PHUNZIRO 10
Kulankhula Mwaumoyo
KULANKHULA mwaumoyo kumasonyeza mzimu wa nkhaniyo. Ngakhale kuti kukamba nkhani ya mfundo zomveka ndi kofunika, dziŵani kuti kalankhulidwe kaumoyo ndi kamene kamakopa chidwi cha omvera. Mosasamala kanthu za chikhalidwe cha kumene munakulira kapena umunthu wanu, mukhoza kudziŵa kulankhula mwaumoyo.
Lankhulani ndi Mzimu wa Nkhaniyo. Polankhula kwa mkazi wachisamariya, Yesu anati amene alambira Yehova ayenera kum’lambira “mumzimu ndi m’choonadi.” (Yoh. 4:24) Ayenera kulambira ndi mitima yoyamikira, ndi mogwirizana ndi choonadi chopezeka m’Mawu a Mulungu. Ngati munthu ali ndi kuyamikira kozama koteroko, kumaonekera m’kalankhulidwe kake. Amalakalaka kufotokozera ena zimene Yehova watigaŵira mwachikondi. Nkhope yake, manja, ndi mawu ake, zonse zimaonetsa mmene akumvera mumtima mwake.
Nanga zimatheka bwanji kuti munthu wokonda Yehova amenenso amakhulupirira zimene akunena n’kukhala wopola m’kalankhulidwe? Chifukwa chakuti sikokwanira kungokonzekera zimene akukanena. Ayeneranso kudziloŵetsa iye mwini m’nkhaniyo, iyenera kum’khudza mtima. Tinene kuti wapatsidwa nkhani yokamba za nsembe ya Yesu Kristu ya dipo. Pamene akulankhula nkhaniyo, m’maganizo mwake asangokhala ndi mfundo zokhazokha za nkhaniyo, akhalenso ndi chiyamikiro chozama pa ntchito ya nsembe ya Yesu kwa iye ndi omvera ake. Akumbukire mmene amathokozera Yehova Mulungu ndi Kristu Yesu kaamba ka makonzedwe odabwitsa ameneŵa. Afunikira kuganizira za ulemerero wa chiyembekezo cha moyo chimene nsembeyo imatheketsa kwa anthu onse—chimwemwe chosatha ndi moyo wathanzi m’paradaiso wodzabwezeretsedwa padziko lapansi! Choncho, ayenera kuika mtima wake wonse pankhaniyo.
Kunena za mlembi Ezara, mphunzitsi mu Israyeli, Baibulo limanena kuti “adaikiratu mtima wake kuchifuna chilamulo cha Yehova, ndi kuchichita, ndi kuphunzitsa m’Israyeli.” (Ezara 7:10) Ifenso tikamatero—kukonzekera, osati mfundo zokha komanso mitima yathu—tizilankhula kuchokera pansi pa mtima. Kulankhula choonadi kochokera pansi pa mtima koteroko kumathandiza omvera athu kukonda choonadi kuchokera pansi pa mtima.
Ganizirani za Omvera Anu. Mbali ina yofunika kwambiri pakulankhula mwaumoyo ndiyo kukhala wotsimikiza kuti omvera anu afunikiradi kumvetsa zimene mwawatengera. Izi zimatanthauza kuti pokonzekera nkhani yanu, musamangosanja mfundo zofunikira, komanso muyenera kupemphera kwa Yehova kuti akutsogolereni kufotokoza mfundozo m’njira yopindulitsa awo amene mukawalankhulire nkhaniyo. (Sal. 32:8; Mat. 7:7, 8) Pendani chifukwa chake omvera anu afunikira kumvera nkhaniyo, mmene ingawapindulire, ndi mmene mungaikambire m’njira imene angamvetse cholinga chake.
Pendani nkhaniyo kufikira mutapeza mfundo ina yokusangalatsani. Isachite kukhala mfundo yatsopano, koma kafotokozedwe kake kangakhale katsopano. Ngati mukonzekera mfundo imene ingathandizedi omvera anu kulimbikitsa ubwenzi wawo ndi Yehova, kuyamikira zogaŵira zake, kuthana ndi mavuto a moyo m’dziko lakaleli, kapena kukhala aluso mu utumiki wa kumunda, pamenepo muli ndi chifukwa chabwino chokambira nkhani yanu mwaumoyo.
