Mutu 18
“Siali a Dziko Lapansi”
USIKU woti aphedwa maŵa lake, Yesu anapempherera ophunzira ake. Podziŵa kuti Satana adzawavutitsa kwambiri, Yesu anati kwa Atate wake: “Sindipempha kuti muwachotse iwo m’dziko lapansi, koma kuti muwasunge iwo kuletsa woipayo. Siali a dziko lapansi monga Ine sindili wa dziko lapansi.” (Yohane 17:15, 16) N’chifukwa chiyani kusiyana ndi dziko n’kofunika kwambiri? Chifukwa chakuti Satana ndiye wolamulira wa dzikoli. Ndiye Akristu sangafune kukhala mbali ya dziko lomwe iye akulilamulira.—Luka 4:5-8; Yohane 14:30; 1 Yohane 5:19.
2 Yesu sanali wa dziko lapansi ndipo zimenezi sizinatanthauze kuti sanali kukonda ena. Iyetu anachiritsa odwala, anaukitsa akufa, ndipo anaphunzitsa anthu za Ufumu wa Mulungu. Anapereka ngakhale moyo wake m’malo mwa anthu. Koma iye sanakonde maganizo ndi ntchito zoipa za anthu amene anali ndi mzimu wa dziko la Satana. Motero iye anachenjeza za kukhala ndi zilakolako zoipa, kukonda chuma, ndi kufuna kutchuka. (Mateyu 5:27, 28; 6:19-21; Luka 20:46, 47) N’zosadabwitsatu kuti Yesu anapeŵanso ndale za dzikoli. Ngakhale kuti iye anali Myuda, sanaloŵerere mikangano yandale ya Aroma ndi Ayuda.
“Ufumu Wanga Suli wa Dziko Lino Lapansi”
3 Talingalirani zimene zinachitika pamene atsogoleri achipembedzo a Ayuda anagwira Yesu n’kupita naye kwa Pontiyo Pilato, yemwe anali kazembe wa Roma. Zoona zake zinali zakuti atsogoleriwo anakhumudwa chifukwa Yesu anaulula chinyengo chawo. Pofuna kusonkhezera kazembeyo kuti alange Yesu, iwo ananeneza Yesuyo kuti: “Tinapeza munthu uyu ali kupandutsa anthu a mtundu wathu, ndi kuwaletsa kupereka msonkho kwa Kaisara, nadzinenera kuti Iye yekha ndiye Kristu mfumu.” (Luka 23:2) N’zoonekeratu kuti ili linali bodza, chifukwa pamene anthu anafuna kulonga Yesu ufumu chaka chapitacho, iye anakana. (Yohane 6:15) Anadziŵa kuti adzakhala Mfumu yakumwamba m’tsogolo. (Luka 19:11, 12) Ndiponso, Yehova, osati anthu, ndiye anali kudzamulonga ufumuwo.
4 Patangotsala masiku atatu kuti Yesu am’gwire, Afarisi anayesa kulankhulitsa Yesu mawu oti amupezerepo mlandu pankhani yokhoma msonkho. Koma iye anati: “Tandionetsani Ine rupiya latheka [ndalama ya Aroma]. Chithunzithunzi ndi cholemba chake n’chayani?” Iwo atanena kuti “cha Kaisara,” iye anati: “Chifukwa chake perekani kwa Kaisara zake za Kaisara, ndi kwa Mulungu zake za Mulungu.”—Luka 20:20-25.
5 Ndithudi, Yesu sanaphunzitse kuti anthu azipandukira boma. Pamene asilikali ndi anthu ena anakagwira Yesu, Petro anasolola lupanga nakantha nalo mmodzi wa anthuwo, n’kumudula khutu. Koma Yesu anati: “Tabweza lupanga lako m’chimakemo, pakuti onse akugwira lupanga adzawonongeka ndi lupanga.” (Mateyu 26:51, 52) M’maŵa mwake Yesu anafotokozera Pilato chifukwa chake anachita zimenezi. Anati: “Ufumu wanga suli wa dziko lino lapansi; ufumu wanga ukadakhala wa dziko lino lapansi, anyamata anga akadalimbika nkhondo, kuti ndisaperekedwe kwa Ayuda.” (Yohane 18:36) Pilato anavomereza kuti panalibe “chifukwa cha zinthu zimene” anamunenera Yesu. Koma pokakamizidwa ndi gulu la anthulo, Pilato anapereka Yesu kuti akapachikidwe.—Luka 23:13-15; Yohane 19:12-16.
