Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wt mutu 13 tsamba 120-127
  • Khamu Lalikulu Loimirira ku Mpando Wachifumu wa Yehova

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Khamu Lalikulu Loimirira ku Mpando Wachifumu wa Yehova
  • Lambirani Mulungu Woona Yekha
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kuzindikira Khamu Lalikulu
  • Afunika Kukhala Oyenerera
  • Phindu Limene Akupeza Panopa
  • Khamu Lalikulu Pamaso pa Mpando Wachifumu wa Yehova
    Ogwirizana m’Kulambiridwa kwa Mulungu Yekha Wowona
  • Khamu Lalikulu Kwambiri
    Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso
  • “Ndinaona Khamu Lalikulu la Anthu”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2019
  • Khamu Lalikulu Lopereka Utumiki Wopatulika
    Nsanja ya Olonda—1995
Onani Zambiri
Lambirani Mulungu Woona Yekha
wt mutu 13 tsamba 120-127

Mutu 13

Khamu Lalikulu Loimirira ku Mpando Wachifumu wa Yehova

NKHANI yaikulu pamoyo wa atumiki okhulupirika a Mulungu kuyambira pa Abele mpaka pa Yohane Mbatizi inali kuchita chifuniro cha Mulungu. Komabe onsewo anamwalira, ndipo akuyembekeza kudzaukitsidwa m’dziko lapansi latsopano la Mulungu. A gulu la 144,000, omwe adzalamulira limodzi ndi Kristu mu Ufumu wakumwamba wa Mulungu, nawonso ayenera kufa kaye asanalandire mphoto yawo. Komatu Chivumbulutso 7:9 chimaonetsa kuti m’masiku otsiriza ano padzakhala “khamu lalikulu” la anthu a mitundu yonse amene sadzafa koma adzayembekezera kukhala ndi moyo kosatha padziko lapansi. Kodi ndinu mmodzi wa iwo?

Kuzindikira Khamu Lalikulu

2 Mu 1923, atumiki a Yehova anazindikira kuti “nkhosa” zotchulidwa m’fanizo la Yesu pa Mateyu 25:31-46 ndiponso “nkhosa zina” zomwe Yesu anazitchula pa Yohane 10:16 ndi anthu amene adzapatsidwa mwayi wokhala ndi moyo kosatha padziko lapansi. Mu 1931 anazindikiranso kuti anthu olembedwa chizindikiro pa mphumi pawo otchulidwa pa Ezekieli 9:1-11, ndi omwewo amene adzakhala ndi moyo padziko lapansi. Ndiyeno mu 1935 atumiki a Yehova anazindikira kuti khamu lalikulu lili m’gulu la nkhosa zina zimene Yesu ananena. Lerolino, a khamu lalikulu loyanjidwa limeneli alipo mamiliyoni ambiri.

3 Pa Chivumbulutso 7:9, khamu lalikulu silikusonyezedwa kuti lili kumwamba. Silifunika kuchita kukhala kumwamba kuti ‘liimirire ku mpando wachifumu.’ Kungoti Mulungu amaliona pamene lilipo. (Salmo 11:4) Tingaone kuti khamu lalikulu, lomwe “palibe munthu anakhoza kuliŵerenga,” si gulu lakumwamba mwa kuyerekeza chiŵerengero chake chomwe sichinatchulidwe ndi zimene zalembedwa pa Chivumbulutso 7:4-8 ndiponso pa Chivumbulutso 14:1-4. Pamalemba ameneŵa akunena kuti anthu otengedwa padziko lapansi kupita kumwamba alipo 144,000.

4 Chivumbulutso 7:14 chimanena za a khamu lalikulu kuti: “Iwo ndiwo akutuluka m’chisautso chachikulu.” Akupulumuka masautso aakulu zedi mwa onse amene anthu anakumanapo nawo. (Mateyu 24:21) Poyamika Mulungu ndi Kristu chifukwa chowapulumutsa, zolengedwa zonse zokhulupirika za kumwamba zidzagwirizana nawo kunena kuti: “Amen: Thamo ndi ulemerero, ndi nzeru, ndi chiyamiko, ndi ulemu, ndi chilimbiko, ndi mphamvu zikhale kwa Mulungu wathu kufikira nthaŵi za nthaŵi. Amen.”—Chivumbulutso 7:11, 12.

