GAWO 3
“Ali Ndi Mtima Wanzeru”
Nzeru zenizeni ndi chimodzi mwa zinthu zamtengo wapatali zimene munthu ayenera kuyesetsa kuti akhale nazo. Nzeru zimenezi zimachokera kwa Yehova yekha. M’gawoli tikambirana mozama zokhudza nzeru zopanda malire za Yehova Mulungu, amene pofotokoza za iye, munthu wokhulupirika Yobu, ananena kuti: “Iye ali ndi mtima wanzeru.”—Yobu 9:4.