Bwanji ngati mwapatsidwa mbali yokaŵerenga pamaso pa gulu? Kuti mukaŵerenge mwaumoyo, mufunikira kukonzekera zambiri osati kutchula chabe mawu molondola ndi kuwalumikiza bwino. Ŵerengani nkhaniyo ndi kuimvetsa. Ngati mukaŵerenga Baibulo, fufuzani za gawo limene mukaŵerengelo. Onetsetsani kuti mukumvetsa tanthauzo loyambirira. Onani mmene nkhaniyo ilili yopindulitsa inu ndi omvera anu, ndipo iŵerengeni ndi cholinga chothandiza omvera anu kuona phindu lake.
Kodi mukukonzekera utumiki wa kumunda? Pendaninso nkhani imene mukakambirane ndi anthu ndi malemba oti mukagwiritse ntchito. Lingaliraninso zimene zili m’maganizo mwa anthu. Kodi panyuzi pamveka nkhani zotani? Kodi ndi mavuto anji amene anthu akulimbana nawo? Pamene mwakonzekera kufotokozera anthu kuti Mawu a Mulungu amathandiza anthu pa mavuto amene amawadetsa nkhaŵa, mumakhala wofunitsitsa kuti muwafotokozere, ndipo kulankhula mwaumoyo kumangochitika mwachibadwa.
Lankhulani Mwaumoyo mwa Kusonyeza Mzimu wa Nkhaniyo. Kulankhula mwaumoyo kumaonekera bwino lomwe mwa kusonyeza mzimu wa nkhaniyo. Zimenezi ziyenera kuonekera pankhope panu. Lankhulani motsindika koma osati molamula.
Kusamala n’kofunika. Ena amakonda kulankhula mwamphamvu pa chilichonse. Anthu oterowo angafunikire kuwathandiza kuzindikira kuti ngati munthu alankhula mwamphamvu kwambiri kapena ngati aonetsa kukhudzika mtima mopitirira, omvera ake amalingalira za iye m’malo mwa uthenga wake. Komanso, aja amene amachita manyazi afunikira kuwalimbikitsa kuti azilankhula momasuka.
Kulankhula mwaumoyo kumayambukira. Ngati muyendera limodzi ndi omvera ndipo mukulankhula nkhani yanu mwaumoyo, omvera anunso udzawayambukira mzimuwo. Apolo anaonetsa umoyo m’kulankhula kwake, ndipo anatchedwa wodziŵa kulankhula. Ngati muli wotentha ndi mzimu wa Mulungu, kulankhula kwanu kwaumoyo kudzalimbikitsa omvera kuti achitepo kanthu.—Mac. 18:24, 25; Aroma 12:11.
Kulankhula Mwaumoyo Koyenerana ndi Nkhaniyo. Samalani kuti musalankhule mokweza kwambiri m’nkhani yonseyo moti omvera anu achite kutopa nanu. Mukatero, uphungu uliwonse umene mungawalimbikitse kuti aulabadire udzagwera pamakutu ogontha. Zimenezi zimaonetsa kufunika kokonza nkhani yosinthasintha makambidwe ake. Peŵani chizoloŵezi chokamba nkhani mwamphwayi. Ngati musankha mfundo zanu mosamala, mudzakhala ndi chidwi pamfundozo. Koma mfundo zina zimangofuna kuzikamba mwaumoyo kwambiri kuposa zina, ndipo zimenezi ziyenera kulukidwa mwaluso m’nkhani yonseyo.
Makamaka mfundo zazikulu muyenera kuzifotokoza mwaumoyo. Nkhani yanu iyenera kukhala ndi zikweza zimene muyenera kukwera pang’onopang’ono. Popeza kuti zikwezazo ndizo mfundo zazikulu za nkhani yanu, kaŵirikaŵiri ndizo zimakhala mfundo zolimbikitsira omvera anu. Mutakhutiritsa omvera anu, muyenera kuwalimbikitsa, kuwasonyeza mapindu a kugwiritsa ntchito zimene mwafotokoza. Kulankhula kwanu mwaumoyo kudzakuthandizani kuwafika pamtima omvera anu. Kulankhula mwaumoyo sikuyenera kukhala kokakamizira. Payenera kukhala chifukwa chake, ndipo nkhani yanu idzakupatsani chifukwacho.