Afunika Kukhala Oyenerera

5 Khamu lalikulu likutetezedwa pa chisautso chachikulu mogwirizana ndi miyezo yolungama ya Yehova. Baibulo limafotokoza bwino makhalidwe amene anthu odzapulumukawo ayenera kukhala nawo. Motero n’zotheka kuti anthu okonda chilungamo achitepo kanthu tsopanoli kuti adzapulumuke. Kodi iwo afunika kuchitanji?

6 Nkhosa ndi zofatsa komanso zimagonjera. Chotero pamene Yesu ananena kuti iye ali ndi nkhosa zina zimene si za gulu lakumwamba, anatanthauza anthu amene makamaka adzagonjera ziphunzitso zake osati kungofuna chabe kukhala ndi moyo wosatha padziko lapansi. Iye anati: “Nkhosa zanga zimva mawu anga, ndipo Ine ndizizindikira, ndipo zinditsata Ine.” (Yohane 10:16, 27) Aŵa ndi anthu amene amamvadi zonena za Yesu n’kumazichita, ndipo amakhala ophunzira ake.

7 Kodi ndi makhalidwe ena ati amene aliyense wa otsatira Yesu ameneŵa afunika kukhala nawo? Mawu a Mulungu amati: “Muvule, kunena za makhalidwe anu oyamba, munthu wakale, . . . nimuvale munthu watsopano, amene analengedwa monga mwa Mulungu, m’chilungamo, ndi m’chiyero cha choonadi.” (Aefeso 4:22-24) Amakhala ndi makhalidwe amene amalimbitsa umodzi pakati pa atumiki a Mulungu, makhalidwe monga “chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, chiletso.”—Agalatiya 5:22, 23.

8 A khamu lalikulu amathandiza anthu ochepa omwe adzapita kumwamba amene akutsogolera ntchito yolalikira. (Mateyu 24:14; 25:40) A nkhosa zina amachita zimenezi, ngakhale kuti amadziŵa kuti ena adzawatsutsa chifukwa pamene masiku otsiriza ano anali kuyamba, Kristu Yesu ndi angelo ake anachotsa Satana ndi ziwanda zake kumwamba. Izi zinadzetsa “tsoka [pa] mtunda . . . chifukwa Mdyerekezi watsikira [kumeneko], wokhala nawo udani waukulu, podziŵa kuti kam’tsalira kanthaŵi.” (Chivumbulutso 12:7-12) Motero Satana akumka natsutsa kwambiri atumiki a Mulungu pamene mapeto a dzikoli akuyandikira.

9 Ngakhale pali chizunzo choopsa, ntchito yolalikira ikumkabe patsogolo. Pakutha kwa nkhondo yoyamba ya padziko lonse, panali anthu olalikira Ufumu zikwi zoŵerengeka chabe, koma tsopano afika m’mamiliyoni, chifukwa Yehova analonjeza kuti: “Palibe chida chosulidwira iwe chidzapindula.” (Yesaya 54:17) Ngakhale membala wa khoti lalikulu la Ayuda anavomereza kuti palibe angalepheretse ntchito ya Mulungu. Anauza Afarisi za ophunzira a m’zaka 100 zoyambirirazo kuti: ‘Muwalole akhale; pakuti ngati uphungu umenewu kapena ntchito iyi ichokera kwa anthu, idzapasuka; koma ngati ichokera kwa Mulungu simungathe kuwapasula; kuti kapena mungapezeke otsutsana ndi Mulungu.’—Machitidwe 5:38, 39.

10 A khamu lalikulu akusonyezedwa kuti akulembedwa chizindikiro chakuti adzapulumuke. (Ezekieli 9:4-6) “Chizindikiro” chimenecho ndi umboni wakuti iwo ndi odzipatulira kwa Yehova, anabatizidwa n’kukhala ophunzira a Yesu, ndipo akuyesetsa kukhala ndi umunthu wonga wa Kristu. Amamvera ‘mawu ochokera Kumwamba’ amene amanena za ufumu wadziko lonse wa chipembedzo chonyenga wa Satana kuti: “Tulukani mmenemo, anthu anga; kuti mungayanjane ndi machimo ake, ndi kuti mungalandireko ya miliri yake.”—Chivumbulutso 18:1-5.

11 Ndiponso, Yesu anauza otsatira ake kuti: “Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.” (Yohane 13:35) Komatu, anthu a zipembedzo za dzikoli amaphana okhaokha pankhondo, ndipo nthaŵi zambiri chifukwa chake chimangokhala chakuti winayo ndi nzika ya dziko lina. Mawu a Mulungu amati: “Mmenemo aoneka ana a Mulungu, ndi ana a Mdyerekezi: yense wosachita chilungamo sali wochokera mwa Mulungu; ndi iye wosakonda mbale wake. . . . Tikondane wina ndi mnzake: osati monga Kaini anali wochokera mwa woipayo, namupha mbale wake.”—1 Yohane 3:10-12.

12 Yesu anati: “Mtengo wabwino uliwonse upatsa zipatso zokoma; koma mtengo wamphuchi upatsa zipatso zoipa. Sungathe mtengo wabwino kupatsa zipatso zoipa, kapena mtengo wamphuchi kupatsa zipatso zokoma. Mtengo uliwonse wosapatsa chipatso chokoma, audula, nautaya kumoto. Inde chomwecho pa zipatso zawo mudzawazindikira iwo.” (Mateyu 7:17-20) Zipatso zimene zipembedzo za dzikoli zimatulutsa zimaonetsa kuti izo ndi ‘mitengo’ yamphuchi, yomwe posachedwapa Yehova aiwononge pa chisautso chachikulu.—Chivumbulutso 17:16.

13 Chivumbulutso 7:9-15 chikutchula zinthu zimene zidzapulumutsa khamu lalikulu. Akuwaonetsa onse pamodzi “akuimirira ku mpando wachifumu” wa Yehova, kutanthauza kuti amakweza ulamuliro wake wachilengedwe chonse. Iwo “anatsuka zovala zawo, naziyeretsa m’mwazi wa Mwanawankhosa,” kuonetsa kuti amazindikira kuti nsembe ya Yesu ndiyo imateteza machimo. (Yohane 1:29) Anadzipatulira kwa Mulungu ndipo anasonyeza zimenezi mwa kumizidwa m’madzi. Motero kwa Mulungu iwo ali oyera, ndipo zimenezi zikusonyezedwa ndi zovala zawo zoyera, komanso iwo ‘amamutumikira Iye usana ndi usiku.’ Kodi pali zimene mungachite kuti moyo wanu ugwirizane kwambiri ndi zimene zalongosoledwazi?

Phindu Limene Akupeza Panopa

14 Muyenera kuti mwaona phindu lapadera limene anthu omwe akutumikira Yehova amalipeza ngakhale panopa. Mwachitsanzo, mutaphunzira za zolinga zolungama za Yehova, munazindikira kuti tsogolo lanu lingakhale labwino kwambiri. Inu tsopano muli ndi cholinga chenicheni pamoyo wanu, chomwe ndi kutumikira Mulungu woona mosangalala uku mukuyembekezera moyo wosatha m’paradaiso padziko lapansi. Inde, Mfumu Yesu Kristu ‘adzatsogolera [khamu lalikulu] ku akasupe a madzi a moyo.’—Chivumbulutso 7:17.

15 A khamu lalikulu amapindula kwambiri ndi chikondi, kugwirizana, ndiponso kumvana kumene kuli pakati pa atumiki a Yehova padziko lonse lapansi. Popeza kuti tonse timadya chakudya chauzimu chimodzimodzi, tonse timamvera malamulo amodzimodzi komanso mfundo za makhalidwe abwino zimodzimodzi zimene zili m’Mawu a Mulungu. N’chifukwa chake sitili ogaŵikana ndi mfundo zandale kapena za dziko lina lililonse. Ndiponso, timakhalabe ndi makhalidwe apamwamba potsata miyezo imene Mulungu amaikira anthu ake. (1 Akorinto 6:9-11) Motero m’malo moti pakati pawo pakhale mikangano, kusagwirizana, ndi makhalidwe ena oipa ofala m’dzikoli, tingati anthu a Yehova ali m’paradaiso wauzimu. Taonani mmene akufotokozera zimenezi pa Yesaya 65:13, 14.

16 Sikuti anthu otumikira Yehova ali angwiro. Nawonso amakhudzidwa ndi mavuto a m’dzikoli, monga kukumana ndi zothetsa nzeru kapenanso nkhondo. Iwonso amadwala, amavutika, ndiponso amafa. Koma amakhulupirira kuti m’dziko latsopano Mulungu “adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa.”—Chivumbulutso 21:4.

17 Ngakhale moyo wanu utatayika panopa chifukwa cha ukalamba, matenda, ngozi, kapena kuzunzidwa, Yehova adzakuukitsani m’Paradaiso. (Machitidwe 24:15) Pamenepo mudzapitiriza kusangalala ndi phwando lauzimu mu Ulamuliro wa Kristu wa Zaka 1,000. Chikondi chanu pa Mulungu chidzakula poona zolinga zake zikukwaniritsidwa kufika pa ulemerero wake. Ndipo madalitso amene Yehova adzabweretsa pamoyo wanu panthaŵiyo, adzawonjezera kwambiri chikondi chanu pa iye. (Yesaya 25:6-9) Koma ndiyetu atumiki a Mulungu ali ndi tsogolo losangalatsa kwambiri!

Bwerezani Zimene Mwakambirana

• Kodi Baibulo limagwirizanitsa khamu lalikulu ndi chochitika chapadera chiti?

• Ngati tikufunadi kudzakhala mmodzi wa anthu oyanjidwa ndi Mulungu a khamu lalikululo, kodi n’chiyani chimene tiyenera kuchita panopa?

• Kodi madalitso amene a khamu lalikulu akupeza panopa ndiponso amene adzakhala nawo m’dziko latsopano la Mulungu ndi ofunika kwa inuyo?

[Mafunso]

1. (a) Kodi atumiki a Mulungu akale anafunikira ayambe atani kuti alandire mphoto yawo, nanga a 144,000 nawonso afunikira kutani? (b) Koma kodi a “khamu lalikulu” amene ali ndi moyo panopa zidzawathera bwanji?

2. Kodi atumiki a Yehova anayamba azindikira chiyani kuti khamu lalikulu la pa Chivumbulutso 7:9 lidziŵike bwinobwino?

3. N’chifukwa chiyani mawu akuti “akuimirira ku mpando wachifumu” sakunena za gulu lakumwamba?

4. (a) Kodi “chisautso chachikulu” chimene khamu lalikulu likupulumukamo n’chiyani? (b) Monga momwe Chivumbulutso 7:11, 12 chikunenera, kodi ndani akuona khamu lalikulu n’kulambira nalo limodzi?

5. Kodi tingadziŵe bwanji zimene zimafunika kuti munthu akhale wa khamu lalikulu?

6. N’chifukwa chiyani kuyerekeza khamu lalikulu ndi nkhosa kuli koyenera?

7. Kodi otsatira Yesu afunika kukhala ndi makhalidwe ati?

8. Kodi a khamu lalikulu adzakumana n’chiyani pamene akuthandiza otsalira?

9. Kodi atumiki a Mulungu ntchito yolalikira uthenga wabwino akuikhoza motani, nanga n’chifukwa chiyani?

10. (a) Kodi “chizindikiro” chimene a khamu lalikulu ali nacho chimatanthauza chiyani? (b) Kodi atumiki a Mulungu amamvera motani ‘mawu ochokera Kumwamba’?

11. Kodi n’chiyani chofunika kwambiri chimene a khamu lalikulu amachita poonetsa kuti ndi atumiki a Yehova?

12. Kodi ‘mitengo’ yachipembedzo imene ikubereka zipatso zoipa Yehova adzaitani pa chisautso chachikulu?

13. Kodi a khamu lalikulu amasonyeza motani kuti onse pamodzi “akuimirira ku mpando wachifumu” wa Yehova?

14. Kodi phindu lina lapadera limene atumiki a Yehova amapeza ngakhale panopa ndi lotani?

15. Kodi Mboni za Yehova zikupindula motani mwa kutsatira mfundo za m’Baibulo zokhudza ndale ndiponso makhalidwe abwino?

16. Ngakhale kuti m’dzikoli muli mavuto, kodi a khamu lalikulu amayembekezera chiyani?

17. Mosasamala kanthu chimene chingatichitikire panopa, kodi ndi tsogolo losangalatsa lotani limene anthu olambira Mulungu woona adzakhale nalo?

[Chithunzi patsamba 123]

Anthu mamiliyoni ambiri a khamu lalikulu amalambira Mulungu woona mogwirizana

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena