Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ol gawo 8 tsamba 25-28
  • Siyani Chipembedzo Chonyenga; Tsatani Chipembedzo Choona

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Siyani Chipembedzo Chonyenga; Tsatani Chipembedzo Choona
  • Njira ya ku Moyo Wosatha—Kodi Mwaipeza?
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Masukani ku Chipembedzo Chonyenga
  • Onongani Zonse Zogwiritsidwa Ntchito pa Kulambira Konyenga
  • Gwirizanani ndi Anthu a Yehova
  • Njira Yoyenera Yolambirira Mulungu
    Zimene Baibulo Limaphunzitsa
  • Muzitumikira Yehova Osati Satana
    Kodi Mizimu ya Akufa Ilipodi?
  • Kulambira Kumene Mulungu Amavomereza
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Kanani Chipembedzo Chonyenga!
    Mungathe Kukhala Bwenzi la Mulungu!
Onani Zambiri
Njira ya ku Moyo Wosatha—Kodi Mwaipeza?
ol gawo 8 tsamba 25-28

CHIGAWO 8

Siyani Chipembedzo Chonyenga; Tsatani Chipembedzo Choona

1. Pankhani ya kulambira, kodi anthu afunika kusankha chiyani masiku ano?

YESU anati: “Iye wosakhala pamodzi ndi Ine akana Ine.” (Mateyu 12:30) Tili kumbali ya Yehova kapena ya Satana. Anthu ambiri amaganiza kuti akutumikira Mulungu movomerezeka, koma Baibulo limati Satana ali “wonyenga wa dziko lonse.” (Chivumbulutso 12:9) Anthu mamiliyoni amakhulupirira kuti akulambira Mulungu, koma kwenikweni akutumikira Satana Mdyerekezi! Anthu masiku ano afunika kusankhapo chimodzi: Kutumikira Yehova, “Mulungu wa choonadi,” kapena Satana, “atate wake wa bodza.”​—Salmo 31:5; Yohane 8:44.

Masukani ku Chipembedzo Chonyenga

2. Kodi ina mwa njira zimene Satana amayesera kuletsa anthu kulambira Yehova ndi iti?

2 Mukasankha kutumikira Yehova, ndiye kuti mwasankha bwino chifukwa Mulungu adzakuyanjani. Koma Satana sasangalala ena akamatumikira Mulungu; amawadzetsera mavuto. Ina mwa njira zimene iye amachitira zimenezi ndi kusonkhezera ena, ngakhale mabwenzi athu ndi achibale, kutinyodola kapena kutikaniza. Yesu anachenjeza kuti: “Apabanja ake a munthu adzakhala adani ake.”​—Mateyu 10:36.

3. Ngati achibale anu kapena mabwenzi akuletsani kulambira Mulungu, kodi inu mudzatani?

3 Kodi zimenezi zikakuchitikirani mudzatani? Anthu ambiri akudziŵa kuti kalambiridwe kawo n’kolakwa, koma akuzengereza kusiya. Amaganiza kuti akatero ndiye kuti ali osakhulupirika kwa achibale awo. Kodi zimenezo ndi nzeru? Inuyo mukanadziŵa kuti achibale anu anali kumwa mankhwala osokoneza bongo, kodi simukanawachenjeza kuti mankhwalawo adzawapweteka? Simukanagwirizana nawo n’kumamwera limodzi mankhwalawo, mukanatero ngati?

4. Nthaŵi imene Yoswa anali moyo anawauza chiyani Aisrayeli pankhani ya kulambira?

4 Yoswa analimbikitsa Aisrayeli kusiya kapembedzedwe kolakwika ndi miyambo ya makolo awo. Anati: “Tsopano, opani Yehova ndi kum’tumikira ndi mtima wangwiro ndi woona; nimuchotse milungu imene makolo anu anaitumikira tsidya lija la mtsinje, ndi m’Aigupto; nimutumikire Yehova.” (Yoswa 24:14) Yoswa anali wokhulupirika kwa Mulungu, ndipo Yehova anam’dalitsa. Tikakhala okhulupirika kwa Yehova, adzatidalitsa ifenso.​—2 Samueli 22:26.

Ziphunzitso za Chipembedzo—Zoona ndi Zonama

  • Wa Mboni za Yehova akuphunzitsa Baibulo mayi wina komanso ana ake

    Utatu: Zipembedzo zambiri zimaphunzitsa kuti Mulungu ali Utatu. Zimati “Atate ndi Mulungu, Mwana [Yesu] ndi Mulungunso, ndi Mzimu Woyera ndi Mulungu, koma kuti kulibe Milungu itatu koma Mulungu mmodzi basi.”

    Baibulo silitchula n’komwe liwu la “Utatu,” ndipo siliphunzitsa kuti Yehova ali atatu mwa mmodzi. Yehova yekha ndiye Mulungu. Lemba la 1 Akorinto 8:6 limati: “Kwa ife kuli Mulungu mmodzi, Atate.” Yehova ndiye Wamkulukulu. Yesu si Mulungu ayi koma ndi “Mwana wa Mulungu.” (1 Yohane 4:15) Momwemonso, mzimu woyera si Mulungu. Ndipotu mzimu woyerawo si munthu. Ndiyo mphamvu ya Mulungu yogwira ntchito.​—Machitidwe 1:8; Aefeso 5:18.

