Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • be tsamba 33-tsamba 38 ndime 4
  • Mmene Mungafufuzire

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mmene Mungafufuzire
  • Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kugwiritsa Ntchito Baibulo Monga Chida Chathu Chachikulu Chofufuzira
  • Kuphunzira Kugwiritsa Ntchito Zida Zina Zofufuzira
  • Malaibulale Ena a Zinthu Zauzimu
  • Sungani Faelo Yanuyanu
  • Lankhulani ndi Anthu
  • Pendani Choyamba Zimene Mwapeza
  • Buku Lothandiza Kufufuza Nkhani
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2014
  • ‘Kufunafuna Mawu Okondweretsa, Mawu Owongoka’
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Kodi Laibulale ya pa Nyumba ya Ufumu Ingatithandize Bwanji?
    Kodi Ndani Akuchita Chifuniro cha Yehova Masiku Ano?
  • Mmene Mungalinganizire Laibulale Yateokratiki
    Nsanja ya Olonda—1994
Onani Zambiri
Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
be tsamba 33-tsamba 38 ndime 4

Mmene Mungafufuzire

MFUMU SOLOMO “anatchera makutu nafunafuna nalongosola miyambi yambiri.” Chifukwa chiyani? Chifukwa anali ndi chidwi cholemba ‘zowongoka ndi mawu oona.’ (Mlal. 12:9, 10) Luka nayenso ‘analondalonda mosamalitsa zinthu zonse kuyambira pachiyambi’ kuti afotokoze zochitika m’moyo wa Kristu momveka bwino. (Luka 1:3) Atumiki a Mulungu aŵiriŵa anali kufufuza.

Kodi kufufuza n’kutani? Ndiko kufunafuna mosamalitsa mfundo za nkhani. Kumaphatikizapo kuŵerenga, ndiponso kumafuna kugwiritsa ntchito malangizo a kafufuzidwe. Kungaphatikizeponso kufunsira kwa anthu ena.

Kodi ndi zochitika ziti zimene zimafuna kufufuza? Nazi zitsanzo zingapo. Phunziro lanu laumwini kapena kuŵerenga kwanu Baibulo kungadzutse mafunso ofunikira m’maganizo mwanu. Munthu wina amene mungam’lalikire angakufunseni funso limene mungafune kudzaperekapo yankho lachindunji. Mwinanso mungapatsidwe nkhani yoti mukakambe.

Pendani nkhani imene mwapatsidwa kukaikambayo. Mwina nkhaniyo ndi yokhudza mbali zambiri. Kodi mungaikonze motani kuti igwirizane ndi mikhalidwe ya kwanuko. Ikonzeni bwino mwa kuchita kafukufuku. Mutaloŵetsapo chochitika chimodzi kapena ziŵiri, kapena chitsanzo chogwirizana bwino ndi nkhani yanuyo komanso chokhudza miyoyo ya omvera, mfundo imene poyamba ingaoneke ngati yachidziŵikire ingakhale ndi mbali zapadera, ngakhalenso zolimbikitsa. Mwina nkhani imene mukuikonzekerayo anailembera aŵerengi a padziko lonse, koma inuyo muyenera kuitambasula, kuloŵetsapo zitsanzo, ndi kuonetsa mmene mfundozo zingagwirire ntchito pampingo umodzi kapena kwa munthu mmodzi. Kodi muyenera kuyambira pati?

M’malo mongothamangira kufufuza, lingalirani kaye za omvera anu. Kodi zomwe akuzidziŵa kale ndi zotani? Kodi ndi zotani zimene afunikira kuti adziŵe? Ndiyeno pezani cholinga chanu. Kodi ndicho kufotokozera nkhani omvera? kapena kuwakhutiritsa? kapena kutsutsa nkhani ina? kapena kuwalimbikitsa? Kufotokozera nkhani kumafuna kupereka mfundo zomveketsa bwino nkhaniyo. Ngakhale kuti mfundo zazikulu zingamveke bwinobwino, mungafunikirebe kumveketsa bwino za pamene ndi mmene angachitire zimene mukunenazo. Kukhutiritsa omvera kumafuna kufotokoza zifukwa zake chinthu chilili choncho, komanso kupereka umboni wake. Kutsutsa nkhani kumafuna kudziŵa bwino mbali zonse ziŵiri za nkhaniyo ndi kupenda mosamala umboni woperekedwawo. Inde, sitimangofuna kupereka zifukwa zamphamvu ayi, komanso timafuna kupeza njira zofotokozera mfundo zathu mokoma mtima. Kulimbikitsa kumaphatikizapo kufika munthu pamtima. Kumatanthauza kukopa omvera anu ndi kuwapangitsa kulakalaka kuchita zimene mukufotokoza. Zitsanzo zenizeni za anthu amene anatsatira njira imeneyo, ngakhale anakumana ndi mavuto, zingathandize kuwafika pamtima omvera.

Kodi mwakonzeka tsopano kuti muyambe kufufuza? Osati kwenikweni. Lingalirani kuti ndi mfundo zochuluka motani zimene mukufuna kupeza. Chinthu chinanso chofunika kuchiganizira ndicho nthaŵi. Ngati mukakamba nkhaniyo kwa anthu ena, kodi mukayenera kuikamba m’mphindi zingati? Mphindi 5? Mphindi 45? Kodi nthaŵiyo ndi yoikidwiratu, muja zimakhalira pamsonkhano wampingo, kapena mwina ikhoza kusintha, ngati pa phunziro la Baibulo kapena pa ulendo waubusa?

Chomalizira, ndi zida zofufuzira zotani zimene muli nazo? Kuwonjezera pa zomwe muli nazo panyumba, kodi zilipo zina mu laibulale ya pa Nyumba ya Ufumu? Kodi abale omwe akhala akutumikira Yehova zaka zambiri angakuloleni kugwiritsa ntchito zida zawo zofufuzira? Kodi kwanuko kuli laibulale ya onse kumene mungakaŵerenge mabuku ofufuzamo?

Kugwiritsa Ntchito Baibulo Monga Chida Chathu Chachikulu Chofufuzira

Ngati zimene mukufunazo zikukhudza tanthauzo la lemba, yambani ndi Baibulo lenilenilo.

Pendani Mbali Zosiyanasiyana za Lembalo. Dzifunseni kuti: ‘Kodi mawuŵa analembera ndani? Kodi mavesi ozungulira akusonyeza kuti n’chiyani chinapangitsa kuti mawuwo alankhulidwe, kapena chimene chinachititsa anthuwo kukhala ndi maganizo otero?’ Mfundo ngati zimenezi zingatithandize kumvetsa lemba, ndiponso zimachititsa nkhani imene mungakambe kukhala yogwira mtima.

Mwachitsanzo, Ahebri 4:12 kaŵirikaŵiri amagwidwa mawu pofuna kusonyeza mphamvu ya Mawu a Mulungu kuti amagwira mtima ndi kusintha miyoyo ya anthu. Mbali zina zokhudza lembalo zimatithandiza kuzindikira mozama mfundo imeneyo. Mbali zinazo zimatchula zimene Aisrayeli anakumana nazo pazaka 40 zimene anathera m’chipululu asanaloŵe m’dziko limene Yehova analonjeza Abrahamu. (Aheb. 3:7–4:13) “Mawu a Mulungu,” kapena kuti lonjezo lake lokawaloŵetsa m’dziko la mpumulo malinga ndi pangano limene anapangana ndi Abrahamu, sanafe ayi; anali amoyobe ndipo amapita kokakwaniritsidwa. Aisrayeliwo anali ndi zifukwa zokwanira zoti akhulupirire mawuwo. Komabe, pamene Yehova anali kuwatsogolera kuchokera ku Igupto kupita ku phiri la Sinai, kupitirira mpaka kufika pafupi ndi Dziko Lolonjezedwa, iwo anam’pandukira mobwerezabwereza. Choncho, mmene anachitira ndi njira imene Mulungu anakwaniritsira mawu ake kunavumbula zimene zinali m’mitima yawo. Lerolinonso, lonjezo la mawu a Mulungu limavumbula zimene zili m’mitima ya anthu.

Ŵerengani Malemba Owonjezera. Mabaibulo ena ali ndi malemba owonjezera m’madanga apakati. Kodi lanulo lili nawo? Ngati lili nawo, angakuthandizeni. Taonani chitsanzo m’Baibulo lachingelezi lotchedwa New World Translation of the Holy Scriptures. Petro Woyamba 3:6 amasonyeza kuti Sara ndi chitsanzo chabwino chimene akazi achikristu ayenera kutengera. Lemba lowonjezera la m’danga lapakati la Genesis 18:12 limachirikiza mfundo imeneyo mwa kusonyeza kuti Sara anatcha Abrahamu kuti ambuye “m’mtima mwake.” Mfundo yake pamenepo ndi yakuti, kudzichepetsa kwake kunali kochokera pansi pa mtima. Kuwonjezera pa kukudziwitsani mfundo zoterozo, malemba owonjezerawo angakulozereni malemba oonetsa kukwaniritsidwa kwa ulosi wa Baibulo kapena chitsanzo cha pangano la Chilamulo. Komabe, dziŵani kuti malemba ena owonjezera cholinga chawo si kupereka malongosoledwe ngati amenewo. Iwo amangosonyeza malingaliro ofananako kapena mfundo zokhudza mbiri ya munthu kapena malo.

Fufuzani mwa Kugwiritsa Ntchito Namlozera wa Baibulo. Namlozera wa Baibulo ndi ndandanda ya mawu a m’Baibulo osanjidwa m’dongosolo la alifabeti. Akhoza kukuthandizani kupeza malemba okhudzana ndi nkhani imene mukuifufuza. Pamene muwapenda malembawo, mudzaphunziranso mbali zina zothandiza. Mudzaona umboni wa kugwirizana kwa mawu a choonadi chopezeka m’Mawu a Mulungu. (2 Tim. 1:13) Baibulo la New World Translation, chakumapeto kwake, lili ndi ndandanda ya mawu a m’Baibulo. M’Chicheŵa, anamlozera ngati uja wopezeka chakumapeto kwa buku la Kukambitsirana za m’Malemba angakhale othandiza pa kufufuza kwanu.

Kuphunzira Kugwiritsa Ntchito Zida Zina Zofufuzira

Bokosi la patsamba 33 lili ndi mndandanda wa zida zina zofufuzira zimene “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” wapereka. (Mat. 24:45-47) Zambiri mwa zidazo zili ndi ndandanda ya zam’kati, ndipo zambiri zili ndi namlozera kumapeto kwake woti akuthandizeni kupeza mfundo. Pakutha kwa chaka chilichonse, mlozera nkhani amalembedwa mu Nsanja ya Olonda ndi mu Galamukani! amene amasanja nkhani zonse za chakacho.

Kudziŵa mitundu ya nkhani zimene zimapezeka m’zofalitsa zophunzirira Baibulo kungatithandize kupeza msanga zomwe tikufufuzazo. Mwachitsanzo, tinene kuti mukufuna mudziŵe za ulosi, chiphunzitso, khalidwe lachikristu, kapena mmene mfundo za makhalidwe abwino za m’Baibulo zimagwirira ntchito. Kaŵirikaŵiri, zimenezo zimapezeka mu Nsanja ya Olonda. Galamukani! imafotokoza zochitika za tsiku ndi tsiku, mavuto apanthaŵiyo, chipembedzo, sayansi, ndi anthu a m’mayiko osiyanasiyana. Mafotokozedwe okhudza imodzi ndi imodzi ya nkhani za Uthenga Wabwino m’dongosolo la zaka amapezeka m’buku lakuti Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako. Mafotokozedwe a vesi ndi vesi a mabuku athunthu a m’Baibulo amapezeka m’zofalitsa ngati Revelation—Its Grand Climax At Hand!, Samalani Ulosi wa Danieli!, ndi buku la magawo aŵiri lakuti Ulosi wa Yesaya—Muuni wa Anthu Onse. M’buku la Kukambitsirana za m’Malemba, mudzapeza mayankho okhutiritsa pa mafunso ambiri okhudza Baibulo amene anthu ochuluka amafunsa mu utumiki wa kumunda. Pofuna kumvetsa za zipembedzo zina, ziphunzitso zawo, ndi mbiri yawo, onani buku lakuti Mankind’s Search for God. Mbali zina za mbiri yamakono ya Mboni za Yehova zikupezeka m’bulosha lakuti Mboni za Yehova—Zikuchita Chifuniro cha Mulungu Mogwirizana pa Dziko Lonse Lapansi. Kuti mudziŵe mmene ntchito yolalikira uthenga wabwino padziko lonse yakhala ikuyendera, onani Nsanja ya Olonda yaposachedwa ya January 1. Buku lakuti Insight on the Scriptures limafotokoza mbali zosiyanasiyana zokhudza anthu, malo, zinenero, kapena zochitika zakale za m’Baibulo. Lilinso ndi mapu osiyanasiyana a malo otchulidwa m’Baibulo.

Namlozera Wotchedwa “Watch Tower Publications Index.” Namlozera ameneyu, wofalitsidwa m’zinenero zopitirira 20, adzakulozerani nkhani m’zofalitsa zathu zosiyanasiyana. Ali ndi magawo aŵiri, mlozera mawu ndi mlozera malemba. Kuti mugwiritse ntchito mlozera mawu, pezani mawu okhudza nkhani imene mukufuna kuifufuza. Kuti mugwiritse ntchito mlozera malemba, pezani pa mndandanda wa malemba, lemba limene mukufuna kulimvetsa bwino. Ngati mfundo ina inafalitsidwa m’chinenero chanu pankhani imeneyo kapena lembalo m’kati mwa zaka za namlozerayo, mudzapeza mndandanda wa zofalitsa zimene mungafufuzemo. Yang’anani pa mndandanda wa zizindikiro za mabuku kumayambiriro kwa namlozerayo kuti mudziŵe mayina a zofalitsazo. (Mwachitsanzo, mungadziŵe kuti w99 3/1 15, ndi Nsanja ya Olonda ya 1999, March 1, tsamba 15.) Mitu yaikulu, monga wakuti “Field Ministry Experiences (Zokumana Nazo mu Utumiki Wakumunda),” ndi wakuti “Life Stories of Jehovah’s Witnesses (Mbiri za Moyo wa Mboni za Yehova),” ingakhale yothandiza pokonzekera nkhani zolimbikitsa mpingo.

Popeza kufufuza nkhani kumatenga maganizo kwambiri, samalani kuti musaloŵerere ku nkhani zina. Zikani maganizo anu pacholinga chofufuza mfundo zofunikira pankhani imene mukuŵerenga. Ngati namlozerayo akukusonyezani gwero lakutilakuti, pitani ku masamba osonyezedwawo, kenako gwiritsani ntchito mitu yaing’ono ndi masentensi (ziganizo) otsegulira ndimezo kuti mupeze mfundo zimene mukufuna. Ngati chimene mukufufuzacho ndi tanthauzo la lemba la m’Baibulo, choyamba pezani lembalo patsamba limene mwapatsidwa. Kenako pendani mawu ozungulira lembalo.

Laibulale ya pa CD yotchedwa “Watchtower Library.” Ngati muli ndi kompyuta, mungakhale ndi mwayi wogwiritsa ntchito laibulale ya pa CD imeneyi, imene ili ndi zofalitsa zathu zambiri. Njira yake yofufuzira ndi yosavuta, ndipo mukhoza kupeza liwu limodzi, mawu ogwirizana, kapena lemba m’chofalitsa chilichonse cha mu Laibulale imeneyi. Ngati chida chofufuzirachi mulibe m’chinenero chanu, mukhoza kupindula nacho m’chinenero chachikulu cholankhulidwa m’mayiko ambiri chimene mumadziŵa.

Malaibulale Ena a Zinthu Zauzimu

M’kalata yake youziridwa yachiŵiri kwa Timoteo, Paulo anam’pempha mnyamatayo ‘kudza ndi mabuku, makamaka zikopa,’ ku Roma. (2 Tim. 4:13) Paulo anasunga zolemba zina zimene anaziona kukhala zofunika kwambiri. Inunso mukhoza kutero. Kodi mumasunga makope anu a Nsanja ya Olonda, Galamukani!, ndi Utumiki Wathu wa Ufumu ngakhale kuti munawaphunzira kale pamisonkhano yampingo? Ngati mumachita zimenezo, adzakhala zida zanu zofufuzira, kuphatikizapo zofalitsa zina zachikristu zimene muli nazo. Mipingo yambiri imasunga zofalitsa zauzimu m’laibulale ya pa Nyumba ya Ufumu. Zofalitsazi ndi zogwiritsa ntchito onse pampingo, pamene ali pa Nyumba ya Ufumu.

Sungani Faelo Yanuyanu

Khalani atcheru ku nkhani zochititsa chidwi zimene mungagwiritse ntchito polankhula ndi pophunzitsa. Ngati mupeza m’nyuzipepala kapena m’magazini nkhani yofunika, ziŵerengero zofunika, kapena chitsanzo chimene mungagwiritse ntchito mu ulaliki, dulani mbali yofunikayo, kapena pangani fotokope. Lembanipo deti, dzina la magaziniyo, mwinanso dzina la wolemba wake. Pa misonkhano yampingo, lembani mfundo ndi zitsanzo zimene zingakuthandizeni kufotokozera ena choonadi. Kodi munaganizapo za chitsanzo china chabwino, koma panthaŵiyo mulibe mwayi woti muchigwiritse ntchito? Chilembeni, ndipo chisungeni m’faelo yanu. Mukakhala mu Sukulu ya Utumiki wa Mulungu kwa nthaŵi yotalikirapo, mumakonzekera nkhani zochuluka. M’malo motaya mfundo zimene mumalemba, zisungeni. Kufufuza kumene mumachita kumadzathandiza m’tsogolo.

Lankhulani ndi Anthu

Anthu ndi gwero limene mungaphunzireko zinthu zambiri. Pamene Luka anali kulemba nkhani yake ya Uthenga Wabwino, zikuoneka kuti anasonkhanitsa mfundo zambiri mwa kufunsira kwa mboni zoona ndi maso. (Luka 1:1-4) Mkristu mnzanu akhoza kukuunikirani nkhani ina imene mukuifufuza. Malinga n’kunena kwa Aefeso 4:8, 11-16, NW, Yesu amagwiritsa ntchito “mphatso za amuna” potithandiza ‘kukula pa kuzindikira zoona zokhudza Mwana wa Mulungu.’ Tingapeze maganizo othandiza mwa kufunsira kwa aja amene atumikira Mulungu zaka zambiri. Kukambirana ndi anthu kungaonetsenso zimene amalingalira, ndipo zimenezo zingakuthandizeni kukonza nkhani yogwira mtima kwambiri.

Pendani Choyamba Zimene Mwapeza

Anthu pokolola tirigu, amachotsako mankhusu kuti maso a tirigu akhale okha. Chimodzimodzinso zimene mumapeza pa kufufuza kwanu. Musanazigwiritse ntchito, choyamba lekanitsani zofunika ndi zosafunika.

Mukapeza mfundo zoti mukagwiritse ntchito m’nkhani yanu, choyamba dzifunseni kuti: ‘Kodi mfundo imene ndikufuna kukagwiritsa ntchitoyi, ikathandiza nkhani yanga kukhala yogwira mtima? Kapena, ngakhale kuti ndi mfundo yosangalatsa, kodi ikachotsa maganizo a omvera pa nkhani imene ndizikakamba?’ Ngati mukuganiza zokaphatikizamo zochitika zapanthaŵiyo, kapena mfundo zochokera m’nkhani zasayansi kapena zamankhwala zimene zimasintha nthaŵi zonse, tsimikizani kuti mfundozo n’zatsopano. Kumbukiraninso kuti mfundo zina m’zofalitsa zathu za m’mbuyo zimasintha, choncho pezani zimene zafalitsidwa posachedwa pankhaniyo.

Ngati mukufuna kusonkhanitsa mfundo kuchokera ku magwero a kudziko, m’pofunika kusamala kwambiri. Musaiŵale konse kuti Mawu a Mulungu ndi choonadi. (Yoh. 17:17) Yesu akuchita mbali yaikulu pa kukwaniritsidwa kwa chifuniro cha Mulungu. Ndiye chifukwa chake Akolose 2:3 amati: “Zolemera zonse za nzeru ndi chidziŵitso zibisika mwa iye.” Kumbukirani mfundo imeneyo pamene mukupenda zimene mwapeza pa kufufuza kwanu. Ponena za kufufuza ku magwero a kudziko, dzifunseni kuti: ‘Kodi nkhani imeneyi ikukokomeza zinthu, kodi ndi nkhambakamwa chabe, kapena kodi ikunena zapamwamba zokha? Kodi inalembedwa ndi cholinga chadyera kapena chongofuna kupeza malonda? Kodi magwero ena odalirika amavomereza zimenezo? Choposa zonse, kodi imagwirizana ndi choonadi cha Baibulo?’

Pa Miyambo 2:1-5 akutilimbikitsa kufunafuna nzeru mosalekeza, kufunafuna kuzindikira ‘ngati siliva, ndi ngati chuma chobisika.’ Zimenezo zimatanthauza kuti pamenepo pali thukuta, komanso mapindu. Kufufuza ndi ntchito, koma kudzakuthandizani kudziŵa malingaliro a Mulungu pankhani zosiyanasiyana, kuwongolera maganizo olakwa, ndi kumvetsa bwino choonadi. Nkhani zanu zizikhalanso ndi umboni komanso zaumoyo. Zikatero zidzakusangalatsani pokamba komanso zidzamveka zokoma kwa omvera.

PA ZIDA ZOFUFUZIRA IZI, NDI ZITI ZIMENE MULI NAZO?

  • Baibulo la New World Translation of the Holy Scriptures

  • Namlozera wotchedwa Comprehensive Concordance

  • Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!

  • Kukambitsirana za m’Malemba

  • Buku lakuti Jehovah’s Witnesses—Proclaimers of God’s Kingdom

  • Buku la Insight on the Scriptures

  • Namlozera wotchedwa Watch Tower Publications Index

  • Laibulale ya pa CD yotchedwa Watchtower Library

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena