Kodi Muli ndi Mzimu Wosafa?
KODI anthu amakhala ndi moyo kwina akamwalira? Funso limeneli lazunguza anthu kwa zaka zikwi zambiri. Kwa nthaŵi yaitali, anthu kulikonse aganiza za nkhaniyi ndipo akhala ndi zikhulupiriro zosiyanasiyana.
Kuzungulira dziko lonse lapansi, anthu ambiri amakhulupirira kuti “mzimu” umapulumuka munthu akamwalira. Kodi pali chinachake chimene chimachokadi mwa munthu ndi kupitiriza kukhala ndi moyo munthuyo akamwalira? Kodi mzimu wa munthu n’chiyani? Kodi n’chiyani chimachitikira mzimu tikamwalira? Mawu ouziridwa a Mulungu, Baibulo, amapereka mayankho olondola ndiponso okhutiritsa a mafunso ameneŵa.
Kodi Mzimu N’chiyani?
M’Baibulo, mawu otembenuzidwa “mzimu” kwenikweni amatanthauza “mpweya.” Koma amatanthauzanso zambiri osati kupuma chabe. Mwachitsanzo, wolemba Baibulo Yakobo anati: “Thupi lopanda mzimu lili lakufa.” (Yakobo 2:26) Choncho, mzimu ndi umene umachititsa thupi kukhala lamoyo.
Mphamvu yopatsa moyo imeneyi si mpweya umene timapuma umene umaloŵa m’mapapu ayi. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti munthu akaleka kupuma, maselo a thupi amakhalabe ali moyo kwa kanthaŵi—“kwa mphindi zingapo,” malinga ndi buku la maumboni lotchedwa The World Book Encyclopedia. N’chifukwa chake zimatheka kum’tsitsimutsa munthu, ndipo zimatheka kutenga ziwalo za thupi la munthu wina kuziika mwa wina. Koma pamene mphamvu ya moyo ichoka m’maselo a thupi, n’kosatheka kubwezeretsa moyo. Zikatere, mpweya uliwonse sungabwezere moyo ngakhale selo limodzi la thupi. Choncho, mzimu ndi mphanvu ya moyo yosaoneka imene imachititsa maselo a thupi kukhala ndi moyo. Ndipo zimene zimachirikiza mphamvu ya moyo imeneyi ndi kupuma.—Yobu 34:14, 15.
Kodi mzimu umenewu umagwira ntchito mwa anthu okha? Baibulo limatipatsanso yankho lolondola pa funso limeneli. Mfumu yanzeru Solomo inalemba kuti: “Ndani adziŵa mzimu wa ana a anthu wokwera kumwamba, ndi mzimu wa nyama wotsikira kunsi ku dziko?” (Mlaliki 3:21) Motero, onse, anthu ndi nyama ali ndi mzimu. Kodi zimenezi zikutheka bwanji?
Mzimu, kapena mphamvu ya moyo, tingaiyerekeze ndi mphamvu ya magetsi imene imaloŵa m’makina kapena chiwiya chilichonse chamagetsi. Mphamvu ya magetsi yosaonekayo ingagwire ntchito zosiyanasiyana, zikumadalira mtundu wa chiwiya chimene chikulandira mphamvuyo. Mwachitsanzo, mphamvu ya magetsi ingatenthetse chitofu, ingachititse kompyuta kutsegula mapulogalamu ake ndi kuŵerengera zinthu, ndiponso ingachititse wailesi yakanema kuonetsa zithunzi ndi kutulutsa mawu. Ngakhale zili choncho, mphamvu ya magetsiyo sikhala ndi maonekedwe a chiwiya chimene chimalandira mphamvuyo. Imangokhala mphamvu chabe basi. Mofananamo, mphamvu ya moyo ilibe mikhalidwe ya cholengedwa chimene mphamvuyo imachirikiza. Ilibe mikhalidwe yaumunthu, singaganize chilichonse. Onse, anthu ndi nyama “ali ndi mpweya [“mzimu,” NW] umodzi.” (Mlaliki 3:19) Choncho, munthu akamwalira, mzimu wake supitiriza kukhala ndi moyo kumalo ena monga cholengedwa chauzimu.
Nangano, kodi mkhalidwe wa akufa ndi wotani? Ndipo n’chiyani chimachitikira mzimu munthu akamwalira?
“Kufumbiko Udzabwerera”
Pamene munthu woyamba, Adamu, mwadala sanamvere lamulo la Mulungu, Yehova anati kwa iye: “M’thukuta la nkhope yako udzadya chakudya, kufikira kuti udzabwerera kunthaka: chifukwa kuti m’menemo unatengedwa: chifukwa kuti ndiwe fumbi, ndi kufumbiko udzabwerera.” (Genesis 3:19) Kodi Adamu anali kuti Yehova asanamulenge kuchokera kufumbi? Sanali kwina kulikonse! Iye kunalibeko. Chotero pamene Yehova Mulungu ananena kuti Adamu ‘adzabwerera kufumbi,’ iye anatanthauza kuti Adamu adzafa. Adamu sakanasamukira kumalo a mizimu. Pomwalira iye sakanakhalanso ndi moyo kwina kulikonse. Chilango chake chinali imfa—kusakhala wamoyo—osati kusamukira kumalo ena.—Aroma 6:23.
Bwanji za anthu ena amene anamwalira? Mlaliki 9:5, 10 amamveketsa bwino mkhalidwe wa akufa. Pamenepo timaŵerenga kuti: “Akufa sadziŵa kanthu bi . . . Mulibe ntchito ngakhale kulingalira ngakhale kudziŵa, ngakhale nzeru, kumanda.” Choncho, imfa ndiyo kusakhalako. Wamasalmo analemba kuti munthu akamwalira, “mpweya [“mzimu,”] wake uchoka, abwerera kumka kunthaka yake; tsiku lomwelo zotsimikiza mtima zake zitayika.”—Salmo 146:4.
Inde, akufa sazindikira kanthu, sachita china chilichonse. Sadziŵa kanthu. Iwo sangakuoneni, sangakumveni, ndiponso sangalankhule nanu. Sangakuthandizeni kapena kukuvulazani. Ndithudi, simufunikira kuopa akufa. Koma kodi ndi motani mmene mzimu ‘umachokera’ mwa munthu pomwalira?
Mzimu ‘Ubwerera kwa Mulungu’
Baibulo limanena kuti munthu akamwalira, ‘mzimu ubwerera kwa Mulungu amene anaupereka.’ (Mlaliki 12:7) Kodi limatanthauza kuti mzukwa umakwera ndi kudutsa m’mlengalenga mpaka kukafika kwa Mulungu? Kutalitali! Baibulo likamati ‘kubwerera’ silitanthauza kuchoka kwenikweni pamalo ena kupita kwina. Mwachitsanzo, Aisrayeli osakhulupirika anauzidwa kuti: “Bwererani kudza kwa Ine, ndipo Ine ndidzabwerera kwa inu, ati Yehova wa makamu.” (Malaki 3:7) ‘Kubwerera’ kwa Aisrayeli kwa Yehova kunatanthauza kusiya njira zawo zoipa ndi kuyambanso kutsatira njira zolungama za Mulungu. Ndipo ‘kubwerera’ kwa Yehova kwa Aisrayeli, kunatanthauza kuwakomeranso mtima anthu ake. Mbali zonse ziŵirizi, ‘kubwerera’ kunali kusintha maganizo, osati kuchoka kwenikweni pamalo ena kupita kwina.
Mofananamo, pamene mzimu ‘ubwerera’ kwa Mulungu sikuti umachokadi padziko lapansi kupita kumwamba ayi. Kumbukirani kuti mzimu ndi mphamvu ya moyo. Mphamvu imeneyo ikachoka mwa munthu, Mulungu yekha ndi amene angathe kuibwezeretsa mwa iye. Motero, mzimu ‘umabwerera kwa Mulungu’ m’lingaliro lakuti ngati munthuyo ati adzakhale ndi moyo m’tsogolo, zikudalira Mulungu basi.
Mwachitsanzo, talingalirani zimene Malemba amanena za imfa ya Yesu. Wolemba uthenga wabwino Luka, anati: “Yesu anafuula ndi mawu aakulu, anati, Atate, m’manja mwanu ndipereka mzimu wanga. Ndipo pakutero anapereka mzimu wake.” (Luka 23:46) Pamene mzimu wa Yesu unachoka, iye sananyamuke ulendo kupita kumwamba. Yesu sanauke kwa akufa mpaka tsiku lachitatu. Ndipo panapita masiku enanso 40 asanakwere kumwamba. (Machitidwe 1:3, 9) Komabe pomwalira, Yesu mwachidaliro anaika mzimu wake m’manja mwa Atate ake, ali ndi chikhulupiriro chonse kuti Yehova adzabwezeretsa moyo wake.
Ndithudi, Mulungu yekha ndi amene angabwezeretse moyo wa munthu. (Salmo 104:30) Zimenezitu zimatipatsa chiyembekezo chachikulu!
Chiyembekezo Chodalirika
Baibulo limanena kuti: “Ikudza nthaŵi, imene onse ali m’manda [a chikumbukiro, NW] adzamva mawu ake [a Yesu], nadzatulukira.” (Yohane 5:28, 29) Inde, Yesu Kristu analonjeza kuti onse amene ali m’chikumbumtima cha Yehova adzauka, kapena kuti adzakhalanso amoyo. M’malo mwa mauthenga achisoni akuti auje ndi auje amwalira, kudzakhala malipoti osangalatsa akuti auje ndi auje auka. Zidzakhala zosangalatsatu kulandira okondedwa athu ochokera kumanda!
Kodi mungakonde kudziŵa zambiri mmene mungapindulire ndi chiyembekezo chimene Mulungu watipatsachi? Talemberani ku adiresi ili m’musiyi kuti mulandire kabuku kakuti Mizimu ya Akufa—Kodi Ingakuthandizeni Kapena Kukuvulazani? Kodi Iyo Ilikodi?
Kusiyapo ngati kutasonyezedwa mwanjira ina, mawu onse a Baibulo ogwidwa muno ngochokera mu Revised Union Nyanja Version.