Ophunzira Atsatira Zimene Yesu Anawaphunzitsa
6 Motero ophunzira a Yesu anazindikira zimene zinafunika kuti munthu asakhale wa dziko lapansi. Munthu anafunika kupeŵa mzimu wa dziko ndi ntchito zake, zomwe zinaphatikizapo zosangalatsa zachiwawa ndi zolaula zimene zinali kuchitika m’mabwalo a zamaseŵera a ku Roma. Ophunzira a Yesu ankawanena kuti anali kudana ndi anthu chifukwa chopeŵa zimenezi. Komatu iwo sanali kuda anthu anzawo ayi; anali kugwira ntchito zolimba pothandiza ena kuti apindule ndi makonzedwe a Mulungu a chipulumutso.
7 Otsatira Yesu anali kuzunzidwa monga iye anazunzidwira, ndipo anali kuwazunza nthaŵi zambiri ndi akuluakulu a boma omwe anauzidwa zonama. Komatu, cha m’ma 56 C.E., mtumwi Paulo analembera kalata Akristu a ku Roma ndipo anawalimbikitsa ‘kumvera maulamuliro aakulu [olamulira andale]; pakuti palibe ulamuliro wina koma wochokera kwa Mulungu.’ Sikuti Yehova ndiye amakhazikitsa maboma a dzikoli, koma akuwalola kukhalapo mpaka pamene Ufumu wake wokhawo ndiwo udzalamulira dziko lonse lapansi. Choncho Paulo anali ndi chifukwa chabwino polangiza Akristu kuti azilemekeza akuluakulu a boma ndi kumakhoma misonkho.—Aroma 13:1-7; Tito 3:1, 2.
8 Komabe, kumvera olamulira andale kuli ndi malire ake. Pamene malamulo a Yehova sakugwirizana ndi malamulo a anthu, amene amatumikira Yehova afunika kumvera malamulo Ake. Taonani zimene limanena buku lotchedwa kuti On the Road to Civilization—A World History zokhudza Akristu oyambirira: “Akristu anali kukana kugwira nawo ntchito zina zimene nzika za Roma zimagwira. Akristuwo . . . anali kuona kuti akaloŵa usilikali, ndiye kuti ataya chikhulupiriro chawo. Sanali kukhala ndi maudindo andale. Sanali kulambira mfumu.” Pamene khoti lalikulu la Ayuda ‘linalamula’ ophunzira a Yesu kuti aleke kulalikira, iwo anayankha kuti: “Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu.”—Machitidwe 5:27-29.
9 Pa zandale ndi pa nkhondo, ophunzirawo sanaloŵererepo m’pang’ono pomwe. Mu 66 C.E., Ayuda a ku Yudeya anapandukira Kaisara. Posapita nthaŵi asilikali a Roma anazinga Yerusalemu. Kodi n’chiyani chimene anachita Akristu omwe anali mu mzindawo? Anakumbukira malangizo a Yesu oti akachokemo mu mzindawo. Pamene Aromawo anayamba ausiya kaye mzindawo, Akristu anathaŵa nawoloka mtsinje wa Yordano n’kupita kumapiri a Pella. (Luka 21:20-24) Kusaloŵererapo kwawo kunakhala chitsanzo kwa Akristu okhulupirika a m’tsogolo.
Akristu Saloŵerera Ndale M’masiku Otsiriza Ano
10 Kodi mbiri ya zimene zakhala zikuchitika imasonyeza kuti pali gulu lililonse masiku otsiriza ano limene potsanzira Akristu oyambirira silinaloŵerere m’pang’ono pomwe m’zadzikoli? Inde, Mboni za Yehova zatero. M’nthaŵi yonseyi iwo akhala akulalikira kuti Ufumu wa Mulungu ndiwo wokha umene udzabweretsa mtendere wosatha, chitukuko chenicheni, ndiponso chimwemwe chosatha kwa anthu okonda chilungamo. (Mateyu 24:14) Koma pa mikangano imene mayiko amachita, iwo sanaloŵererepo ngakhale pang’ono.
11 Mosiyana kwambiri ndi Mbonizo, atsogoleri azipembedzo za dzikoli akhala akuloŵerera kwambiri m’ndale. M’mayiko ena, amalimbikira kuchita kampeni kuti anthu ena asankhidwe paudindo kapena kuti asasankhidwe. Mpaka atsogoleri achipembedzo ena ali ndithu ndi maudindo andale. Ena akakamiza anthu andale kuti avomereze zimene atsogoleri achipembedzowo akufuna. Koma Mboni za Yehova sizichita nawo ndale. Ndiponso siziletsa anthu ena iwo akamafuna kuloŵa chipani cha ndale, kufuna udindo wandale, kapena kuponya mavoti pachisankho. Yesu ananena kuti ophunzira ake sadzakhala a dziko lapansi, choncho Mboni za Yehova sizichita nawo ndale.
12 Monga ananeneratu Yesu, mayiko akhala akumenyana nthaŵi ndi nthaŵi. Ngakhalenso magulu a m’dziko limodzimodzi athirana nkhondo. (Mateyu 24:3, 6, 7) Nthaŵi zambiri, atsogoleri achipembedzo akhalira kumbuyo dziko lina kapena gulu lina motsutsa linalo, ndipo alimbikitsa anthu awo kuchita zomwezo. Ndiye chachitika n’chiyani? Anthu a chipembedzo chimodzimodzi aphana pankhondo chabe chifukwa chakuti wina ndi wadziko lina kapena ndi wafuko lina. Izi n’zosemphana ndi zimene Mulungu amafuna.—1 Yohane 3:10-12; 4:8, 20.
13 Komabe, Mboni za Yehova sizinaloŵerere ngakhale pang’ono pa mikangano yonse. Nsanja ya Olonda yachingelezi ya November 1, 1939, inati: “Onse amene ali kumbali ya Ambuye sadzaloŵererapo mayiko akamamenyana.” A Mboni za Yehova m’mayiko onse ndiponso nthaŵi ina iliyonse nkhaniyi amaionabe moteremu. Salola kuti ndale ndi nkhondo za dzikoli zomwe zimagaŵanitsa anthu zipasule ubale wawo wa padziko lonse. Iwo ‘akusula malupanga awo kukhala zolimira, ndi nthungo zawo kukhala anangwape.’ Popeza saloŵererapo, iwo saphunziranso nkhondo.—Yesaya 2:3, 4; 2 Akorinto 10:3, 4.
14 Kodi china chachitika n’chiyani chifukwa cha kusaloŵerera kwawo m’zadzikoli? Yesu anati: “Popeza simuli a dziko lapansi, . . . [ilo] likudani inu.” (Yohane 15:19) Mboni za Yehova zambiri zaikidwa m’ndende chifukwa chotumikira Mulungu. Ena azunzidwa, ngakhalenso kuphedwa kumene, mofanana ndi mmene zinalili kwa Akristu oyambirira. Izi zili choncho chifukwa Satana, “mulungu wa nthaŵi ino ya pansi pano,” amatsutsa atumiki a Yehova omwe siali a dziko lapansi.—2 Akorinto 4:4; Chivumbulutso 12:12.
15 Atumiki a Yehova ndi osangalala kuti siali a dziko lapansi, chifukwa mitundu yake yonse ikupita ku Armagedo komwe idzathera. (Danieli 2:44; Chivumbulutso 16:14, 16; 19:11-21) Popeza kuti ifeyo timapeŵa dzikoli, tidzapeŵanso tsoka limenelo. Pokhala anthu ogwirizana padziko lonse, ndife okhulupirika ku Ufumu wakumwamba wa Mulungu. N’zoona kuti mwa kusakhala a dziko lapansi, dzikoli limatinyoza ndi kutizunza. Komabe zimenezi zidzatha posachedwapa, chifukwa dziko loipa lilipoli lomwe Satana akulilamulira lidzawonongedwa ndipo silidzakhalakonso. Koma amene akutumikira Yehova adzakhala ndi moyo kosatha m’dziko lake latsopano lolungama lolamulidwa ndi Ufumu wa Mulungu.—2 Petro 3:10-13; 1 Yohane 2:15-17.
Bwerezani Zimene Mwakambirana
• Kodi Yesu anasonyeza motani zimene zimafunika kuti munthu ‘asakhale wa dziko lapansi’?
• Kodi Akristu oyambirira anali ndi maganizo otani okhudzana ndi (a) mzimu wa dziko, (b) olamulira a dzikoli, ndi (c) kukhoma misonkho?
• Kodi a Mboni za Yehova masiku ano apereka umboni m’njira zotani kuti monga Akristu saloŵerera m’ndale?
[Mafunso]
1. (a) Yesu asanafe, kodi n’chiyani chimene anapempherera ophunzira ake? (b) N’chifukwa chiyani ‘kusakhala a dziko lapansi’ n’kofunika kwambiri?
2. Kodi Yesu sanali wa dziko lapansi m’njira zotani?
3. (a) Kodi atsogoleri achipembedzo a Ayuda ananeneza Yesu zotani kwa Pilato, ndipo n’chifukwa chiyani? (b) N’chiyani chikusonyeza kuti Yesu sanafune kukhala mfumu yaumunthu?
4. Kodi maganizo a Yesu anali otani pa kukhoma misonkho?
5. (a) Kodi Yesu anaphunzitsa ophunzira ake chiyani panthaŵi imene anali kum’gwira? (b) Kodi Yesu anati chiyani pofotokoza chifukwa cha zimene anachita? (c) Kodi mlanduwo unatha bwanji?
6. Kodi Akristu oyambirira anasonyeza motani kuti anapeŵa mzimu wa dziko koma kuti anali kukonda anthu?
7. (a) Kodi n’chiyani chimene chinachitikira ophunzira a Yesu oyambirira chifukwa chakuti sanali a dziko lapansi? (b) Kodi maganizo awo anali otani pa olamulira andale komanso pankhani yokhoma misonkho, nanga n’chifukwa chiyani?
8. (a) Kodi Akristu ayenera kumvera maulamuliro aakulu kufika mpaka pati? (b) Kodi Akristu oyambirira anatsatira motani chitsanzo cha Yesu?
9. (a) Kodi zomwe anachita Akristu a ku Yerusalemu m’chaka cha 66 C.E. anazichita chifukwa cha chiyani? (b) Kodi zimenezo zili chitsanzo chofunika kwambiri m’njira yotani?
10. (a) Kodi Mboni za Yehova zimatanganidwa ndi ntchito iti, ndipo n’chifukwa chiyani? (b) Kodi iwo saloŵerera pa chiyani?
11. (a) Kodi kusaloŵerera m’ndale kwa Mboni kukusiyana motani ndi zomwe amachita atsogoleri azipembedzo? (b) Kodi Mboni za Yehova sizitani anthu ena akamachita za ndale?
12. Kodi n’chiyani chachitika chifukwa chakuti zipembedzo za dzikoli zimaloŵerera m’ndale?
13. Kodi umboni umaonetsanji za kusaloŵerera m’ndale kwa Mboni za Yehova?
14. Kodi n’chiyani chachitikira a Mboni za Yehova chifukwa chokhala osiyana ndi dzikoli?
15. (a) Kodi mitundu yonse ikupita kuti, ndipo Mboni za Yehova zimayesetsa kupeŵa chiyani? (b) N’chifukwa chiyani kukhala wosiyana ndi dziko ili nkhani yofunika kwambiri?
[Chithunzi patsamba 165]
Yesu anafotokoza kuti iye limodzi ndi otsatira ake “siali a dziko lapansi”