Mutu 12
Zimene Ubatizo Wanu Umatanthauza
M’CHAKA cha 29 C.E., Yesu anabatizidwa. Anamizidwa mu mtsinje wa Yordano ndi Yohane Mbatizi. Yehova mwiniyo anali kuonerera ndipo anavomereza zimenezo. (Mateyu 3:16, 17) Motero Yesu anapereka chitsanzo choti ophunzira ake onse atsatire. Patapita zaka zitatu ndi theka, Yesu anapatsa ophunzira ake malangizo aŵa: “Mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine Kumwamba ndi padziko lapansi. Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera.” (Mateyu 28:18, 19) Kodi munabatizidwa mogwirizana ndi zimene Yesu analamula palembali? Ngati simunabatizidwe, kodi mukukonzekera kutero?
2 Mulimonse mmene zilili kwa inu, aliyense amene akufuna kutumikira Yehova ndi kudzakhala m’dziko lake latsopano lolungama afunika kudziŵa bwino za ubatizo. Ena mwa mafunso ofunika kuyankhidwa ndi aŵa: Kodi ubatizo wa Akristu lerolino umatanthauza zimenenso ubatizo wa Yesu unatanthauza? Kodi kubatizidwa “m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera” kumatanthauzanji? Kodi kukwaniritsa zimene ubatizo wa m’madzi wa Akristu umaimira kumafuna chiyani?
Maubatizo Amene Yohane Anachita
3 Pafupifupi miyezi isanu ndi umodzi Yesu asanabatizidwe, Yohane Mbatizi anali kulalikira m’chipululu cha Yudeya kuti: “Tembenukani mitima; chifukwa Ufumu wa Kumwamba wayandikira.” (Mateyu 3:1, 2) Anthu anamva zimene Yohane ananena ndipo analabadira. Anaulula machimo awo, analapa, ndipo anapita kwa Yohane kuti awabatize mu mtsinje wa Yordano. Ubatizo umenewo unali wa Ayuda.—Luka 1:13-16; Machitidwe 13:23, 24.
4 Ayudawo anafunika kulapa mwamsanga. Paphiri la Sinai m’chaka cha 1513 B.C.E., makolo awo analoŵa m’pangano lokhudza mtundu wonsewo, limene anachita kulumbirirana ndi Yehova Mulungu. Koma chifukwa chakuti anachita machimo aakulu zedi, analephera kukwaniritsa mbali yawo ya panganolo, motero panganolo linawatsutsa. Pofika m’masiku a Yesu, zinthu sizinali bwino ayi. “Tsiku lalikulu ndi loopsa la Yehova” limene Malaki analosera linali pafupi. M’chaka cha 70 C.E., “tsiku” limenelo linafika pamene asilikali a Roma anawononga Yerusalemu ndi kachisi wake, ndiponso Ayuda oposa miliyoni imodzi. Yohane Mbatizi, munthu wachangu pa kulambira koona, anatumizidwa nthaŵi ya chiwonongeko chimenecho isanafike kuti ‘akakonzeretu Ambuye anthu okonzeka.’ Iwo anafunika kulapa machimo awo amene anachimwira pangano la Chilamulo cha Mose ndi kukhala okonzeka kulandira Mwana wa Mulungu, Yesu, amene Yehova anali kuwatumizira.—Malaki 4:4-6; Luka 1:17; Machitidwe 19:4.
5 Mwa anthu amene anapita kukabatizidwa kwa Yohane panali Yesu mwiniyo. Koma n’chifukwa chiyani? Podziŵa kuti Yesu analibe machimo oti aulule, Yohane anati: “Ndiyenera ine kubatizidwa ndi Inu, ndipo Inu mudza kwa ine kodi?” Koma ubatizo wa Yesu unali woti uimire zosiyana ndi zimenezo. Choncho Yesu anayankha kuti: “Balola tsopano: pakuti kuyenera ife kukwaniritsa chilungamo chonse motero.” (Mateyu 3:13-15) Chifukwa chakuti Yesu analibe machimo, ubatizo wake sunaimire kulapa machimo; ndiponso iye sanafunike kudzipatulira kwa Mulungu, popeza mtundu wake unali kale wodzipatulira kwa Yehova. M’malo mwake, ubatizo wake pamene anali ndi zaka 30 zakubadwa unali wapadera. Unaimira zoti iye anali kudzipereka kwa Atate wake wa kumwamba kuti achite chifuniro Chake chinanso.
6 Chifuniro cha Mulungu pa Kristu Yesu chinali kuchita ntchito yokhudza Ufumu. (Luka 8:1) Komanso chinali kupereka nsembe moyo wake wangwiro waumunthu kukhala dipo ndiponso maziko a pangano latsopano. (Mateyu 20:28; 26:26-28; Ahebri 10:5-10) Yesu sanaone mwachibwanabwana zimene ubatizo wake wa m’madzi unaimira. Sanalole maganizo ake kukopeka ndi zinthu zina. Mpaka pamene moyo wake padziko lapansi unatha, anachitabe chifuniro cha Mulungu, ndipo kulalikira za Ufumu wa Mulungu ndiyo inali ntchito yake yaikulu.—Yohane 4:34.
Ubatizo wa M’madzi wa Ophunzira Achikristu
7 Ophunzira oyambirira a Yesu anabatizidwa m’madzi ndi Yohane kenako anawalozera kwa Yesu monga anthu amene anali kuyembekezera kudzakhala mu Ufumu wa kumwamba. (Yohane 3:25-30) Molangizidwa ndi Yesu, ophunzira ameneŵanso anabatiza anthu, ndipo ubatizowu unali kuimira zomwenso ubatizo wa Yohane unaimira. (Yohane 4:1, 2) Komabe, kuyambira pa Pentekoste wa m’chaka cha 33 C.E., anayamba kukwaniritsa ntchito imene anapatsidwa yobatiza “m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera.” (Mateyu 28:19) Kupenda tanthauzo la zimenezi kukupindulitsani kwambiri.
8 Kodi kubatizidwa “m’dzina la Atate” kumatanthauzanji? Kumatanthauza kuzindikira dzina lake, udindo wake, ulamuliro wake, cholinga chake, ndi malamulo ake. Taonani zophatikizidwamo zake. (1) Ponena za dzina lake, Salmo 83:18 limati: “Inu nokha, dzina lanu ndinu Yehova, ndinu Wam’mwambamwamba padziko lonse lapansi.” (2) Pa za udindo wake, Yeremiya 10:10 amati: “Yehova ndiye Mulungu woona.” (3) Tikuuzidwa za ulamuliro wake pa Chivumbulutso 4:11 kuti: “Muyenera inu, Ambuye wathu, ndi Mulungu wathu, kulandira ulemerero ndi ulemu ndi mphamvu; chifukwa mudalenga zonse, ndipo mwa chifuniro chanu zinakhala, nizinalengedwa.” (4) Tiyeneranso kuzindikira kuti Yehova ndiye Wopatsa Moyo, ndipo ali ndi cholinga chotipulumutsa ku uchimo ndi imfa: “Chipulumutso n’cha Yehova.” (Salmo 3:8; 36:9) (5) Tifunika kuvomereza kuti Yehova ndiye Wopereka Malamulo Wamkulu: “Yehova ndiye woweruza wathu, Yehova ndiye wotipatsa malamulo, Yehova ndiye mfumu yathu.” (Yesaya 33:22) Chifukwa chakuti ali ndi maudindo onsewo, tikulimbikitsidwa kuti: “Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse.”—Mateyu 22:37.
9 Kodi kubatizidwa “m’dzina . . . la Mwana” kumatanthauza chiyani? Kumatanthauza kuzindikira dzina la Yesu Kristu, udindo wake, ndiponso ulamuliro wake. Dzina lake, lakuti Yesu, limatanthauza kuti “Yehova Ndiye Chipulumutso.” Udindo umene ali nawo anakhala nawo chifukwa chakuti iye ndiye Mwana wobadwa yekha wa Mulungu, woyamba kulengedwa mwa zonse zimene Mulungu analenga. (Mateyu 16:16; Akolose 1:15, 16) Yohane 3:16 amatiuza za Mwana ameneyu kuti: “Mulungu anakonda dziko lapansi [la anthu owomboleka] kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.” Chifukwa chakuti Yesu anafa ali wokhulupirika, Mulungu anamuukitsa kwa akufa ndi kumupatsa ulamuliro watsopano. Malinga n’kunena kwa mtumwi Paulo, Mulungu ‘anamukweza Yesu’ pa malo apamwamba zedi m’chilengedwe chonse; ndi wachiŵiri kwa Yehova. N’chifukwa chake ‘m’dzina la Yesu, bondo lililonse liyenera kupinda . . . ndi malilime onse ayenera kuvomera kuti Yesu Kristu ali Ambuye, kuchitira ulemu Mulungu Atate.’ (Afilipi 2:9-11) Izi zikutanthauza kumvera malamulo a Yesu, omwe amachokera kwa Yehova mwiniyo.—Yohane 15:10.
10 Kodi kubatizidwa “m’dzina . . . la Mzimu Woyera” kumatanthauzanji? Kumatanthauza kuzindikira ntchito ya mzimu woyera. Ndipo kodi mzimu woyera n’chiyani? Mzimu woyera ndi mphamvu yogwira ntchito ya Yehova; ndiyo mphamvu yomwe amakwaniritsira zolinga zake. Yesu anauza omutsatira kuti: “Ine ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani inu Nkhoswe ina, kuti akhale ndi inu ku nthaŵi yonse, ndiye Mzimu wa choonadi.” (Yohane 14:16, 17) Kodi ukanawathandiza kuchitanji? Yesu anawauzanso kuti: “Mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera atadza pa inu: ndipo mudzakhala mboni zanga m’Yerusalemu, ndi m’Yudeya lonse, ndi m’Samariya, ndi kufikira malekezero ake a dziko.” (Machitidwe 1:8) Pogwiritsa ntchito mzimu woyera, Yehova anauziranso zimene zinalembedwa m’Baibulo: “Kale lonse chinenero sichinadza ndi chifuniro cha munthu; koma anthu a Mulungu, ogwidwa ndi Mzimu Woyera, analankhula.” (2 Petro 1:21) Motero tikamaphunzira Baibulo ndiye kuti tikuzindikira ntchito ya mzimu woyera. Njira ina imene timasonyezera kuti tikuzindikira mzimu woyera ndiyo kupempha Yehova kutithandiza kuti tikhale ndi “chipatso cha Mzimu,” chomwe ndi “chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, chiletso.”—Agalatiya 5:22, 23.
11 Amene anali oyamba kubatizidwa mogwirizana ndi malangizo a Yesu anali Ayuda ndiponso anthu oloŵa Chiyuda, kuyambira m’chaka cha 33 C.E. Pasanapite nthaŵi yaitali, Asamariya anapatsidwa mwayi wokhala ophunzira achikristu. Ndiyeno, m’chaka cha 36 C.E., nawonso Akunja osadulidwa anayamba kuitanidwa. Asanabatizidwe, Asamariya ndi Akunja anafunika kudzipatulira kwa Yehova mwa kufuna kwawo kuti am’tumikire pokhala ophunzira a Mwana wake. Mpaka pano ubatizo wa m’madzi wa Akristu ukuimirabe zimenezi. Kumiza m’madzi munthu yense wathunthu ndi chizindikiro choyenera chakuti munthuyo anadzipatulira mwa kufuna kwake, chifukwa ubatizo uli ngati kuikidwa m’manda. Kuviikidwa kwanu m’madzi amene mukubatizidwamo kumaimira kuti mwafa mwasiya moyo wanu wakale. Kuvuulidwa m’madzimo kumaimira kuti mwakhalanso wamoyo kuti muchite chifuniro cha Mulungu. Onse amene amakhala Akristu oona amalandira “ubatizo umodzi” umenewu. Pamene akubatizidwa iwo amakhala Mboni zachikristu za Yehova, atumiki oikidwa ndi Mulungu.—Aefeso 4:5; 2 Akorinto 6:3, 4.
12 Ubatizo woterowo m’maso mwa Mulungu uli ndi mphamvu yaikulu yopulumutsa. Mwachitsanzo, atanena kuti Nowa anamanga chingalawa mmene iye ndi banja lake anapulumukiramo Chigumula, mtumwi Petro analemba kuti: ‘Chimenenso chifaniziro chake chikupulumutsani tsopano, ndicho ubatizo, kosati kutaya kwa litsiro lake la thupi, komatu funso lake la chikumbumtima chokoma kwa Mulungu, mwa kuuka kwa Yesu Kristu.’ (1 Petro 3:21) Chingalawa chinapereka umboni wosatsutsika wakuti Nowa anagwira mokhulupirika ntchito imene Mulungu anamupatsa. Ntchito yokonza chingalawa itatha, “dziko lapansi la masiku aja, pomizika ndi madzi, lidawonongeka.” (2 Petro 3:6) Koma Nowa ndi banja lake, “amoyo asanu ndi atatu, anapulumutsidwa mwa madzi.”—1 Petro 3:20.
13 Lerolino, amene amadzipatulira kwa Yehova chifukwa chokhulupirira Kristu woukitsidwayo, amabatizidwa posonyeza kudzipatulira kumeneko. Akatero amayamba kuchita chifuniro cha Mulungu m’masiku athu ano ndipo amapulumutsidwa ku dziko loipali. (Agalatiya 1:3, 4) Iwo saloŵeranso kokawonongeka limodzi ndi dziko lamakono loipali. Amapulumutsidwa ku zimenezi ndipo Mulungu amawapatsa chikumbumtima chabwino. Mtumwi Yohane amatsimikizira atumiki a Mulungu kuti: “Dziko lapansi lipita, ndi chilakolako chake; koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthaŵi yonse.”—1 Yohane 2:17.
Kukwaniritsa Maudindo Athu
14 Ndi kulakwa kuganiza kuti munthu akangobatizidwa ndiye kuti basi chipulumutso wachipeza. Ubatizo umakhala waphindu pokhapokha ngati munthu wadzipatuliradi zenizeni kwa Yehova kudzera mwa Yesu Kristu ndiyeno n’kumachita chifuniro cha Mulungu; n’kukhala wokhulupirika mpaka mapeto. “Iye wakulimbika chilimbikire kufikira kuchimaliziro, yemweyo adzapulumuka.”—Mateyu 24:13.
15 Chifuniro cha Mulungu pa Yesu chinaphatikizapo mmene iye anagwiritsira ntchito moyo wake monga munthu. Moyowo unali woti uphedwe kukhala nsembe. Kwa ifeyo, matupi athu afunika kuperekedwa kwa Mulungu, ndipo ife tifunika kukhala ndi moyo wodzimana mwa kuchita chifuniro cha Mulungu. (Aroma 12:1, 2) Ndithudi, sitingachite chifuniro cha Mulungu ngati tichitira dala ngakhale pang’ono pokha zinthu zimene dzikoli limachita kapena ngati chifukwa cha dyera tiika moyo wathu pa kuchita zinthu zathuzathu zimene timakonda kwinaku n’kumatumikira Mulungu mwamwambo chabe. (1 Petro 4:1-3; 1 Yohane 2:15, 16) Myuda wina atafunsa zimene ayenera kuchita kuti akapeze moyo wosatha, Yesu anavomereza kuti makhalidwe abwino ndi ofunika. Kenako anatchula chinthu china chofunika kwambiri: kukhala wophunzira wachikristu, wotsatira Yesu. Ichi ndicho chachikulu pamoyo. Sichingakhale chachiŵiri, choyamba n’kukhala kufunafuna zinthu zofunika pamoyo ayi.—Mateyu 19:16-21.
16 Titsindikenso kunena kuti chifuniro cha Mulungu pa Yesu chinali kugwira ntchito yofunika kwambiri yokhudza Ufumu wa Mulungu. Yesu mwiniyo anadzozedwa kukhala Mfumu. Koma pamene anali padziko lapansi, analinso wachangu popereka umboni wokhudza Ufumuwo. Tifunika kugwira ntchito yofananayo yochitira umboni, ndipo tili ndi zifukwa zonse zogwirira ntchitoyi ndi mtima wonse. Mwa kuchita zimenezi, timasonyeza kuti timayamikira ulamuliro wa Yehova ndiponso kuti timakonda anthu anzathu. (Mateyu 22:36-40) Timaonetsanso kuti ndife ogwirizana ndi olambira anzathu padziko lonse lapansi, omwe onse ndi olengeza Ufumu. Mogwirizana padziko lonse, timalimbikirabe kuti tikapeze moyo wosatha padziko lapansi pano mu Ufumuwo.
Bwerezani Zimene Mwakambirana
• Kodi pali kufanana kotani ndiponso kusiyana kotani pakati pa ubatizo wa Yesu ndi ubatizo wa m’madzi lerolino?
• Kodi kubatizidwa “m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera” kumatanthauzanji?
• Kodi chimafunika n’chiyani kuti munthu athe kukwaniritsa maudindo amene ubatizo wa Akristu wa m’madzi umam’patsa?
[Mafunso]
1. N’chifukwa chiyani aliyense payekha ayenera kufunitsitsa kubatizidwa m’madzi?
2. Pankhani yokhudza ubatizo, kodi ndi mafunso ati ofunika kuyankhidwa?
3. Kodi Yohane anali kubatiza ndani?
4. N’chifukwa chiyani Ayuda m’zaka 100 zoyambirira anafunika kulapa mwamsanga?
5. (a) Pamene Yesu anapita kukabatizidwa, n’chifukwa chiyani Yohane anakayikira kuti amubatize? (b) Kodi ubatizo wa Yesu unaimira chiyani?
6. Kodi Yesu anaikirapo mtima motani pa kuchita chifuniro cha Mulungu?
7. Kuchokera pa Pentekoste wa m’chaka cha 33 C.E., kodi Akristu anauzidwa kuchitanji pankhani ya ubatizo?
8. Kodi kubatizidwa “m’dzina la Atate” kumatanthauzanji?
9. Kodi kubatizidwa “m’dzina . . . la Mwana” kumatanthauza chiyani?
10. Kodi kubatizidwa “m’dzina . . . la Mzimu Woyera” kumatanthauzanji?
11. (a) Kodi tanthauzo lenileni la ubatizo m’masiku athu ano n’lotani? (b) Kodi ndi motani mmene ubatizo ulili ngati kufa ndi kuukitsidwa?
12. Kodi ubatizo wa m’madzi wa Akristu umafanana ndi chiyani, ndipo zimafanana motani?
13. Kodi Mkristu amapulumutsidwa ku chiyani mwa ubatizo wa m’madzi?
14. N’chifukwa chiyani munthu akangobatizidwa sindiye kuti chipulumutso wachipeza?
15. (a) Kodi lerolino chifuniro cha Mulungu pa Akristu obatizidwa n’chiyani? (b) Kodi kukhala wophunzira wachikristu tiyenera kukuona motani?
16. (a) Kodi Akristu onse ali ndi udindo wotani wokhudza Ufumu? (b) Monga mmene masamba 116 ndi 117 akusonyezera, kodi njira zina zabwino ndi ziti zogwirira ntchito ya Ufumu? (c) Kodi tikamachita nawo ndi mtima wonse ntchito yochitira umboni timasonyezanji?
[Zithunzi pamasamba 116, 117]
NJIRA ZINA ZOLENGEZERA UFUMU
Khomo ndi khomo
Kwa achibale
Kwa anzathu a kuntchito
Kwa anzathu a kusukulu
M’misewu
Maulendo obwereza kwa anthu achidwi
Maphunziro a Baibulo a panyumba