PHUNZIRO 1
Kuŵerenga Molondola
MALEMBA amati cholinga cha Mulungu n’chakuti anthu a mitundu yonse ‘afike pozindikira choonadi.’ (1 Tim. 2:4) Mogwirizana ndi zimenezo, pamene tiŵerenga Baibulo mokweza, cholinga chathu chomveketsa chidziŵitso cholondola chiyenera kulimbikitsa kaŵerengedwe kathu.
Luso la kuŵerenga mokweza m’Baibulo ndi mabuku ena ofotokoza za m’Baibulo n’lofunika kwa achichepere ndi achikulire omwe. Monga Mboni za Yehova, tili ndi udindo wouza ena za Yehova ndi njira zake. Zimenezo kaŵirikaŵiri zimachitika mwa kuŵerengera munthu mmodzi kapena gulu la anthu. Timakhalanso ndi kuŵerenga kotero m’banja. Mu Sukulu ya Utumiki wa Mulungu, abale ndi alongo, achinyamata ndi achikulire, amakhala ndi mwayi wolandira malangizo owathandiza kupititsa m’tsogolo kaŵerengedwe kawo.
Kuŵerengera ena Baibulo mokweza, kaya munthu mmodzi kapena mpingo, ndi chinthu chofunika kwambiri. Baibulo linauziridwa ndi Mulungu. Komanso, “mawu a Mulungu ali amoyo, ndi ochitachita, . . . nazindikiritsa zolingirira ndi zitsimikizo za mtima.” (Aheb. 4:12) Mawu a Mulungu ali ndi chidziŵitso cha mtengo wapatali chosapezeka ku gwero lina lililonse. Amathandiza munthu kudziŵa Mulungu woona yekhayo ndi kupalana naye ubwenzi wabwino, ndi kukhozanso kuthana ndi mavuto a moyo. Amafotokoza njira yopezera moyo wosatha m’dziko latsopano la Mulungu. Choncho, tikhaletu ndi cholinga choŵerenga Baibulo mmene tingathere.—Sal. 119:140; Yer. 26:2.
Mmene Mungaŵerengere Molondola. N’zambiri zofunika kuti munthu aŵerenge bwino, koma kuŵerenga molondola ndiko sitepe loyamba. Kumeneko ndi kuyesetsa kuŵerenga ndendende mmene mawu awalembera. Musalumphe mawu, kutchula mawu mosamalizitsa, kapena kuŵerenga mawu molakwitsa chifukwa amaoneka ofanana ndi ena.
Kuti muŵerenge mawu molondola, mufunikira kumvetsa bwino nkhaniyo. Zimenezo zimafuna kukonzekera bwino. M’kupita kwa nthaŵi, mmene mukukulitsa luso loponya maso patsogolo ndi kuona kumene nkhaniyo ikupita, luso lanu loŵerenga molondola lidzakwera.
Zizindikiro za m’kalembedwe n’zofunika kwambiri m’chilankhulo cholemba. Zizindikirozo zingasonyeze mofunika kupuma ndi utali wa kupumako. M’zinenero zina, kulephera kusintha kamvekedwe ka mawu malinga ndi zizindikiro zawo kungasinthe funso n’kukhala ndemanga chabe, kapena kungasinthiretu tanthauzo lonse la chiganizo chonse. Komabe, nthaŵi zina zizindikirozo zimakhalapo kungotsatira galamala. M’zinenero zambiri n’kosatheka kuŵerenga molondola popanda kusamalira mingoli, ponse paŵiri yolembedwa ndi yongozindikira malinga ndi nkhaniyo. Mingoliyo imapereka mamvekedwe oyenerera a mawu. Phunzirani mmene zizindikiro za m’kalembedwe zimagwiritsidwira ntchito m’chinenero chanu. Chimenechi ndiye chinsinsi cha kaŵerengedwe katanthauzo. Kumbukirani kuti cholinga chanu ndi kumveketsa malingaliro, osati kungotchula mawu.
Kuyeseza n’kofunika kuti mupititse patsogolo luso la kuŵerenga molondola. Choyamba ŵerengani ndime imodzi yokha, kenako iŵerengeninso mobwerezabwereza kufikira mutaiŵerenga mosalakwitsa chilichonse. Ndiyeno pitani pa ndime yotsatira. Pomaliza, yesani kuŵerenga ndime zingapo popanda kulumphira, kubwereza, kapena kutchula molakwitsa mawu alionse. Mutachita zimenezo, pemphani wina kuti azikutsatirani poŵerenga ndi kunena zimene mwalakwitsa.
M’madera ena a dziko lapansi, anthu ena amakhala ndi vuto poŵerenga chifukwa cha maso osaona bwino ndi kuŵala kochepa. Ngati chithandizo chingaperekedwe pa vuto limeneli, anthuwo akhoza kumaŵerenga bwinobwino.
M’kupita kwa nthaŵi, abale omwe amaŵerenga bwino angapatsidwe mbali zoŵerenga nkhani zophunzira pa Phunziro la Buku la Mpingo ndi pa Phunziro la Nsanja ya Olonda. Koma kuti mbali imeneyi ichitike bwino, pamafunikira zoposa kungotchula mawu molondola. Kuti mukhale woŵerenga bwino pamaso pa anthu mumpingo, muyenera kukhala ndi chizoloŵezi cha kuŵerenga panokha. Zimenezi zimaphatikizapo kuzindikira kuti liwu lililonse mu sentensi lili ndi ntchito yake. N’kosatheka kumveketsa bwino tanthauzo lonse ngati mulumpha mawu ena. Ngati mulakwitsa poŵerenga mawu ena, ngakhale poŵerenga panokha, tanthauzo la sentensiyo limasokonezeka. Kulakwitsa kuŵerenga kungakhale chifukwa chosasamala zizindikiro za m’kalembedwe kapena kusamvetsa bwino nkhaniyo. Yesetsani kumvetsa tanthauzo la liwu lililonse mu sentensi. Onaninso mmene zizindikiro za m’kalembedwe zimakhudzira tanthauzo la sentensiyo. Kumbukirani kuti kaŵirikaŵiri chimene chimamveketsa malingaliro ndi gulu la mawu. Zindikirani zimenezi kuti poŵerenga mokweza muziŵerenga magulu a mawu, osati limodzilimodzi. Mwachionekere, kumvetsa zimene mukuŵerenga ndilo sitepe lofunikira kwambiri pofuna kupereka chidziŵitso cholondola pamene mukuŵerengera ena.
Anali mkulu wa chidziŵitso wa mumpingo wachikristu amene mtumwi Paulo anam’lembera kuti: “Usamalire kuŵerenga.” (1 Tim. 4:13) Mwachionekere, iyi ndi mbali imene tonsefe tingapite nayo patsogolo.