  • Mzimu: Zipembedzo zambiri zimaphunzitsa kuti mzimu ndi chinachake chimene chili mwa munthu ndipo sichifa. Baibulo limaphunzitsa kuti mzimu ndiwo mphamvu ya moyo imene imathandiza thupi kukhala lamoyo koma sutha kuchita kalikonse popanda thupi. Ndiponso, limaphunzitsa kuti akufa satha kuchita kalikonse.​—Mlaliki 9:10; Yakobo 2:26.

  • Moto wa Helo: Zipembedzo zonyenga zimaphunzitsa kuti mizimu ya anthu oipa imazunzika kosatha kuhelo. Baibulo limati akufa “sadziŵa kanthu bi.” (Mlaliki 9:5) Limaphunzitsanso kuti “Mulungu ndiye chikondi.” (1 Yohane 4:8) Yehova, Mulungu wachikondi, sangazunze ena ndi moto.

Bokosi: Kodi Baibulo limaphunzitsa chiyani za Utatu, mzimu, ndi moto wa helo?

Onongani Zonse Zogwiritsidwa Ntchito pa Kulambira Konyenga

Mayi akuotcha zinthu zake za matsenga

5. N’chifukwa chiyani tifunika kuwononga zinthu zonse zamatsenga?

5 Kumasuka ku chipembedzo chonyenga kumafunanso kuti tiwononge zinthu zonse zamatsenga zimene tingakhale nazo, monga zithumwa, mphinjiri, mphete zamatsenga ndi makoza, ndi zinthu zina ngati zimenezi. Kuchita zimenezi n’kofunika kwambiri chifukwa kumasonyeza kuti tikudalira Yehova ndi mtima wathu wonse.

6. Kodi Akristu oyambirira anatani nawo mabuku awo a zamatsenga?

6 Nazi zimene Akristu ena oyambirira anachita atasankha kutsata chipembedzo choona. Baibulo limati: “Ambiri a iwo akuchita zamatsenga anasonkhanitsa mabuku awo, nawatentha pamaso pa onse.”​—Machitidwe 19:19.

7. Tingachite chiyani ngati ziŵanda zikutivutitsa?

7 Ena amene amayamba kutumikira Yehova ndipo m’mbuyomu akhala akuchita ufiti kapena zamatsenga, ziŵanda zingawavutitse. Zikakuchitikirani zimenezo, itanani Yehova mofuula popemphera, kutchula dzina lakelo ndipo iye adzakuthandizani.​—Miyambo 18:10; Yakobo 4:7.

8. Kodi Akristu amaona motani mafano ndi zithunzithunzi zogwiritsidwa ntchito pa kulambira konyenga?

8 Amene akufuna kutumikira Yehova asasunge kapena kugwiritsa ntchito fano kapena chithunzithunzi chilichonse chogwiritsidwa ntchito pa kulambira konyenga. Akristu oona ‘amayenda mwa chikhulupiriro si mwa chionekedwe.’ (2 Akorinto 5:7) Amalemekeza lamulo la Mulungu loletsa kugwiritsa ntchito fano lamtundu uliwonse polambira.​—Eksodo 20:4, 5.

Gwirizanani ndi Anthu a Yehova

Mayi ndi mwana wake akukonza chakudya

9. Kodi Baibulo limapereka langizo lotani ngati munthu akufuna kukhala wanzeru?

9 Baibulo limati: “Ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru.” (Miyambo 13:20) Ngati tikufuna kukhala anzeru, tifunika kuyenda, kapena kugwirizana, ndi Mboni za Yehova. Anthu ameneŵa ndiwo akuyenda panjira ya kumoyo.​—Mateyu 7:14.

10. Kodi Mboni za Yehova zingakuthandizeni bwanji kutumikira Mulungu?

10 Mboni zimasamaladi anthu. Cholinga cha ntchito yawo ndi kuthandiza anthu oona mtima kumvetsa mfundo za choonadi cha m’Baibulo chopatsa moyo wosatha. Mboni zingakuthandizeni mwa kuphunzira nanu Baibulo kwaulere. Zidzakuthandizani kuyankha mafunso anu ndi kukusonyezani mmene mungagwiritsire ntchito nzeru ya m’Baibulo pamoyo wanu.​—Yohane 17:3.

11. Kodi misonkhano yachikristu idzakuthandizani bwanji?

11 Kumisonkhano yawo, imene nthaŵi zambiri imachitikira ku Nyumba ya Ufumu, mudzaphunzira zambiri ponena za njira za Yehova. Chikhumbo chanu chotsata chipembedzo choona chidzalimba. Ndipo mudzaphunziranso mmene mungathandizire ena kudziŵa mfundo za choonadi cha m’Baibulo.​—Ahebri 10:24, 25.

Anthu akuchita misonkhano pa Nyumba ya Ufumu

12. Kodi pemphero lingakuthandizeni bwanji kutumikira Mulungu?

12 Popitiriza kuphunzira zambiri za chifuniro ndi cholinga cha Yehova, mosakayika mudzamvetsa ndi kuyamikira kwambiri njira zake zachikondi. Ndiponso, chikhumbo chanu chochita zokondweretsa Mulungu ndi kupeŵa zosam’kondweretsa chidzakula. Kumbukirani kuti mutha kulankhula ndi Yehova m’pemphero kum’pempha kuti akuthandizeni kuchita chabwino ndi kupeŵa choipa.​—1 Akorinto 6:9, 10; Afilipi 4:6.

Banja likuwerenga Baibulo

Kodi mufunika kuchita chiyani kuti mutsate kulambira koona?

13. Kodi mufunika kuchita chiyani kuti mukondweretse mtima wa Yehova?

13 M’kupita kwa nthaŵi, pamene mukukula mwauzimu, simudzalephera kuona kuti mufunika kukhala Mboni yodzipatulira ndi yobatizidwa ya Yehova. Mwa kugwirizana ndi anthu ake, mudzakondweretsa mtima wa Yehovayo. (Miyambo 27:11) Mudzakhala pakati pa anthu osangalala amene Mulungu amati za iwo: “Ndidzakhalitsa mwa iwo, ndipo ndidzayendayenda mwa iwo; ndipo ndidzakhala Mulungu wawo, ndi iwo adzakhala anthu anga.”​—2 Akorinto 6:16.

Ndinamasuka ku Ziŵanda

A Josephine Ikezu ali ndi ana awo

Tsiku lina usiku ndili mtulo pabedi ndi amuna anga, ndinamva liwu likuitana katatu kutchula dzina langa. Kenako ndinangoona kuti denga lang’ambika, ndipo chinthu choyaka moto chonga mpira n’kundigwera pamimba. Amuna angawo sakanatha kuona zonsezi. Koma kuyambira pamenepo, ndinayamba kumva kutentha kwambiri miyezi ingapo.

Patapita miyezi isanu ndi umodzi, ndinamvanso liwu lija likundiitana. Pomwepo, nyumba yonse inaoneka ngati ili m’madzi akuya. M’madzimo munatuluka chinsato chachikulu ndipo chinazerenga dzanja langa. Ndinayesa kulikutumula dzanja langalo kuti chichoke koma sizinathandize. Mantha anandigwira. Ndiye madzi aja ndi njoka ija zinazimiririka, ndipo ndinaponyedwa pansi mwamphamvu. Ndinakhala chikomokere maola angapo ndithu. Ndiyeno liwu lija linandiuza kupitanso ku kachisi wa mizimu m’mudzimo. Kachisi ameneyu anali wochiritsira. Nditaufunsa mzimuwo dzina lake, unandiuza dzina lotanthauza “mwinichuma koma wopanda mwana.” Unalonjeza kuti udzandilemeretsa mwa kundipatsa mphamvu zochiritsa.

Choncho anthu odwala ochokera kumadera apafupi ndi akutali anali kubwera. Asanafike panyumba panga, anali kuoneka m’kalirole wanga wapadera. Ndiye munthu amati akafika, ndinali kumenyetsa chikhato changa ndi chake, ndipo ndikangotero, basi matenda ake aja kapena vuto lake komanso mankhwala ake anali kudziŵika kwa ine. Mzimuwo unali kundiuzanso ndalama zoti anthu alipire.

Chifukwa chokhoza kuchiritsa, ndinali kulandira ndalama ndi mphatso zambirimbiri. Ndinakhaladi “mwinichuma,” komanso ndinadzamvetsa tanthauzo la mawu akuti “wopanda mwana.” Ndimati ndikakhala ndi mwana, mkulu wake anali kumwalira. Zimenezi zinandisautsa kwambiri. Zaka zonse 12 zimene ndinatumikira mzimuwu, ana anga asanu ndi mmodzi anamwalira.

Ndinayamba kupemphera kwa Mulungu kuti andithandize. Ndinapemphera ndi mtima wanga wonse. Tsiku lina Mboni za Yehova zinagogoda pakhomo panga. Ngakhale kuti ndinali kuzipitikitsa, tsikulo ndinaganiza zomvetsera. Pokambirana, ndinaphunzira kuti ndinali kutumikira chiŵanda! Nditamva zimenezo, ndinasankha kusiya kukhulupirira mizimu.

Koma nditauuza zimenezi mzimu uja, unandichenjeza kuti sindiyenera kuchita zimenezo. Ndiye ine ndinauuza kuti: “Zipitani, chatha chibwenzi.”

Kenako ndinatentha zonse zimene ndinali kugwiritsa ntchito poombeza ula. Ndinaphunzira Baibulo ndi Mboni, ndinakhala mtumiki wa Yehova, ndipo ndinabatizidwa mu 1973. Tsopano ndili ndi ana asanu athanzi. Amuna anganso anakhala Mboni yobatizidwa.​—Wasimba nkhaniyi ndi Josephine Ikezu.

Bokosi: Kodi mayi wina anachita chiyani kuti amasuke ku ziŵanda?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena