthu chofunika kwambiri pofuna kunola luso lokumbukira zinthu. Ngati tikhala ndi chizoloŵezi chokhala watcheru, kukhala ndi chidwi pa anthu ndi zinthu zimene zikuchitika, maganizo athu amakhala okangalika. Tikamatero, tizilabadira mwachidwi pamene tikuŵerenga kapena kumva kanthu kena ka phindu lokhalitsa.
N’chosadabwitsa ngati munthu wina ali ndi vuto losakumbukira mayina a anthu. Komabe, monga Akristu, timadziŵa kuti anthu ndi ofunika kwambiri—inde, Akristu anzathu, komanso aja amene timawalalikira, ndi enanso amene timachita nawo zinthu zofunika pa moyo wa tsiku ndi tsiku. Kodi n’chiyani chingatithandize kukumbukira mayina ofunika kwambiri kwa ife? Mtumwi Paulo anatchula mayina a anthu 26 a mpingo umene analembera kalata. N’zoonekeratu kuti anali ndi chidwi pa iwo chifukwa sanangodziŵa mayina awo, koma anatchulanso mbali zina za moyo wa ambiri mwa amenewo. (Aroma 16:3-16) Ena mwa oyang’anira oyendayenda a Mboni za Yehova a lerolino amakumbukira kwambiri mayina a anthu, ngakhale kuti amasintha mpingo mlungu uliwonse. Kodi chimawathandiza ndi chiyani? Ayenera kuti amakhala ndi chizoloŵezi chotchula dzina la munthu kaŵirikaŵiri pamene alankhula naye koyamba. Amachita khama logwirizanitsa dzina la munthu ndi nkhope yake. Komanso, amatsagana ndi anthu osiyanasiyana mu utumiki wa kumunda ndi kukhalira nawo limodzi pachakudya. Pamene mukumana ndi munthu wina, kodi mudzakumbukira dzina lake? Choyamba khalani ndi chifukwa chabwino chofuna kukumbukirira dzina lake; kenako yesani njira zomwe tatchulazo.
N’kofunikanso kukumbukira zimene mumaŵerenga. N’chiyani kodi chingakuthandizeni kuchita bwino pambali imeneyi? Zinthu ziŵiri n’zofunikira, chidwi ndi kumvetsa. Muyenera kukhala ndi chidwi pa zimene mukuŵerenga kuti maganizo anu onse azikike pa zimenezo. Simungathe kusunga zinthu ngati maganizo anu apita kwina pamene mukuŵerenga. Mungathe kumvetsa bwino zimene mukuŵerenga ngati muzigwirizanitsa ndi zinthu zimene mukuzidziŵa kale. Poŵerenga muzidzifunsa kuti: ‘Kodi ndi motani ndipo ndi liti pamene ndingagwiritse ntchito mfundozi pamoyo wanga? Kodi ndingazigwiritse ntchito motani pothandiza wina?’ Luso la kumvetsa zinthu limakulanso ngati muŵerenga mawu angapo nthaŵi imodzi, m’malo mwa liwu limodzilimodzi. Mukatero, muzimvetsa malingaliro mwamsanga ndi kuzindikira mfundo zazikulu, moti zizikumbukika mosavuta.
Khalani ndi Nthaŵi Yobwereza M’maganizo Zimene Mwaŵerenga
Akatswiri a maphunziro amanenetsa kuti kubwereza mwamaganizo n’kofunika kwambiri. Pakafukufuku wina, pulofesa wa pa koleji anaonetsa kuti kubwereza mwamsanga m’maganizo kwa mphindi imodzi chabe kumaŵirikiza zimene munthu angathe kukumbukira. Choncho, mutangotsiriza kuŵerenga nkhani, kapena mbali ya nkhani, m’maganizo mwanu bwerezani mfundo zazikulu kuti zikhomerezeke. Ganizirani mmene mungafotokozere m’mawu anu mfundo zatsopano zimene mwaphunzira. Mwa kuyesa kukumbukira mfundo mutangotha kuziŵerenga, mumatalikitsa nthaŵi imene mungazikumbukire mfundozo.
Ndiyeno patapita masiku angapo, yesani kupeza mpata wakuti mukumbukirenso zimene munaŵerenga mwa kuzifotokozera munthu wina. Mukhoza kuchita zimenezo kwa wina wa pabanja panu, wa mumpingo, mnzanu wa kuntchito, mnzanu wa kusukulu, wokhala naye pafupi, kapena munthu amene munakumana naye mu utumiki wa kumunda. Yesani kubwereza osati mfundo zazikulu zokha komanso malingaliro a m’Malemba amene akukhudza mfundozo. Kuchita zimenezi kudzakupindulitsani inuyo, kukuthandizani kukhomereza zinthu zofunika m’chikumbumtima chanu; kudzapindulitsanso ena.
Sinkhasinkhani Zinthu Zofunika
Kuwonjezera pa kubwereza mwamaganizo zimene munaŵerenga ndi kuuzako anthu ena, mudzaona kuti kusinkhasinkha zinthu zofunika zimene munaphunzira n’kopindulitsa. N’zimene olemba Baibulo, Asafu ndi Davide, anachita. Asafu anati: ‘Ndidzakumbukira zimene adazichita Ambuye; Inde, ndidzakumbukira zodabwitsa zanu zoyambira kale. Ndipo ndidzalingalira ntchito yanu yonse, ndi kulingalirabe zimene munazichita Inu.’ (Sal. 77:11, 12) Davidenso analemba kuti: ‘Ndilingalira za Inu mawulonda a usiku,’ natinso ‘ndikumbukira masiku a kale lomwe; zija mudazichita ndilingirirapo.’ (Sal. 63:6; 143:5) Kodi inunso mumatero?
Kulingalira kozama koteroko pa ntchito za Yehova, makhalidwe ake, ndi njira zimene wasonyezera chifuniro chake kumapindulitsa m’njira zambiri, kuwonjezera pa kuthandiza kukumbukira mfundo zofunika. Ngati mukhala ndi chizoloŵezi cha kulingalira motero, mudzakhomereza zinthu zofunika kwenikweni mumtima mwanu. Kudzakuthandizani kuumba munthu wabwino wam’kati. Zimene zidzakhala m’chikumbumtima mwanu zidzasonyeza malingaliro anu enieni am’katikati.—Sal. 119:16.
Mmene Mzimu Woyera Umathandizira
Pankhani yokumbukira mfundo za choonadi zokhudza ntchito za Yehova ndi zinthu zimene Yesu Kristu analankhula, sitili opanda chithandizo. Usiku wa tsiku limene Yesu anafa, anauza otsatira ake kuti: “Izi ndalankhula nanu, pakukhala ndi inu. Koma Nkhosweyo, Mzimu Woyera, amene Atate adzam’tuma m’dzina langa, Iyeyo adzaphunzitsa inu zonse, nadzakumbutsa inu zinthu zonse zimene ndinanena kwa inu.” (Yoh. 14:25, 26) Mateyu ndi Yohane analipo pamenepo. Kodi mzimu woyera unawathandizadi? Inde unatero! Patapita zaka ngati zisanu ndi zitatu, Mateyu anatsiriza kulemba nkhani yoyamba yofotokoza moyo wa Kristu, kuphatikizapo zochitika zamtengo wapatali zosaiŵalika ngati Ulaliki wa pa Phiri ndi chizindikiro cha mbali zambiri chosonyeza kukhalapo kwa Kristu ndi chimaliziro cha dziko lino. Patapita zaka 65 kuchokera pa imfa ya Yesu, mtumwi Yohane analemba Uthenga Wabwino, kuphatikizapo zimene Yesu ananena usiku womaliza umene atumwiwo anali ndi Ambuyeyo asanamwalire. Mosakayika, onse aŵiri Mateyu ndi Yohane anali kukumbukira bwino lomwe zimene Yesu ananena ndi kuchita pamene anali nawo, koma mzimu woyera unawathandiza kwambiri kuti asaiŵale mfundo zofunika zimene Yehova anafuna kuti zikhale m’Mawu ake olembedwa.
Kodi mzimu woyera umatumikirabe monga mthandizi wa atumiki a Mulungu lerolino? Mosakayikira konse, umatero! N’zoona kuti mzimu woyera suika m’maganizo mwathu zinthu zimene sitinaphunzirepo, koma umatithandiza kukumbukira zinthu zofunika zimene tinaphunzira m’mbuyomu. (Luka 11:13; 1 Yoh. 5:14) Ndiyeno, pamene kukhala kofunikira, luso lathu la kulingalira limalimbikitsidwa kuti ‘tikumbukire mawu onenedwa kale ndi aneneri oyera, ndi lamulo la Mbuye ndi Mpulumutsi.’—2 Pet. 3: 1, 2.
‘Musamaiŵale’
Yehova anachenjeza Israyeli mobwerezabwereza kuti: ‘Musamaiŵale.’ Si kuti iye anawayembekezera kukumbukira bwino lomwe chinthu china chilichonse ayi. Koma iwo sanayenera kutanganidwa kwambiri ndi zinthu zaumwini moti n’kuiŵala zimene Yehova anawachitira m’mbuyomo. Anafunikira kukumbukirabe mmene Yehova anawapulumutsira pamene mngelo wake anapha ana achisamba onse mu Igupto, ndi pamene Yehova analekanitsa Nyanja Yofiira kuti iwo awoloke, koma anamiza m’madzi Farao limodzi ndi gulu lake lankhondo. Aisrayeliwo anafunikira kukumbukira kuti Mulungu anawapatsa Chilamulo chake pa phiri la Sinai ndi kuti ndiye anawatsogolera m’chipululu mpaka kukawaloŵetsa m’Dziko Lolonjezedwa. Anayenera kusaiŵala m’lingaliro lakuti kukumbukira kwawo zinthuzo kunayenera kuwathandiza pamoyo wawo wa tsiku ndi tsiku.—Deut. 4:9, 10; 8:10-18; Eks. 12:24-27; Sal. 136:15.
Ifenso tiyenera kusamala kuti tisamaiŵale. Pamene tikulimbana ndi zovuta za moyo, tifunikira kukumbukira Yehova, kukumbukira kuti ali Mulungu wa mtundu wanji, ndi chikondi chimene anasonyeza mwa mphatso ya Mwana wake, amene anapereka dipo kaamba ka machimo athu kuti tikapeze moyo wosatha wangwiro. (Sal. 103:2, 8; 106:7, 13; Yoh. 3:16; Aroma 6:23) Kuŵerenga Baibulo nthaŵi zonse ndi kutenga mbali mokangalika pamisonkhano yampingo ndi mu utumiki wa kumunda kudzatithandiza kumakumbukira nthaŵi zonse mfundo za choonadi zamtengo wapatali zimenezo.
Pamene mufunikira kupanga zosankha, zazikulu kapena zazing’ono, kumbukirani mfundo za choonadi zimenezo, ndipo lolani kuti zilimbikitse kalingaliridwe kanu. Musamaiŵale ayi. Dalirani Yehova kuti akutsogolereni. M’malo moona zinthu ndi maso aumunthu kapena kungodalira zofuna za mtima wopanda ungwiro, dzifunseni kuti, ‘Kodi ndi uphungu wotani kapena mfundo ya makhalidwe abwino ya m’Mawu a Mulungu iti imene iyenera kundithandiza kupanga chosankha?’ (Miy. 3:5-7; 28:26) N’zosatheka kuti mukumbukire zinthu zimene simunaŵerengepo kapena kumvapo. Koma pamene mukula m’nzeru za choonadi ndi m’chikondi kwa Yehova, nkhokwe ya nzeru imene mzimu wa Mulungu ungamakuthandizeni kutapamo zinthu pozikumbukira idzakula, ndipo chikondi chanu pa Yehova chokulirakulirabe chidzakulimbikitsani kuchita zinthu mogwirizana nacho.